Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Njira ya Chikondi Silephera
    Nsanja ya Olonda—1999 | February 15
    • 4. Kodi Baibulo limafotokozanji ponena za kaduka?

      4 Atanena mawu ake oyamba ponena za chikondi, Paulo analembera Akorinto kuti: “Chikondi sichidukidwa.” (1 Akorinto 13:4) Munthu angadukidwe ndi zimene ena apeza kapena zimene achita. Kudukidwa kumeneku kumawononga​—kuthupi, mumtima, ndiponso mwauzimu.​—Miyambo 14:30; Aroma 13:13; Yakobo 3:14-16.

      5. Kodi chikondi chingatithandize motani kuthetsa nsanje pamene taona kuti udindo wina wateokalase watipitirira?

      5 Ponena za zimenezi, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimachita nsanje ndikaona kuti maudindo ena ateokalase andipitirira?’ Ngati mwayankha kuti inde, musataye mtima. Wolemba Baibulo Yakobo akutikumbutsa kuti anthu onse opanda ungwiro ‘amachita nsanje.’ (Yakobo 4:5) Kukonda mbale wanu kungakuthandizeni kukhalanso ndi maganizo abwino. Kungakupangitseni kukondwera ndi amene akukondwera ndi kusaona ngati mwanyozedwa pamene wina alandira dalitso kapena chiyamikiro.​—Yerekezerani ndi 1 Samueli 18:7-9.

      6. Kodi ndi mkhalidwe woipa wotani umene unabadwa mumpingo wa ku Korinto wa m’zaka za zana loyamba?

      6 Paulo anawonjezera kuti chikondi “sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.” (1 Akorinto 13:4) Ngati tili ndi luso linalake kapena timadziŵa kuchita zinthu zakutizakuti, palibe chifukwa chodzitamandira nazo. Mwachionekere, limeneli ndilo linali vuto la amuna ena ofuna malo apamwamba amene anali ataloŵa mumpingo wakale wa ku Korinto. Mwina anali aluso kwambiri pofotokoza zinthu kapena ankayendetsa zinthu bwino kwambiri. Kudzionetsera kwawo kuyenera kuti nakonso kunapangitsa mpingowo kugaŵanika. (1 Akorinto 3:3, 4; 2 Akorinto 12:20) Zinthu zinafika poipa kwambiri moti pambuyo pake Paulo anadzudzula Akorintowo chifukwa cha ‘kulolana nawo opanda nzeru,’ amene Paulo powatsutsa anawatcha “atumwi oposatu.”​—2 Akorinto 11:5, 19, 20.

      7, 8. Sonyezani mogwiritsa ntchito Baibulo mmene tingagwiritsire ntchito maluso ena alionse achibadwa pochirikiza m’gwirizano.

      7 Zofananazo zingachitikenso lerolino. Mwachitsanzo, ena angamakonde kudzitamandira pa zimene achita mu utumiki kapena chifukwa cha maudindo awo m’gulu la Mulungu. Ngakhale ngati tili ndi luso linalake kapena timadziŵa kuchita zinthu zina zimene ena mumpingo amalephera, kodi chimenecho chingakhale chifukwa chodzikuzira? Ndi iko komwe, tiyenera kugwiritsa ntchito maluso alionse achibadwa amene tingakhale nawo pochirikiza mgwirizano​—osati kudzitukumula nawo.​—Mateyu 23:12; 1 Petro 5:6.

      8 Paulo analemba kuti ngakhale kuti mpingo uli ndi ziŵalo zambiri, “Mulungu analumikizitsa thupi.” (1 Akorinto 12:19-26) Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti ‘kulumikizitsa’ limatanthauza kusanganiza bwino, monga momwe amachitira posanganiza zinthu za maonekedwe osiyanasiyana kuti zikongole. Choncho palibe munthu mumpingo amene ayenera kudzikuza chifukwa cha maluso ake ndi kuyesa kulamulira ena. Kunyada ndi kufuna malo apamwamba n’zosafunika m’gulu la Mulungu.​—Miyambo 16:19; 1 Akorinto 14:12; 1 Petro 5:2, 3.

  • Njira ya Chikondi Silephera
    Nsanja ya Olonda—1999 | February 15
    • 11. (a) Kodi chikondi chokoma mtima komanso chosachita zosayenera tingachisonyeze m’njira zotani? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti sitikondwera ndi chinyengo?

      11 Paulo analembanso kuti chikondi chili “chokoma mtima” ndi kutinso “sichichita zosayenera.” (1 Akorinto 13:4, 5) Inde, chikondi sichidzatilola kukhala amwano, owola mkamwa, kapena opanda ulemu. M’malo mwake, tidzaganiziranso malingaliro a ena. Mwachitsanzo, munthu wachikondi adzapeŵa kuchita zinthu zimene zingavutitse chikumbumtima cha ena. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 8:13.) Chikondi “sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi.” (1 Akorinto 13:6) Ngati tikonda malamulo a Yehova, sitidzaona chisembwere ngati nkhani yaing’ono ndiponso sitidzakondwera ndi zinthu zimene Mulungu amadana nazo. (Salmo 119:97) Chikondi chidzatithandiza kukondwera ndi zinthu zomangirira osati zowononga.​—Aroma 15:2; 1 Akorinto 10:23, 24; 14:26.

  • Njira ya Chikondi Silephera
    Nsanja ya Olonda—1999 | February 15
    • 16. Kodi chikondi chingatithandize kukhala oleza mtima m’mikhalidwe yotani?

      16 Kenako, Paulo anatiuza kuti “chikondi chikhala chilezere.” (1 Akorinto 13:4) Chimatipangitsa kupirira ziyeso, mwinamwake kwa nthaŵi yaitali. Mwachitsanzo, Akristu ambiri akhala m’mabanja okhala ndi zipembedzo zosiyana kwa zaka zambiri. Ena ndi mbeta, osati modzifunira, koma chifukwa chakuti sakupeza wokwatirana naye woyenera “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; 2 Akorinto 6:14) Ndiyeno pali awo amene akuvutika ndi matenda ofooketsa. (Agalatiya 4:13, 14; Afilipi 2:25-30) Ndithudi, m’dongosolo lopanda ungwiroli, palibe munthu amene alibe mkhalidwe wina wofunika kupirira.​—Mateyu 10:22; Yakobo 1:12.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena