Chifukwa Chake Ziyenera Kukambidwa
“Chitsulo chinola chitsulo; Chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.”—Miyambo 27:17, Baibulo.
MIPENI sinoleka mwakumangoiwombanitsa. Pamafunika kuinola pang’onopang’ono kuti inoleke. Chimodzimodzinso ndi anthu, pali njira zabwino ndi zoipa zonolera malingaliro mwakukambirana, makamaka pankhani zovuta ngati chipembedzo.
Choyamba, tiyenera kulemekeza kaye munthu winayo ndiye n’kusonyeza ulemu umenewo m’mawu ndi muzochita. “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa,” limatero Baibulo. (Akolose 4:6) Mawu onenedwa mokoma ndi okoleretsa sakhala olamula, ngakhale pamene wonenayo akudziŵa kuti akunena zoona ndi kuti winayo akulakwa.
Tingasonyezenso kukoma mtima malinga ndi momwe timamvetserera. Sitingakhale tikumvetsera mokoma mtima ngati tidula mawu kapena ngati tikumvetsera koma kwinaku tikuganizanso mfundo ina yotsutsa. N’zosakayikitsa kuti amene akulankhulayo adzazindikira kuti sitikusamala zimene akunena ndipo mwina adzangoleka. Komanso sitiyenera kukakamiza kapena kukalipira munthu kuti asinthe maganizo ake. Komanso, osaiŵala kuti ndi ‘Mulungu amene amapangitsa choonadi kukula’ mumtima mwa womvetserayo.—1 Akorinto 3:6.
Tili ndi chitsanzo chabwino cha mtumwi Paulo, amene ankagwiritsa ntchito “kukambitsirana” ndi ‘kukopa’ mu utumiki wake. (Machitidwe 17:17; 28:23, 24) Paulo ankakambirana ndi anthu za chipembedzo kulikonse kumene ankawapeza, monga ngati kumsika ndiponso pa nyumba zawo. (Machitidwe 17:2,3; 20:20) Mboni za Yehova zimayesetsa kutsanzira chitsanzo chimenecho mwa kupita kumene anthu angapezeke ndi kukambirana nawo za m’Malemba.
Pewani Kusamvetsetsa
Mtundu wa Aisrayeli unali utangokhazikika kumene m’Dziko Lolonjezedwa pamene panabuka kusamvetsetsana pankhani ya guwa la nsembe ndipo nkhondo yapachiweniweni inali pafupi kuyambika. Anthu okhala tsidya lina la Mtsinje wa Yordano anamanga guwa, koma mitundu inayo inalingalira molakwa kuti linali guwa la chipembedzo chonyenga. Choncho anakonzekera nkhondo kuti alange abale awo. Komabe anachita zinthu mwanzeru. Gulu limene linkafuna kukathira anzawo nkhondolo linatumiza kaye nthumwi kukafunsa chifukwa chake anamanga guwa la nsembe. Iwo anasangalala kumva kuti guwalo linali chabe chikumbutso—“mboni”—kukumbutsa mitundu yonse kuti ndi ogwirizana mwa Yehova Mulungu. Kukambiranako kunatetezera kuti pasachitike nkhondo—ndipo miyoyo yambiri inatetezeka!—Yoswa 22:9-34.
Chimodzimodzinso, kusagwirizana lerolino kumabutsa chidani ndi tsankho. Mwachitsanzo, anthu ena pang’ono amaona Mboni za Yehova monga anthu oumirira zachipembedzo mosalingalira bwino chifukwa cha malipoti akuti amakana magazi. Koma amene anafunsapo Mboni pankhani imeneyi anasangalala ndiponso kudabwa kuti zimenezi zinalembedwa m’Baibulo, ndi kutinso pali njira zina, zothandiza zimene zingagwiritsidwe ntchito. (Levitiko 17:13, 14; Machitidwe 15:28, 29) Chifukwa chakuti magazi sanali kupezeka, wolemba nkhani wina anati: “Tiyamika Mulungu chifukwa Mboni za Yehova zakhala patsogolo pakufufuza njira zina zoti n’kugwiritsa ntchito m’malo mwa magazi.”
Komanso, ena amakana kulankhula ndi Mboni chifukwa chakuti anauzidwa kuti Mboni za Yehova sizikhulupirira Yesu Kristu. Limeneli ndi bodza lalikulu kwambiri! Kunena zoona, Mboni zimanenetsa kuti Yesu ndi wofunika kwambiri pachipulumutso chathu, zikumalongosola kuti ndi mwana wa Mulungu, amene Mulungu anam’tuma kudziko lapansi monga dipo la anthu ku uchimo ndi imfa. Mwakulankhula ndi Mboni pa nkhaniyi, ena amamvetsetsa bwino ndi kusiya malingaliro olakwika amene anali nawo.—Mateyu 16:16; 20:28; Yohane 3:16; 14:28; 1 Yohane 4:15.
Choonadi—N’chotchuka Kapena N’chosatchuka?
Chimadabwitsa anthu ambiri n’chakuti pankhani ya chipembedzo, chomwe chimakhala chotchuka ndichonso chimakhala cholakwika. Yesu Kristu iye mwiniyo anaphunzitsa kuti: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”—Mateyu 7:13, 14.
M’tsiku la Nowa, anthu asanu ndi atatu okha ndiwo amene ankalankhula choonadi—Nowa, mkazi wake, ana ake aamuna atatu, ndi akazi awo. Chenjezo limene ankapereka ndiponso ntchito yawo yomanga chingalawa mosakayikira inapangitsa kuti anthu aziwanena, mwina kuwanyoza. Komabe Nowa ndi banja lake sanaope; anapitiriza kulalikira ndi kumanga. (Genesis 6:13,14; 7:21-24; 2 Petro 2:5) Chomwechonso, ndi anthu atatu okha anamvera malangizo a Mulungu ndipo anapulumuka chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora.—Genesis 19:12-29; Luka 17:28-30.
Bwanji za nthaŵi yathu? Mwininyumba wina pouza wa Mboni za Yehova wina anati, “Kristu akanabwera n’thupi laumunthu lerolino, anthu akanamuphanso.” Munthu ameneyu ankaona kuti chiphunzitso cha Yesu ndi makhalidwe ake apamwamba akanakhala osakondweretsa kwenikweni lero monga anali zaka 2,000 zapitazo. Kodi mukuvomereza?
Ngati n’choncho, mukukhoza, chifukwa Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.”—mawu amenewa akuoneka kukhala oona. (Mateyu 24:9) Atsogoleri a Chiyuda ku Roma anauza Paulo ponena za Chikristu kuti: “Pakuti za mpatuko uwu . . . , aunenera ponse ponse.” (Machitidwe 28:22) Komabe kusakondedwa kwa Chikristu sikunalepheretse otsatira Kristu kulalikira zikhulupiriro zawo kwa ena. Komanso sikunalepheretse oona mtima kulankhula ndi Akristu.—Machitidwe 13:43-49.
Uthenga wa Yesu lerolino ndi wofunika kuposa kale lonse. Chifukwa? Chifukwa zochitika za dziko zimasonyeza kuti tsopano tikukhala “m’masiku otsiriza” a dongosolo ili la zinthu ndi kuti masiku ano adzafika pachimake pamene kuipa kudzachotsedwa padziko lapansi. Yesu anayerekezera nthaŵi yathu ndi masiku a Nowa. (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:37-39) Choncho iyi si nthaŵi yomangokhulupirira zinthu osafufuza, chifukwa omwe adzalandire moyo wosatha ndi okhawo amene amadziŵa Mulungu ndi amene ‘amam’lambira mumzinu ndi m’choonadi.’—Yohane 4:24; Atesalonika 1:6-9.
Mmene Tingapezere Njira Yolongosoka
Francis Bacon, filosofa wachingelezi wolemba nkhani, woweruza, ndiponso wolamulira wa m’zaka za zana la 17, analangiza omwe amafunafuna choonadi kuti ayenera “kumalingalira bwino mokhazikika.” Thomas Jefferson, amene anali pulezidenti wa U.S., anati: “Kufufuza ndi kuona zifukwa zake mosakondera ndiko kokha kungapangitse kuti mupewe cholakwika. . . . Izo ndizo adani enieni a zolakwika.” Choncho ngati tikufunadi choonadi, tiyenera “kulingalira bwino mokhazikika” ndiponso “kufufuza ndi kuona zifukwa zake mosakondera.”
Atazindikira kuti kuchita zinthu motero n’kofunika, wasayansi wa ku Britain Sir Hermann Bondi anati: “Popeza kuti chikhulupiriro chimodzi chokha ndicho chingakhale choona, ndiye kuti anthu ambiri amakhulupirira kwambiri ndiponso moona mtima chinthu china cholakwika m’zipembedzo zodziŵika. Ukhoza kupeza kuti umalakwa, kupeza kuti mosasamala kanthu zoti chikhulupiro chako chinali chozika mizu motani ukhoza kukhala kuti umalakwa.”
Kodi munthu angadziŵe bwanji kuti alidi panjira ‘yopapatiza yomuka nayo kumoyo’? Yesu anati Mulungu ayenera kulambiridwa ‘mumzimu.’ Kulingalira zinthu bwino kukhoza kupangitsa munthu kuzindikira kuti ngati ziphunzitso ziŵiri zili zosiyana, sizingatheke kuti zonsezo zikhale zoona. Mwachitsanzo, mwina anthu ali ndi moyo umene umapulumuka pa imfa kapena alibe. Mwina Mulungu adzachitapo kanthu pa zochita za anthu kapena ayi. Mwina Mulungu ndi wa Utatu kapena ayi. Anthu ofunafuna choonadi amafuna mayankho ogwira mtima a mafunso ofunika amenewo. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Mulungu anatipatsa mayankho m’Mawu ake, Baibulo.a
Popeza kuti “lemba lililonse adaliuzira Mulungu,” njira yabwino yofufuzira ziphunzitso ndiko kufufuza moyerekezera ndi Baibulo. (2 Timoteo 3:16) Mukamachita zimenezo, ndiko kuti ‘mukuzindikira chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.’ (Aroma 12:2) Kodi mutha “kupeza inu eni” kuti zimene mumakhulupirira ndi zimenedi Baibulo limanena? Ngati mumatha kuchita zimenezo ndi chinthu chofunika kwambiri chifukwa Mulungu safuna kuti muzisocheretsedwa pamodzi ndi “dziko lonse.”—Chivumbulutso 12:9.
Kodi Pafunikira Kukhala Aphunzitsi?
Yesu sanangopatsa ophunzira ake mabuku ndi kunena kuti: “Mayankho amafunso anu ali mmenemu. Pitani ndipo mukawapeza nokha.” M’malo mwake, iye modekha ndi mokoma mtima ankawaphunzitsa mawu a Mulungu. Zotsatira zake, amene anavomereza chiphunzitso chake anatsanzira njira zake pamene nawonso ankaphunzitsa ena. Lingalirani za chitsanzo cha wophunzira wake Filipo. Iye analankhula ndi m’dindo wa ku Aitiopiya woona mtima amene anali atazolowera kale Malemba chifukwa anali ataonanapo kale ndi Ayuda. Komabe munthuyo ankafunikira chithandizo. Choncho Filipo—woimira mpingo wachikristu—anatsogozedwa kupita kukamuthandiza. M’dindo ameneyu akanakhala kuti sanali kufuna kukambirana za chipembedzo, sakanaphunzira za udindo wa Yesu mu chifuniro cha Mulungu. M’dindo wa ku Aitiopiya ameneyo anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri kwa ena onse amene akufunafuna choonadi!—Machitidwe 8:26-39.
Kodi inu ndinu wolakalaka kukamba za chikhulupiriro chanu ndi kufunsa mafunso monga mmene anachitira M’aitiopiya uja? Mudzapindula zambiri ngati mudzachita choncho. Mboni za Yehova zimakhala zokondwa kukambirana za m’Baibulo ndi anthu amene moona mtima amafuna kudziŵa chimene limanena. Mboni sizinena maganizo awo kuti ndiwo muwakhulupirire. M’malo mwake iwo amayesetsa kuonetsa anthu zimene Baibulo palokha limanena.
Mdindo wa ku Aitiopiya anaphunzira zambiri zofunika zokhudza Yesu Kristu, monga mmene Mulungu adzamugwiritsira ntchito pokhudzana ndi chipulumutso chathu. Lerolino, zofuna za Mulungu zili pafupi kumalizidwa. Zinthu zochititsa mantha ndi zodabwitsa zili pafupi kuchitika pano padziko lapansi. Nkhani yotsatira isonyeza kuti zidzakhudza aliyense padziko lapansi. Komabe, mmene zidzatikhudzire zidzadalira khalidwe lathu ndi zimene tikuchita.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna umboni wakuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, chonde onani m’buku lakuti Baibulo—Mawu a Mulungu kapena a Munthu?, Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 7]
Mdindo wa ku Aitiopiya anavomera kukambirana za m’Baibulo