Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Ndani amene anali “khumi ndi aŵiri” amene Yesu anawonekerako, monga mmene atchulidwira mu 1 Akorinto 15:5?
Kuwonekera komwe kukutchulidwa pa 1 Akorinto 15:5 kukuwoneka kukhala kumene kunalembedwa pa Yohane 20:26-29, pamene pamakhudza Tomasi. Komabe, ichi chikulozera kwa atumwi monga gulu ndipo mwachidziŵikire kuphatikizapo Matiya.
M’kukambitsirana chiukiriro, Paulo analemba za kuwonekera kwa Yesu kwa anthu pambuyo pa kuwukitsidwa Kwake. Mtumwiyo ananena kuti Kristu “anawonekera kwa Kefa, pamenepo kwa khumi ndi aŵiriwo. Pamenepo anawoneka pa nthaŵi imodzi kwa abale oposa mazana asanu.”—1 Akorinto 15:5, 6.
Kuchokera pakati pa awo omwe anatsatira iye monga ophunzira, Yesu anasankha atumwi 12. (Mateyu 10:2-5) Yudase Isikariote anali mmodzi wa 12, koma iye anadzakhala wonyenga, akumapereka Yesu, ndipo kenaka anadzipachika. (Mateyu 26:20-25; 27:3-10) Chotero panthaŵi ya imfa ndi kuwukitsidwa kwa Kristu, panali kokha atumwi okhulupirika 11 kuchokera pa 12 oyambirirawo. Yesu anawonekera kwa ophunzira osiyanasiyana pakati pa kuwukitsidwa kwake ndi kukwera kwake kumwamba. Pambuyo pa chimenecho atumwi anazindikira kufunika kwa kulowetsa m’malo mwa Yudase. Ndi chitsogozo chaumulungu, Matiya anasankhidwa, ndipo “anaŵerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.”—Machitidwe 1:6-26.
Ena chotero anadabwa nchifukwa ninji Paulo analemba kuti Yesu anawoneka kwa “khumi ndi aŵiri,” popeza panthaŵi imeneyo Yudase anali atafa ndipo Matiya anali asanasankhidwe. Kunena mwachindunji, panthaŵi imeneyo panali kokha “atumwi khumi ndi mmodzi” amene poyambirirapo anaikidwa ndi kutumizidwa ndi Yesu.—Luka 6:13-16.
Chiri chachibadwa kulankhula za gulu lonse pamodzi ngakhale ngati chiwalo chimodzi palibe. (“Bungwe lolamulira lagamulapo kuti . . . ” “Bungwe la akulu linakunama . . . ”) Chotero katchulidwe kakuti “khumi ndi aŵiri” kangakhale kanagwiritsiridwa ntchito m’kulozera ku gulu lonse la atumwi, ngakhale ngati mmodzi kapena aŵiri panalibe pa chochitikacho. (Yerekezani ndi Machitidwe 6:1-6.) Pamene Yesu choyamba anawonekera kwa ophunzira m’chipinda chotsekedwa, “Tomasi, mmodzi wa khumi ndi aŵiriwo, . . . sanali nawo.” Masiku asanu ndi atatu pambuyo pake iye analipo ndipo kusatsimikizirika kulikonse kunakhazikitsidwa. (Yohane 20:19-29) Ngakhale kuti Matiya anali asanaikidwe kulowa m’malo a Yudase, iye anali wophunzira wa nthaŵi yaitali. (Machitidwe 1:21, 22) Popeza iye anali woyanjana mwathithithi ndi atumwi oyambirira ndipo mwamsanga pambuyo pake “anaŵerengedwa limodzi” nawo, ndemanga yolozera m’mbuyo yonena za kuwoneka kwa Yesu kwa “khumi ndi aŵiri” mwachiwonekere inaphatikizapo Matiya.