Danani Nayo Kotheratu Njira Yochititsa Manyazi ya Dziko
“Popeza simupitirizabe kuthamanga nawo m’njira imodzimodziyo ya kusefukira kwa chitaiko, iwo akudabwa nakuchitirani mwano.”—1 PETRO 4:4, NW.
1. Ndimotani mmene Baibulo limalongosolera njira yakale ya ku dziko mu imene Akristu ambiri a m’zana loyamba anali kuthamangamo?
“KUSEFUKIRA kwa chitaiko.” Mmenemo ndi mmene mtumwi Petro akulongosolera mkhalidwe wochititsa manyazi mu umene ambiri m’zana loyamba anali asanakhale Akristu. Matembenuzidwe ena amalankhula za icho monga “chithaphwi cha kumwerekera mopambanitsa m’zosangulutsa” (The New American Bible); “malo osungira zoipa a kumwerekera m’zosangulutsa” (The New Testament, ya Kleist ndi Lilly). Nchiyani chimene chinali m’kusefukira kwa chitaiko kumeneku? Mtumwiyo akutchula mwachindunji kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosalekeka.—1 Petro 4:3, 4.
2. Nchifukwa ninji Akristu lerolino ayenera kuyamikiridwa?
2 Ndi kusiyana kotani kumene kulipo pakati pa dziko lino ndi mpingo Wachikristu wowona! Petro motentha anayamikira Akristu kwa amene anali kuwalembera chifukwa cha kusapitiriza kuthamanga ndi mabwenzi awo akale a ku dziko kupyolera m’chithaphwi chimenechi, malo osungira zoipa amenewa, a zoipa. Chimatikondweretsa ife mokulira kupereka chiyamikiro chofananacho kwa Akristu lerolino, pamene mikhalidwe iri yoipirapo kuposa mmene inaliri m’zana loyamba. Mboni za Yehova zikuika patsogolo kuyesayesa kwa luntha kuchita kulambira koyera ndi kosadetsedwa kovomerezedwa ndi Mulungu wathu ndi Atate, komwe kumaphatikizapo ‘kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.’ (Yakobo 1:27) Muyezo wapamwamba wa makhalidwe abwino umabweretsa ulemu wokulira ku dzina la Yehova.
3. Kodi nchiyani chimene chinali chopangitsa cha chisoni kwa Paulo, monga mmene chiririnso kwa ife lerolino?
3 Kuti asunge muyezo wawo wapamwamba wa makhalidwe monga gulu loyera, ngakhale kuli tero, anthu a Mulungu nthaŵi zina amayenera kudzudzula kapena ngakhale kuchotsa oŵerengeka omwe anadzilola iwo eni kunyengedwanso kuloŵa m’machitachita a kusefukira kwa chitaiko a dziko iri. Ichi chiri chopangitsa cha chisoni, ndipo timamva monga mmene mtumwi Paulo anachitira pamene anawona mkhalidwe wofananawo m’zana loyamba. Iye analemba kuti: “Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtengo wozunzirapo wa Kristu; chitsiriziro chawo ndicho kuwonongeka, mulungu wawo ndiyo mimba yawo, ulemerero wawo uli m’manyazi awo, amene alingilira za padziko.” (Afilipi 3:18, 19) Ndimotani mmene ife, monga munthu payekha, tingapeŵere chinthu choterocho kuchitika kwa ife? Mwa kuphunzira kutsanzira Yesu m’kukonda miyezo yapamwamba ya chilungamo ya Yehova ndi mwa kudana ndi kuipa kwa dziko iri.—Ahebri 1:9.
Musayang’ane M’mbuyo
4. (a) Nchifukwa ninji pali kuthekera kwa kunyengedwa kwathu kutembenukira ku machitachita oipa a dziko iri? (b) Nchiyani chimene chidzatithandiza ife kupeŵa kumangilira chikhumbo choipa?
4 Musachepetse mphamvu ya chimo. Zokoka zadziko iri ziri zamphamvu ndipo zambiri; Mdyerekezi ali wamachenjera ndi waukali; mtima wa munthu uli wonyenga. (1 Yohane 2:15-17; 1 Petro 5:8; Yeremiya 17:9) Pamene mtima ukhazikika m’chikhumbo chake kaamba ka chinachake, iwo kaŵirikaŵiri sumvetsera kuti ulingalire. Chimenecho ndicho chifukwa chake timalandira zokumbutsa zambiri m’Mawu a Mulungu kutithandiza ife kusunga mitima yathu yodzipereka kwa Yehova ndi kuchita chifuniro chake. Chiri chofunika koposa kusalola chikhumbo choipa ngakhale kuyamba kumangirira mu mtima. (Yakobo 1:14, 15; Mateyu 5:27-30) Tiyenera kupitirizabe kulimbikitsa mitima yathu ndi zifukwa zimene tiyenera kukondera chimene chiri chabwino ndi kudana kotheratu ndi kukaniratu njira zoipa zadziko iri. Mtumwi Paulo anafupikitsa ichi m’njira iyi: “Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa, gwirizana nacho chabwino.”—Aroma 12:9.
5. Nchifukwa ninji chiri chanzeru kupanga kusanthula kosamalitsa kwa zisonkhezero ndi zikhumbo zathu?
5 M’chiyang’aniro cha ngozi ya kutembenuka kuchoka ku njira ya Chikristu, chiri chanzeru kwa aliyense wa ife kupitirizabe kusanthula zisonkhezero zathu, zikhumbo zathu, zonulirapo zathu. Kodi inu mwaumwini muli monga Akristu amene Petro anali wokhoza kuwayamikira kaamba ka kusabwerera ku mkhalidwe wofananawo “kusefukira kwa chitaiko”? Kapena kodi inu pa nthaŵi zina mumasonyeza mkhalidwe wa mkazi wa Loti, yemwe anayang’ana m’mbuyo mokhumbira ku zinthu zomwe anali kupulumutsidwako?—Genesis 19:26; Luka 17:31-33.
Kuipa Kuchulukira mu “Masiku Otsiriza”
6, 7. (a) Ndi kawonedwe kotani kulinga ku zosangalatsa kamene Baibulo limanena kuti kadzazindikiritsa “masiku otsiriza”? (b) Ndimotani mmene anthu a m’dziko amasonyezera kalingaliridwe kawo koipa ndi kachitidwe?
6 Talingalirani kwa kamphindi ponena za dziko mu limene timadzipeza ife eni kumapeto kwa zana lino la 20. Ndi unyinji wotani nanga wa kuipa! Monga mmene mtumwi Paulo ananeneratu, amuna ndi akazi ali “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” Ndithudi, ‘anthu oipa ndi onyenga akuipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.’—2 Timoteo 3:1, 4, 13.
7 Chigololo, dama, kugonana kwa ofanana ziwalo, kugonana kwa akazi okhaokha, ndi kuchotsa mimba—izi ndi mawu ena akhala kalongosoledwe ka panyumba. Zinthu zoterozo zimalankhulidwa mwaufulu ndipo movomerezedwa pa wailesi ndi wailesi ya kanema ndi m’mabwalo a zipembedzo ndi maphunziro. Zithunzithunzi za maliseke ziri bizinesi yaikulu ndipo zopezeka kwa onse. Ena a makanema otchuka koposa, zitsanzo za pa platifomu, ndi maprogramu osatsa malonda a pa wailesi ya kanema amaphatikizapo nkhani zogwirizana ndi mkhalidwe wa chisembwere winawake. Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kuti sitiri mbali ya ichi! Ndipo ndi molimbika chotani nanga mmene tifunikira kumenyera kutsimikizira kuti chisonkhezero choipa choterocho sichikuyambukira mitima yathu!
8. Ponena za machitachita oipa a dziko iri, nchiyani chimene Baibulo limanena kuti tiyenera kuchita ndi chimene sitiyenera kuchita?
8 Akristu anzeru amalabadira chenjezo la Paulo: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima . . . [Pitirizani kutsimikizira chomwe chiri cholandirika kwa Ambuye, NW.] . . . potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru.” M’malomwake, Paulo ananena kuti, tiyenera kulingalira za zinthu zomwe ziri zowona, zolungama, zoyera, zokongola, ndi zomveka zokoma.—Aefeso 5:3-16; Afilipi 4:8.
9. Nchiyani chimene chingachitike ngati tisankha zosangulutsa zokaikiritsa?
9 Kodi inu mosamalitsa mumasunga m’maganizo uphungu wabwino umenewu pamene musankha zosangulutsa? Kumbukirani, utali umene timamvetsera ku zinthu zoipa, umakhalanso ukulu umene njira yamoyo ya dziko imawoneka yolandirika, osati yoipa nkomwe. Ife tingafikire pa kuyamba kukhumbira mwachinsinsi kapena kutsanzira otchuka m’maseŵera kapena zosangulutsa omwe amachita zinthu zoterozo. Khalani amaso ku chirichonse cha chikhoterero choterocho.
Musakodwe ndi Nzeru ya Dziko Lino
10. Nchiyani chimene chinali nthanthi ya moyo yochitidwa ndi Epikureya wa m’zana loyamba?
10 M’tsiku la Paulo ambiri anagonjera ku nthanthi ya Epikureya, yemwe anakhala ndi moyo kaamba ka zosangulutsa, kukhutiritsa malingaliro. Pamene imfa ikupitirirani, iwo anatero, chirichonse chimatha ku utali womwe mumayambukiridwa. Chotero bwanji osapeza zosangulutsa zonse zothekera kuchokera pamene mudakali ndi moyo, pakuti m’mawa mungafe.
11. Ndimotani mmene anthu ambiri a m’dziko lerolino amatsanzirira Epikureya m’kalingaliridwe ndi kachitidwe kawo?
11 Ambiri lerolino ali ndi kawonedwe kofananako. Iwo mopanda manyazi amadzimwerekeretsa iwo eni mu zosangulutsa za mtundu uliwonse, ndi lingaliro lochepa ponena za mmene mkhalidwe wawo umayambukirira ena. Kwa iwo, Mulungu kulibe, kapena ngati iye aliko, samapereka chitsimikiziro cha kusamalira ponena za zochita za anthu. Popeza munthu ali chotulukapo cha chisinthiko—monga mmene iwo amanenera—iwo kwenikwenidi safunikira kuyankha kwa wina aliyense kupatulapo iwo eni ndi chitaganya mu chimene iwo amakhala. Palinso chodzikhululukira kaamba ka kuchita monga zinyama. Ngati makhalidwe oipa a chisembwere amene Baibulo limatsutsa abweretsa chisangalalo ku malingaliro, motsimikizirika iwo safunikira kuletsedwa. Nchifukwa ninji kumakhala m’moyo wodzimana ndi wokwiitsidwa, anthu oterowo amalingalira, pamene tonse a ife timathera m’malo amodzimodziwo—manda?
12, 13. (a) Nchiyani chimene chiri ngozi ngati Akristu avumbulutsidwa ku kulingalira kwa kudziko? (b) Nchiyani chimene chinali muzu wa vuto mu Korinto? (c) Nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa kutichinjiriza ife ku kukhala oyambukiridwa ndi kawonedwe ka dyera ka moyo?
12 Chiri chofunikira kudziŵa kuti Akristu ena mu Korinto anawoneka kukhala anayambukiridwa ndi kalingaliridwe ka mtundu umenewu. M’kulembera ku mpingo kumeneko, Paulo anadziŵitsa kuti “ngati akufa saukitsidwa,” chotero kungakhale lingaliro lanzeru ku kalankhulidwe kofala ka m’tsikulo: “Tidye timwe, pakuti mawa timwalira.” Koma iye mwamsanga anavumbulutsa kulingalira konyenga kumeneku: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsya makhalidwe okoma. Ukani molungama ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziŵitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.”—1 Akorinto 15:32-34.
13 Dziŵani mmene Paulo akufikira ku muzu weniweni wa vuto la Akristu a ku Korinto amenewo. Kulingalira kwawo kolakwa kunabwera kuchokera ku mayanjano oipa. Tingaphunzire kuchokera ku ichi. Ngati sitiri osamalira, tingayambe kulingalira kuti tiyenera kulawako zina za zosangulutsa zoletsedwa tisanakalambe kusangalala ndi izo kapena tisanafe. Ngati tiri ndi chikhoterero china cha kulingalira m’njira imeneyi, tifunikira kusintha mwamsanga njira yathu ya kalingaliridwe. Motani? Kumbukirani kuti kawonedwe kadyera kameneka kamanyalanyaza miyezo yolungama ya Mulungu. Kamasonyeza kusoweka kwa chikhulupiriro m’malonjezo otsimikizirika a Mulungu, kuphatikizapo chiyembekezo cha chiukiriro. Ngakhale kuchokera ku kawonedwe kokhoza kugwirirapo ntchito, awo amene amakhala m’moyo wa kusefukira kwa chitaiko amabweretsa kwa iwo eni kuwawidwa mtima kwambiri ndi mavuto. Kuti apeze kayang’anidwe kolondola, iwo afunikira “kuwuka molungama.” Iwo sangalingalire molondola ndi mogalamuka ngati iwo “alibe chidziŵitso cha Mulungu.”
14. Ndani amene sadzalandira madalitso a Ufumu wa Mulungu, komabe nchiyani chimene Paulo anadziŵitsa ponena za moyo wapapitapo wa ena?
14 Kumayambiriro mu kalata yake kwa Akorinto, mtumwi Paulo anachimveketsa icho kuti adama, achigololo, olambira mafano, ogonana ofanana ziwalo, mbala, osirira, oledzera, olalatira, ndi olanda, onse amene analimo ambiri mu Korinto sadzakhala mbali ya Ufumu wa Mulungu. Iye anawonjezera kuti: “Ndipo ena a inu munali otere. Koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa.” Kuyeretsedwa kwawo m’njira imeneyi kunasonyeza mphamvu ya Mawu a Mulungu ndi nsembe ya dipo. (1 Akorinto 6:9-11) Ndithudi, kubwerera ku zodetsa za dziko lakale kukakhala ukulu wa kupusa!
15. Ndi chilankhulo chaluso chotani chimene Petro anagwiritsira ntchito kulongosola mkhalidwe wa awo amene amabwerera ku machitachita odetsedwa a dziko iri?
15 Petro ananena kuti: “Pakuti ngati adatha kuthaŵa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zawo zidzaipa koposa zoyambazo. Chidawayenera iwo cha nthanthi yowona: ‘Galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.’” (2 Petro 2:20, 22) Chinenero champhamvu! Komabe, mawu amphamvu amakhala oyenerera nthaŵi zina kusindikiza pa ife kuwopsya kwa uphungu woperekedwa. Chenjezo limeneli loperekedwa kwa Akristu m’zana loyamba liri loyenera kwambiri kwa ife lerolino.
Timatuta Zimene Tafesa
16. Ndi mwanjira zotani mmene munthu ‘amatutira zimene wafesa’ pamene akukhala ndi moyo wa kusefukira kwa chitaiko?
16 Akristu amawona mowazungulira iwo umboni wakuti njira ya moyo ya mkhalidwe woipa, wa kusefukira kwa chitaiko kwa dziko lino uli wowopsya, wakupha. (Aroma 1:18-32) M’gawo la kugonana lokha, tangolingalirani za kupweteka mtima ndi kuvutika komwe kumatulukapo pamene palibe ulemu kaamba ka lamulo la Mulungu la makhalidwe abwino: nyumba zosweka, mimba za pa thengo, kuchotsa mimba, kugwirira chigololo, kuipsya ana, ndi matenda opatsirana mwa kugonana, kokha kundandalika zinthu zochepa. Kenaka pali mavuto a umoyo omwe amabwera pamene thupi lagwiritsiridwa ntchito molakwa mwa kudya ndi kumwa mopambanitsa, ndi kutenga anamgoneka kaamba ka chisangalalo cha iwo. Kupereka njira ku umbombo kaŵirikaŵiri kumatulukapo mu kuba ndi kunyenga. Palibe kunyalanyaza lamulo la Mulungu kulikonse kumene sikumatulukapo mu kuvulazika kwina kwa kuthupi kapena kwa malingaliro kwa wolakwayo. Icho chiridi monga mmene mtumwi Paulo anakumbutsira Akristu: “Musanyengedwe: Mulungu sanyozeka. Pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa mzimu, chochokera mu mzimu adzatuta moyo wosatha.”—Agalatiya 6:7, 8.
17. Nchifukwa ninji Mkristu ayenera kusonkhezeredwa kukhala ndi moyo mwa miyezo yolungama ya Mulungu?
17 Ku mbali ina, ndi zifukwa zamphamvu zotani nanga zimene Malemba amapereka kaamba ka kusunga miyezo ya Mulungu. Ziri zowonadi chotani nanga zimene Mawu a Mulungu amanena: “Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri”! (Miyambo 28:20) Awo amene amadana ndi njira yochititsa manyazi ya dziko iri amapeŵa zotulukapo zoipa za moyo wa kusefukira kwa chitaiko. Iwo amasangalala ndi unansi wabwino ndi abale awo ndi alongo, ndi Mulungu wawo, Yehova. M’kuwonjezerapo, iwo ali ndi chiyembekezo chachikulu cha kulandira mphoto ya moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. Tsopano popeza tiri mkati mwenimweni mwa mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu, awo a “nkhosa zina” ali ndi chiyembekezo chapadera cha kukhala ndi moyo kupyola “chisautso chachikulu” ndi kusafanso. Iwo ali ndi chikhulupiriro chotheratu kuti, ngati imfa ibwera isanafike nthaŵiyo, Mulungu akulonjeza kuukitsa onse ali m’manda a chikumbukiro. (Yohane 5:28, 29; 10:16; Chivumbulutso 7:14) M’chiyang’aniro cha zonsezi, nchifukwa ninji wina aliyense akagonjera ku lingaliro longodutsa la kudziloŵetsa m’machitachita oipa a dziko iri?—Aroma 6:19-23; 1 Petro 4:1-3.
18. (a) Ndimotani mmene Yehova adzasonyezera chiŵeruzo chake motsutsana ndi “anthu osapembedza” pa “chisautso chachikulu”? (b) Ponena za chiŵeruzo, ndimotani mmene Yehova akudzilongosolera iyemwini m’mawu ake omalizira olembedwa m’Baibulo?
18 Baibulo mwachiwonekere limasonyeza kuti tikukhala m’mbali yomalizira ya chimene chimatchedwa “mapeto a dongosolo la kachitidwe ka zinthu.” (Mateyo 24:3, NW) Petro ananena kuti “koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika ku moto, zosungika kufikira tsiku la chiŵeruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” (2 Petro 3:7) Pamene tsiku loyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali limeneli lidzawonekera, kudzinenera kwakuti munthu angachite osadalira Mulungu ndipo kuti mkhalidwe wake woipa, wa chiwawa uli chabe chotulukapo cha chisinthiko zidzapita mu utsi m’mwamba. (Akolose 3:5, 6) Mvetserani mmene Mulungu iyemwini akulongosolera, m’mawu ake olembedwa omalizira m’Baibulo, zotulukapo kwa awo amene amatumikira iye ndi awo amene satero: “Tawonani! Ndidza msanga; ndipo mphoto yanga ndiri nayo yakupatsa yense monga mwa ntchito yake. . . . Odala iwo amene atsuka miinjiro yawo, kuti akakhale nawo ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akaloŵe mu mzinda pazipata. Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.”—Chivumbulutso 22:12-15.
19. Nchiyani chimene chiyenera kukhala chigamulo chathu pamene tikuyang’anizana ndi mtsogolo?
19 Pamene mikhalidwe yoipa ya dziko iri ikuipirabe, khalani olimba kugamulapo kukondweretsa Yehova mwa kuchita zimene ziri zoyera, zolemekezeka, ndi zolondola. Pitirizanibe kufikira mphoto ya moyo. Kanani kukokedweranso mu “kusefukira kwa chitaiko” kwa dziko iri, komwe kuli dzenje la imfa. Mungapambane mu nkhondo yolimbana ndi kulingalira kwa kusefukira kwa chitaiko ngati mudana nayo kotheratu njira yochititsa manyazi ya dziko iri!
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Nchifukwa ninji pali ngozi ya kudziloŵetsa m’machitachita ochititsa manyazi a dziko iri?
◻ Nchifukwa ninji tifunikira kukhala osamalira m’kusankha zosangulutsa?
◻ Ndi kulingalira kwa kupha kotani kumene mopepuka kungatisonkhezere ife ngati tiyanjana ndi a Epikureya amakono?
◻ Nchiyani chimene chiri chiŵeruzo cha Yehova motsutsana ndi awo amene mosalapa amatembenukira ku njira yochititsa manyazi ya dziko iri?
◻ Ndi madalitso otani amene ali kutsogolo kwa awo amene amadzipatula kuchokera ku mkhalidwe woipa wa dziko iri?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Kudana nayo kotheratu njira yochititsa manyazi ya dziko iri kudzathandiza atumiki a Mulungu kupeza choloŵera m’dziko latsopano lolungama
[Chithunzi patsamba 18]
Zosangulutsa zochititsa manyazi za dziko zinganyenge Akristu osakhazikika