Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/1 tsamba 10-15
  • Kristu Mokangalika Akutsogolera Mpingo Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kristu Mokangalika Akutsogolera Mpingo Wake
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira za Umulungu za Kulamulira Mokangalika
  • Bungwe Lolamulira Lowoneka ndi Maso
  • Utsogoleri Waumwini wa Kristu
  • Kristu Anachirikiza Ziwalo za Bungwe Lolamulira
  • Chosankha Chachilendo
  • Kristu Mokangalika Akadatsogolerabe Mpingo Wake
  • Kodi Ndi Ndani Akutsogolera Anthu a Mulungu Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • “Mtsogoleri Wanu Ndi Mmodzi, Khristu”
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/1 tsamba 10-15

Kristu Mokangalika Akutsogolera Mpingo Wake

“Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu . . . anampatsa iye akhale mutu pa zonse [ku mpingo, NW].”​—AEFESO 1:17, 22.

1. Kodi ndimotani mmene ziwalo zina za matchalitchi a Dziko la Chipembedzo zingayankhire funso lakuti, ‘Kodi ndani amene ali mtsogoleri wanu?’ koma ndimotani mmene Mboni za Yehova zimayankhira?

MBONI ZA YEHOVA sizizindikira munthu aliyense monga mtsogoleri wawo. Mkhalidwe wawo wa gulu sufanana ndi wa papa wa Tchalitchi cha Roma Katolika, makolo a matchalitchi a Eastern Orthodox, kapena atsogoleri amatchalitchi ena ndi mipatuko ya Dziko la Chipembedzo. Chigwirizano chawo chiri kwa Yesu Kristu, Mutu wa mpingo Wachikristu, yemwe anati: “Mtsogoleri wanu ndi Mmodzi, Kristu.”​—Mateyu 23:10.

2. Nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimazindikira Kristu monga Mutu wa mpingo Wachikristu, koma kodi ndi mafunso otani amene angafunsidwe?

2 Pa Pentekoste mtumwi Petro anatsimikizira: “Pakuti Davide sanakwera kumwamba ayi, koma anena yekha, ‘[Yehova, NW] anati kwa Mbuye wanga: “Khalani ku dzanja lamanja langa, kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.”’ Pamenepo lizindikiritse banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampachika.” (Machitidwe 2:34-36) Koma pamene tikuzindikira kuti mu 33 C.E. Yesu anapangidwa kukhala Mbuye ndi Mutu wa mpingo, kodi tiri oyedzamira kulingalira za iye kukhala atangokhala chabe kudzanja lamanja la Yehova, kuyembekezera kaamba ka kukhazikitsidwa kwake mfumu mu 1914? Kodi tiri ozindikira kotheratu kuti kuyambira pachiyambi Kristu mokangalika anatsogolera mpingo wake?

Njira za Umulungu za Kulamulira Mokangalika

3. Kodi nchiyani chimene Yesu analonjeza kutumiza kwa ophunzira ake, ndipo ndimotani mmene timadzrtrira kuti iye sanali kulankhula ponena za munthu?

3 Madzulo amodzi isanafike imfa yake, Yesu ananena kwa atumwi ake okhulupirika: “Kuyenera kwa inu kuti ndichoke ine. Pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.” (Yohane 16:7) Iye anayenera kutumiza osati munthu koma mphamvu yogwira ntchito. Iye anachimveketsa ichi bwino lomwe asanakwere kumwamba, akumanena kwa ophunzira ake osonkhana: “Ndipo onani ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m’mudzi muno kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera kumwamba.”—Luka 24:49.

4. Kodi mzimu woyera unagwiritsiridwa ntchito motani kuchokera pa Pentekoste ndi kupitirizabe?

4 Ophunzira okhulupirika a Yesu anakhala mu mbali ya Yerusalemu kufikira Pentekoste. Tsiku limenelo “iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera,” monga mwalonjezano. Petro anatsimikizira: “Popeza anakwezedwa [Yesu] ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la mzimu woyera, natsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.” (Machitidwe 2:4, 33) Mwanjira imeneyi Yehova anadzoza Akristu oyambirira amenewa monga ana ake auzimu. (Agalatiya 4:6) Ndiponso, Yesu analandira mzimu kuchokera kwa Atate wake monga njira ya kulamulira mokangalika mpingo wake pa dziko lapansi kuchokera ku malo ake a kumwamba ku dzanja lamanja la Mulungu.

5, 6. (a) Kodi ndi njira ina iti imene inaperekedwa kwa Kristu kuimutheketsa iye kulamulira mpingo wake padziko lapansi? (b) Perekani zitsanzo zachindunji za mmene Yesu anagwiritsirira ntchito njira imeneyi m’malo mwa ophunzira ake ndi m’kuchirikiza ntchito yolalikira.

5 Mkuwonjezerapo, mtumwi Petro analemba ponena za Yesu: “Amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m[mwamba, pali angelo, ndi mauhunuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.” (1 Petro 3:22) Chotero, angelo ali, njira ina imene Yehova anaipereka kwa Kristu ya kutsogozera mpingo wake Wachikristu mokangalika.

6 Mofananamo, pamene tiwerenga mu bukhu la Machitidwe kuti “m’ngelo wa Yehova” kapena “m’ngelo wa Mulungu” anachita m’kuchirikiza ntchito Yachikristu yolalikira kapena kulowerera m’malo mwa ziwalo za mpingo Wachikristu, pali chifukwa chirichonse chokhulupirira kuti angelo oterowo anagwira ntchito pansi pa chitsogozo cha Kristu Yesu. (Machitidwe 5: 19; 8:26; 10:3-7, 22; 12:7-11; 27:23, 24) Monga “Mikaeh m’ngelo wamkulu,” Kristu ali ndi angelo omwe amawalamulira, ndipo anagwiritsira ntchito iwo mokangalika kutsogoza mpingo Wachikristu mu zana loyamba C.E.​—Yuda 9; 1 Atesalonika 4:16.

Bungwe Lolamulira Lowoneka ndi Maso

7. Kodi ndi njira ina iti imene Kristu akugwiritsira ntchito kupereka chitsogozo ku mpingo wake, ndipo kodi ndi malemba ati amene amalankhula ponena za “ntchito yoyang’anira” imeneyi?

7 Malemba amasonyezanso kuti Yesu Kristu anagwiritsira ntchito gulu la amuna monga bungwe lolamulira kupereka chitsogozo ku mpingo wake padziko lapansi. Choyamba, bungwe lolamulira limeneli limawoneka kukhala linapangidwa ndi atumwi 11 okha. Pamene anali kufunafuna chifuniro cha Yehova ponena za yemwe akalowa m’malo mwa Yudase Isikariote, Petro anagwira mawu a Salmo 109:8, NW, omwe amati: “Malo ake a uyang’anirowina wake awatenge.” Kenaka, m’pempherokwa Yehova, Petro ndi anzake anafunsa Mulungu kusankha munthu “alowe m’malo autumiki uwu ndi utumiki, kuchokera komwe Yudase anapatukira.” Matiya anaikidwa kutumikira “pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.”​—Machitidwe 1:20, 24-26.

8. Kodi ndi zitsanzo ziwiri ziti zoyambirira zimene zimasonyeza mmene Yesu anagwiritsirira ntchito ziwalo zowonekera za bungwe lolamulira?

8 Mbali yoyamba yolembedwa ya kugwira ntchito kwa atumwi 12 amenewa mu “ntchito yoyang’anira imeneyi” monga bungwe lolamulira panali pamene iwo anaika amuna oyeneretsedwa mwauzimu kutumikira abale awo mkati mwa mpingo woyambirira. (Machitidwe 6:1-6) Nthawi yachiwiri inali pamene Filipo anayamba kulalikira Kristu kwa Asamariya. Monga chotulukapo cha ichi, “atumwi mu Yerusalemu . . . anatumiza Petro ndi Yohane kwa iwowa.” Kokha pambuyo pa kuika manja pa Asamariya kwa oimira a ziwalo za bungwe lolamulira amenewo iwo ‘anayamba kulandira mzimu woyera.’​—Machitidwe 8:5, 14-17.

Utsogoleri Waumwini wa Kristu

9. Kodi Kristu nthawi zonse anachita kanthu kupyolera mwa angelo kapena bungwe lolamulira? Perekani chitsanzo.

9 Chotero, kuyambira pa chiyambi penipeni pa mpingo Wachikristu, Kristu anali ndi mzimu woyera, angelo, ndi bungwe lolamulira lowoneka ndi maso kumuthandiza iye kutsogolera mokangalika ophunzira ake padziko lapansi. Panthawi ina iye anachitapo kanthu mwaumwini. Mwachitsanzo, Kristu mwaumwinianatembenuza Saulo wa ku Tariso. (Machitidwe 9:3-6) Masiku atatu pambuyo pake Yesu analankhula mwachindunji kwa “wophunzira wina” wotchedwa Hananiya. Kuvumbulutsa kwa iye ntchito ya mbali zitatu yomwe anali nayo m’maganizo kaamba ka Saulo, Yesu anati: “Iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli.” (Machitidwe 9:10-15) Kristu anamuitana Saulo kaamba ka ntchito yapadera. Saulo chotero anakhala mtumwi, kapena wotumizidwa, wodziwika bwino monga mtumwi Paulo.

10. Kodi ndimotani mmene Kristu mwaumwini anayang’anira ntchito yolalikira?

10 Kristu mwaumwini anayang’anira ntchito yolalikira. Kupyolera mwa mzimu woyera wolandiridwa kuchokera kwa Atate wake Yehova, iye anayambitsa maulendo aumishonale a Paulo ndi kutenga chikondwerero chaumwini mwa iwo. Timawerenga: “Mzimu woyera unati: ‘Mundipatulire ine Barnaba ndi Saulo ku ntchito imene ndiwaitanirako.’ . . . Pomwepo iwo, oitanidwa ndi mzimu woyera, anatsikira ku Selukeya, ndipo pochokerapo anapita m’ngalawa” paulendo woyamba wa umishonale. (Machitidwe 13: 2-4) Ndithudi, mzimu woyera, mphamvu yogwira ntchito ya Yehova, ‘sukananena’ nkomwe chinachake kapena ‘kutumiza’ winawake iwo wokha. Mmodzi amene anagwiritsira ntchito mzimu kutsogoza zinthu mwachiwonekere anali Kristu, Mutu wa mpingo.

11. Kodi nchiyani chimene chinachitika mkati mwaulendo wachiwiri wa umishonale wa Paulo, ndipo kodi ndimotani mmene ichi chimasonyezera mowonekera kuti Yesu anagwiritsira ntchito mzimu woyera kutsogolera ntchito yolalikira?

11 Kugwiritsira ntchito kumeneku kwa mzimu ndi Yesu pamene iye mokangalika anatsogolera Akristu oyambirira kwasonyezedwa bwino mu mbiri yaulendo wachiwiri wa umishonale wa Paulo. Pambuyo pa kuchezeranso mipingo mu Lukaoniya (chigawo cha ku Asia Minor) yomwe inakhazikitsidwa mkati mwa ulendo woyamba wa umishonale, Paulo ndi anzake oyenda nawo mwachiwonekere analingalira za kupita kumadzulo kudzera mu gawo la Chiroma la Asia. Chifukwa ninji iwo sanapite mogwirizana ndi makonzedwe awo? “Chifukwa analetsedwa ndi mzimu woyera kuti asalalikire mawu m’Asiya.” (Machitidwe 15:36, 40, 41; 16:1-6) Koma kodi ndani amene anagwiritsirantchito mzimu woyera wa Yehova kuwatsogolera iwo? Versi lotsatira limayankha. Ilo liku sonyeza kuti pamene iwo anali kulowera kumpoto, kulingalira kuti akalalikire ku Bituniya, “mzimu wa Yesu sunawaloleza.” (Machitidwe 16:7) Inde, Yesu Kristu anali kugwiritsira mzimu umene iye analandira kuchokera kwa Atate wake kutsogoza ntchito yolalikira mokangalika. Iye ndi Atate wake Yehova anafuna kuti mbiri yabwino ilalikidwe mu Europe, chotero Paulo analandira masomphenya otsogolera kumeneko.​—Machitidwe 16:9, 10.

Kristu Anachirikiza Ziwalo za Bungwe Lolamulira

12, 13. Pa nthaŵi ya ulendo woyamba wa Paulo ku Yerusalemu monga Mkristu, kodi nchiyani chimene chinachitika chomwe chinasonyeza mmene Kristu anachirikizira zosankha zopangidwa ndi abale amathayo a mu mzinda umene wo?

12 Panthawi imene mtumwi Paulo anakumana koyamba ndi ophunzira mu Yerusalemu, iwo mwachimvekere sanali ofunitsitsa kukumana naye. “Koma Barnaba anamtenga, napita naye kwa atumwi.” (Machitidwe 9:26, 27) Paulo anatha masiku 15 ndi mtumwi Petro. Anakumananso ndi mbale wopeza wa Yesu Yakobo, panthawiyo anali m’modzi wa akulu a mpingo wa ku Yerusalemu. (Agalatiya 1:18, 19) Ndime zotsatira mu Machitidwe zimasonyeza kuti akulu a ku Yerusalemu anakhala mbali ya bungwe lolamulira la mpingo Wachikristu woyambirira, limodzi ndi atumwi 12.​—Machitidwe 15:2; 21:18.

13 Mkati mwakukhala kwake kwa milungu iwiri mu Yerusalemu, Paulo anachitira umboni kwa Ayuda olankhula Chigriki, koma “anayesayesa kumupha iye.” Luka akuwonjezera kuti “koma mmene abale anachidziwa, anapita naye ku Kaisareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso.” (Machitidwe 9:28-30) Koma kodi ndani amene anali kumbuyo kwa chosankha chanzeru chimenechi? Zaka zingapo pambuyo pake, pamene anali kulankhula nkhani yofana nayo m’moyo wake, Paulo ananena kuti Yesu anawoneka kwa iye ndi kumlangiza iye kuchoka mu Yerusalemu mofulumira. Pamene Paulo anakana, Yesu anawonjezera: “Pita, chifukwa ine ndidzakutuma iwe unke kutali kwa amitundu.” (Machitidwe 22:17-21) Kristu anali kutsatira nkhanizo mosamalitsa kuchokera ku 12, 13. Pa nthaŵi ya ulendo woyamba wa Paulo ku Yerusalemu monga Mkristu, kodi nchiyani chimene chinachitika chomwe chinasonyeza mmene Kristu anachirikizira zosankha zopangidwa ndi abale amathayo a mu mzinda umene wo? mwamba ndipo anagwirapo ntchito ponse pawiri kupyolera mwa abale amathayo mu Yerusalemu ndi mwakulankhula mwachindunji kwa Paulo.

14. Kodi ndi kufanana kotani pakati pa mbiri ya mu Machitidwe ndi Agalatiya kumene kumasonyeza kuti Kristu anali kutsogolera zinthu m’chigwirizano ndi kukumana kwa bungwe lolamulira pa mdulidwe?

14 Mofananamo, kuwerenga kosamalitsa kwa Malemba kumasonyeza mowonekera bwino kuti Kristu anali kumbuyo kwa msonkhano wofunika kwambiri wa bungwe lolamulira wopangidwa kukhazikitsa funso lonena zakuti kaya Akristu Achikunja ayenera kugonjera ku mdulidwe ndi Chilamulo cha Mose kapena ayi. Bukhu la Machitidwe limasonyeza kuti pamene nkhaniyo inabuka, “iwo [mosakaikira ziwalo za mathayo, kapena akulu, a ku mpingo wa ku Antiokeya] anapatula Paulo ndi Barnaba, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.” (Machitidwe 15:1, 2) Koma pamene Paulo ananena ponena za mikhalidwe yomwe inatsogolera ku kupita, kwake ku Yerusalemu kukathetsa nkhani ya mdulidwe, iye anati: “Koma ndinakwera kunkako movumbulutsa.” (Agalatiya 2: 1-3; yerekezani ndi 1:12.) Monga Mutu wokangalika wa mpingo, Kristu anafuna kuti nkhani ya chiphunzitso yofunika kwambiri imeneyi ikhazikitsidwe ndi bungwe lonse lolamulira lowoneka ndi maso. Kupyolera mwa mzimu woyera, iye anatsogolera malingaliro a amuna odzipereka amenewo m’kupanga chosankha chawo.​—Machitidwe 15:28, 29.

Chosankha Chachilendo

15, 16. (a) Kodi nchiyani chimene bungwe lolamulira linamufuna Paulo kuchita pambuyo pa kubwerera kwake kuchokera ku ulendo wake wachitatu wa umishonale? (b) Kodi nchifukwa ninji langizo limeneli lingawoneke kukhala lachilendo, ndipo nchifukwa ninji Paulo anagwirizana ndi ilo? (c) Kodi ndi funso lotani limene limabukapo?

15 Chitsanzo china chosangalatsa cha chitsogozo chokangalika cha Kristu cha zinthu kuchokera kumwamba chiri chimene chinachitika pambuyo paulendo wachitatu wa umishonale wa Paulo. Luka akulongosola kuti pamene anabwerera kuchoka ku Yerusalemu, Paulo anapanga cholembera chathunthu ku ziwalo za bungwe lolamulira panthawiyo. Luka analemba: “Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo. Ndipo atawalankhula iwo, anawafotokozera chimodzi chimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake.” (Machitidwe 21:17-19) Pambuyo pa kumva kwa Paulo, bungwe losonkhanalo linamupatsa iye langizo lachidule, likumati: “Uchite ichi tikuuza iwe.” Anamulamulira iye kupita ku kachisi ndipo mwapoyera kusonyeza kuti iye sanali “kuphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana awo, kapena asayende monga mwa miyambo.”​—Machitidwe 21:20-24.

16 Wina angakaikire nzeru ya alangizi imeneyi. Monga mmene tawonera kale, zaka zambiri kumayambiriro Yakobo, ndipo mwinamwake akulu ena omwe analipo pa zochitika zonse ziwiri, anamuchotsa Paulo kuchoka ku Yerusalemu chifukwa chakuti moyo wake una wopsyezedwa ndi “Ayuda olankhula Chigriki.” (Machitidwe 9:29) Mosasamala kanthu za ichi, Paulo anagwirizana ndi lamulolo, m’chigwirizano ndi zimene iye anali atanena kale pa 1 Akorinto 9:20. Koma magwero ofanana amatulutsa zotulukapo zofanana. “Ayuda ochokera [ku gawo la Chiroma] la Asiya” anayambitsa chipolowe ndipo anayesa kumupha Paulo. Kokha kachitidwe kofulumira ka asilikari a Chiroma kanamupulumutsa iye kukulipsyiridwa. (Machitidwe 21:26-32) Popeza kuti Kristu ali Mutu wokangalika wa mpingo, kodi nchifukwa ninji iye anapangitsa bungwe lolamulira kumufuna Paulo kupita mu kachisi?

17. Kodi ndimotani mmene chosankha chachilendo chimenechi chinatembenukira kukhala chaumulungu, ndipo kodi ichi chimasonyezanji?

17 Yankho limawonekera mu zimene zinawoneka pa usiku wachiwiri pambuyo pa kumangidwa kwa Paulo. Iye anapereka umboni wabwino kwa khamu lomwe linafuna kumupha iye ndipo, tsiku lotsatira, ku bwalo lamilandu. (Machitidwe 22:1-21; 23:1-6) Kwanthawi yachiwiri iye anali pafupi kulipsyiridwa. Koma usiku umenewo, Yesu anawonekera kwa iye ndi kunena: “Limbika mtima! Pakuti monga wandichitira umboni pa Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.” (Machitidwe 23:11) Kumbukirani ntchito ya mbali zitatu imene Kristu ananeneratu kaamba ka Paulo. (Machitidwe 9:15) Paulo anali atachitira ulemu dzina la Kristu kwa “amitundu” ndipo kwa “ana Aisrayeli,” koma nthawi inali itafika tsopano kaamba ka iye kuchitira umboni “kwa mafumu.” Chifukwa cha chosankha chimenecho ndi bungwe lolamulira, Paulo anali wokhoza kuchitira umboni kwa nthumwi za Chiroma Felike ndi Festo, kwa Mfumu Herode Agripa II, ndipo, pomalizira, kwa Wolamulira wa Chiroma Nero. (Machitidwe mitu 24-26; 27:24) Kodi ndani amene angakaikire kuti Kristu anali kumbuyo kwa zonsezi?

Kristu Mokangalika Akadatsogolerabe Mpingo Wake

18. Kodi nchiyani chimene Yesu Kristu ananena asanakwere kumwamba?

18 Asanasiye ophunzira ake ndi kukwera ku dzanja lamanja la Atate wake, Yesu Kristu anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu. Ndipo onani! Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimariziro cha nthawi ya pansi pano.”—Mateyu 28:18-20.

19. Kodi ndimotani mmene Kristu anasonyezera mphamvu zake zopatsidwa ndi Mulungu mu zana loyamba, ndipo kodi nchiyani chimene tidzalingalira mu nkhani yotsatira?

19 Bukhu la Machitidwe, lolongosola mbiri yakale ya zaka zoyambirira za Chikristu, limasonyeza mopanda chikaikiro kuti Kristu anagwiritsira ntchito mphamvu zake kutsogoza mpingo wake mokangalika padziko lapansi. Iye anachita ichi kupyolera mwa mzimu woyera, angelo, ndi bungwe lolamulira lopangidwa ndi atumwi 12 ndi akulu ku mpingo wa ku Yerusalemu. Yesu ananena kuti iye adzakhala ndi ophunzira ake kufikira mapeto a dongosolo iri la kachitidwe kazinthu, kumene tiri tsopano. Mu nkhani yotsatira, tidzawona ndimotani mmene iye adakali Mutu wokangalika wa mpingo Wachikristu ndiponso ndi mmene iye akutsogozera “nkhosa” zake lerolino.

Nsonga Zoyenera Kukumbukira

◻ Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizizindikfra munthu monga mtsogoleri wawo?

◻ Kodi ndimotani mmene Kristu anagwiritsirira ntchito mzimu woyera kutsogoza mpingo Wachikristu woyambirira?

◻ Kodi ndimotani mmene Kristu anagwiritsirira ntchito angelo m’kutsogoza Akristu a mu zana loyamba?

◻ Kodi ndimotani mmene Kristu anagwiritsirira ntchito bungwe lolamulira lowoneka ndi maso m’kutsogoza mpingo wake wa padziko lapansi?

◻ Kodi ndimotani mmene Kristu mwaumwini amatsogozera zinthu nthawi zina?

[Mapu patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ulendo Wachiŵri wa Umishonale wa Paulo

Antiokeya

Selukeya

KILIKIYA.

Tariso

Derbe

KAPADOKIYA

PAMFULIYA

GALATIYA

Lustra

Ikoniyo

Antiokeya

ASIYA

BITUKIYA NDI PONTO

Trowa

MAKEDONIYA

Filipi

Tesalonika

[chithunzi patsamba 10]

Kristu anatsogoleranso mpingo wake kupyolera mwa bungwe lolamulira lowoneka ndi maso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena