Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 9/15 tsamba 29-31
  • Aristarko Bwenzi Lokhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aristarko Bwenzi Lokhulupirika
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchokera ku Grisi Kupita ku Yerusalemu
  • Ulendo wa ku Roma
  • ‘Kapolo Mnzake’ wa Paulo
  • ‘Chotonthoza’
  • Mukhoza Kuthandiza Anthu Komanso Kuwalimbikitsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Yendani M’njira za Yehova
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Limbani Mtima Chifukwa Yehova Akuthandizani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Antchito Anzake a Paulo—Kodi Anali Ayani?
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 9/15 tsamba 29-31

Aristarko Bwenzi Lokhulupirika

PAKATI pa antchito anzake okhulupirika a mtumwi Paulo panali Aristarko. Kodi mumalingalira chiyani mukamva dzina lake? China chilichonse? Kodi munganene chimene anachita pa mbiri yachikristu m’nthaŵi zoyambirira? Ngakhale kuti Aristarko sangakhale mmodzi wa anthu a m’Baibulo amene timawadziŵa bwino, iye anakhudzidwa pazochitika zingapo zosimbidwa m’Malemba Achigiriki Achikristu.

Motero, kodi Aristarko anali yani? Anali paunansi wotani ndi Paulo? Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Aristarko anali bwenzi lokhulupirika? Ndipo kodi ndi maphunziro otani amene tingatengepo pakupenda chitsanzo chake?

Dzina la Aristarko likuloŵa m’nkhani ya m’buku la Machitidwe pamene panali phokoso ndi chisokonezo cha gulu lotengeka maganizo mumzinda wa Efeso. (Machitidwe 19:23-41) Kupanga tiakachisi ta siliva ta mulungu wonyenga Artemi kunali malonda aphindu kwambiri kwa Demetriyo ndi amisiri ena a ku Efeso. Motero, pamene ulaliki wa Paulo mumzindawo unachititsa ambiri kuleka kulambira kosayenera kumeneku kwa mulungu wamkazi, Demetriyo anasonkhezera amisiri anzake. Anawauza kuti ulaliki wa Paulo sikuti uthetsa malonda awo chabe komanso zitheka kuti kulambira Artemi kutha.

Posampeza Paulo, khamu la anthu lokwiyalo lidagwira mabwenzi ake Aristarko ndi Gayo kupita nawo kubwalo la maseŵera. Popeza aŵiriwa anali pangozi, mabwenzi a Paulo anamchonderera ‘kusadziponya ku bwalo la maseŵerako.’

Yerekezerani kuti zikuchitikira inu. Kwa maola monga aŵiri, gulu losokonekeralo linali kukuwa, “Wamkulu ndi Artemi wa ku Efeso.” Kupezeka pakati pa anthu otengeka maganizo amenewo popanda ngakhale mpata wolankhula modzitetezera, ndithudi chiyenera kuti chinali chokumana nacho choopsa kwa Aristarko ndi Gayo. Ayenera kuti anali kukayika ngati atulukepo ndi moyo. Mwamwaŵi anatero. Ndithudi, kumvekera bwino kwa nkhani ya Luka kwapangitsa akatswiri ena kulingalira kuti anafunsira kwa mboni zoona ndi maso, mwinamwake kwa Aristarko ndi Gayo iwo eni.

Pomaliza mlembi wa mzindawo anathetsa phokosolo. Ziyenera kuti zinatsitsa mitima ya Aristarko ndi Gayo kumumva iye akuwachirikiza kuti ali osalakwa ndiye kenako kuona msokonezo wowazingawo uli kutha.

Kodi inu mukanamva bwanji pambuyo pa chokumana nacho chofanana ndi chimenechi? Kodi mukananganiza kuti simungakhale mmishonale mnzake wa Paulo, kuti kunali kwangozi kwambiri, ndi kuti kunali bwino kwa inu kufunafuna moyo wa bata? Koma Aristarko sanatero! Pokhala anali wa ku Tesalonika, ayenera kuti anali kudziŵa za kuopsa kwa kufalitsa uthenga wabwino. Pamene Paulo ankalalikira mumzinda wa kwawo zaka ziŵiri zapitazo, nakonso chiwawa chinabuka. (Machitidwe 17:1-9; 20:4) Aristarko anaumirira kumbali ya Paulo mokhulupirika.

Kuchokera ku Grisi Kupita ku Yerusalemu

Miyezi pang’ono pambuyo pa chiwawa cha mmisiri wa siliva, Paulo anali ku Grisi ndipo anali pafupi kukwera ngalawa yopita ku Suriya ndi kupita ku Yerusalemu pamene ‘anampangira chiwembu Ayuda.’ (Machitidwe 20:2, 3) Kodi ndani amene tikumpeza ali ndi Paulo mu zochitika zoopsa zino? Aristarko!

Chiopsezo chatsopanochi chinachititsa Paulo, Aristarko, ndi mabwenzi awo kusintha malingaliro awo, choyamba kupyola Makedoniya, ndiye kenako kumaimaima m’mphepete mwa nyanja ku Asia Minor asanakwere ngalawa pa Patara kupita ku Foinike. (Machitidwe 20:4, 5, 13-15; 21:1-3) Cholinga cha ulendo umenewu mwachionekere chinali kukapereka zopereka za Akristu a ku Makedoniya ndi Akayo kwa abale awo osoŵa ku Yerusalemu. (Machitidwe 24:17; Aroma 15:25, 26) Gulu lalikulu linkayenda pamodzi, mwinamwake chifukwa chakuti anali atapatsidwa ntchito imeneyo ndi mipingo yosiyanasiyana. Mosakayika, kuyenda m’gulu lalikulu chotere kunali kuperekanso chitetezo chachikulu.

Aristarko anali ndi mwaŵi waukulu woperekeza Paulo kuchokera ku Grisi kupita ku Yerusalemu. Komabe, ulendo wawo wotsatira unali woti udzawayendetsa kuchokera ku Yudeya mpaka ku Roma.

Ulendo wa ku Roma

Nthaŵi ino zochitika zake zinali zosiyanako. Paulo anali mu ndende ku Kaisareya kwa zaka ziŵiri, ndipo anachita apilo kwa Kaisara, ndipo anayenera kutumizidwa ku Roma ali mu nsinga. (Machitidwe 24:27; 25:11, 12) Yesani kuganizira mmene mabwenzi a Paulo amamvera. Ulendo wochokera ku Kaisareya kupita ku Roma unali wautali ndiponso wovutitsa maganizo, wosadziŵika zotsatirapo zake. Ndani akanapita naye kumakamlimbikitsa ndi kumthandiza? Amuna aŵiri anasankhidwa kapena anadzipereka okha modzifunira. Anali Aristarko ndi Luka, wolemba Machitidwe.​—Machitidwe 27:1, 2.

Kodi Luka ndi Aristarko anatha bwanji kukwera chombo chimodzi paulendo woyamba wa ku Roma? Wolemba mbiri yakale Giuseppe Ricciotti akulingalira kuti: “Anthu aŵiri ameneŵa anakwera monga mapasenjala wamba . . . kapena, mwinanso, analoledwa mwa chifundo cha kazembe wa nkhondo amene ananyengezera kuti ndi akapolo a Paulo, popeza lamulo linkalola nzika ya Roma kuthandizidwa ndi akapolo aŵiri.” Paulo ayenera kuti analimbikitsidwa chotani mwa kukhalapo kwawo ndiponso ndi chilimbikitso chawo!

Luka ndi Aristarko anasonyeza chikondi chawo kwa Paulo modzimana ndiponso moika miyoyo yawo pangozi. Kwenikweni, anakumana ndi ngozi pamene, iwo pamodzi ndi bwenzi lawo landendelo, chombo chinawaswekera pa chisumbu cha Melita.​—Machitidwe 27:13–28:1.

‘Kapolo Mnzake’ wa Paulo

Pamene Paulo analemba makalata ake kwa Akolose ndi kwa Filemoni mu 60-61 C.E., Aristarko ndi Luka anali adakali nayebe ku Roma. Aristarko ndi Epafra akunenedwa kukhala ‘andende anzake.’ (Akolose 4:10, 14; Filemoni 23, 24) Motero, kwa kanthaŵi, Aristarko mwachionekere anakhala m’ndende ndi Paulo.

Ngakhale kuti Paulo anali wandende ku Roma kwa zaka ngati ziŵiri, analoledwa kukhala m’nyumba ya lendi, kumene anatha kufalitsa uthenga wabwino kwa alendo. (Machitidwe 28:16, 30) Motero Aristarko, Epafra, Luka, ndiponso ena anatumikira Paulo, kumthandiza ndi kumchirikiza.

‘Chotonthoza’

Pambuyo pakupenda zochitika zosiyanasiyana zimene Aristarko akupezekamo m’mbiri youziridwa ya m’Baibulo, kodi pamakhala chithunzi chanji? Malinga ndi mlembi W.D. Thomas, Aristarko “akuonekera monga munthu amene anatha kukumana ndi chizunzo ndi kutulukapo ali ndi chikhulupiriro cholimbabe ndiponso chosankha chake chotumikira chili chosafooka. Akupezeka kukhala munthu yemwe anakonda Mulungu osati pa mtendere pokha, pamene zinthu zonse zinali kuyenda bwino, komanso ponyozedwa ndi pochitidwa chiwawa.”

Paulo akunena kuti Aristarko pamodzi ndi ena anali ‘chotonthoza’ (m’Chigiriki, pa·re·go·riʹa) kwa iye, chochotsa chisoni. (Akolose 4:10, 11) Motero mwa kumtonthoza ndi kumlimbikitsa Paulo, Aristarko anali bwenzi lenileni panthaŵi ya mavuto. Kukhala ndi mtumwiyu ndi kukhala naye paubwenzi kwa zaka zambiri kuyenera kuti kunali kokhutiritsa ndi kolimbikitsa mwauzimu.

Mwina sitingakhale ndi zokumana nazo zochititsa chidwi ngati za Aristarko. Komabe, kukhulupirika kotero kwa abale auzimu a Kristu ndi ku gulu la Yehova ndi kofunika kwa onse mumpingo wachikristu lerolino. (Yerekezerani ndi Mateyu 25:34-40.) Alambiri anzathu amene timawadziŵa, nkothekera kuti nthaŵi ina adzakumana ndi mavuto kapena kupsinjika maganizo, mwina chifukwa cha imfa ya wokondedwa, matenda, kapena ziyeso zina. Mwa kusawasiya ndi kuwapatsa thandizo, chitonthozo, ndi chilimbikitso tikhoza kusangalala ndiponso tingadzisonyeze kukhala mabwenzi okhulupirika.​—Yerekezerani ndi Miyambo 17:17; Machitidwe 20:35.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena