Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mumathandiza Kuti Misonkhano Yachikhristu Ikhale Yolimbikitsa?
    Nsanja ya Olonda—2010 | October 15
    • Misonkhano Imene Cholinga Chake Ndi ‘Kutithandiza, Kutilimbikitsa Ndiponso Kutitonthoza’

      13. (a) Kodi misonkhano yathu iyenera kukhudza bwanji anthu? (b) Tchulani funso lofunika kwambiri kwa akulu.

      13 Paulo ananena kuti cholinga chachikulu cha misonkhano ya mpingo ndi ‘kutithandiza, kutilimbikitsa ndiponso kutitonthoza.’c (1 Akor. 14:3) Kodi akulu achikhristu masiku ano angatani kuti mbali zawo pa misonkhano zizikhala zolimbikitsa ndiponso zotonthoza kwa abale ndi alongo? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione za msonkhano umene Yesu anachititsa atangoukitsidwa kumene.

      14. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachitika Yesu asanachititse msonkhano? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mitima ya atumwi inakhala m’malo ‘Yesu atayandikira ndi kulankhula nawo’?

      14 Choyamba, ganizirani zimene zinachitika Yesu asanachititse msonkhanowu. Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, atumwi “anathawa ndi kumusiya yekha” ndipo mogwirizana ndi ulosi iwo ‘anabalalika aliyense kupita kunyumba kwake.’ (Maliko 14:50; Yoh. 16:32) Ndiyeno ataukitsidwa, Yesu anaitana atumwi, omwe pa nthawiyo anali achisoni, ku msonkhano wapadera.d ‘Atumwi 11 anapita ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anakonza zoti akakumane nawo.’ Ndiyeno atafika, “Yesu anayandikira ndi kulankhula nawo.” (Mat. 28:10, 16, 18) Taganizirani mmene atumwiwo anamvera Yesu atachita zimenezi. Kodi Yesu anakambirana nawo za chiyani?

      15. (a) Kodi Yesu anakambirana nkhani ziti ndi ophunzira ake nanga ndi zinthu ziti zimene sanatchule? (b) Kodi msonkhano umenewu unakhudza bwanji atumwi?

      15 Yesu anayamba ndi mawu akuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine.” Kenako anawapatsa ntchito yoti achite. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” Ndiyeno pomaliza anawauza mawu olimbikitsa akuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse.” (Mat. 28:18-20) Kodi mwaona zimene Yesu sanachite? Iye sanakalipire atumwiwo, kapena kupezerapo mwayi pa msonkhanowu kuti akayikire zolinga zawo. Komanso iye sanawonjezere chisoni chawo mwa kuwakumbutsa za kufooka kwa chikhulupiriro chawo. M’malomwake, Yesu anawatsimikizira kuti iye pamodzi ndi Atate wake amawakonda mwa kuwapatsa udindo waukulu. Kodi zimenezi zinawakhudza bwanji atumwiwo? Iwo analimbikitsidwa, kuthandizidwa ndiponso kutonthozedwa kwambiri moti patapita kanthawi, iwo anayambiranso “kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.”​—Mac. 5:42.

      16. Popeza Yesu anachititsa msonkhano wotsitsimula, kodi akulu masiku ano amamutsanzira bwanji pa nkhaniyi?

      16 Potsanzira Yesu, akulu masiku ano amaona kuti nthawi ya misonkhano imawapatsa mpata wotsimikizira okhulupirira anzawo kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake. (Aroma 8:38, 39) Choncho akamakamba nkhani zawo pa misonkhano, akulu amanena kwambiri zabwino zimene abale awo amachita osati zimene amalephera. Iwo sakayikira zolinga za abale awo. M’malomwake, iwo amasonyeza kuti amaona Akhristu anzawo kuti ndi anthu okonda Yehova ndiponso amafuna kuchita zinthu zabwino. (1 Ates. 4:1, 9-12) N’zoona kuti akuluwo nthawi zina amafunika kupereka malangizo okhudza mpingo wonse. Koma ngati ndi anthu ochepa chabe amene akufunika kulangizidwa, ndi bwino kupereka malangizowo mwachindunji kwa anthu amene akuwafunikira. (Agal. 6:1; 2 Tim. 2:24-26) Polankhula ndi mpingo wonse, akulu ayenera kukhala ndi cholinga choyamikira mpingowo ngati pakufunika kutero. (Yes. 32:2) Iwo amayesetsa kulankhula m’njira imene ingachititse kuti pamapeto pa misonkhano, aliyense azimva kuti watsitsimulidwa ndiponso walimbikitsidwa.​—Mat. 11:28; Mac. 15:32.

  • Kodi Mumathandiza Kuti Misonkhano Yachikhristu Ikhale Yolimbikitsa?
    Nsanja ya Olonda—2010 | October 15
    • c Buku lina limafotokoza kusiyana pakati pa “kulimbikitsa” ndi “kutonthoza.” Bukuli limanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kutonthoza” ndi mawu “achikondi kwambiri kuposa mawu amene anawamasulira kuti [kulimbikitsa].”​—Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words; Yerekezerani ndi Yohane 11:19.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena