‘Kodi Ndichitenji Kuti Ndipulumuke?’
‘KODI ndichitenji kuti ndipulumuke?’ Funso limeneli linafunsidwa kalelo m’chaka cha 50 C.E. ndi wosunga ndende mu Filipi, Makedoniya. Panali patangochitika chivomezi chachikulu, ndipo makomo andende imene anali kuyang’anira anatseguka. Akumaganiza kuti andendewo athaŵa, wosunga ndendeyo anali pafupi kudzipha. Koma mmodzi wa andendewo, mtumwi Paulo, anafuula kuti: “Usadzipweteka wekha; tonse tiri muno.”—Machitidwe 16:25-30.
Paulo ndi wandende mnzake, Sila, anali atabwera ku Filipi kudzalalikira uthenga wa chipulumutso, ndipo iwo anali m’ndende chifukwa cha zinenezo zabodza zotsutsana nawo. Akumayamikira kuti andendewo sanathaŵe, wosunga ndendeyo anafuna kumva uthenga wa Paulo ndi Sila. Kodi nchiyani chimene iye akafunikira kuchita kuti apeze chipulumutso cholalikidwa ndi amishonale Achikristu aŵiri amenewa?
Anthu lerolino akadafunikirabe chipulumutso chimene Paulo ndi Sila ankalalikira. Komabe, mwachisoni, ambiri amawona nkhani ya kupulumuka mokaikira kwambiri. Iwo amanyansidwa ndi kunyada ndi umbombo wa atsogoleri a chipembedzo ambiri amene amadzinenera kukhala akuwaphunzitsa mmene angapulumukire. Ena amanyanyala kutengeka maganizo kopanda pake kowanda pakati pa zipembedzo zambiri za evanjeliko zimene zimagogomezera lingaliro la chipulumutso. Mtola nkhani Wachingelezi Philip Howard ananena kuti otchedwa kukhala alengezi oterowo “amawukira malingaliro ndi manja osaina macheke m’malo mwa maganizo a omvetsera awo.”—Yerekezani ndi 2 Petro 2:2.
Ndipo ena amazizwa ndi masinthidwe amene nthaŵi zina amachitikira anthu amene amakhulupirira kuti anali ndi chochitika cha “kupulumutsidwa.” M’bukhu lawo lakuti Snapping, Flo Conway ndi Jim Siegelman akulankhula za zokumana nazo zambiri zachipembedzo—kuphatikizapo “kupulumutsidwa”—komwe kwafikira kukhala kotchuka m’zaka makumi oŵerengeka zapitazo. Iwo amalemba ponena za “mbali yoipa” ya zokumana nazo zoterozo ndi kunena kuti anthu “amakwalidwira” m’masinthidwe aumunthu a mwadzidzidzi omwe amalephera kupereka kukwaniritsidwa ndi kuunikiridwa zolonjezedwa koma m’malomwake amatulutsa chinyengo, maganizo otsekeka, ndi kusakhoza kuyang’anizana ndi zenizeni. Olembawo akuwonjezera kuti: “Tingalongosole dongosololo kukhala lotseka maganizo, la kusalingalira.”
Mmenemo simmene zinaliri pamene Akristu a m’zaka za zana loyamba anapeza chipulumutso. Wosunga ndende wa ku Filipi ‘sanatseke maganizo ake’ pamene mtumwi Paulo anayankha funso lake lakuti, ‘Kodi ndichitenji kuti ndipulumuke?’ Ndipo Paulo ndi Sila sanalinganize ‘kuwukira malingaliro ake’ ndi kupempha chopereka cha ndalama chachikulu. M’malomwake, “anamuuza iye mawu a [Yehova, NW].” Akumalingalira ndi munthuyo, iwo anamthandiza kumvetsetsa bwino makonzedwe a Mulungu kaamba ka chipulumutso.—Machitidwe 16:32.
“Ukhulupirire Ambuye Yesu”
Amishonale Achikristu amenewo anatsegula maganizo a wosunga ndendeyo kuwona chowonadi chamaziko chonena za chipulumutso. Chinali chowonadi chimodzimodzicho chimene mtumwi Petro analongosola pamene mpingo Wachikristu unakhazikitsidwa poyambapo. Petro anasonya ku mbali yeniyeni ya Yesu Kristu mu nkhani ya chipulumutso, akumamutcha “Mkulu wa moyo.” Mtumwiyo anatinso: “Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 3:15; 4:12) Paulo ndi Sila anatsogolera wosunga ndende wa ku Filipiyo kwa Mkulu mmodzimodziyo wa chipulumutso pamene iwo anati: “Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka.”—Machitidwe 16:31.
Komabe, kodi kumatanthauzanji, kukhulupirira Ambuye Yesu? Kodi nchifukwa ninji palibe dzina lirilonse kusiyapo la Yesu mwa limene tingapulumukire? Kodi potsirizira pake aliyense adzafikira chipulumutso? Kodi atumwiwo anakhulupirira lingaliro la “ukapulumutsidwa kamodzi, wapulumutsidwa nthaŵi zonse”? Amenewa ali mafunso ofunika popeza kuti, mosasamala kanthu za chenicheni chakuti mawu ndi zochita za atsogoleri achipembedzo ambiri amakono zaluluzitsa mawuwo, tifunikirabe chipulumutso. Tonsefe tifuna yankho lokhutiritsa, ndi lanzeru ku funso lakuti: ‘Kodi ndichitenji kuti ndipulumuke?’