Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/15 tsamba 5-7
  • Kodi Mafano Angakuyandikitseni Pafupi ndi Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mafano Angakuyandikitseni Pafupi ndi Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ouma Mtengo, Okongola, Koma Opanda Pake
  • Lingaliro la Akatolika
  • Amanyengedwa ndi Mdani
  • Kuyandikira Pafupi ndi Mulungu
  • Zifaniziro
    Galamukani!—2014
  • Kulemekeza Mafano—Nkhani Yamkangano
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Mafano Polambira Mulungu?
    Galamukani!—2008
  • Kawonedwe Kachikristu ka Mafano
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/15 tsamba 5-7

Kodi Mafano Angakuyandikitseni Pafupi ndi Mulungu?

MAFANO ambirimbiri a ku Igupto, Babulo, ndi Girisi ngodzala m’nyumba zowonetsera zinthu zamakedzana lerolino. Zifanizo zimene panthaŵi ina zinalemekezedwa mwachangu tsopano zikuwonetsedwa monga ntchito wamba za luso lamakedzana. Mphamvu zawo zinali zongoyerekezeredwa ndi amene ankazilambira. Pamene anthu amene ankazilemekeza anazimiririka potsirizira pake, mphamvu yongoyerekezeredwa ya mafanowo inazimiririka nayonso. Mafanowo anazindikiridwa kukhala opanda mphamvu​—zimene analidi nthaŵi zonse​—zinthu zopanda moyo zamtengo, mwala, kapena chitsulo.

Bwanji ponena za mafano amene amalemekezedwa ndi kulambiridwa ndi anthu lerolino? Kodi mafano ameneŵa ali amphamvupo pa mafano amakedzana a ku Igupto, Babulo, ndi Girisi? Kodi akhaladi othandiza m’kuyandikiritsa anthu kwa Mulungu?

Pamene mbadwo uliwonse upita, anthu awonekera kukhala akutalikiratalikirana ndi Mulungu. Ndipo kodi nchiyani chimene mafano onse m’dziko angachitepo pankhaniyo? Ngati sasamalidwa, amakutidwa ndi fumbi ndipo pomalizira pake nkuchita dzimbiri kapena kuwola. Sangadzisamalire okha, osati ngakhale kuchitira anthu kalikonse. Komabe, chofunika kwambiri nchakuti, kodi Baibulo limanenanji pankhaniyi?

Ouma Mtengo, Okongola, Koma Opanda Pake

Mosadabwitsa, Baibulo limavumbula mafano kukhala opanda pake ndi osakhoza mpang’ono pomwe kuthandiza owalambira kuyandikira kwa Mulungu. Ngakhale kuti mafano achipembedzo ali kaŵirikaŵiri ouma mtengo ndi okongola, Baibulo limasonyeza kupanda pake kwawo pamene limati: ‘Mafano awo ndiwo a siliva ndi golidi, ntchito za manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nawo, koma osapenya; makutu ali nawo, koma osamva; mphuno ali nazo, koma osanunkhiza; manja ali nawo, koma osagwira; mapazi ali nawo, koma osayenda; kapena sanena pammero pawo. Adzafanana nawo iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira.’​—Salmo 115:4-8.

Baibulo silimangovumbula mafano kukhala achabe koma limalankhulanso motsutsa zifanizo ndi ozilambira kuti: ‘Mafanoŵa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawawope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lake losemasema; pakuti fanizo lake loyenga liri bodza, mulibe mpweya mwa iwo. Ndiwo chabe, ndiwo chiphamaso.’​—Yeremiya 10:5, 14, 15.

Lingaliro la Akatolika

Nzowona, ambiri amene amagwadira mafano achipembedzo, kupemphera kwa iwo, kuwayatsira makandulo, ndi kuwapsompsona samadziyesa iwo eni kukhala opembedza kapena olambira mafano. Mwachitsanzo, Akatolika amanena kuti amalemekeza mafano a Kristu ndi Mariya, osati chifukwa chakuti mafanowo ndimulungu winawake, koma chifukwa cha amene mafanowo amaimira. The World Book Encyclopedia imanena kuti “m’Tchalitchi cha Roma Katolika, mafano amalemekezedwa monga zizindikiro za anthu omwe amaimira.” Atsogoleri achipembedzo Achikatolika aphunzitsa kuti kulemekeza fano nkolondola malinga ngati kulemekezako nkocheperapo ndi kuja koperekedwa kwa Mulungu mwiniyo.

Mfundo njakuti mafano ameneŵa akulemekezedwa. Ngakhale bukhu lanazonse la New Catholic Encyclopedia limavomereza kuti kulemekeza koteroko kuli “mchitidwe wakulambira.” Komabe, Yesu Kristu anatsutsa kugwiritsira ntchito mafano monga zothandiza kumfikira Mulungu pamene anati: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” (Yohane 14:6) Pamenepa, nzosadabwitsa kuti Akristu a m’zaka zana loyamba ananyansa kugwiritsiridwa ntchito kwa mafano polambira.

Komabe, zipembedzo za Chikristu Chadziko lerolino zili ndi mafano ambiri kuposa zipembedzo zina zonse. Inde, mosasamala kanthu ndi umboni wonse wa m’mbiri ndi wa Malemba wosonyeza kupusa kwa kupereka ulemu ku fano, odzitcha Akristu padziko lonse amapitirizabe kugwada ndi kupemphera pamaso pa mafano pofunafuna Mulungu mowona mtima. Chifukwa ninji?

Amanyengedwa ndi Mdani

Mneneri Yesaya ananena kuti olambira mafano a m’nthaŵi yake analephera kuwona kupusa kwa machitidwe awo chifukwa maso awo ‘anapakidwa thope, kuti sangawone, ndi m’mitima mwawo kuti sangadziŵitse.’ (Yesaya 44:18) Kodi ndani amene ayenera kuti ndiye akusonkhezera anthu motero? Bungwe lotsutsa mafano la mu 754 C.E. linanena kuti kulemekeza mafano kunayamba ndi Satana pofuna kuti anyenge anthu kuŵachotsa kwa Mulungu wowona. Kodi chigamulo chimenechi chinali cholondola?

Inde, pakuti chimagwirizana ndi Baibulo lowuziridwa, limene linanena zaka mazana ambiri kalelo kuti mdani wamkulu wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, ‘wachititsa khungu maganizo’ a anthu kotero kuti chowonadi ‘chisawaŵalire.’ (2 Akorinto 4:4) Choncho polemekeza fano, munthuyo amatumikiradi zofuna za ziŵanda mmalo moyandikira kwa Mulungu.​—1 Akorinto 10:19, 20.

Kuyandikira Pafupi ndi Mulungu

Mafano sangatithandize kuyandikira pafupi ndi Mulungu. Mlengi Wamkuluyo, Yehova Mulungu, amanyansidwa ndi kulemekeza mafano. (Deuteronomo 7:25) “Yehova ndiye Mulungu wansanje.” (Nahumu 1:2) Iye amati: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 42:8) Mofananamo, Baibulo limachenjeza kuti amene amapereka ulemu ku mafano ‘sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.’​—Agalatiya 5:19-21.

Komabe, Yehova alinso Mulungu wachifundo ndi wokhululukira. Baibulo limasimba za amene anasiya mafano awo natembenukira kwa Mulungu ndipo anayesedwa olungama ataleka machitamachita awo akupembedza mafano. (1 Akorinto 6:9-11; 1 Atesalonika 1:9) Analabadira mawu a Yesu akuti: ‘Mulungu ndiye Mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.’​—Yohane 4:24.

Phunziro lakhama la Baibulo limawonetsa kuti kuyandikira pafupi ndi Mulungu sikovuta. (Machitidwe 17:26-28) Iye ali ndi umunthu wabwino, wachikondi, ndi wofikirika, ndipo amatiitanira kwa iye natiyembekezera kukulitsa naye unansi wathithithi.​—Yesaya 1:18.

Mboni za Yehova zikupemphani kufika pakudziŵa Atate wathu wakumwamba monga Munthu, kuphunzira dzina lake, Yehova, ndi mikhalidwe yake ndi zochita zake ndi anthu. Kupyolera mwa Mawu ake, Baibulo, mudzamvetsa chifukwa chake simufunikiradi zothandiza zowoneka, monga zifanizo ndi zithunzithunzi, pomfikira Mulungu. Inde, “yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”​—Yakobo 4:8.

[Bokosi patsamba 6]

Olemba Mbiri Amanena Kuti . . .

◻ “Ndifundo yodziŵika bwino kuti Chibuda, choyamba m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi BCE, chinalibe fano la wochiyambitsa mpaka pafupifupi zaka za zana loyamba CE.”

“Kwa zaka mazana ambiri, munalibiretu mafano m’chikhulupiriro cha Chihindu.”

“Chihindu ndi Chibuda zinayamba zopanda mafano ndipo mwapang’onopang’ono zinalandira mafano m’kulambira kwawo. Chikristu chinachita chimodzimodzi.”​—The Encyclopedia of Religion, lolembedwa ndi Mircea Eliade.

◻ “Kuchokera m’zolembedwa zosiyanasiyana za Baibulo nkwachiwonekere kuti kulambira kowona kwa Mulungu kunalibe mafano. . . . Mu NT [Chipangano Chatsopano] namonso, kulambiridwa kwa milungu yachilendo ndi mafano nkoletsedwa.​—New Catholic Encyclopedia.

◻ “Mafano anali osadziŵika m’kulambira kwa Akristu oyambirira.”​—Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, lolembedwa ndi McClintock ndi Strong.

◻ “Ngakhale m’Chipangano Chatsopano, kapena m’zolembedwa zowona zirizonse za nyengo yoyambirira ya Chikristu, simungapezedwe chizindikiro chirichonse cha kugwiritsira ntchito zifanizo kapena zithunzithunzi m’kulambira kwa Akristu, poyera kapena mwamtseri.”​—A Concise Cyclopedia of Religious Knowledge, lolembedwa ndi Elias Benjamin Sanford.

◻ “Akristu oyambirira akananyansidwa ndi lingaliro chabe lakuika mafano m’matchalitchi, ndipo akanawona kuwagwadira kapena kupemphera kwa iwo kukhala kofanana ndi kupembedza mafano.”​—History of the Christian Church, lolembedwa ndi John Fletcher Hurst.

◻ “M’tchalitchi choyambirira, kupanga ndi kulemekeza zithunzithunzi za Kristu ndi oyera mtima kunatsutsidwa nthaŵi zonse.”​—The New Encyclopædia Britannica.

◻ “Ngakhale kuti Tchalitchi choyambirira sichinatsutse luso lakujambula, chinalibe mafano a Kristu.”​—Schaff-Herzog Encyclopedia of Religious Knowledge.

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu anagogomezera kuti Mulungu akufunafuna amene ‘alambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena