Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 368-tsamba 374
  • Uchete

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uchete
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • “Chipulumutso N’cha Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amakana Mwaulemu Kuchita Nawo Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lawo?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • “Siali a Dziko Lapansi”
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • “Siali a Dziko Lapansi”
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 368-tsamba 374

Uchete

Tanthauzo: Mkhalidwe wa amene samatenga mbali kapena kupereka chichirikizo kwa alionse amagulu aŵiri kapena oposerapo otsutsana. Chiri chowonadi cha m’mbiri yakale ndi yamakono chakuti mu mtundu uliwonse ndi m’mikhalidwe yonse Akristu owona ayesayesa kusunga uchete wotheratu m’kumenyana kwa pakati pa magulu otsutsana a dziko. Iwo samadodometsa zimene ena amachita ponena za kukhala ndi phande m’madzoma akukonda dziko lawo, kutumikira m’magulu a ankhondo, kugwirizana ndi chipani chandale zadziko, kuloŵa m’kupikisana nawo malo m’kusankhiridwa paudindo m’ndale zadziko, kapena kuchita voti. Koma iwo amalambira Yehova yekha, Mulungu wa Baibulo; iwo apatulira miyoyo yawo yonse kwa iye ndi kupereka chichirikizo chokwanira ku Ufumu wake.

Kodi ndimalemba ati amene asonkhezera mkhalidwe wa Akristu kulinga ku ulamuliro wa maboma a dziko?

Aroma 13:1, 5-7: “Anthu onse amvere maulamuliro a akulu [olamulira a boma]; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu . . . Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbu mtima. . . . Perekani kwa anthu onse mangaŵa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuwopa kwa eni ake a kuwopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.” (Palibe boma limene likanakhalako popanda chilolezo cha Mulungu. Mosasamala kanthu za khalidwe la olamulira alionse pa okha, Akristu awona awasonyeza ulemu chifukwa cha udindo umene ali nawo. Mwachitsanzo, mosasamala kanthu za mmene maboma agwiritsirira ntchito ndalama za msonkho, olambira Yehova anakhoma misonkho yawo mowona mtima mobwezera mautumiki amene aliyense anapindula nawo.)

Marko 12:17: “Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Motero nthaŵi zonse Akristu avomereza kuti sikokha kuti ayenera “kubwezera” ndalama mumpangidwe wa misonkho kumaboma a dziko komanso kukwaniritsa mathayo aakulu amene iwo ali nawo kulinga kwa Mulungu.)

Mac. 5:28, 29, NW: “[Olankhulira bwalo lapamwamba Lachiyuda] anati: ‘Tinakulamulirani ndithu [atumwi] inu kusaphunzitsa pamaziko a dzina iri [la Yesu Kristu], ndipo komabe tawonani! Mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mwatsimikiza kudzetsa mwazi wa munthu uyu pa ife.’ Mwakuyankha Petro ndi atumwi enawo anati: ‘Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.’ (Pamene panakhala kuwombana kwachindunji pakati pamalamulo a olamulira aumunthu ndi malamulo a Mulungu, Akristu owona atsatira chitsanzo cha Atumwi mwa kuika kumvera Mulungu poyamba.)

Kodi ndimalemba ati amene nthaŵi zonse akhala osonkhezera mkhalidwe wa Akristu owona kulinga ku kukhala ndi phande m’nkhondo zokhetsa mwazi?

Mat. 26:52: “Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Kodi pakanakhala chifukwa chachikulu chirichonse chomenyera nkhondo choposa kutetezera Mwana wa Mulungu? Komabe, panopa Yesu anasonyeza kuti ophunzira amenewa sanafunikire kutembenukira kuzida zankhondo za nkhondo yakuthupi.)

Yes. 2:2-4: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga yamapiri . . . Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Anthu alionse pa okha ochokera kumitundu yonse ayenera kudzisankhira okha njira imene adzalondola. Awo amene alabadira chiweruzo cha Yehova amapereka umboni wakuti iye ndiye Mulungu wawo.)

2 Akor. 10:3, 4: “Pakuti pakuyendayenda m’thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi, pakuti zida zankhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga.” (Ponopa Paulo akulongosola kuti sanagwiritsire ntchito konse zida zankhondo zakuthupi monga ngati chinyengo, mawu odzikweza, kapena zida zankhondo zokhetsera mwazi, kuchinjiriza mpingo kuziphunzitso zonyenga.)

Luka 6:27, 28: “Ine [Yesu Kristu] ndinena kwa inu akumva, Kondanani nawo adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.”

Kodi sizowona kuti Yehova analoleza Israyeli wakale kuchita nkhondo?

Yehova analamula Israyeli wakale kugwiritsira ntchito nkhondo kuti alande dziko limene iyemwini adalipereka monga choloŵa chawo ndi kupereka chiweruzo pa anthu amene zizoloŵezi zawo zoluluzika ndi kuchitira mwano Mulungu wowona zinachititsa Yehova kuŵawona kukhala osayenereranso kukhala moyo. (Deut. 7:1, 2, 5; 9:5; Lev. 18:24, 25) Komabe, chifundo chinasonyezedwa kwa Rahabi ndi kwa Agibeyoni chifukwa chakuti anasonyeza chikhulupiriro mwa Yehova. (Yoswa 2:9-13; 9:24-27) M’pangano Lachilamulo Mulungu anapereka malangizo a nkhondo zimene akavomereza, akumatchula anthu osaphatikizidwamo ndi dongosolo lomenyera nkhondoyo. Zimenezo zinalidi nkhondo zopatulika za Yehova. Zimenezo siziri choncho ndi nkhondo zokhetsa mwazi za mtundu uliwonse lerolino.

Pakukhazikitsidwa kwa mpingo Wachikristu, mkhalidwe watsopano unayambika. Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose. Otsatira a Kristu anafunikira kupanga ophunzira mwa anthu a m’mitundu yonse; chotero m’nthaŵi yokwanira olambira a Mulungu wowona akapezeka m’mitundu yonse imeneyo. Komabe, kodi nchiyani chimene chiri cholinga cha mitunduyo pamene ipita kunkhondo? Kodi ndicho kukwaniritsa chifuniro cha Mlengi wa dziko lonse lapansi kapena kupititsa patsogolo zabwino zautundu? Ngati Akristu owona amtundu umodzi akapita kunkhondo yomenyana ndi mtundu wina, akakhala akumenyana ndi okhulupirira anzawo, motsutsana ndi anthu amene anapempherera chithandizo kwa Mulungu m’modzimodziyo amene iwo anapemphererako. Moyenerera, Kristu anauza otsatira ake kusiya lupanga. (Mateyu 26:52) Chifukwa chake, iyemwini pokhala wolemekezedwa kumwamba, akapereka chiweruzo pa oluluza Mulungu wowona ndi chifuniro Chake.—2 Ates. 1:6-8; Chiv. 19:11-21.

Ponena za kutumikira m’magulu a nkhondo, kodi mbiri yadziko imasonyezanji ponena za mkhalidwe wa Akristu owona?

“Mapendedwe osamalitsa a chidziŵitso chonse chopezeka amapitirizabe kusonyeza kuti, kufikira nthaŵi ya Marcus Aurelius [wolamulira Wachiroma kuyambira 161 mpaka 180 C.E.] palibe Mkristu amene anali msilikali; ndipo palibe msilikali, amene pambuyo pa kukhala Mkristu, anakhalabe muutumiki wankhondo.”—The Rise of Christianity (London, 1947), E. W. Barnes, p. 333.

“Ife amene tinali okonda nkhondo, ndi kuphana, ndi kuchita zoipa zirizonse, aliyense wa ife padziko lonse lapansi tinasanduliza zida zathu zonga zankhondo—malupanga athu kukhala zolimira ndipo mikondo yathu kukhala zotipulira,—ndipo timapititsa patsogolo kupembedza, chilungamo, chifundo, chikhulupiriro, ndi chiyembekezo, zimene tiri nazo kuchokera kwa Atate Mwiniyo kupyolera mwa Iye amene anapachikidwa.”—Justin Martyr mu “Dialogue With Trypho, a Jew” (wa zaka za zana la 2 C.E.), The Ante-Nicene Fathers (Grand Rapids, Mich.; kusindikizidwanso kwa kope la Edinburgh la 1885), lolembedwa ndi A. Roberts ndi J. Donaldson, Vol. I, p. 254.

“Iwo anakana kukhala ndi mbali iriyonse yokangalika m’kuyendetsa ulamuliro wa boma kapena usilikali wa chitetezo wa ufumuwo. . . . kunali kosatheka kuti Akristu, akanachita ntchito yausilikali, yauchiwanga, kapena yaukalonga, popanda kukana ntchito yopatulikayo.”—History of Christianity (New York, 1891), Edward Gibbon, pp. 162, 163.

Kodi ndimalemba ati amene nthaŵi zonse akhala osonkhezera mkhalidwe wa Akristu owona kulinga kukuphatikizidwa m’nkhani ndi zochitika za ndale zadziko?

Yoh. 17:16, NW: “Sali mbali yadziko, monga momwedi ine [Yesu] sindiri mbali yadziko.”

Yoh. 6:15: “Yesu, pozindikira kuti [Ayuda] ali kufuna kudza kudzamgwira iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.” Pambuyo pake, iye anauza bwanamkubwa Wachiroma kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi, ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.”—Yoh. 18:36.

Yak. 4:4, NW: “Akazi a chigololo, kodi simudziŵa kuti ubwenzi ndi dziko ndiwo udani ndi Mulungu? Chifukwa chake, yense, wofuna kukhala bwenzi la dziko, akudziika kukhala mdani wa Mulungu.” (Kodi nchifukwa ninji nkhaniyi iri yoopsa motero? Chifukwa chakuti, monga momwe 1 Yohane 5:19 amanenera, “dziko lonse ligona m’mphamvu ya woipayo.” Pa Yohane 14:30, Yesu anatcha Satana kukhala ‘wolamulira wa dziko.’ Chotero, mosasamala kanthu za kagulu kamene munthu angachirikize, kodi kwenikweni iye amadza pansi pa ulamuliro wayani?)

Ponena za kuphatikizidwa m’ndale zadziko, kodi olemba mbiri a dziko akusimbanji ponena za mkhalidwe wa awo amene anadziŵika kukhala Akristu oyambirira?

“Chikristu choyambirira kuchimvetsetsa kunali kochepa ndipo chinawonedwa kukhala choyanjidwa mochepera ndi awo amene analamulira dziko lachikunja. . . . Akristu anakana kutenga mbali m’ntchito zina za nzika za Roma. . . . Iwo sanakhale ndi udindo wa ndale zadziko.”—On the Road to Civilization, A World History (Philadelphia, 1937), A. Heckel ndi J. Sigman, pp. 237, 238.

“Akristu anaima patali ndipo anali olekana ndi boma, monga fuko launsembe ndi lauzimu, ndipo kuyenera kuvomerezedwa kuti Chikristu chinawonekera kukhala chokhoza kusonkhezera moyo wa anthu kokha mumkhalidwe umene, unali wabwino kopambana, kwenikweni mwakuyesayesa kukhomereza malingaliro opatulika owonjezerekawonjezereka kwa nzika za dziko.”—The History of the Christian Religion and Church, During the Three First Centuries (New York, 1848), Augustus Neander, lotembenuzidwa kuchokera m’Chijeremani ndi H. J. Rose, p. 168.

Kodi ndimalemba ati amene nthaŵi zonse akhala osonkhezera mkhalidwe wa Akristu owona kulinga kumadzoma oloŵetsamo mbendera ndi nyimbo zautundu?

1 Akor. 10:14: “Thaŵani kupembedza mafano.” (Ndiponso Eksodo 20:4, 5)

1 Yoh. 5:21: “Tiana, dzisungireni nokha kupeŵa mafano.”

Luka 4:8: “Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo iye yekhayekha uzimtumikira.”

Wonaninso Danieli 3:1-28.

Kodi zizindikiro zokonda dziko lako zoterozo ndi mazoma ziridi ndi tanthauzo lachipembedzo?

“[Wolemba mbiri] Carlton Hayes anasonyeza kalekale kuti dzoma la kulambira mbendera ndi la kulumbira m’masukulu a Amereka ndiro chochitika chachipembedzo. . . . Ndipo kuti madzoma a masiku onse amenewo ngachipembedzo atsimikiziridwa potsirizira pake ndi Khoti Lapamwamba m’mipambo ya milandu.”—The American Character (New York, 1956), D. W. Brogan, pp. 163, 164.

“Mbendera zoyambirira zinali pafupifupi chinthu chachipembedzo kotheratu. . . . Mbendera yautundu ya ku Mangalande kwa zaka mazana angapo—mtanda wofiira wa St. George—inali yachipembedzo; kwenikweni chithandizo chachipembedzo chomawonekera kukhala chitafunidwa kupangitsa mbendera zautundu kukhala zopatulika, ndipo chiyambi cha zochuluka chingafufuzidwe kukafika pa kukhala chizindikiro chopatulika.”—Encyclopædia Britannica (1946), Vol. 9, p. 343.

“M’Dzoma lapoyera lotsogozedwa ndi wachiŵiri kwa prezidenti wa Khoti [Lankhondo Lapamwamba], pa November 19, ulemu unasonyezedwa kumbendera ya ku Brazil. . . . Pambuyo pa kukwezedwa kwa mbenderayo, Nduna Yaikulu ya Gulu Lankhondo Tristao de Alencar Araripe inanena bwino ponena za chikumbukiro chosonyezedwa mwanjira imeneyi: ‘ . . . mbendera zafikira kukhala milungu m’chipembedzo chokonda dziko lako zimene zimakakamiza kulambira . . . mbendera imalemekezedwa ndi kulambiridwa . . . Mbendera imalambiridwa, monga momwedi Dziko Lobadwira limalambiridwira.’”—Diario da Justiça (Federal Capital, Brazil), February 16, 1956, p. 1906.

Ponena za mazoma a kukonda dziko lako, kodi mbiri yadziko imenenanji za mkhalidwe wa awo odziŵika kukhala Akristu oyambirira?

“Akristu anakana . . . kupereka nsembe kwa—mfumu zimene mwapang’ono lerolino ziri zofanana ndi kukana kupereka sawatcha ku mbendera kapena kubwereza lumbiro la kukhulupirika. . . . Akristu oŵerengeka kwambiri anakana chikhulupiriro chawo, ngakhale kuli kwakuti guwa lansembe loyaka moto pamwamba pake linali kusungidwa kaŵirikaŵiri m’bwalolo kuti aligwiritsire ntchito. Zokha zimene mkaidi anafunikira kuchita ndizo kuwaza lubani pang’ono chabe pamakala ndipo anali kupatsidwa Chikalata cha Nsembe ndi kulekedwa amuke waufulu. Kunali kufotokozedwanso mosamalitsa kwa iye kuti sanali kulambira mfumuyo; kungovomereza chabe kukhala mulungu kwa mfumuyo monga mutu wa boma la Roma. Komabe, panalibe Akristu alionse amene anadzipereka kulandira mwaŵi wakuwonjoka.—Those About to Die (New York, 1958), D. P. Mannix, pp. 135, 137.

“Mchitidwe wa kulambira mfumu unaloŵetsamo kuwazidwa kwa lubani lapang’ono chabe kapena madontho ochepa a vinyo paguwa lansembe limene linaimikidwa pamaso pa fano la mfumuyo. Mwinamwake chifukwa cha kutalikirana kwathu ndi chochitikacho, sitimawona kusiyana kulikonse ndi . . . kutukula mkono kupereka sawatcha kumbendera kapena kwa wolamulira wina wa boma wapadera, monga chisonyezero cha ulemu, kulemekeza, ndi kukonda dziko lako. Mwinamwake anthu ambiri m’zaka za zana loyamba analingalira motero, koma Akristu sanatero. Anawona nkhani yonseyo kukhala kulambira kwachipembedzo, kuvomereza wolamulirayo kukhala mulungu ndipo motero kukhala osakhulupirika kwa Mulungu ndi Kristu, ndipo iwo anakana kukuchita.”—The Beginnings of the Christian Religion (New Haven, Conn.; 1958), M. F. Eller, pp. 208, 209.

Kodi uchete wa Akristu watanthauza kuti iwo ali osakondwerera ubwino wa anansi awo?

Ndithudi ayi. Iwo amadziŵa bwino lomwe ndipo amayesayesa mowona mtima kugwiritsira ntchito lamulo lobwerezedwa ndi Yesu lakuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mat. 22:39) Ndiponso uphungu wolembedwa ndi mtumwi Paulo wakuti: “Tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pabanja la chikhulupiriro.” (Agal. 6:10) Iwo akhala ndi chitsimikiziro chakuti zabwino koposa zimene iwo angachitire anansi awo ndizo kugaŵana nawo mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, umene udzathetsa kosatha mavuto oyang’anizana ndi anthu ndi umene umatsegulira chiyembekezo chodabwitsa cha moyo wamuyaya kwa ochilandira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena