Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 9/1 tsamba 29-31
  • Kodi Mudzapitirizabe Kuyenda m’Chowonadi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mudzapitirizabe Kuyenda m’Chowonadi?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Londolani Chitsanzo cha Yesu
  • Tsanzirani Mtumwi Paulo
  • Mamiliyoni Akukonzekera Kukhala ndi Moyo m’Paradaiso
  • Samalirani Thanzi Lanu Lauzimu
  • Kodi Mukupirira?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Musaleme Kuthamanga Makani a Moyo!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Chitirani Umboni Yehova Ndipo Musaleme
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 9/1 tsamba 29-31

Kodi Mudzapitirizabe Kuyenda m’Chowonadi?

“NDIRIBE chimwemwe choposa ichi, chakuti . . . ana anga . . . alikuyenda m’chowonadi.” (3 Yohane 4) Anatero mtumwi Yohane chakumapeto kwa moyo wake wautali. Chipiriro chopitirizabe cha ‘ana ake,’ awo amene anawadziŵitsa “chowonadi,” chinamdzetsera chisangalalo chachikulu. Yehova nayenso amakondwera pamene alambiri ake akhalabe m’chowonadi. Ayenera kukhala wokondwera chotani nanga lerolino pamene awona gulu lalikulu, lofika m’chiŵerengero cha mamiliyoni, likutsatira njira yanzeru imeneyo!​—Miyambo 27:11.

Komabe, pamene kuli kwakuti anthu a Mulungu monga gulu akumamatira kuchowonadi mosagwedezeka, Akristu alionse paokha akubwerera m’mbuyo ngakhale kusiya kulambira kowona. Izi sizosayembekezereka, popeza kuti zofananazo zinachitika m’zaka za zana loyamba. (2 Timoteo 4:10; Ahebri 2:1) Komabe, chenicheni chakuti ena akubwerera m’mbuyo chimagogomezera kufunika kwakuti onse asumike maganizo pamkhalidwe wawo wauzimu. Paulo analimbikitsa Akristu onse kuti: “Dziyeseni nokha.” (2 Akorinto 13:5) Mkristu aliyense ayenera kudzifunsa funso lakuti: ‘Kodi ndingatsimikizire motani kuti ndidzapitirizabe kuyenda m’chowonadi?’

Ena abwerera m’mbuyo kapena kuleka kuyenda m’chowonadi chifukwa chakuti analefulidwa​—mwinamwake ndi mavuto a thanzi, kapena kuwombana kwa maumunthu. Ena abwerera m’mbuyo chifukwa chakuti anacheutsidwa. Akufuna kusangalala ndi zokondweretsa za dongosolo lazinthu liripoli lisanathe. Kodi tingapeŵe motani kubwerera m’mbuyo? Kuti tiyankhe, tiyeni tipende chitsanzo chimene Yesu anatisiyira.

Londolani Chitsanzo cha Yesu

Yesu anayang’anizana ndi mikhalidwe yovuta kwambiri. Iye anafunikira kusamalira kuwombana kwa maumunthu pakati pa otsatira ake, limodzinso ndikupirira udani ndi kusekedwa ndi adani ake. Anafunikiranso kulimbana ndi ziyeso za dziko lino. Ndithudi, anapatsidwa chuma ndi kutchuka pamlingo wapamwamba umene oŵerengeka okha akhala nazo. (Mateyu 4:8-11; Yohane 6:14, 15) Komabe, Yesu anaumirirabe kuyenda m’chowonadi. Kodi nchiyani chimene chinamthandiza kuchita motero?

Mtumwi Paulo akutiwuza pamene akulemba kuti: “Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:1, 2) M’chochitika cha Yesu, kukumbukira “chimwemwe choikidwacho pamaso pake,” mphotho zapamwamba zomuyembekezera, kunamthandiza kupitirizabe kuyenda m’chowonadi. “Chimwemwe choikidwacho pamaso pake” chinaposa kwambiri zolefula kapena zocheutsa zakanthaŵi zimene anafunikira kuyang’anizana nazo.

Kusumika maganizo pa mphothoyo kungatithandize kupirira, monga momwe kunachitira Yesu. (Chivumbulutso 22:12) Kufotokoza mwafanizo, talingalirani woyenda panjira yovuta yapaphiri. Iye akutopa ndipo akulefulidwa. Sitepi lirilonse lichitidwa mwakuyesayesa, ndipo njirayo ikuwonekera kukhala yosatha. Kenaka afika pamwamba ndikuyang’ana chakutali kutsogolo nawona tauni limene akupitako. Mwadzidzidzi ulendowo ukhala wosavutirapo. Kuwonekera bwino kwa malo amene amkako kukumthandiza kuiŵala kutopa kwake. Mofananamo Mkristu adzakupeza kukhala kosavutirapo kupitirizabe kuyenda m’chowonadi ngati asumika maganizo pa malo amene akumkako.

Tsanzirani Mtumwi Paulo

Wina amene anapirira zambiri zimene zikanamlefula anali mtumwi Paulo. Iye anafunikira kulaka mipatuko ndi kuwombana kwa maumunthu pakati pa abale, limodzinso ndi kupirira vuto lowopsa lathanzi, chizunzo, mavuto akuthupi, ndi zothetsa nzeru zina ndipo ngakhale chitsutso chochokera mkati mwa mipingo. (1 Akorinto 1:10; 2 Akorinto 10:7-12; 11:21-29; 12:7-10) Kodi nchifukwa ninji Paulo sanalefulidwe kufikira pamlingo wakuleka? Iye akufotokoza kuti: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Iye sanayese kusenza nkhaŵa zake yekha. Mmalo mwake, Paulo anayang’ana kwa Yehova kumchirikiza.​—Salmo 55:22.

Magwero aumulungu a nyonga amene Paulo anapempha kumthandiza kupirira aliponso ndi lerolino. Baibulo limati: “[Yehova] alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziwombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” (Yesaya 40:29-31) Ngati tiyang’ana kwa Yehova kuti atipatse nyonga kupyolera mwa phunziro laumwini, kufika pamisonkhano, ntchito Zachikristu zachangu, ndipo​—makamaka​—pemphero, tidzakhoza kupirira ziyeso ndi zolefula zimene zingabwere panthaŵi ndi nthaŵi.​—Salmo 1:1-3; Aroma 10:10; 1 Atesalonika 5:16, 17; Ahebri 10:23-25.

Mamiliyoni Akukonzekera Kukhala ndi Moyo m’Paradaiso

Satana ndiye mulungu wa dongosolo la zinthu liripoli, m’limene Akristu ali chabe alendo, alendo ogonera. (2 Akorinto 4:4) Chifukwa chake, sitiyenera kudabwa ngati nthaŵi zina tiyang’anizana ndi zolefula kapena zocheutsa. Paulo analemba m’bukhu la Ahebri kuti: “Pakuti pano tiribe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.” (Ahebri 13:14) Kukumbukira kuti chiyembekezo chathu sichiri m’dziko lino lakale koma m’limene lirinkudzalo kumatithandizanso kusabwerera m’mbuyo.

M’njira zina, Akristu ali ofanana ndi osamuka amene amachoka m’dziko lakwawo kukafunafuna moyo wabwinopo kwinakwake. Mwachibadwa, kutero ndiko chinthu chovuta kuchita. Kumaphatikizapo kupachira katundu kapena kutaya katundu wake wonse ndikutsazikana ndi nyumba yozoloŵereka, limodzinso ndi mabwenzi ndi achibale. Kumaphatikizaponso kupita kudziko lachilendo, kukakhala pakati pa anthu amene mwina sangamlandire, ndikuphunzira chinenero chatsopano ndi umoyo wosazoloŵereka. Komabe, ambiri amapanga kusamuka koteroko kokha kuti ayembekezere kuwongolera mkhalidwe wawo wakuthupi m’dziko lino.

Awo amene amasamuka, kunena kwake titero, kusiya dongosolo la zinthu liripoli ndikukhala mbali ya anthu a Mulungu amayang’anizana ndi zitokoso zofananazo. Iwo amapanga masinthidwe a njira ya moyo kuti agwirizane ndi miyezo yoyera ya Mawu a Mulungu, ndipo amaphunzira “lirime loyera” la chowonadi. (Zefaniya 3:9; 1 Akorinto 6:9-11) Ndiponso, amagwira ntchito zolimba, kutumikira mfumu yaikulu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu Kristu. Ndiponso, m’zochitika zambiri achibale awo ndi mabwenzi awo akale amawakana, kotero kuti, mchenicheni amafunikira kuwatsazika.

Komatu Akristu amapeza mapindu ochuluka kuposa amene amasamukira zifukwa zachuma. Choyamba, iwo amaloŵa m’chitaganya chimene chimawakonda ndi kuwasamalira. (Luka 18:29, 30) Chofunika kwambiri, amaloŵa mu unansi wathithithi ndi Yehova, Mulungu wa chilengedwe chonse. Amapeza mtendere wamaganizo ndi chidaliro ponena zamtsogolo pamene ayang’ana mtsogolo kukukwaniritsidwa kwa malonjezo abwino koposa a Mulungu. (Afilipi 4:8, 9) Amene amamvetsetsa bwino lomwe mfundo zimenezi sadzalola zocheutsa kapena zolefula kuwabwezera m’mbuyo kwachikhalire. Sadzapambutsidwa panjira yopapatiza imene itsogolera kumoyo.​—Mateyu 7:13, 14; 1 Yohane 2:15-17.

Samalirani Thanzi Lanu Lauzimu

Ngati tisamalira thanzi lathu lakuthupi pamaziko okhazikika, timakhala ndi kuthekera kwakukulu kulaka matenda. Ndipo ngati tidwala, timachira mofulumirapo. Mofananamo, ngati tisamalira thanzi lathu lauzimu, kusumika maganizo athu pamadalitso amene timasangalala nawo tsopano ndi mtsogolo, ndipo ngati tiphunzira kudalira panyonga ya Yehova mmalo mwa yathu, tidzakhala okhoza bwinopo kusamalira mavuto amene amabuka. Sitingapeŵe kotheratu mikhalidwe yocheutsa ndi yolefula. Koma ngati tasamalira thanzi lathu lauzimu bwino lomwe pasadakhale, zinthu zoterozo sizidzatigonjetsa.

Kumbukukirani, Yehova amasangalala pamene alambiri ake apirira. Chotero tikondweretsetu mtima wake mwakupitirizabe kuyenda m’chowonadi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena