Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Mulungu Alibe Tsankho”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • 1-3. Kodi Petulo anaona masomphenya otani, nanga kumvetsa tanthauzo lake n’kofunika bwanji?

      TSIKU lina masana m’nthawi ya chilimwe m’chaka cha 36 C.E., Petulo ankapemphera ali padenga lafulati la nyumba ina imene inali m’mbali mwa nyanja mumzinda wa Yopa. Kwa masiku angapo, iye anali mlendo panyumba imeneyi, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti analibe mtima wa tsankho. Mwiniwake wa nyumbayo anali Simoni ndipo ntchito yake inali yofufuta zikopa. Ayuda ena sakanalola kuti akhale panyumba ya munthu wofufuta zikopa.a Komabe, Petulo anali atatsala pang’ono kuphunzira mfundo yofunika kwambiri pa nkhani yoti Yehova ndi wopanda tsankho.

  • “Mulungu Alibe Tsankho”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
    • a Ayuda ena ankadana ndi anthu ofufuta zikopa chifukwa ntchitoyi inkawachititsa kuti azigwira zikopa, nyama zakufa komanso ankagwiritsa ntchito zinthu zina zonyansa pogwira ntchitoyi. Anthu ofufuta zikopa ankaonedwa kuti ndi osayenera kufika pakachisi, ndipo malo awo ogwirira ntchito ankafunika kukhala kunja kwa mzinda pa mtunda pafupifupi mamita 20. Mwina chimenechi chinali chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti nyumba ya Simoni ikhale “m’mbali mwa nyanja.”​—Mac. 10:6.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena