Sungani Mosamala Moyo Weniweni
KODI moyo uno ndiwo wokha umene ulipo? Mwa kutilimbikitsa ‘kugwira moyo weniweniwo,’ Baibulo limasonyeza kuti palinso zambiri. (1 Timoteo 6:17-19) Ngati moyo wathu umene ulipowu usali moyo weniweni, kodi moyo weniweni ndi uti?
Nkhani ya m’lemba lili pamwambali ikusonyeza kuti ndiwo “moyo wosatha” umene munthu wowopa Mulungu ayenera kuugwiritsitsa. (1 Timoteo 6:12) Kwa aunyinji, umenewu ukutanthauza moyo wosatha padziko lapansi. Adamu, munthu woyambayo, anali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wa padziko lapansi. (Genesis 1:26, 27) Iye akafa kokha ngati akadya za “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 2:17) Koma chifukwa chakuti Adamu ndi mkazi wake, Hava, mosamvera anadya za mtengo umenewo, Mulungu anapereka chiweruzo cha imfa. ‘M’tsiku lomwe anadya,’ anafa m’lingaliro la Mulungu ndipo anayamba kuloŵa mu imfa ya kuthupi. Moyo wawo sunalinso wa mkhalidwe umene anali nawo pachiyambi.
Njira ya ku “Moyo Weniweni”
Kuti apangitse “moyo weniweni” kukhala wothekera, Yehova Mulungu anapanga makonzedwe opulumutsira mtundu wa anthu. Kuti tithandizidwe kuzindikira makonzedwe ameneŵa, tiyeni tiyerekezere fakitale yaing’ono. Makina ake onse amene alimo ngwosagwira bwino ntchito ndipo akudzetsa zovuta kwa owagwiritsira ntchito ake chifukwa chakuti wantchito wina woyambirira, zaka zapitazo ananyalanyaza buku lake la malangizo ndipo anawononga makina onse. Ogwiritsira ntchito makina omwe alipowo angangoyesayesa kugwira ntchitoyo ndi makina omwe ali nawowo. Mwini fakitale akufuna kukonzanso makinawo kuti athandize antchito ake, ndipo akupatula ndalama zina pambali zofunikira cholinga chimenecho.
‘Wogwiritsira ntchito makina’ woyamba, Adamu, sanasunge mosamalitsa moyo umene anapatsidwa. Chifukwa chake, anapatsira mbadwa zake moyo wopanda ungwiro, mofanana ndi makina osagwira bwino ntchito. (Aroma 5:12) Mofanana ndi ogwiritsira ntchito makina apambuyo pake m’fakitaleyo, amene sakanawongolera mkhalidwewo, mbadwa za Adamu sizinakhoze kudzipezera moyo weniweni. (Salmo 49:7) Kuti awongolere mkhalidwe woonekeratu kukhala wopanda chiyembekezo umenewu, Yehova anatumiza Mwana wake wobadwa yekha kudziko lapansi kukaombolera anthu moyo wosatha. (Luka 1:35; 1 Petro 1:18, 19) Mwa kufa imfa yansembe kaamba ka mtundu wa anthu, Mwana wa Mulungu wobadwa yekhayo, Yesu Kristu, anapereka ndalama zake—moyo wolingana ndi umene Adamu anataya. (Mateyu 20:28; 1 Petro 2:22) Pokhala ndi nsembe yamtengo wapatali imeneyi, Yehova tsopano ali ndi maziko operekera moyo weniweni.
Kwa mtundu wa anthu womvera, nsembe ya dipo ya Yesu idzatanthauza moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. (Salmo 37:29) Chiyembekezo chimenechi chikuperekedwa kwa onse amene adzapulumuka “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” yotchedwa Harmagedo. (Chivumbulutso 16:14-16) Idzachotsa kuipa konse padziko lapansi. (Salmo 37:9-11) Awo okhala m’chikumbukiro cha Mulungu amene akufa nthaŵi imeneyo isanafike adzaukitsidwa kuloŵa m’Paradaiso wobwezeretsedwanso padziko lapansi ndipo adzakhala ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo weniweni umene wasungidwa kaamba ka anthu onse omvera Mulungu.—Yohane 5:28, 29.
Kufunika kwa Kusamalira Moyo Wathu Womwe Ulipowu
Zimenezi sizikutanthauza kuti kuli koyenera kwa ife kunyalanyaza kupatulika kwa moyo wathu womwe ulipowu. Kodi mwini fakitale angathere nthaŵi ndi ndalama akumapanganso makina kaamba ka wantchito amene sangawasamalire? M’malo mwake, kodi wolemba ntchitoyo sadzaika makina opangidwansowo m’manja mwa munthu amene adzachita monga momwe angathere kusunga bwinobe makina akalewo?
Moyo uli mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. Monga magwero abwino a mphatso imeneyo, iye akufuna kuti tiisunge bwino. (Salmo 36:9; Yakobo 1:17) Polankhula za nkhaŵa ya Yehova kaamba ka anthu padziko lapansi, Yesu anati: “Ngakhale matsitsi onse a pamutu panu aŵerengedwa.” (Luka 12:7) Yehova analamulira Aisrayeli kusapha, kumenedi kunaphatikizapo kusadzipha. (Eksodo 20:13) Zimenezi zimatithandiza kupeŵa kuona kudzipha monga chosankha china m’moyo.
Podziŵa chikondwerero chachikondi cha Yehova pa ubwino wathu, anthu owopa Mulungu amagwiritsira ntchito malamulo amkhalidwe a Baibulo popenda machitachita amakono. Mwachitsanzo, chifukwa chakuti Akristu oona amafunikira ‘kudzikonzera okha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu,’ amapeŵa fodya ndi anamgoneka omwerekeretsa osokoneza maganizo.—2 Akorinto 7:1.
Chikondwerero cha Mulungu pa moyo wa munthu chimaonedwanso mu uphungu wake wa kusunga “mtima wabwino” ndi kupeŵa khalidwe loipa. (Miyambo 14:30; Agalatiya 5:19-21) Mwa kumamatira kumiyezo imeneyi yapamwamba, timatetezeredwa pa zinthu zonga mkwiyo wovulaza mwakuthupi ndi nthenda zopatsirana mwa kugonana.
Nkhaŵa ya Yehova kaamba ka moyo wa anthu ake njoonekeranso m’chilangizo chake choletsa kudyetsa ndi kumwetsa. (Deuteronomo 21:18-21; Miyambo 23:20, 21) Akristu amachenjezedwa kuti anthu aumbombo ndi zidakwa sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu, ndiko kuti, sadzalandira konse moyo weniweni. (1 Akorinto 6:9, 10; 1 Petro 4:3) Mwa kulimbikitsa uchikatikati, Yehova amatiphunzitsa kuti tipindule ife eni.—Yesaya 48:17.
Pamene tichita zinthu mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu, timasonyeza kuti timasunga mosamalitsa moyo wathu womwe ulipowu. Zoonadi, wofunika kwambiridi ndiwo moyo weniweni. Popeza kuti uwo uli wosatha, Akristu oona amagwirizanitsa kufunika kwake kwambiri ndi moyo wawo womwe ulipowu. Pamene Yesu Kristu anapereka nsembe moyo wake, anagonjera ku chifuniro cha Yehova. Kumvera kwa Atate wake kunatanthauza zambiri kwa iye kuposa mmene unalili moyo wake padziko lapansi pano. Njira ya Yesu inadzetsa chiukiriro chake ndi kulandira kwake moyo wosafa kumwamba. (Aroma 6:9) Imfa yake imatanthauzanso moyo wosatha ku mtundu wa anthu womvera umene umasonyeza chikhulupiriro mu nsembe yake ya dipo.—Ahebri 5:8, 9; 12:2.
Lamulo Lofunika Kwambiri pa Mwazi
Moyenerera, otsatira a Yesu amasonyeza kaganizidwe kake. Amafuna kukondweretsa Mulungu mu zinthu zonse, monga momwe Kristu anachitira. Ndithudi, zimenezi zimasonyeza chifukwa chake iwo amakana kuthiridwa mwazi, kumene madokotala ena amakutcha kuti kopulumutsa moyo. Tiyeni tione mmene munthu amasonyezera kuti amasunga mosamalitsa moyo weniweni mwa kukana kuthiridwa mwazi.
Mofanana ndi Yesu Kristu, Akristu oona amafuna kukhala amoyo m’maso mwa Mulungu, ndipo zimenezo zimafuna kumvera Iye mokwanira. Mawu a Mulungu amalamula otsatira a Kristu kuti: “Musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.” (Machitidwe 15:28, 29) Kodi nchifukwa ninji lamulo limeneli lonena za mwazi linaphatikizidwa pamalamulo ogwira ntchito pa Akristu?
Chilamulo choperekedwa kwa Aisrayeli chinafuna kusala mwazi. (Machitidwe 17:13, 14) Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose. Koma amazindikira kuti lamulo loletsa kudya mwazi linayambirira Chilamulo; pachiyambi linali litaperekedwa kwa Nowa pambuyo pa Chigumula. (Genesis 9:3, 4; Akolose 2:13, 14) Lamulo limeneli linagwira ntchito kwa mbadwa zonse za Nowa, kumene mitundu yonse ya padziko lapansi inachokera. (Genesis 10:32) Ndiponso, Chilamulo cha Mose chimatithandiza kuona chifukwa cha kuumirira kwa Mulungu pa kupatulika kwa mwazi. Ataletsa Aisrayeli kudya mwazi wa mtundu uliwonse, Mulungu anati: “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.” (Levitiko 17:11) Mwazi unapatulidwa ndi Mulungu kaamba ka kugwiritsiridwa ntchito ya nsembe pa guwa la nsembe. Lamulo lake pa kupatulika kwa mwazi limasonyeza ulamuliro wake pa moyo wonse wa padziko lapansi. (Ezekieli 18:4; Chivumbulutso 4:11) Poona moyo wathu m’lingaliro la Yehova, timazindikira kuti suli wathu komano wangoikiziridwa kwa ife ndi Mulungu.
Monga momwe wogwiritsira ntchito makina wa m’fanizo lathu alili ndi thayo pa makina, ife taikiziridwa thayo pa moyo wathu womwe ulipowu. Kodi mungachitenji ngati makina anu anafunikira kukonzedwa ndipo makaniki akupereka lingaliro la kukonza makinawo mwa kugwiritsira ntchito zipangizo zimene kwenikweni zili zoletsedwa m’buku la malangizo a wogwiritsira ntchito makina? Kodi simungapite kwa amakaniki ena kuti mukaone ngati makinawo angakonzedwe mogwirizana ndi malangizo a m’buku? Moyo wa munthu ngwofunika kwambiri ndi wocholoŵana kuposa makina. M’Mawu ake ouziridwa, buku la malangizo osamalirira anthu kukhala amoyo, Mpangi wathu amaletsa kugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi kuti uchirikize moyo. (Deuteronomo 32:46, 47; Afilipi 2:16) Kodi sikwanzeru kumamatira ku zofunika za buku la malangizo limenelo?
Kunena zoona, Akristu odwala amene akupempha chisamaliro cha mankhwala chopanda mwazi pa nthenda yawo sakukana kupatsidwa mankhwala onse. Iwo akungopempha kupatsidwa mankhwala amene adzasonyeza kulemekeza moyo wawo—ponse paŵiri watsopano lino ndi wamtsogolo. Madokotala amene molimba mtima amalemekeza kaimidwe kosonyezedwa ndi Akristu akuchitira umboni za mapindu a kuwasamalira mogwirizana ndi pempho lawo. “Kudziŵana ndi Mboni za Yehova kunandichititsa kudziŵa za makhalidwe ena atsopano,” akutero dokotala wina wa opaleshoni amene anali kukonda kwambiri kuthira mwazi odwala. Tsopano iye amayesa kusamalira ngakhale anthu amene sali Mboni popanda mwazi.
Kusunga Mosamalitsa Moyo Weniweni
Kodi ndi makhalidwe atsopano otani amene dokotala wa opaleshoni ameneyu anapeza posamalira Mboni za Yehova? Iye tsopano akuzindikira kuti kusamalira wodwala kumaloŵetsamo osangoti mbali chabe ya thupi imene ili ndi nthenda koma munthu yense amene. Kodi wodwala sayenera kuloledwa kupempha chisamaliro chabwino koposa kaamba ka ubwino wake wakuthupi, wauzimu, ndi wamalingaliro?
Kwa Kumiko wa zaka 15, kuthiridwa mwazi kuti achiritse leukemia yake yakuphayo kunali njira yosankhidwa yoipitsitsa. Kuyesa kutalikitsa moyo wake mwanjira imeneyi kwa milungu ingapo, miyezi ingapo, kapena ngakhale zaka zingapo sikunali koyenera kutayirapo kanthu kena kokhalitsa. Pokhala atapatulira moyo wake wapanthaŵiyo kwa Yehova Mulungu monga mmodzi wa Mboni zake, analemekeza kupatulika kwa moyo ndi mwazi. Ngakhale kuti atate wake ndi achibale ena anatsutsa mwamphamvu kaimidwe kake, Kumiko anachirimikabe. Dokotala wake panthaŵi ina anamfunsa kuti: “Ngati Mulungu wako amakhululukira machimo, kodi sangakukhululukire ngakhale ngati ulandira mwazi?” Kumiko anakana kulolera molakwa kumene kukanakhalanso kukana chikhulupiriro chake chozikidwa pa Baibulo. ‘Poonetsera mawu a moyo,’ iye anachirimikabe. (Afilipi 2:16) Agogo ake aakazi osakhulupirira anati, “Kumiko sangataye konse chikhulupiriro chake.” Posapita nthaŵi mkhalidwe wa maganizo wa atate ake ndi agogo ake aakaziwo ndiponso wa madokotala amene anali kumsamalira unasintha.
Chikhulupiriro champhamvu cha Kumiko mwa Yehova Mulungu, amene angathe kumuukitsa kwa akufa, chinasonkhezera mitima ya ambiri. Pamene anali ndi moyo, iye anadandaulira atate ake kuti: “Ngakhale ngati ndifa, ndidzaukitsidwa m’Paradaiso. Komano ngati inu muwonongedwa pa Harmagedo, sindidzakuonaninso. Chotero chonde phunzirani Baibulo.” Atate akewo ankangonena kuti: “Ukachira, ndidzatero.” Koma pamene Kumiko anamwalira ndi nthenda yake yosachiritsikayo, atate ake anaika m’bokosi la maliro kakalata kolembedwa kuti: “Kumiko, ndidzakuona m’Paradaiso.” Pambuyo pa maliro, iwo analankhula kwa amene anali pamaliropo ndipo anati: “Ndinalonjeza Kumiko kuti ndidzamuona m’Paradaiso. Ngakhale kuti sindikukhulupirirabe zimenezi chifukwa chakuti sindinaphunzire zokwanira, ndatsimikiza kuti ndizipende. Chonde ndithandizeni.” Enanso a m’banja lake anayamba kuphunzira Baibulo.
Kumiko analemekeza moonadi moyo ndipo anafuna kukhalabe ndi moyo. Anayamikira zonse zimene madokotala ake anachita kuti apulumutse moyo wake wapanthaŵiyo. Komabe, mwa kuchita mogwirizana ndi malangizo a buku la malangizo la Mlengi, anasonyeza kuti anasunga mosamalitsa moyo weniweni. Kwa anthu mamiliyoni ambiri, umenewo udzakhala moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Kodi mudzakhala pakati pawo?