Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mpingo “Unayamba Kukhala Pamtendere”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • 12 Hananiya anavomera kugwira ntchito imene anapatsidwa ndipo anadalitsidwa. Kodi inuyo mumamvera lamulo lakuti tichitire umboni mokwanira, ngakhale kuti ntchito imeneyi imakudetsani nkhawa? Ena amada nkhawa kwambiri akaganiza zopita kunyumba ndi nyumba kukakumana ndi anthu amene sakuwadziwa. Enanso zimawavuta kulalikira anthu pamalo ochitira malonda, mumsewu komanso kuchita ulaliki wa patelefoni kapena wolemba makalata. Hananiya anayesetsa kuthetsa mantha ndipo anathandiza Saulo kuti alandire mzimu woyera.b Iye anakwanitsa kugwira ntchitoyi chifukwa chakuti ankadalira kwambiri Yesu ndipo ankaona Saulo ngati m’bale wake. Mofanana ndi Hananiya, ifenso tingathetse mantha ngati timakhulupirira kuti Yesu akutsogolera ntchito yolalikira, ngati timamvera chisoni anthu komanso ngati timakhulupirira kuti ngakhale anthu amene amaoneka mochititsa mantha akhoza kusintha n’kukhala abale athu.​—Mat. 9:36.

  • Mpingo “Unayamba Kukhala Pamtendere”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • b Nthawi zambiri atumwi ndi amene anali ndi udindo wopereka mphatso ya mzimu woyera kwa anthu ena. Koma pa nthawiyi, zikuoneka kuti Yesu anapatsa Hananiya mphamvu zopereka mphatso ya mzimu kwa Saulo. Saulo atakhala wokhulupirira, panapita nthawi yaitali ndithu asanakumane ndi atumwi 12 aja. Komabe, n’kutheka kuti pa nthawi yonseyi iye ankalalikira mwakhama. Choncho Yesu anaonetsetsa kuti Saulo ali ndi mphamvu zimene zingamuthandize kugwira ntchito yolalikira imene anam’patsa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena