Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/1 tsamba 27-32
  • Chaka Choliza Lipenga cha Akristu Chifika Pachimake mu Zaka Chikwi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chaka Choliza Lipenga cha Akristu Chifika Pachimake mu Zaka Chikwi
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nsembe Kaamba ka Onse!
  • 1919​—Ufulu Woyambirira
  • Chaka Choliza Lipenga Kaamba ka Mamiliyoni
  • Mbali Zokwezeka za Chaka Choliza Lipenga cha Akristu
  • Pambuyo pa Kufika Pachimake kwa Zaka Chikwi kwa Chaka Choliza Lipenga
  • Chaka Choliza Lipenga cha Yehova—Nthawi Yathu Yakusangalala
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yehova Anakonza Zoti Tikhale ndi Ufulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Chaka cha Ufulu Komanso Ufulu Womwe Tidzakhale Nawo M’tsogolo
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/1 tsamba 27-32

Chaka Choliza Lipenga cha Akristu Chifika Pachimake mu Zaka Chikwi

1. Kodi nchiyani chomwe Ayuda a ku Republic ya ku Israel sanayese kukhazikitsanso, ndipo nchifukwa ninji?

NGAKHALE mu Republic la Israel (yokhazikitsidwa mu 1948), Ayuda ambiri omwe amadzilingalira iwo eni kukhala ali pansi pa Chilamulo cha Mose sanakhazikitsenso chikondwerero cha Chaka Choliza Lipenga. Ndipo pangakhale zopotoka zambiri ngati iwo atayesera kutero. Mavuto a zachuma okulira angayambe, popeza chiyenerero cha katundu chikulowetsedwamo. Republic la Israel silimalamulira dziko lonse lomwe linakhalidwa ndi mafuko 12 akale. Kulibekonso kachisi wokhala ndi wansembe wamkulu wa fuko la Levi, popeza kuti zizindikiritso za mafuko a anthuwo zinataika.

2. Ndi motani m’mene Akristu ena anayamba kale kukumbukira Chaka Choliza Lipenga chophiphiritsidwa ndi chija cha Israyeli wakale?

2 Kodi ndi kuti kumene chimenecho chimatisiya ife, pomwepo, ponena za madalitso akukumbukira Chaka Choliza Lipenga? Tikukumbukira kuti Chaka Choliza Lipenga chakale chinali phwando la pa chaka laufulu​—Aisrayeli omwe anadzigulitsa iwo okha ku ukapolo ana masulidwa ndipo dziko lacholowa linabwezeretsedwa. (Levitiko 25:8-54) Mu nkhani yapitayo tinaona kuti kakonzedwe kameneka kanatha limodzi ndi chipangano cha Chilamulo cha Mose mu 33 C.E. (Aroma 7:4, 6; 10:4) Kenaka chipangano chatsopano chinakhazikitsidwa kumene Mulungu akanakhululukira machimo a anthu okhulupirira, kuwadzoza iwo ndi mzimu woyera, ndi kuwalandira iwo monga ana ake kuwatenga kupita kumwamba. (Ahebri 10:15-18) Komabe mwakutero awo opindula kuchoka ku kakonzedwe ka chipangano chatsopano ndi a “kagulu ka nkhosa” a 144, 000 “omwe agulidwa kuchokera ku dziko lapansi.” Chotero ndi motani m’mene mamiliyoni a Akristu ena omvera angapezere ufulu wophiphiritsidwa ndi Chaka Choliza Lipenga?​—Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1-4.

Nsembe Kaamba ka Onse!

3. Kodi nsembe ya Yesu iri yokhutiritsa motani ndipo ya utali wotani?

3 Mu nthawi imene Chikristu chisanayambe, pindulitso la Tsiku la Chitetezero la chaka ndi chaka linatha kwa chaka chimodzi chokha. Mapindu a nsembe ya dipo ya Ambuye Yesu Kristu akupitirizabe, ku nthawi zonse. Chotero Wansembe Wamkulu, Yesu, sanafunikira kukhalanso munthu kachiwiri, akudzipereka iye mwini, ndipo kenaka kubwerera kumwamba kukapereka mtengo wa nsembe yake cha ka ndi chaka kwa Mopatulikitsa mwa Yehova Mulungu. Monga m’mene Malemba amanene ra: “Kristu, [popeza tsopano, NW] anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa sichitanso ufumu pa iye.”​—Aroma 6:9; Ahebri 9:28.

4, 5. (a) Kodi ndi choturukapo chotani chomwe chakhalapo mwakugwiritsira ntchito nsembe ya Yesu kuchokera pa Pentekoste wa 33 C.E.? (b) Tiri ndi chizindikiritso chotani chakuti nsembe yake idzagwiritsidwa ntchito mokulirapo?

4 Chotero, mu zaka kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene okhulupirira anakhala ophunzira odzozedwa ndi mzimu wa Ambuye Yesu wokwezedwa, iwo anayamba kukumbukira Chaka Choliza Lipenga cha Chikristu. Pa mene ‘anamasulidwa kuchokera ku lamulo lauchimo ndi la imfa,’ iwo asangalala ndi ufulu wolimbikitsa. (Aroma 8:1, 2) Iwo alengezanso uthenga wa Chikristu kotero kuti ena anga khululukidwenso machimo awo, kudzozedwa, ndipo kukhala ana a uzimu a Mulungu. Kodi ichi chimatanthauza, kuti, ngati wina sali gulu lokhazikitsidwala 144, 000, iye sangasangalale ndi ufuluwo tsopano?

5 Odziwikiratu m’chigwirizano ichi ndiwo mau a mtumwi Paulo pa Aroma 8:19-21: “Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindilira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chigonjetsedwa kuutsiru, [kukhala ochimwa ndipo osakhoza kuchotsa chimo.]” Paulo anagogomezera kuti panali “chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi ku lowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” Ufulu wotero, motero, siuli kokha kwa awo omwe akukhala “ana a Mulungu,” kumwamba. Mau ozolowereka a pa Yohane 3:16 amatsimikizira chimenecho. Ndipo, monga kwatchulidwa, mtumwi Yohane wodzozedwa ananena kuti Kristu anafa “kaamba ka machimo athu, koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi”—​1 Yohane 2:2.

1919​—Ufulu Woyambirira

6, 7. Kuyambira mu 1919, kodi ndi ufulu wa mtundu wanji womwe wakhala uli kulalikidwa, ndipo ndi chifukwa ninji makamaka kuyambira pamenepo?

6 Mu nthawi za makono odzozedwa omwe akukumbukira Chaka Choliza Lipenga cha Akristu akhala akulengeza mbiri yabwino ya ufumu, makamaka kuyambira mu 1919. ‘Chifukwa ninji kuyambira nthawi imeneyo?’ Mwina mungadabwe ngati munabadwa posachedwapa. Tiyeni tiwone, kusunga m’maganizo kuti chikondwerero chanu cha ufulu chikulo wetsedwamo.

7 Kwa zaka makumi ochuluka lisanafike tsiku limenelo, odzozedwa a Yehova analengeza chowonadi cha Baibulo, monga ngati chomwe chiri mu ndandanda ya Studies in the Scrip tures (1886-1917). Iwo anagawiranso timabu ku topatsa chidziwitso ndi matrakiti. Mkati mwa Nkhondo ya Dziko I, kunabwera chitsu tso, kuyesedwa ndi kusefedwa, ndi kufooka kwa ntchito zawo. Koma mu 1919 otsalira odzozedwa anapita patsogolo ndi changu cha tsopano cha kulalikira chowonadi cha Baibulo Monga momwe Yesu mu 30 C.E. akananena kuti iye anadzozedwa kulalikira “kumasulidwa kwa andende ndi kubwezeretsedwa kupenya kwa akhungu,” mo fananamo odzozedwa amakonowa akanatero. Pambuyo pa msonkhano wosangalatsa pa September 1-7, 1919,a iwo anapitirizabe patsogolo mu ntchito yo lalikira chowonadi chomwe chinamasula anthu osawerengeka.​—Luka 4:18.

8, 9. Ndi mwalingaliro lotani m’mene ambiri amasulidwira, ndipo ndi zithandizo zotani zo mwe zagwiritsidwa ntchito kulalikira ufulu ume newo?

8 Talingalirani, mwachitsanzo, chothandizira kuphunzira Baibulo Zeze wa Mulungu (1921), lomwe linapereka chowonadi chofunika kwambiri monga ngati kuti zinali zingwe khumi pa zeze. Bukhulo linazindikiritsa kuti “ambiri anaopsyezedwa kuliphunzira Baibulo” mwa ziphunzitso zakuti “chilango kaamba ka woipa . . . chinali chitonzo kapena chizunzo mu helo woyaka ndi moto wosazimika ndi sulfure.” Awerengi amakope chifupifupi 6, 000, 000 a bukhu limeneli anaphunzira kuti chiphunzitso chimenecho “sichikanakhala chowona kwa chifupifupi zifukwa zinayi zosiyana ndipo zodzi wika bwino: (1) chifukwa chiri chosamveka; (2) chifukwa chiri chotsutsana ndi chilungamo; (3) chifukwa chiri chosemphana ndi prinsipulo la chikondi; ndipo (4) chifukwa chiri kotheratu chopanda malemba.” Mungalingalire ndi chimasuko chotani m’mene icho chinaliri kwa anthu omwe anakula m’mantha a chizunzo cha muyaya mu helo kapena kubuula mu purigatoriyo!

9 Inde, kulalikira kwa changu kwa chowonadi cha m’Baibulo ndi odzozedwa amenewa ku namasula anthu kuzungulira dziko lonse lapansi omwe anali akapolo ku ziphunzitso zonyenga, kumatsenga, ndi zochitachita zopanda malemba (monga ngati kulambira makolo, ku opa mizimu kapena mizimu yoipa, ndi kubeledwa kwa ndalama ndi atsogoleri a chipembedzo.) Mitu yeniyeni ya zina zazothandizira kuphunzira Baibulo zimaunikira mphamvu ya kumasula yomwe inali nayo pa mamiliyoni ambirib Chotero mau a Yesu anatsimikizira kukhala owona, pamene iye ananena kwa ophunzira ake kuti ‘adzachita ntchito zokulira’ kuposa m’mene iye anachitira. (Yohane 14:12) Kuyerekezedwa ndi ntchito yoyambirira yomasula ya uzimu yomwe Yesu anachita m’kulalikira mwa “kumasula andende,” atumiki a Mulungu amakono aichita iyo ku mlingo wokulira—kumafikira mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi.

10. Ndi chifukwa ninji tingayembekezere ufulu woonjezera ndipo wokulirapo womwe udzakuma nizidwa?

10 Takumbukirani, ngakhale kuli tero, kuti mu zana loyamba kumasula kopitirizapo kuna yamba pa Pentekoste wa 33 C.E. Pamenepo Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chinayamba kwa “kagulu ka nkhosa” omwe machimo awo anakhululukidwa, kutsogolera ku kukhala kwawo “ana a Mulungu” kumwamba. Bwanji ponena za m’nthawi yathu? Kodi mamiliyoni a Akristu ena odzipereka angamasulidwe kuchokera ku ukapolo wa chimo ndipo mwakutero kukumbukira chaka chachikulu Choliza Lipenga? Inde, ndipo mtumwi Petro anasonyezachimenecho pamene iye analankhula ponena za “nthawi zakudzanso zinthu zonse zimene Mulungu analankhula za izo mkamwa mwa aneneri ache oyera [akale, NW].”​—Machitidwe 3:21

Chaka Choliza Lipenga Kaamba ka Mamiliyoni

11. Ndi motani m’mene Levitiko mutu 25, amaperekera lingaliro lakuti tingayang’ane kutsogolo kaamba ka ufulu womwe umapitirira ufulu wa Israyeli wauzimu?

11 Chiri chozindikirika kuti kawiri mu Levitiko mutu 25 Aisrayeli anakumbutsidwa kuti kuchokera m’kayang’anidwe ka Yehova iwo anali “akapolo” ake omwe iye anawamasula kuchokera ku Aigupto. (Versi 42 ndi 55) Mutu wa Chaka Choliza Lipenga umenewu umatchulanso “nzika” ndi ‘alendo okhala pakati pawo.’ Oterowo amapeza kufananako lerolino ndi “khamu lalikulu” lomwe likugawana ndi Israyeli wa uzimu m’kulalikira mbiri yabwino ya Chikristu.

12. Kuyambira 1935, ndi zoturukapo za chimwe mwe zotani zomwe zakhala ziri kupita patsogolo?

12 Kuyambira mu 1935 “mbusa wabwino” Yesu Kristu wasonkhanitsa mumayanjano okangalika limodzi ndi otsalira odzozedwa awo amene iye akuwatchula kukhala “nkhosa zina.” Izi iye ayenera “kubweretsa,” ndipo zidzakhala “gulu limodzi” pansi pa “mbusam’modzi.” (Yohane 10:16) “Nkhosa zina” tsopano zafika chiwerengero cha mamiliyoni. Ngati muli wa khamu lachimwemwe limenelo, inu mukuwerengeredwa monga wolungama ngati bwenzi la Mulungu, ndipo monga mbali ya chilengedwe cha munthu, mukuyang’ana kutsogolo kudzakhala “omasulidwa ku ukapolo wa ku chivundi” mkati mwa kubwera kwa “nthawi ya kubwezedwanso kwa zinthu zonse” pa dziko lapansi. Ichi sichiri chiyembekezo chopanda maziko.​—Aroma 8:19-21; Machitidwe 3:20, 21.

13. Ndi dalitso liti limene mwapadera tingalizi ndikire kukhala likuoneka pambuyo pa “chisau tso chachikulu?”

13 Pamene mtumwi Yohane anaona 144, 000 omwe akusangalala ndi Chaka Choliza Lipenga cha Chikristu limodzi ndi chiyembekezo cha kumwamba, iye analongosola “khamu lalikulu,” akumati: “Awa ndi wo amene akutuluka m’chisautso chachikulu ndipo iwo achapa mi njiroyawo nayiyeretsa m’mwazi wa Mwanawa nkhosa. Ndicho chifukwa chache ali ku mpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amutumikira iye usana ndi usiku mu kachisi wache.”​—Chivumbulutso 7:14, 15.

14, 15. Nchifukwa ninji awo a “khamu lalikulu” ali ndi chifukwa chapadera cha kusangalalira tsopano?

14 Angakhale tsopano, pambuyo pa chisau tso chachikulu, awa akusonyeza chikhulupiriro mu mwazi wokhetsedwa wa Kristu ndipo mwakutero kupeza phindu kuchokera ku imfa yake yothira nsembe. Iwo amasangalalanso mwa kukhala atamasulidwa kuchokera ku Babulo Wamkulu, mwakukhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Yehova Mulungu, ndi m’mwayi wawo wakugawana m’kukwaniritsidwa kwa Mateyu 24:14 mwa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu mapeto asanafike

15 Komabe, bwanji ponena za ziyembekezo za khamu lalikulu pokhala litamasulidwa kuchoka ku chimo lobadwa nalo ndi kupanda ungwiro? Kodi nthawi imeneyo iri pafupi? Tiri ndi chifukwa chabwino cha kuona kuti tiri nawo pakati pathu ena ambadwo wa mtundu wa anthu umene Yesu Kristu ananeneratu kuti sudzatha mpaka zinthu zonse zimenezi zidza kwaniritsidwe. (Mateyu 24:34) Komabe, mapeto okulira a “mapeto a dongosolo ili la zinthu” ayenera kukhala ali pafupi kwenikweni.​—Mateyu 24:3.

Mbali Zokwezeka za Chaka Choliza Lipenga cha Akristu

16. Ndi kuti kumene tikuima mu kugwira ntchito kwa chifuno cha Mulungu, ndipo ndi chiyani chomwe chiri kutsogolo?

16 “Nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” ikubwera mwamsanga, ndipo otsalira a “kagulu ka nkhosa,” limodzinso ndi “khamu lalikuru” omwe ali anzawo okhulupirika, omvera adzapitiriza kusu nga umphumphu wawo kulinga kwa Yehova Mulungu ndi kuyang’ana kutsogolo kudzakhala ndi chitetezero cha umulungu. Iwo mwachidwi amadikirila kugonjetsa kophwanya kwa Yehova kwa magulu onse a adani, ku kuyeretsedwa kwake monga Wolamulira wa Dziko Lonse. Ndi mbali yoonekera chotani m’mene iyi idzakhalira ku chisangalalo cha ufulu wa Chikristu!​—Chivumbulutso 16:14; 19:19-21; Habakuku 2:3.

17. Ndi motani m’mene mamiliyoni adzalandilira ufulu mu Chaka Choliza Lipenga chokulirapo

17 Ulamuliro wa Mfumu yopambana Yesu Kristu pa dziko loyeretsedwa udzatsatira, limodzi ndi kulamulira kwa dziko lonse kwa Yehova kutakhazikitsidwanso, ndipo limodzi ndi Yesu Kristu akulamulira dziko lonse lapa nsi monga Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Kenaka iye mwachindunji adzagwiritsira ntchito choyenera cha nsembe yake kwa mamiliyoni a anthu, kuphatikizapo oukitsidwakuchoka kwa akufa, omwe adzasonyeza chikhulupiriro ndipo omwe modzipereka adzalandira kukhululukidwa kwa machimo komwe Mulungu adzapereka kudzera mwa Kristu. Ichi chidzatsimikiziridwa pamene Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipa dzakhalanso maliro kapena kulira kapena zo wawitsa.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Ngati chimenecho sichiri ufulu weniweni, kodi ndi chiyani?

18. Kuyerekeza ndi chochitika cha mu Chaka Choliza Lipenga chakale, ndi chiyani chomwe chidzaoneka pa dziko lapansi mu dongosolo latso pano la zinthu?

18 Kuwonjezerapo, dziko lapansi silidzala muliridwa, kuonongedwa, ndi kusakazidwa ndi anthu aumbombo, magulu, ndi maboma a anthu. (Chivumbulutso 11:18) Koma, m’malo mwake, lidzabwezeretsedwa kwa olambira owona. Iwo adzaikidwa oyang’anira limodzi ndi ntchito zopatsa chisangalalo m’kugawana m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesaya: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yamphesa ndi kudya zipatso zache. Iwo sadzamanga ndi wina kukhalamo; ndipo sadzaoka ndi wina kudya. . . iwo sadzagwira ntchito pachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndi wo mbeu ya odalitsidwa a Yehova.” (Yesaya 65:21-25) Pofika ku mapeto kwa Zaka Chikwi za Ufumu, zotsatira zonse za chimo lacholowa limodzi ndi kupanda ungwiro zidzakhala zitachotsedwa kotheratu ndipo omvera a Mulungu pa dziko lapansi adzakondwerera kufika pachimake kwenikweni ku mene Chaka Choliza Lipenga chidzathera. Chotero ufulu wophiphiritsidwa ndi Chaka Choliza Lipenga udzakhala utakwaniritsidwa.​—Aefeso 1:10.

Pambuyo pa Kufika Pachimake kwa Zaka Chikwi kwa Chaka Choliza Lipenga

19, 20. Ndi motani m’mene Satana limodzi ndi ziwanda adzayesera kusokoneza madalitso omwe adzaturukapo kuchokera ku Chaka Choliza Lipe nga cha Zaka Chikwi, koma ndi choturukapo chotani?

19 Chivumbulutso 20:1-3 imaneneratu kuti Satana Mdyerekezi, wolamulira wa malo aziwanda, adzachotsedwapo kwa nyengo ya zaka chikwi za kulamulira kwa Kristu pakati pa anthu. Pamene, Mdyerekezi limodzi ndi ziwanda zache adzaloledwa pakanthawi kubweranso, pa mapeto pa Zaka Chikwi, mizimu yoyipa imeneyi idzaona dziko lapansi, osati mu mkhalidwe umene iyo inalisiira, koma kukongola kosaneneka, paradaiso wa dziko lonse lapansi. Iyo idzaona dziko lapansi lokhalidwa ndi “khamu lalikulu” lokhulupirika ndi mabiliyoni a anthu oukitsidwa kuchokera kwa akufa amene Yesu Kristu anafera monga nsembe ya dipo. Pofika ku mapeto kwa Zaka Chikwi, Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chidzakhala chitafikira cholinga chake chakumasula kotheratu mtundu wa anthu kuchokera ku zoturukapo za chimo. (Aroma 8:21) Chidzakhala chochiti tsa manyazi mwa uchiwanda motani kwa wina aliyense kuyesa kuononga mkhalidwe wabwino umenewu! Koma mwachilolezo cha Mulungu wamphamvuyonse, Mdyerekezi adzakupanga kuyesa komalizira kupanga chimenechi, ndipo m’kuwawidwa kosaphula kanthu iye adzamenya. Ku mlingo umenewu chalembedwa pa Chivumbulutso 20:7-10, 14:

20 “Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi adzamasulidwa Satana m’ndende yache, natuluka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawaso nkhanitsa achite nkhondo. Chiwerengero cha wo cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja. Ndipo anakwera nafalikira m’dziko nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi woko ndedwawo. Ndipo unatsika moto kumwamba nuwanyeketsa. Ndipo Mdyerekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure

21. Pambuyo pa mapeto a Chaka Choliza Lipenga cha Chikristu limodzi ndi Zaka Chikwi, ndi yankho lotani lopangidwa ndi ana a Mulungu a kumwamba lomwe lidzakumbukiridwa la Yobu 38:7?

21 Ufulu weni weni, wobweretsedwa mwa makonzedwe a Chaka Choliza Lipenga, udzapitirira kusangalalidwa kuli konse; zolengedwa zonse zidzakhala za ufulu ndipo zidzalemekeza amene iye yekha ali ndi dzina lakuti Yehova. (Masalmo 83:18) Chimenecho chidzakhala chowona pamene Yehova apitirizabe kuchita zifuno zake kuzungulira dziko lonse lapansi. Pa kulengedwa kwa dziko lapansi, mtundu wa anthu usanakhazikitsidwe pa ilo, “nyenyezi za m’mawa zinayimba limodzi mokondwera, ndipo ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe” pa kuoneka kokongola. (Yobu 38:7) Ndi mokulira chotani nanga m’mene iwo adzachitira chimenecho mwakuona dziko lapansi lokhalidwa ndi amuna ndi akazi omwe asonyeza ndi kutsimikizira kudzipereka kwawo kotheratu ndi umphumphu wawo wa Mulungu wamphamvuyonse.

22. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala kaimidwe kathu, m’chigwirizano ndi chitamando chopezeka pa Masalmo 150:1-6?

22 Zinthu zonse kukhala zitatengedwa m’chiwerengero cha kuwala konka mtsogolo komwe kukuperekedwa pa Malemba, ife sitingachitire mwina mwake koposa kutumpha ndi chimwemwe mwamsanga limodzi ndi miyamba ndi kunena, Haleluya! Ili ndi chenjezo kwa ife limene bukhu la Masalmo likutseka nalo: “Haleluya. Lemekezani Mulungu m’malo ache oyera; mlemekezeni m’thambo la mphamvu yache. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zache zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wache waunjinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mle mekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang’ombe; mlemekezeni ndi zoyimbira za zingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka; mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemekeze Ambuye. Haleluya.”​—Masalmo 150:1-6, Tanakh Bible (1985), Jewish Publication Society ya ku America.

[Mawu a M’munsi]

a Magazini yatsopano inatulutsidwa kumeneko yomwe ikanadzakhala “monga liu mu chipululu cha chisokonezo, ntchito yake [kukhala] kulengeza Zaka Zokoma ziri nkudza.” Lerolino magazini imeneyo ikutchedwa Galamukani!

b Millions Now Living Will Never Die (1920); Deliverance (1926); Freedom for the Peoples (1927); Liberty (1932); “The Truth Shall Make You Free” (1943); What Do the Scriptures Say About “Survival After Death”? (1955); Moyo Wosatha​—Mu Ufulu wa Ana a Mulungu (1966); Coonadi Cimene Cimatsogo lera ku Moyo wa Muyaya (1968); The Path of Divine Truth Leading to Liberation (1980).

Kodi Mukanayankha Motani?

◻ Kodi nkuchokera ku chiyani komwe ophunzira a Yesu anamasulidwa pa Pentekoste wa 33 C.E., kuloza ku ku yambidwa kwa chiyani kaamba ka iwo?

◻ Nchifukwa ninji pali chifukwa cha kuyembekezerera ufulu wokulirapo ku posa womwe unaoneka mu zana loya mba?

◻ Kodi ndi chimasuko cha mtundu wa nji chomwe chakhala chiri kuchitika ku yambira 1919?

◻ Ndi motani ndipo ndi liti pamene “nkhosa zina“ zidzapindula kuchokera ku Chaka Choliza Lipenga chokulira?

◻ Pambuyo pakufika pachimake kwa Chaka Choliza Lipenga, kodi dziko la pansi lidzakhala ngati chiyani?

[Chithunzi patsamba 29]

Ufulu wolalikidwa pa Cedar Point, 1919

[Chithunzi patsamba 30]

“Nkhosa zina” zigawana mu Chaka Choliza Lipenga cha Zaka Chikwi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena