Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Malinga ndi Agalatiya 6:8, “wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa mzimu, chochokera mu mzimu adzatuta moyo wosatha.” Kodi ndi “mzimu” uti umene ukutanthauzidwa, ndipo tingatute motani moyo mwa uwo?
Mawu a Chihebri ndi Chigiriki amene amasuliridwa kuti “mzimu” ali ndi matanthauzo osiyanasiyana, onga: (1) mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, (2) mphamvu ya moyo imene ili mwa anthu kapena nyama, (3) mphamvu yosonkhezera maganizo a munthu, ndi (4) munthu wauzimu, kapena mngelo. Loyamba mwa ameneŵa—mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu—ndilo tanthauzo limene timapeza pa Agalatiya 6:8.
Monga momwe nkhaniyo ilili, onani Agalatiya 3:2, pamene tipeza kuonekera koyamba kwa “mzimu” m’buku la Agalatiya. Paulo anafunsa Akristu kuti: “Kodi munalandira mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?” Ndiyeno, pa Agalatiya 3:5, anagwirizanitsa “mzimu” umenewo ndi kuchita ntchito zamphamvu. Chotero “mzimu” umene anatchula unali mzimu woyera, mphamvu yogwira ntchito yosaoneka ya Mulungu.
Pambuyo pake, pa Agalatiya 5:16, Paulo anasiyanitsa mzimu ndi thupi. Timaŵerenga kuti: “Ndinena, Muyendeyende ndi mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.” Mwa kunena kuti “chilakolako cha thupi” iye anatanthauza thupi la munthu lochimwa. Motero, pa Agalatiya 5:19-23, anandandalika “ntchito za thupi” mosiyana ndi “chipatso cha mzimu.”
Chifukwa chake, pa Agalatiya 6:8, munthu “wakufesera kwa thupi” ayenera kukhala uja amene amalola zilakolako zaumunthu zauchimo kumtsogolera, akumachita “ntchito za thupi.” Iye angakumane ndi zotulukapo zovunda za khalidwe lotero, ndipo ngati sasintha, iye sadzapeza moyo konse mu Ufumu wa Mulungu.—1 Akorinto 6:9, 10.
Monga Akristu odzipereka tiyenera kulakalaka ‘kufesera kwa mizimu wa Mulungu.’ Zimenezo zimaloŵetsamo kukhala ndi moyo mwa njira imene imalola mzimu woyera kugwira ntchito momasuka m’moyo wathu, ukumatithandiza kusonyeza chipatso chake. Tiyenera kukumbukira zimenezo pamene tikusankha zimene tiyenera kuŵerenga kapena maprogramu apawailesi yakanema amene tiyenera kupenyerera. Timafesera kwa mzimu pamene titchera khutu pamisonkhano yampingo ndi kuyesayesa kugwiritsira ntchito uphungu wa akulu oikidwa ndi mzimu.—Machitidwe 20:28.
Nkokondweretsa kuti Agalatiya 6:8 amamaliza ndi lonjezo lakuti pamene tifesera mogwirizana ndi mzimu woyera, tidzakhala pamzera wa ‘kututa moyo wosatha [mwa mzimu, NW].’ Inde, mwa dipo la Kristu, Mulungu adzapereka moyo wosatha mwa kugwira ntchito kwa mzimu woyera.—Mateyu 19:29; 25:46; Yohane 3:14-16; Aroma 2:6, 7; Aefeso 1:7.