Yehova Akugwiritsira Ntchito “Chopusa” Kupulumutsa Okhulupirirawo
“Pakuti popeza m’nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziŵa Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirawo mwa chopusa cha kulalikira.”—1 AKORINTO 1:21.
1. Kodi ndim’lingaliro lotani limene Yehova akagwiritsirira ntchito “chopusa,” ndipo tidziŵa motani kuti dzikoli mwa nzeru zake silinamdziŵe Mulungu?
CHIYANI? Kodi Yehova angagwiritsire ntchito chopusa? Osati kwenikweni! Koma angatero ndipo amagwiritsira ntchito chimene chimawonekera kukhala chopusa kudziko. Amatero kotero kuti apulumutse anthu amene amamdziŵa ndi kumkonda. Mwanzeru yadziko, dziko silingakhoze kudziŵa Mulungu. Yesu Kristu anamveketsa zimenezi pamene ananena m’pemphero kuti: “Atate wolungama, dziko lapansi silinadziŵa Inu.”—Yohane 17:25.
2. Kodi zingawoneke motani kuti njira za Yehova ndi za dziko zikugwirizana, koma kodi zenizeni nzotani?
2 Mawu a Yesu amasonyeza kuti njira za Yehova nzosiyana ndi za dziko. Mawonekedwe akunja angasonyeze monga ngati chifuno cha Mulungu ndi cha dzikoli nzogwirizana. Kungawonekere kuti zolinga za dzikoli ziri ndi dalitso la Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Mulungu adzakhazikitsa boma lolungama limene lidzadzetsa mtendere, chimwemwe, ndi kukhupuka kwa mtundu wa anthu padziko lapansi. (Yesaya 9:6, 7; Mateyu 6:10) Mofananamo, dziko likulengeza chifuno chake cha kupatsa anthu mtendere, kukhupuka, ndi boma labwino mwanjira yotchedwa dongosolo latsopano ladziko. Koma zifuno za Mulungu ndi zija za dziko ziri zosiyana. Chifuno cha Mulungu ndicho kuti alemekezeke monga Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chaponseponse. Adzachita chimenechi mwakugwiritsira ntchito boma lake lakumwamba limene lidzafafaniza maboma onse adziko lapansi. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 4:11; 12:10) Chotero Mulungu alibe kanthu kalikonse kogwirizana ndi dzikoli. (Yohane 18:36; 1 Yohane 2:15-17) Ndicho chifukwa chake Baibulo limanena za mitundu iŵiri yanzeru—“nzeru ya Mulungu” ndi “nzeru yadziko.”—1 Akorinto 1:20, 21.
Cholakwika Chachikulu ndi Nzeru Yadziko
3. Ngakhale kuti nzeru ya dziko ingawoneke kukhala yochititsa chidwi, kodi nchifukwa ninji dongosolo latsopano ladziko lolonjezedwa ndi anthu silingakhale lokhutiritsa?
3 Kwa awo amene satsogozedwa ndi nzeru ya Mulungu, nzeru yadziko imawonekera kukhala yokondweretsa. Pali nthanthi zadziko zomveka zolemekezeka zimene zimakopa malingaliro a anthu. Pali zikwi zambiri za masukulu a maphunziro apamwamba opereka chidziŵitso chochokera kwa anthu amene ambiri amawalingalira kukhala anzeru zakuya zaumunthu. Malaibulale aakulu ngodzaza thothotho ndi chidziŵitso chosonkhanitsidwa cha zochitika za anthu m’mazana ambiri azaka. Komabe, mosasamala kanthu ndi zimenezi, dongosolo latsopano ladziko limene olamulira adziko akulilingalira lingakhale kokha ulamuliro wa anthu opanda ungwiro, othimbirira ndi uchimo, anthu amene amafa. Chifukwa chake, dongosolo limenelo likakhala lopanda ungwiro, likumabwereza zophophonya zambiri zakale ndipo losakwaniritsa zosoŵa zonse za anthu.—Aroma 3:10-12; 5:12.
4. Kodi dongosolo latsopano ladziko lolingaliridwa ndi anthu likaipitsidwa ndi chiyani, ndipo ndi chotulukapo chotani?
4 Dongosolo latsopano ladziko lolingaliridwa ndi anthu silingaipitsidwe kokha ndi zofooka za anthu komanso ndi zolengedwa zauzimu zoipa—inde, Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda zake. Satana wachititsa khungu malingaliro a anthu kotero kuti asakhulupirire “uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu.” (2 Akorinto 4:3, 4; Aefeso 6:12) Chotulukapo chake, dziko likukanthidwa ndi mavuto otsatizanatsatizana. Pamene likulimbana ndi mavutowo, dziko likuvutika ndi zotulukapo zake zopweteka mkuyesayesa kwake kwatsoka kudzilamulira popanda chithandiza cha Mulungu ndi popanda kulingalira chifuno chaumulungu. (Yeremiya 10:23; Yakobo 3:15, 16) Motero, monga momwe mtumwi Paulo ananenera, ‘mwanzeru yake dziko silinadziŵa Mulungu.’—1 Akorinto 1:21.
5. Kodi cholakwika chachikulu ndi nzeru ya dzikoli nchiyani?
5 Pamenepa, kodi nchiyani chiri cholakwika chachikulu ndi nzeru ya dziko lino, kuphatikizapo zolinganiza zake za dongosolo latsopano ladziko? Ndicho chakuti dziko limanyalanyaza chimene sichingathe kunyalanyazidwa ndi kupezabe chipambano—ufumu waukulu koposa wa Yehova Mulungu. Limakana mouma khosi kuzindikira ufumu waumulungu. Dzikoli mwadala limasiya Yehova m’zolinganiza zake zonse ndi kudalira pa luso ndi makonzedwe ake. (Yerekezerani ndi Danieli 4:31-34; Yohane 18:37.) Baibulo limasonyeza momvekera bwino kuti “chiyambi cha nzeru ndicho kuwopa Mulungu.” (Miyambo 9:10; Salmo 111:10) Komabe, dziko silinaphunzire chofunikira chachikulu chimenechi cha nzeru. Chifukwa chake, popanda chichirikizo chaumulungu, kodi lingapambane bwanji?—Salmo 127:1.
Kulalikira Ufumu Nkupusa kapena Nkopindulitsa?
6, 7. (a) Kodi amene akutsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu akulalikira chiyani, koma kodi dziko limawawona motani? (b) Kodi atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko amalalikira malinga ndi nzeru ya yani, ndipo ndi chotulukapo chotani?
6 Kumbali ina, awo amene amadziŵa Mulungu amasonyeza nzeru ya Mulungu ndi kusankha kutsogozedwa nayo. Monga momwe Yesu ananenera, akulalikira “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu . . . m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” (Mateyu 24:14, NW; 28:19, 20) Kodi kulalikira kumeneko nkopindulitsa tsopano, pamene dziko lathu lapansi ladzala ndi upandu, kuipitsidwa, umphaŵi, ndi kuvutika kwa anthu? Kwa anzeru adziko kulalikira kumeneku kwa Ufumu wa Mulungu kumawonekera kukhala kupusa kwenikweni, kosapindulitsa. Amalingalira olalikira Ufumu wa Mulungu monga anthu opandapake amene amadodometsa boma ndi kuchedwetsa kupita patsogolo kwake kofikira boma la ndale zadziko labwinopo. Mzimenezi amachirikizidwa ndi atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko, amene amalalikira mogwirizana ndi nzeru yadziko ndipo samauza anthu zimene afunikira kuti adziŵe za dziko latsopano la Mulungu ndi boma lake la Ufumu, ngakhale kuti zimenezi ndizo zinali chiphunzitso chachikulu cha Kristu.—Mateyu 4:17; Marko 1:14, 15.
7 Wolemba mbiri H. G. Wells ananena za kulephera kumeneku kwa atsogoleri achipembedzo a chikristu Chadziko. Analemba kuti: “Chowonekeratu poyera ndicho kufunika kwakukulu kumene Yesu anakuika pa kuphunzitsa za chimene iye anachitcha Ufumu Wakumwamba, ndi kulephera kwa matchalitchi ambiri Achikristu m’kachitidwe ndi kaphunzitsidwe kawo.” Komabe, ngati anthu a mbadwo uno ayenera kupeza moyo, choyamba ayenera kumva za Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu, ndipo kuti akwaniritse zimenezo, munthu ayenera kulalikira mbiri yabwino ya Ufumuwo.—Aroma 10:14, 15.
8. Kodi nchifukwa ninji kulalikira mbiri yabwino ya Mulungu kuli chinthu chopindulitsa kwambiri kuchita lerolino, koma kodi nkachitidwe kotani kamene kangakhale kosapindulitsa?
8 Pamenepa, kulalikira mbiri yabwino ya Mulungu, ndiko chinthu chopindulitsa kwambiri kuchita lerolino. Zimenezi ziri choncho chifukwa chakuti uthenga wa Ufumu umapereka chiyembekezo chenicheni chimene chimadzaza mitima ya anthu ndi chisangalalo mkati mwa masiku otsiriza ano pamene kuli “nthaŵi zowaŵitsa” kuchita nazo. (2 Timoteo 3:1-5; Aroma 12:12; Tito 2:13) Pamene kuli kwakuti moyo m’dzikoli ngwokaikiritsa ndi waufupi, moyo m’dziko latsopano la Mulungu udzakhala wosatha, wozunguliridwa ndi chisangalalo, zakudya zochuluka, ndi mtendere pompano padziko lapansi. (Salmo 37:3, 4, 11) Monga momwe Yesu Kristu ananenera, “Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wache?” Ngati munthu ataya kuyenera kwa kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu, kodi dzikoli limene likuchoka limakhala ndi phindu lanji? Chisangalalo cha munthu wotero cha nthaŵi ino cha zinthu zakuthupi chiri chopandapake, chosaphula kanthu, ndi chonyenga.—Mateyu 16:26; Mlaliki 1:14; Marko 10:29, 30.
9. (a) Pamene mwamuna amene anaitanidwa kukhala wotsatira wa Yesu anapempha kusiidwa kwakanthaŵi, kodi Yesu anamlangiza kuchitanji? (b) Kodi yankho la Yesu liyenera kutiyambukira motani?
9 Mwamuna wina amene Yesu anamuitana kuti akhale wotsatira wake anati: “Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga.” Kodi Yesu anamlangiza kuchitanji? Podziŵa kuti munthuyo akakhala akusiya ntchito yofunika kwambiri kokha kuti akadikirire kufikira makolo ake atafa, Yesu anayankha kuti: “Leka akufa aike akufa eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:59, 60) Awo amene amasonyeza nzeru mwakumvera Kristu sangaleke kukwaniritsa ntchito yawo yakulalikira uthenga Waufumu. Nzeru yaumulungu imawapangitsa kudziŵa kuti dzikoli ndi olamulira ake ali pamzere wachiwonongeko. (1 Akorinto 2:6; 1 Yohane 2:17) Ochirikiza ufumu wa Mulungu amadziŵa kuti chiyembekezo chowona chokha cha anthu chiri mkuloŵera kwa Mulungu ndi ulamuliro wake. (Zekariya 9:10) Chotero pamene kuli kwakuti awo okhala ndi nzeru zadziko lino samakhulupirira Ufumu wa Mulungu ndipo samafuna boma lakumwamba limenelo, anthu amene amatsogozedwa ndi nzeru yaumulungu amachita zimene zimadzetsa mapindu enieni kwa anthu anzawo, kuwakonzekeretsa moyo wosatha m’dziko latsopano lolonjezedwa ndi Yehova.—Yohane 3:16; 2 Petro 3:13.
“Chinthu Chopusa kwa Iwo Akutayika”
10. (a) Pamene Saulo wa ku Tariso anatembenuzidwa, kodi anayamba ntchito yotani, ndipo kodi anaiwona motani? (b) Kodi Agiriki amakedzana anali otchuka ndi chiyani, koma kodi ndimotani mmene Mulungu anawonera nzeru yawo?
10 Saulo wa ku Tariso, amene anakhala Paulo mtumwi wa Yesu Kristu, analoŵa ntchito imeneyo yopulumutsa moyo. Kodi nkwanzeru kuganiza kuti pamene Yesu Kristu anatembenuza Saulo, Iye anali kumgaŵira kuchita ntchito yopusa? Paulo sanaganize choncho. (Afilipi 2:16) Panthaŵi imeneyo Agiriki anali kulingaliridwa kukhala amuna anzeru koposa padziko lonse. Anadzitama chifukwa cha anthanthi awo apamwamba ndi anthu anzeru. Ngakhale kuti Paulo analankhula Chigiriki, sanatsatire nthanthi za Chigiriki ndi kuziphunzira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti nzeru yotero yadziko lino njopusa kwa Mulungu.a Paulo anafuna nzeru yaumulungu, imene inamsonkhezera kulalikira mbiri yabwino kunyumba ndi nyumba. Wolalikira Wamkulu woposa onse, Yesu Kristu, anakhazikitsa chitsanzo ndipo anamlangiza kuchita ntchito yofananayo.—Luka 4:43; Machitidwe 20:20, 21; 26:15-20; 1 Akorinto 9:16.
11. Kwenikweni, nchiyani chimene Paulo ananena ponena za ntchito yake yakulalikira ndi nzeru ya dziko?
11 Paulo ananena zotsatirazi ponena za ntchito yake yakulalikira: “Pakuti Kristu sanandituma . . . kulalikira uthenga wabwino, si mu nzeru ya mawu, kuti mtanda wa Kristu ungayesedwe wopanda pake. Pakuti mawu a mtanda [nsembe yadipo ya Yesu] ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tiri kupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu. Pakuti kulembedwa, Ndidzawononga nzeru za anzeru, Ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha. Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi? Pakuti popeza m’nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziŵa Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirawo mwa chopusa cha kulalikira.”—1 Akorinto 1:17-21.
12. Kodi Yehova akukwaniritsanji mwa “chopusa cha kulalikira,” ndipo kodi ofuna “nzeru yochokera kumwamba” adzachitapo kanthu motani?
12 Ngakhale kuti zikumveka zodabwitsa, awo amene dziko limawatcha opusa ndiamene Yehova amawagwiritsira ntchito monga alaliki ake. Inde, mwa chopusa cha utumiki wa olalikira ameneŵa, Mulungu amapulumutsa amene amakhulupirira. Yehova amalinganiza zinthu kotero kuti olalikira “chopusa” samadzitamandira, ndipo anthu ena samatamanda awo amene anawalalikira mbiri yabwino. Zimenezi ziri choncho kuti “thupi lirilonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.” (1 Akorinto 1:28-31; 3:6, 7) Ndithudi, wolalikira amachita mbali yofunika, koma uthenga umene iye wapatsidwa kuti alalikire ndiwo umapezetsa chipulumutso ngati munthuyo aukhulupirira. Amene amafuna “nzeru yakumwamba” sadzanyalanyaza uthenga wa wolalikirayo chifukwa chakuti akuwonekera monga wopusa ndi wopandapake, amene azunzidwa, ndi kupita kunyumba ndi nyumba. Mmalomwake, ofatsa adzalemekeza wolengeza Ufumu monga mlaliki woikidwa ndi Yehova ndi kudza m’dzina la Mulungu. Awona uthenga umene mlaliki wadzetsa mwa mawu apakamwa ndi mabuku kukhala wofunika koposa.—Yakobo 3:17; 1 Atesalonika 2:13.
13. (a) Kodi ndimotani mmene Ayuda ndi Agiriki anawonera kulalikidwa kwa Kristu wopachikidwa? (b) Kodi nkuchokera kumagulu ati a anthu amene ambiri sanaitanidwe kukhala otsatira a Yesu, ndipo nchifukwa ninji?
13 Popitiriza kukambitsirana kwake njira za Mulungu, Paulo anati: “Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru: koma ife tilalikira Kristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa; koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Kristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu. Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zawo; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yawo. Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iyayi; koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofoka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu.”—1 Akorinto 1:22-27; yerekezerani ndi Yesaya 55:8, 9.
14. (a) Zitafunsidwa ponena za chizindikiro cha kuvomerezedwa kwawo, kodi Mboni za Yehova zimaloza kuchiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji Paulo anakana kukondweretsa Agiriki ndi chisonyezero chirichonse cha nzeru ya dziko?
14 Pamene Yesu anali padziko lapansi, Ayuda anafunsa chizindikiro chochokera kumwamba. (Mateyu 12:38, 39; 16:1) Koma Yesu anakana kupereka chizindikiro chirichonse. Mofananamo, Mboni za Yehova lerolino sizimasonyeza chizindikiro chirichonse cha kuvomerezedwa kwawo. Mmalomwake, zimasonya ku ntchito yawo yakulakira mbiri yabwino, monga momwe kwalembedwera m’mavesi a m’Baibulo onga Yesaya 61:1, 2; Marko 13:10; ndi Chivumbulutso 22:17. Agiriki akale anafunafuna nzeru, maphunziro apamwamba m’zinthu za dzikoli. Pamene kuli kwakuti Paulo anaphunzira nzeru zadzikoli, anakana kusangalatsa Agiriki mwakusonyeza nzeruzo. (Machitidwe 22:3) Analankhula ndi kulemba m’Chigiriki chofala cha anthu wamba, mmalo mwa Chigiriki cha akatswiri ophunzira. Paulo anauza Akorinto kuti: “Abale, m’mene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu. . . . Mawu anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mawu okopa a nzeru, koma m’chiwonetso cha mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.”—1 Akorinto 2:1-5.
15. Kodi Petro akuwakumbutsa chiyani onyoza mbiri yabwino, ndipo ndimotani mmene mkhalidwe wamakono uliri wofanana ndi wa m’nthaŵi ya Nowa?
15 M’masiku otsiriza ano, onyoza mbiri yabwino ya dziko latsopano lirinkudza la Mulungu ndi mapeto oyandikira adzikoli akukumbutsidwa ndi mtumwi Petro kuti dziko la m’tsiku la Nowa “pomizidwa ndi madzi, lidawonongeka.” (2 Petro 3:3-7) Poyang’anizana ndi chiwonongeko chowopsa chimenecho, kodi Nowa anachitanji? Anthu ambiri amanganiza kuti anangomanga chingalawa. Koma Petro akuti pamene Mulungu anadzetsa Chigumula padziko lakale, Iye “anasunga Nowa mlaliki wachilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri.” (2 Petro 2:5) M’nzeru zawo zadziko, anthu opanda umulungu amene anakhala Chigumula chisanadze mosakaikira anaseka zimene Nowa analalikira ndi kumutcha wopusa, wosazindikira ndi wosapindulitsa. Lerolino, Akristu owona akuyang’anizana ndi mkhalidwe wofananawo, popeza kuti Yesu anayerekezera mbadwo wathu ndi uja wa mtsiku la Nowa. Komabe, mosasamala kanthu za oseka, kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu sikuli nkhani chabe. Mofanana ndi kulalikira kumene anachita Nowa, kumatanthauza chipulumutso kwa wolalikirayo ndi kwa awo amene amvetsera iye!—Mateyu 24:37-39; 1 Timoteo 4:16.
‘Kukhala Opusa Kuti Mukhale Anzeru’
16. Kodi nchiyani chidzachitikira nzeru ya dzikoli pa Armagedo, ndipo ndani adzapulumuka kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu?
16 Posachedwapa, pa Armagedo, Yehova Mulungu adzawononga “nzeru za anzeru.” Adzathetsa “kuchenjera kwa ochenjera” amene ananenera za mmene dongosolo lawo latsopano ladziko lidzadzetsera mkhalidwe wabwinopo kwa anthu. “Nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyose” idzapsereza ukatswiri, nthanthi, ndi nzeru ya dziko lino. (1 Akorinto 1:19; Chivumbulutso 16:14-16) Awo okha amene adzapulumuka nkhondoyo ndi kupeza moyo m’dziko latsopano la Mulungu ndiaja amene amalabadira chimene dzikoli limatcha chopusa—inde, uthenga wabwino waulemerero wa Ufumu wa Yehova.
17. Kodi Mboni za Yehova zakhala motani ‘zopusa,’ ndipo nchiyani chimene olalikira mbiri yabwino a Mulungu ali otsimikiza kutchita?
17 Mboni za Yehova, zotsogozedwa ndi mzimu wake, sizimachita manyazi kulalikira chimene dzikoli limatcha chopusa. Mmalo mwakuyesa kukhala zanzeru malinga ndi dzikoli, izo zakhala ‘zopusa.’ Motani? Mwakuchita ntchito yolalikira Ufumu kotero kuti zikhale zanzeru, monga momwe Paulo analembera kuti: “Ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m’nthaŵi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.” (1 Akorinto 3:18-20) Alaliki a mbiri yabwino a Yehova amadziŵa phindu lopulumutsa moyo la uthenga wawo ndipo adzapitirizabe kulalikira mosasiya kufikira mapeto a dzikoli ndi nzeru yake pankhondo ya Armagedo. Posachedwapa, Yehova Mulungu adzalemekeza ufumu wake wachilengedwe chonse ndi kupatsa moyo wosatha kwa onse amene tsopano akukhulupirira ndi kuchitapo kanthu pa ‘chopusa cha zimene zikulalikidwa.’
[Mawu a M’munsi]
a Mosasamala kanthu za makambitsirano a nthanthi ndi kufufuza kwa amuna anzeru a Girisi wakale, zolemba zawo zimasonyeza kuti sanapeze maziko enieni aliwonse a chiyembekezo. Pulofesa J. R. S. Sterrett ndi Samuel Angus anasonyeza kuti: “Palibe bukhu limene limasonyeza chisoni chenicheni pa masoka a moyo, kuzilala kwa chikondi, chiyembekezo chonyenga, ndi imfa yopanda chisoni.”—Funk and Wagnalls New “Standard” Bible Dictionary, 1936, tsamba 313.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi pali nzeru za mitundu iŵiri yotani?
◻ Kodi cholakwika chachikulu ndi nzeru yadziko nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kulalikira mbiri yabwino kuli chinthu chopindulitsa kwambiri kuchita?
◻ Kodi nchiyani chidzachitikira nzeru zonse zadziko posachedwapa?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizimachita manyazi kulalikira zimene dziko limatcha zopusa?
[Chithunzi patsamba 23]
Agiriki anafunafuna nzeru ya dziko ndipo kaŵirikaŵiri anawona kulalikira kwa Paulo monga chopusa