Chinachake Choipitsitsa Kuposa Aids
“Kufufuza kunali kovomereza. Inu muli ndi AIDS.” Mawu amenewo a dokotala wanga anamveka m’mutu mwanga pamene ndinanyamula lamya tsiku lina chaka chatha. Ngati kokha ndinamvetsera ku uphungu wa Mulungu ndi kuwugwiritsira ntchito, ndikanapeŵa zimenezi!
NDINALEEDWA monga mmodzi wa Mboni za Yehova mu boma la Washington, ndipo makolo anga anatsimikizira kuti ndinadziŵa zimene zinali zifuno za Mulungu. Chotero chinadza monga chodabwitsa kwa anthu ambiri pamene ndinayamba kukhala mosiyana ndi kuphunzitsidwa kwanga kwa uchichepere.
Kukondedwa ndi achichepere ena a pa sukulu kunali chovuta kwa ine. Ndinayesera mitundu yonse ya zinthu kukhala wolandirika. Inde, palibe chirichonse chomwe chinagwira ntchito, ndipo podzafika nthaŵi imene ndinali wazaka 15, ndinazindikira kuti chirichonse chinali chopanda chiyembekezo. Ndinakhoza ngakhale kuyesera, kudzipha, mosaphula kanthu.
Ndikumaganiza kuti zinthu zingakhaleko bwino, ndinayamba kugwiritsira ntchito fodya ndi mbanje. Ayi ndithu, sizinatero. Pambuyo pa kanthaŵi, ndinagamulapo kuchoka m’gulu la Yehova ndi kuyang’ana kwinakwake kaamba ka chimwemwe. Ndinalengeza kwa mabwenzi anga a kusukulu kuti sindinalinso mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo anawonekera kuchikonda icho.
Moyo wa Chisembwere, Wosakhazikika
Potsirizira pake ndinapeza ntchito ndiponso nyumba yokhala m’mzera cha kunsi, kumene akazi a ganyu onse ndi achigololo ankachezera. Iwo anapitiriza kundiwuza ine mmene chinaliri chopepuka kuchita machenjera kaamba ka ndalama. Ndi thandizo lawo, sichinatenge nthaŵi yotalikira ndisanaphunzire kumwerekerako. Ndinasintha kuchoka pa munthu yemwe anafuna kukondedwa ndi aliyense ndi kukhala wachimwemwe kukhala winawake yemwe ankagwiritsiridwa ntchito ndi aliyense ndipo ndinali wopanda chimwemwe kwenikweni.
Ndinafuna kusintha, kubwerera kumudzi ndi kuyambanso. Ndinakhumba makolo anga ndi moyo womwe ndinali nawo poyambapo. Chotero ndinapemphera kwa Yehova kaamba ka thandizo. Mbali yovuta inali kufikira makolo anga ndi kupempha chikhululukiro chawo. Moyamikirika, iwo anachipeza kukhala chabwino kundikhululukira.
Akulu Achikristu anakumana nane, ndipo ndinalongosola chikhumbo changa kaamba ka kubwezeretsedwa mu mpingo. Sichinali chopepuka kwa iwo kapena kwa ine. Osati kokha kuti ndinali ndi mavuto ndi ziyambukiro za pambali za kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa koma ndinali nditatenganso matenda oipitsitsa opatsirana mwa kugonana. Dokotala wanga anandiwuza ine kuti ngati ndinayembekeza kwa mwezi umodzi wokha, ndikafa. Ndi zoipa zotani nanga zimene ndinadziikamo inemwini!
M’kupita kwa nthaŵi, ndinabwezeretsedwa, ndipo ndinakhoza ngakhale kukwatira mkazi wachichepere kuchokera mu mpingo wapafupi. Zinthu zinkasintha. Komabe, sindinayamikirebe chikondi cha Yehova. Ndinkayesera kuchita zinthu m’njira yanga m’malo mwa kudalira pa iye kaamba ka mphamvu.
Zochepera pa zaka ziŵiri pambuyo pake, ndinasudzula mkazi wanga ndi kuchotsedwanso kaamba ka chisembwere. Ndinali nditagwirizana ndi anthu a kudziko. Chinali kokha chabwinopo pa nthaŵi yoyamba, koma chenjezo la m’Malemba limatsimikizira kukhala lolondola: “Mayanjano oipa aipsya makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33.
Kumira Mwakuya M’kuipa Kachiŵirinso
Mwa kusamukira kutali, ndinalingalira kuti sindikakhoza kuvulaza banja langa mochulukira. Ndinalibe vuto la kupeza ntchito ndi malo okhalako mu San Francisco, California. Wogulitsa mankhwala ogodomalitsa anandiloŵetsa ntchito yoperekera mankhwala ogodomalitsa. Ndinalinso pakati pa gulu lake lotchuka lomwe linkayesera, kwaulere, ‘mankhwala ogodomalitsa okonzedwa’ chatsopano onse omwe ankadza. Tsopano ndinali ndi kutchuka kwa mtundu wina watsopano. Aliyense yemwe anandidziŵa (ndipo panali ochepera) anadziŵa kuti ndinali ndi mankhwala ogodomalitsa. Iwo ankakhoza kudza kwa ine mu makwalala, m’malo omwera moŵa, ndipo ngakhale pa ntchito, akumafuna kugula chinachake kuchokera kwa ine.
Pambali pa icho, sindinachedwe m’pangono pomwe kudziloŵetsa m’chisembwere; inali njira kaamba ka ine ya kudzimva wokondeka. Ndipo ndinakondedwa kwambiri. Ndinaphunzira kugwiritsira ntchito anthu ena kupyolera m’kugonana kuti ndipeze zinthu zomwe ndinafuna. Kwa zaka zingapo ndinakhala mwanjirayi.
Ndimakumbukira bwino lomwe pa chochitika chimodzi ndikumadwala malungo okulira ndi kukhala wofooka kwambiri. Dokotala wanga sanadziŵe chomwe ndinadwala. M’kupita kwa nthaŵi anatha. Sindinakhoze kudziŵa chomwe ndinawunikiridwako kufikira zaka zitatu pambuyo pake.
Mkati mwa nthaŵiyi, ndinayambanso kukhala ndi vuto ndi ziwanda, pa nthaŵi imodzi ndinawukiridwa m’chenicheni. Ndinadzimva kuti chiwanda chinkayesera kuloŵa m’thupi langa. Kunali kumenyera kukakamiza liwu lirilonse kumveka kutuluka mkamwa mwanga. Ndinayesera ndi kuyesera kufikira potsirizira pake ndinali wokhoza kufuula, “Ndithandizeni Yehova!” Chiwandacho mwamsanga chinachoka.
Tangolingalirani mmene ndinadzimverera! Pano ndinali kukhala ndi moyo wachisembwere chakuya ndi kuganizira kokha za inemwini, komabe ndinali ndi lingaliro la kuitanira pa Yehova kaamba ka thandizo! Ndinadzimva wamanyazi kwenikweni. Nchifukwa ninji ndinalingalira kuti Yehova akakhoza kundithandiza? Ndinaloŵa m’kupsyinjika kwakuya. Ndinaika moyo wanga m’ngozi modzifunira, ndikumafuna winawake kuti andiphe.
Chikhumbo cha Kusintha
Tsiku lina, pamene tinkayenda ndi mabwenzi ena, tinadziloŵetsa m’kukambitsirana ponena za zochitika zadziko. Pamene iwo anandifunsa ine chomwe ndinalingalira ponena za mtsogolo, ndinadzipeza inemwini ndikuwawuza ponena za chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi ndi anthu ake. Iwo anazizwa. Koma munthu mmodzi anakwiya nane kwenikweni ndi kunditcha wonyenga! Iye anali wolondola kotheratu. Ndinali kukhala moyo wapaŵiri. Komabe, mozama mkati mwa mtima wanga, ndinadziŵa kuti Yehova anali chipulumutso chathu chokha ndi kuti gulu lake linali malo okha okhalako.
Chifupifupi pa nthaŵiyi moyo wanga ndi miyoyo ya ondizungulira inayamba kusintha. Ambiri a mabwenzi anga ankabwera ndi AIDS. Chinali chovuta kuwona anthu omwe pa nthaŵi imodzi anali aumoyo akumawonda pang’onopang’ono ndi kufa. Ndinadzimva wopanda thandizo kuwatonthoza iwo. Chinali makamaka chokhumudwitsa chifukwa chakuti ndinadziŵa njira yabwino ya moyo. Ndinadziŵa kenaka kuti ndinafuna kubwerera ku chikondi cha Yehova. Koma motani?
Ndinayamba kupemphera kwa Yehova kaamba ka thandizo. Chinali chovuta kwenikweni kuchichita. Ndinadzimva wamanyazi kwenikweni ndi wodetsedwa. Tsiku lina ndinalandira lamya. Inachokera kwa azakhali anga, omwe sindinawonepo pa zaka zoposa zisanu ndi zinayi. Iwo anafuna kubwera kudzandiwona ine. Ngakhale kuti iwo sanagawane chikhulupiriro cha makolo anga, ndinawauza iwo kuti ndinafuna kusintha moyo wanga ndi kubwerera kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Iwo anakhoza kuwona kutsimikizira kwanga ndipo anafuna kuthandiza.
Njira Yaitali Yobwerera
Azakhali anga anandiitana ine kusamukira kwawo kufikira nditabwereranso m’njira yanga yabwino. Pamene anandifunsa kaya ngati chimenecho chikathandiza, ndinangoima pamenepo ndi kulira. Ndinadziŵa kuti iyi inali njira yotulukira yomwe ndinafunikira, chotero ndinasiya oyanjana nawo anga akale. Miyezi yotsatira yoŵerengeka siinali yopepuka, koma ndinali ndi chidaliro kuti Yehova akakhoza kundithandiza ine kuzipyola izo. Ndiganiza kuti Malaki 3:7 amagwira ntchito pano: “Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu.”
Ndinakumana ndi akulu mwamsanga pambuyo pa kusamuka. Ndinawauza chirichonse ponena za inemwini ndi kuti ndinafuna mowonadi kutumikira Yehova. Iwo anadziŵa ndipo inenso ndinadziŵa kuti mwanjira iriyonse kubwezeretsedwa kwanga sikunayenere kudza mwamsanga. Ndinali ndi mbiri yaitali yoipa. Komabe, ndinali wogamulapo nthaŵi ino. Usiku ndi usana uliwonse ndinapemphera mokhazikika kwa Yehova kaamba ka thandizo lake. Ndinali kuganizira kuti ndinali munthu wofooka chotero. Pa inemwini ndilingalira kuti ndiri tero. Koma pamene muli ndi thandizo la Yehova, chimakhala chozizwitsa mmene mumakhalira wamphamvu.
Ndinali nditagwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa kwa zaka zambiri kuchita ndi moyo wa tsiku ndi tsiku. Tsopano ndinafunikira kuchita popanda izo. Ndinali wamantha. Makamu a anthu anandichititsa mantha, ndipo ndinakhoza m’chenicheni kudwala pamene ndinali ndi iwo kwa nthaŵi yaitali. Pa nthaŵi imodzimodziyo, ndinali kuyeseranso kuleka kusuta fodya pambuyo pa kukhala wozoloŵera kusuta kwa chifupifupi mapaketi a ndudu anayi pa tsiku. Chinthu chokha chomwe chinandithandiza ine kulaka zonsezi chinali pemphero ndi kudzikumbutsa inemwini mopitirizabe kuti kachitidwe kanga kosintha kanali kokondweretsa kwa Yehova. Ndinapezanso chitonthozo ndi mtendere mwa kupezeka pa misonkhano mokhazikika. Ngakhale kuti sindinakhoze kulankhula kwa aliyense chifukwa cha kukhala kwanga wochotsedwa, ndinakhozabe kumva chikondi ndi kutentha kwa abale ndi alongo anga a mtsogolo kumeneko.
Potsirizira pake, chifupifupi chaka chimodzi pambuyo pa kutembenuka, Yehova anachiwona kukhala choyenera kutheketsa atumiki ake kundibwezeretsa ine m’gulu lake. Iye anadziŵa nthaŵi yeniyeni ya kundilonjera ine. Iye samalola inu kuyesedwa kuposa pa chimene mungakhoze kupirira. Mwamsanga pambuyo pake, ndinalandira lamya ija kuchokera kwa dokotala kundiwuza ine kuti ndinali ndi AIDS. Ndithudi, chimene Agalatiya 6:7 amanena chiri chowona: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”
Choyamba ndinalira. Mitundu yonse ya malingaliro inapyola m’maganizo anga. Masomphenya a moyo wanga wa kumbuyo anabwera m’maso mwanga. Ndinali nditawona kwa nthaŵi yoyamba chimene nthendayi imachita kwa munthu, limodzinso ndi mmene ena amachitira kwa minkholeyo. Ndinali wopusa chotani nanga kuganizira kuti dziko linali ndi chinachake chogawira! Ndipo ndi kuwononga chotani nanga kwa nthaŵi yopindulitsa!
Kukhutiritsidwa Mosasamala Kanthu za Kukhala ndi AIDS
Ndimadziŵa kuti pali achichepere omwe ali mu mkhalidwe umodzimodziwo wonga umene ndinali, kukhumba kulandiridwa ndi mabwenzi a kudziko. Chonde, musapusitsidwe kukhulupirira kuti chomwe chinachitika kwa ine m’dziko sichidzachitika mofananamo kwenikweni kwa inu ngati munyalanyaza uphungu wa Mulungu. Misampha ya Satana ingakhale yosiyana, koma zotulukapo zimakhala zofanana nthaŵi zonse.
Komabe, ndaphunziranso kuti mosasamala kanthu za kuipa kumene mungakhalire kapena zolakwa zimene mungachite, Yehova Mulungu adzakhozabe kukuthandizani ndi kukukhululukirani ngati inu motsimikizirika mumafuna kumukondweretsa iye ndipo ngati mupita kwa iye m’pemphero lofunitsitsa.
Chirichonse chimene chingachitike kwa ine sichimandivutitsa ine kwenikweni nkomwe. Motsimikizirika, ndimapsyinjika kaŵirikaŵiri, koma ndimalaka iko mofulumira. Chinthu chokha chomwe chimandidetsa nkhaŵa tsopano chiri kukondweretsa Yehova. Iye ali magwero anga enieni a chisangalalo ndi chitonthozo. Ndimadziŵa kuti ngati ndikuchita chirichonse chomwe ndingathe kumukondweretsa iye, ndidzasamaliridwa bwino lomwe ndi kukondedwa ndi iye.
Ndiri woyamikira kwenikweni kuti ndabwerera pakati pa anthu a Yehova chifukwa ngakhale nditafa asanadzilemekeze iyemwini pa Armagedo, ndiri ndi chiyembekezo cha chiukiriro. Mvetserani kwa ine, kukhala popanda chikondi cha Yehova ndi chiyanjo kuli koipitsitsa kuposa kukhala ndi AIDS.—Yothandiziridwa.
[Mawu Otsindika patsamba 28]
Kukondedwa ndi achichepere ena kunali chovuta kwa ine