-
Baibulo Limatiuza Wolamulira wa DzikoliNsanja ya Olonda—2011 | September 1
-
-
Kuchokera nthawi imeneyo, Mdyerekezi akudziwa kuti watsala pang’ono kuwonongedwa. Ngakhale kuti ‘dziko lonse lili m’manja mwake,’ pali anthu mamiliyoni ambiri masiku ano amene akukana ulamuliro wake. Izi zili choncho chifukwa Baibulo lawatsegula m’maso kuti am’dziwe bwinobwino Mdyerekezi komanso kuti adziwe ziwembu zake. (2 Akorinto 2:11) Iwo amakhala ndi chiyembekezo akakumbukira mawu amene Paulo analembera Akhristu anzake, akuti: “Mulungu amene amapatsa mtendere aphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwapa.”b—Aroma 16:20.
-
-
Baibulo Limatiuza Wolamulira wa DzikoliNsanja ya Olonda—2011 | September 1
-
-
b Mawu a Paulo amenewa ndi ofanana ndi ulosi woyambirira wa m’Baibulo wolembedwa pa Genesis 3:15 umene umasonyeza kuti Mdyerekezi adzawonongedwa. Pofotokoza zimene zidzachitikezo, Paulo anagwiritsa ntchito mawu achigiriki amene amatanthauza “kuswa chinthu n’kukhala zidutswazidutswa.”—Vine’s Complete Expository Dictionary of Old and New Testament Words.
-