CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 11-13
Paulo Anali ndi “Munga M’thupi”
Nthawi zambiri Baibulo likamanena za munga kapena kuti minga, limanena za anthu kapena zinthu zosowetsa mtendere komanso zomwe zingavulaze munthu wina. (Num. 33:55; Miy. 22:5; Ezek. 28:24) Pamene Paulo ankalemba kuti anali ndi “munga m’thupi,” ayenera kuti ankanena za atumwi achinyengo komanso anthu ena omwe ankamusokoneza pa ntchito yake monga mtumwi. Kodi malemba otsatirawa akusonyeza zinthu zina ziti zomwe zinali ngati “munga m’thupi” kwa Paulo?
Kodi inuyo mukulimbana ndi vuto lotani?
Mungasonyeze bwanji kuti mumadalira Yehova kuti akuthandizeni kupilira?