Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 284-tsamba 289
  • M’Malirime, Kulankhula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • M’Malirime, Kulankhula
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ngati Wina Anena Kuti—
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa Zotani pa Nkhani ya Malilime?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mphatso ya Malilime Ndimbali ya Chikristu Chowona?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Masiku Ano Mulungu Ndi Amene Amachititsa Anthu Kulankhula Malilime?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kulankhula m’Malilime—Chochitika Chozizwitsa Chomakulakula
    Nsanja ya Olonda—1992
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 284-tsamba 289

M’Malirime, Kulankhula

Tanthauzo: Luso lapadera loperekedwa kupyolera mwa mzimu woyera kwa ophunzira ena mu mpingo woyambirira Wachikristu limene linawakhozetsa kulalikira kapena kulemekeza Mulungu mwanjira zina m’chinenero chimene sichinali chawo.

Kodi Baibulo limanena kuti onse amene akakhala ndi mzimu wa Mulungu ‘akalankhula m’malirime’?

1 Akor. 12:13, 30: “Pakutinso mwa mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kuloŵa m’thupi limodzi . . . Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malirime?” (Ndiponso 1 Akorinto 14:26)

1 Akor. 14:5: “Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malirime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malirime, akapanda kumasulira, kuti mpingo ukalandire chomangirira.”

Kodi kulankhula kogwidwa ndi mzimu m’chinenero chimene munthuyo sanaphunzire konse kumatsimikizira kuti ali ndi mzimu woyera?

Kodi luso la “kulankhula m’malirime” lingachokere kumagwero ena osakhala Mulungu wowona?

1 Yoh. 4:1: “Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse [“mawu ouziridwa,” NW, RS], koma yesani mizimu ngati ichokera kwa Mulungu.” (Wonaninso Mateyu 7:21-23; 2 Akorinto 11:14, 15.)

Pakati pa awo ‘olankhula m’malirime’ lerolino pali Apentekoste ndi Abapatisti, ndiponso Aroma Katolika, Aepiskopolo, Amethodisti, Alutherani, ndi Apresibeteriyani. Yesu ananena kuti mzimu woyera ‘ukatsogoza ophunzira ake m’chowonadi chonse.’ (Yoh. 16:13) Kodi mamembala a chirichonse cha zipembedzo zimenezi amakhulupirira kuti ena amenenso amalankhula “m’malirime” atsogozedwa mu “chowonadi chonse”? Kodi zingatero bwanji, popeza siziri zogwirizana zonse? Kodi nchiyani chimene chiri mzimu umene umawatheketsa kulankhula “m’malirime”?

Mawu ogwirizana onenedwa ndi onse aŵiri Fountain Trust ndi Church of England Evangelical Council anavomereza kuti: “Tikuzindikiranso kuti zochitika zachilendo zofanana zingachitike mwa chisonkhezero cha ziŵanda.” (Gospel and Spirit, April 1977, lofalitsidwa ndi Fountain Trust ndi Church of England Evangelical Council, p. 12) Bukhulo Religious Movements in Contemporary America (lolembedwa ndi Irving I. Zaretsky ndi Mark P. Leone, pogwira mawu L. P. Gerlach) limasimba kuti mu Haiti ‘kulankhula m’malirime’ uli mkhalidwe wa ponse paŵiri m’chipembedzo cha Pentekoste ndi chipembedzo cha makolo.—(Princeton, N.J.; 1974), p. 693; wonaninso 2 Atesalonika 2:9, 10.

Kodi ‘kulankhula m’malirime’ kumene kumachitidwa lerolino nkofanana ndi kumene kunachitidwa ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba?

M’zaka za zana loyamba, mphatso zozizwitsa za mzimu, kuphatikizapo luso la “kulankhula m’malirime,” zinatsimikizira kuti chiyanjo cha Mulungu chinasamutsidwa kuchokera padongosolo Lachiyuda la kulambira kumka pampingo Wachikristu wokhazikitsidwa chatsopanowo. (Aheb. 2:2-4) Popeza kuti cholinga chimenecho chinakwaniritsidwa m’zaka za zana loyamba, kodi kuli kofunika kutsimikizira chinthu chimodzimodzicho mobwerezabwereza m’tsiku lathu?

M’zaka za zana loyamba, luso la “kulankhula m’malirime” linapereka chisonkhezero kuntchito ya m’mitundu yonse ya kuchitira umboni imene Yesu anali atalamula otsatira ake kuichita. (Mac. 1:8; 2:1-11; Mat. 28:19) Kodi ndimo mmene “olankhula m’malirime” amenewo amagwiritsirira ntchito lusolo lerolino?

M’zaka za zana loyamba, pamene Akristu ‘analankhula m’malirime,’ zimene adanena zinali ndi tanthauzo kwa anthu amene anadziŵa zinenerozo. (Mac. 2:4, 8) Kodi siziri zowona lerolino, kuti kaŵirikaŵiri ‘kulankhula m’malirime’ kumaloŵetsamo kulankhulidwa kogwidwa ndi mzimu kofuula kwa mawu osadziŵika.

Baibulo limasonyeza kuti m’zaka za zana loyamba mipingo inali kukhala ndi ‘olankhula m’malirime’ olekezera pa anthu aŵiri kapena atatu amene akatero pamsokhano uli wonse wolinganizidwa; iwo anayenera kukuchita “motsatana,” ndipo ngati panalibe womasulira anafunikira kukhala chete. (1 Akor. 14:27, 28) Kodi zimenezo ndizo zimene zikuchitidwa lero lino?

Wonaninso tsamba 320, 321, pamutu wakuti “Mzimu.”

Kodi mzimu woyera ungakhale ukutsogolera ogwidwa ndi mzimu kuloŵa m’zizoloŵezi zimene ziri zoposa zopezedwa m’Malemba?

2 Tim. 3:16, 17: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pachiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.” (Ngati munthu anena kuti ali ndi uthenga wouziridwa umene umatsutsana ndi zovumbulutsidwa ndi mzimu wa Mulungu kupyolera mwa Yesu ndi atumwi ake, kodi kungakhale kotheka kuti ngwochokera kumagwero amodzimodziwo?)

Agal 1:8: “Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati [“wosiyana ndi,” NE] umene tidakulakirani ife, akhale wotembereredwa.”

Kodi njira ya moyo ya ziŵalo za magulu amene amachirikiza ‘kulankhula m’malirime’ imapereka umboni wakuti ali ndi mzimu wa Mulungu?

Monga kagulu kodi iwo amasonyeza mwapadera zipatso za mzimu zonga kudekha ndi kudziletsa? Kodi mikhalidwe imeneyi imawonekera mosavuta pakati pa anthu amene amafika pamisonkhano yawo kudzalambira?—Agal. 5:22, 23.

Kodi iwo kwenikweni “saali mbali ya dziko”? Chifukwa cha zimenezi kodi iwo akupereka kudzipereka kokwanira ku Ufumu wa Mulungu kapena kodi iwo akuloŵetsedwa m’zochitika za ndale zadziko? Kodi iwo akhala opanda liwongo la mwazi m’nthaŵi yankhondo? Monga kagulu kodi iwo ali ndi mbiri yabwino chifukwa cha kupeŵa mkhalidwe wa chisembwere wa dziko?—Yoh. 17:16; Yes. 2:4; 1 Ates. 4:3-8.

Kodi Akristu owona lerolino amadziŵika ndi luso la “kulankhula m’malirime”?

Yoh. 13:35: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”

1 Akor. 13:1, 8: “Ndingakhale ndilankhula malirime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. Chikondi sichitha nthaŵi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malirime adzaleka.”

Yesu ananena kuti mzimu woyera ukadza pa otsatira ake ndi kuti iwo akakhala mboni zake kumalekezero ake a dziko lapansi. (Mac. 1:8) Iye anawalangiza “kupanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse.” (Mat. 28:19, NW) Iye ananeneratunso kuti ‘mbiri yabwino ya ufumu ikalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse.’ (Mat. 24:14, NW) Kodi ndani lero lino, amene ponse paŵiri monga kagulu ndi munthu aliyense payekha, akuchita ntchito imeneyi? Mogwirizana ndi zimene Yesu adanena, kodi ife tiyenera kufunafuna zimenezi monga umboni wakuti kaguluko kali ndi mzimu woyera?

Kodi ‘kulankhula m’malirime’ kudzapitirizabe kufikira pamene “changwiro” chifika?

Pa 1 Akorinto 13:8 patchulidwa mphatso zozizwitsa zingapo—kunenera, malirime ndi chidziŵitso. Kachiŵirinso vesi 9 imasonya ku ziŵiri za mphatso zimenezi—chidziŵitso ndi kunenera—kumati: “Pakuti ife tidziŵa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.” Kapena monga momwe RS imanenera kuti: “Chifukwa chakuti chidziŵitso chathu ndichopanda ungwiro ndipo ulosi wathu ngwopanda ungwiro.” Ndiyeno vesi 10 limafotokoza kuti: “Pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.” Liwu lakuti ungwiro latembenuzidwa kuchokera ku Lachigiriki lakuti teʹlei·on, limene limapereka lingaliro la kukula kokwanira, uchikwanekwane, kapena ungwiro. Ro, By, ndi NW panopa amalimasulira kuti “kukwanira.” Wonani kuti sindiyo mphatso ya malirime imene ikunenedwa kukhala “yopanda ungwiro,” “yamderamdera,” kapena yosakwanira. Chonenedwacho ndicho “ulosi” ndi “chidziŵitso.” Mwamawu ena, ngakhale ndi mphatso zozizwitsa zimenezo, Akristu oyambirira, anali kokha ndi chidziŵitso cha chifuno cha Mulungu chosakwanira kapena chamderamdera. Koma pamene maulosiwo akakwaniritsidwa, pamene chifuno cha Mulungu chikakwaniritsidwa, pamenepo “changwiro,” kapena chokwanira chikadza. Chotero, mwachiwonekere sichikusonya ku utali umene ‘mphatso ya malirime’ ikapitirizabe.

Komabe, Baibulo limasonyeza utali umene ‘mphatso ya malirime’ ikakhala mbali ya chochitika Chachikristu. Mogwirizana ndi kunena kwa cholembedwa, mphatso imeneyi ndi mphatso zina za mzimu nthaŵi zonse zinali kuperekedwa kwa anthu mwakuika manja kwa atumwi a Yesu Kristu kapena iwo alipo. (Mac. 2:4, 14, 17; 10:44-46; 19:6; wonaninso Machitidwe 8:14-18.) Motero, pambuyo pa imfa yawo ndipo pamene anthu ali onse paokha amene adalandira mphatsoyo mwanjirayo anafa, mphatso zozizwitsa zochokera ku kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu ziyenera kukhala zitafika. Lingaliro lotere likuvomerezana ndi chifuno cha mphatso zimenezo monga momwe kwafotokozedwera pa Ahebri 2:2-4.

Kodi Maliko 16:17, 18 amasonyeza kuti luso la “kulankhula m’malirime” likakhala chizindikiro chodziŵikitsa okhulupirira?

Kuyenera kudziŵika kuti mavesi ameneŵa amasonya osati kokha ku ‘kulankhula m’malirime atsopano’ komanso kugwira njoka ndi kumwa poizoni. Kodi onse amene “amalankhula m’malirime” amalimbikitsanso zimenezi?

Kaamba ka ndemanga zonena za zifukwa zimene mavesi ameneŵa aliri osavomerezeka ndi ophunzira Baibulo onse, wonani tsamba 168, pamutu wakuti “Kuchiritsa.”

Ngati Wina Anena Kuti—

‘Kodi mumakhulupirira kulankhula m’malirime?’

Mungayankhe kuti: ‘Mboni za Yehova zimalankhula zinenero zambiri, koma sitimaloŵetsedwa m’kulankhula kochititsidwa ndi mizimu “m’malirime osadziŵika.” Koma taimani ndifunse kuti, Kodi mumakhulupirira kuti “kulankhula m’malirime” kumene kumachitidwa lerolino kuli kofanana ndi kumene kunachitidwa ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Nazi mfundo zina zoyerekezera zimene ndapeza kukhala zokondweretsa kwambiri. (Mwinamwake gwiritsirani ntchito mfundo zochokera pa tsamba 286.)’

Kapena munganene kuti: ‘Timakhulupirira kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba “analankhula m’malirime” ndi kuti zimenezi zinakwaniritsa zofunika zotsimikizirika kalero. Kodi mumadziŵa chimene zofunika zimenezo zinali?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kunatumikira monga chizindikiro chakuti Mulungu anali atasamutsa chiyanjo chake kuchichotsa padongosolo Lachiyuda kumka pampingo Wachikristu wopangidwa chatsopanowo. (Aheb. 2:2-4)’ (2) ‘Kunali njira yothandiza kufalitsira mbiri yabwino pamlingo wa m’mitundu yonse m’nthaŵi yaifupi. (Mac. 1:8)’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena