-
Analalikira Uthenga Wabwino ku Tesalonika Movutikira KwambiriNsanja ya Olonda—2012 | June 1
-
-
Iwo “anakhamukira kunyumba ya Yasoni [yemwe ankasunga Paulo m’nyumba mwake], kukafuna atumwiwo kuti awatulutsire ku gulu lachipolowelo.” Koma atalephera kum’peza Paulo, anapita kwa akuluakulu a mzindawo. Choncho “anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: ‘Anthu awa amene abweretsa mavuto padziko lapansi kumene kuli anthu, tsopano akupezekanso kuno.’”—Machitidwe 17:5, 6.
Popeza mzinda wa Tesalonika unali likulu la chigawo cha Makedoniya, unkadzilamulira wokha pa zinthu zina ndi zina. Ena mwa anthu amene ankalamulira mzindawu anali anthu amene ankasankhidwa kusamalira nkhani zina ndi zina zochitika mumzindawu. ‘Olamulira a mzinda’b amenewa anali akuluakulu a boma ndipo anali ndi udindo waukulu wokhazikitsa bata mumzindamo komanso kuonetsetsa kuti simukuchitika zinthu zimene zingachititse kuti boma la Roma lilowererepo n’kuwalanda mwayi wochita zinthu zina. Choncho iwo ayenera kuti anakhumudwa atamva kuti pali anthu ena amene akuchita zinthu zimene zingasokoneze mtendere wa mumzindawu.
-
-
Analalikira Uthenga Wabwino ku Tesalonika Movutikira KwambiriNsanja ya Olonda—2012 | June 1
-
-
b M’mabuku achigiriki munalibe mawu amenewa. Komabe anthu anafukula zolemba zakale zokhala ndi mawu amenewa pamalo amene panali mzinda wa Tesalonika ndipo zina mwa zolembazi zinalembedwa m’nthawi ya atumwi. Zinthu zimenezi zimatsimikizira kuti nkhani za m’buku la Machitidwe ndi zolondola.
-