Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 2/1 tsamba 4-7
  • Kukongola Kowona—Mungakukulitse Iko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukongola Kowona—Mungakukulitse Iko
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusintha kwa Umunthu
  • Mikhalidwe Yachikristu
  • Kukongola m’Dziko Loipa
  • Kukulitsa Kukongola kwa Mkatikati
  • Dziko Lokongola Kutsogolo
  • Kukongola Kungakhale Kokha kwa pa Khungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kukongola Kofunika Kwambiri
    Galamukani!—2005
  • Kusatengeka ndi Mafasho
    Galamukani!—2003
  • Kukongola
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 2/1 tsamba 4-7

Kukongola Kowona​—Mungakukulitse Iko

BAIBULO liri ndi uphungu kaamba ka ponse paŵiri amuna ndi akazi mu nkhani ya kuwoneka bwino. Kwa amuna, ilo limadziŵitsa kuti: “[Kukongola, NW] kwa anyamata ndiko mphamvu yawo.” (Miyambo 20:29) Inde, mphamvu ndi thanzi la anyamata lingakhale lokhumbirika kwambiri. Koma kodi nchiyani chomwe chimachitika pamene thanzi la uchichepere limenelo lizimiririka? Mwambo wa Baibulo ukunena kuti: “Imvi ndiyo korona wa ulemerero idzapezedwa m’njira ya chilungamo.” (Miyambo 16:31) Chilungamo chiri mbali ya kukongola kwa mkatikati. Ngati mwamuna wachichepere achikulitsa icho, chidzakhalapobe pamene iye ataikiridwa thanzi lokongola lija la uchichepere.

Ponena za akazi Baibulo limanena kuti: “Kukongola kungonyenga, mawonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi wowopa Yehova adzatamandidwa.” (Miyambo 31:30) Mkazi wachichepere wa mawonekedwe abwino, wokongola ali bwenzi losangalatsa. Koma bwanji ngati pali chinyengo ndi uchabe wadyera wobisala kumbuyo kwa kukongola kwa kuthupiko? Kenaka kukongolako kuli kokha kwa pa khungu, ndipo kumabisa kuipa kwa mkati. Pamene kukongolako kutha, kodi nchiyani chomwe chidzasiidwa? Ndi chabwinoko chotani nanga ngati kuwoneka bwino kugwirizana ndi kukongola kosazimiririka kwa mkati, kozikidwa pa ‘kuwopa Yehova’!

Kusintha kwa Umunthu

Kodi chiri chothekera kukulitsa kukongola kwa mkatikati kumeneku? Inde. M’chenicheni, kwa Akristu, icho chiri chofunikira kuchitidwa. Mulungu amaŵerengera kukongola kowona. “Iye wapanga chirichonse kukongola mu nthaŵi yake.” (Mlaliki 3:11, Revised Standard Version) Iye sadzalandira kulambira kwa awo amene mkhalidwe wawo umabisa mikhalidwe yosakondeka ya mkati.

Mawu a mtumwi Paulo kwa Akolose amatanthauza kufunika kwa kukulitsa kukongola kwa mkatikati. Choyamba, iye akulangiza kuti: “Tayani inunso zonsezi, mkwiyo, kupsya mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m’kamwa mwanu. Musamanamizana wina ndi mnzake. Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.” Inde, aliyense yemwe amachita zinthu zoipa zimenezo ali wonyansa kwa Mulungu​—ndi kwa anthu olingalira molondola. Kenaka, Paulo akupitiriza kuti: “Dzivekeni inu eni ndi umunthu watsopano, umene kupyolera mwa chidziŵitso cholongosoka ukupangidwa kukhala watsopano mwa chifaniziro cha Iye amene anaulenga.” (Akolose 3:8-10, NW) Tiyenera ‘kuvala’ njira ya kuganiza ndi kudzimva komwe kumagwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kodi nchiyani chomwe chimazindikiritsa “umunthu watsopano” umenewu?

Mikhalidwe Yachikristu

Baibulo limandandalitsa mikhalidwe yokongola yambiri yomwe imapanga iwo. Koma maziko kaamba ka kukongola kwa mkatikati kumeneku akulongosoledwa m’mawu a Yesu akuti: “‘Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.’ Iri ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri, lolingana nalo, ndi iri, ‘Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.’” (Mateyu 22:37-39) Chikondi cha Mulungu chimatitsogolera ife kufuna kukhala mtundu wa anthu omwe amamukondweretsa iye. Chikondi choterocho chimatisonkhezera ife kulankhula ponena za iye kwa ena, kuwathandiza iwo, m’kubwezera, kudziŵa Mlengi wawo.​—Yesaya 52:7.

Mikhalidwe ina yomwe imapanga umunthu watsopano yalongosoledwa ndi mtumwi Paulo: “Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso. Pokana zimenezi palibe lamulo.”​—Agalatiya 5:22, 23.

M’kuwonjezerapo, Baibulo limanena mwachindunji kwa amuna kuti: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW] . . . Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda [mpingo, NW] nadzipereka yekha m’malomwake.” (Aefeso 5:23, 25) Ndipo kwa akazi, Baibulo limanena kuti: “Akazi inu mverani amuna anu a inu eni monga kumvera Ambuye . . . Mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.” (Aefeso 5:22, 33) Umakhala moyo wabanja wokhumbirika chotani nanga pamene mwamuna akwaniritsa mathayo ake mu mkhalidwe wachikondi, wopanda dyera, ndi woleza mtima! Ndipo chimakhala chopepuka chotani nanga kwa mwamuna kukwaniritsa thayo lake molondola pamene mkazi avumbula kukongola kwake kwa mkatikati mwa kumuchirikiza iye mwachikondi ndipo osati kukhala wopikisana kapena wosuliza mopambanitsa. Moyo wa banja wokhala pansi pa mikhalidwe yoteroyo ungakhale wokondweretsa mowonadi.

Zitsanzo zogwidwa mawu m’nkhani yapitayo zasonyeza ina ya mikhalidwe imeneyi ikugwira ntchito. Mtsikana wa chiSulami anasonyeza chikondi chokhazikika ndi chakuya kaamba ka mnyamata wake wachibusa pamene mkaziyo anakana kumusiya iye kaamba ka kukongola kwa mabwalo a Solomo. Yosefe anasonyeza ubwino wamkati pamene iye anakana kuchimwa molimbana ndi mbuye wake, Potifa. Iye anasonyezanso kudziletsa pamene anathaŵa m’malo mwa kunyengedwa ndi mkazi wa Potifa. Ndipo iye anasonyeza chitsanzo cha kudzichepetsa, mtendere, ndi kuleza mtima pamene iye anakana kulola zochitika zoipa zambiri m’moyo wake kumukwiyitsa.

Kukongola m’Dziko Loipa

Kodi mikhalidwe yokongola yoteroyo iri yogwira ntchito lerolino? Ena amaganiza kuti ayi. M’malomwake, iwo amayankha ku dziko lodzifuna lokha, lowumirira mu limene iwo amakhala mwa kukulitsa mbali yolimba. Iwo amadzimva kuti ngati ati apulumuke iwo ayenera kukhala osalamulirika, onkitsa, kutenga zoyambirira ndi kugwiririra ku chirichonse chimene iwo angapeze.

Mosiyanako, Baibulo limalimbikitsa kuti: ‘Musachite kanthu monga mwa chotetana kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima yense ayese mnzake womposa iyemwini, munthu yense asapenyerere, zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.’ (Afilipi 2:3, 4) Chiri chifukwa chakuti mtundu wa anthu mwachisawawa sumatsatira uphungu wabwino umenewu chimene chitaganya cha munthu chikuzimiririka moipa.

M’kuwonjezerapo, m’dziko lamakono, kupambana kwa munthu kumayesedwa ndi ndalama kapena malo. Munthu wolemera amalingaliridwa kukhala munthu wachipambano. Ngakhale kuli tero, malinga ndi mmene mapindu enieni aliri okhudzidwa, nchosafunika kotheratu kaya winawake ndi wolemera kapena wosauka. Ndithudi, chuma chiri ndi ngozi zake. Baibulo limachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka.” Ilo likuwonjezera kuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

Ndithudi, anthu omwe ali adyera, ogwiririra, okonda zakuthupi, ndi osalamulirika kaŵirikaŵiri amasangalala ndi “chipambano” chosakhalitsa lerolino. Koma ichi sichiri chipambano chenicheni, popeza kuti zotaika za njira yoipa ya kukhala ndi moyo yoteroyo​—kusatchuka kwaumwini, maukwati osweka, umoyo wa matenda, ndi kukhumudwitsidwa kwa chisawawa​—kuli kokulira kwenikweni. Munthu anapangidwa m’chifanefane cha Mulungu, koma pamene iye aukira mwachiwawa chotero molimbana ndi mikhalidwe imene Mulungu poyambirirapo anaika mwa iye, iye sangakhoze nkomwe kufikiritsa chimwemwe chaumwini.​—Genesis 1:27.

Kukulitsa Kukongola kwa Mkatikati

Ndimotani mmene ife, chotero, tingatsutsire chisonkhezero choipa cha dziko iri ndi kukulitsa mikhalidwe yoyenera, yaumulungu? Pamene Paulo anandandalitsa mikhalidwe ya ‘chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso,’ iye anazitcha izo kukhala “chipatso cha mzimu.” (Agalatiya 5:22, 23) Chotero mzimu wa Mulungu uli woyenerera ngati titi tikulitse mikhalidwe ya mkatikati yokongola imeneyi.

Motani? Chabwino, kuphunzira Baibulo, lomwe linauziridwa kupyolera mwa mzimu wa Mulungu, kudzatithandiza ife kuzindikira mikhalidwe imeneyi ndi kulimbitsa chikhumbo chathu cha kukulitsa iyo. (2 Timoteo 3:16) Mboni za Yehova ziri zachimwemwe nthaŵi zonse kuthandiza mu ntchito yoteroyo, popeza kuti izo zimaiwona iyo kukhala mbali ya utumiki wawo kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo. Kudzisanthula kwaumwini kowona mtima kudzatitheketsa ife kuwona pomwe timalephera, ndipo tingapempherere kaamba ka thandizo la mzimu wa Mulungu m’mbali zimenezi. Kuyanjana ndi alambiri anzathu a Mulungu kudzapereka chirikizo la anzathu lomwe timalifunikira, ndipo pano, kachiŵirinso, mzimu wa Mulungu umathandiza chifukwa chakuti, monga mmene Yesu ananenera, “kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndiri komweko pakati pawo.”​—Mateyu 18:20.

Dziko Lokongola Kutsogolo

Mwachibadwa, palibe ndi mmodzi yense wa ife yemwe adzalaka kotheratu kupanda ungwiro kwathu, koma ngati tikalamira kukulitsa kukongola kwa mkatikati kumeneku, Mulungu adzadalitsa zoyesayesa zathu. Ndipo adzatifupa ife m’njira yodabwitsa. Baibulo limandandalitsa kaamba ka ife chifuno cha Mulungu cha kubweretsa mwamsanga dongosolo latsopano la zinthu lomwe lidzakhala losiyana kotheratu ndi lomwe liripo. Mu ilo, “olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Yesu iyemwini ananena kuti: “Odala ali akufatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.”​—Mateyu 5:5.

Pa nthaŵi imeneyo, kupikisana kosakondweretsa ndi dyera la dongosolo lino la zinthu kudzaloŵedwa m’malo ndi bata lokongola ndi mtendere. “Sizidzaipitsa sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Ndithudi, Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro kapena kulira, kapena chowawitsa. Zoyambazo zapita.”​—Chibvumbulutso 21:4.

Kodi mikhalidwe yoteroyo ikumveka yosangalatsa? Iyo iri yothekera chifukwa chakuti nzika zadziko lapansi za pa nthaŵiyo zidzakhala ndi kukongola kwa mkatikati kozikidwa pa chikondi cha Mulungu ndi cha mnansi. Ndipo Mulungu walonjeza kuti awo omwe akumtumikira iye tsopano, kukulitsa “umunthu watsopano” ndi kukalamira zolimba kutsatira miyezo yake, adzawona kuzindikiridwa kwa lonjezo limenelo. Kuwoneka bwino, kukongola kwakuthupi, sikungabweretse nkomwe madalitso oterowo. Chotero, ndi chifukwa chabwino chotani nanga, cha kukulitsira kukongola kwa mkatikati kumeneko kolemerera, kosatha komwe kuli kosangalatsa chotero kwa anthu oganiza molondola ndi kwa Mulungu iyemwini!

[Chithunzi patsamba 6]

Anthu okongola mwakuthupi ayenera kupewa kukhala adyera ndi osonkhezera molakwa. M’malomwake, iwo ayenera kukulitsa kukongola kwa mkatikati komwe kumakondweretsa Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena