Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 8/1 tsamba 11-16
  • ‘Valani Kudzichepetsa’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Valani Kudzichepetsa’
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mzimu Wofala wa Dziko Lapansi
  • Yehova Ali ndi Odzichepetsa
  • Kuphunzira Kukhala Odzichepetsa
  • Malingaliro Abwino
  • ‘Valani Kudzichepetsa’
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Khalani Odzichepetsadi
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Mungasonyeze Motani Kuti Ndinudi Wodzichepetsa?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Tsatirani Chitsanzo Chimene Yesu Anatipatsa
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 8/1 tsamba 11-16

‘Valani Kudzichepetsa’

“Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”​—1 PETRO 5:5.

1, 2. Kodi ndi malingaliro aŵiri osiyana ati amene amakhudza kwambiri khalidwe la anthu?

PAKATI pa makhalidwe amene Mawu a Mulungu amatitchulira pali ena aŵiri osiyana kwambiri. Zochita za anthu zimakhudzidwa kwambiri ndi onse aŵiri. Khalidwe limodzi ndi “kudzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Dikishonale ina imamasulira mawuwo “chepetsa” kukhala “kuchita zinthu mofatsa kapena kukhala ndi mtima wofatsa: kusanyada modzikudza.” Kudzichepetsa ndi mkhalidwe wofunika kwabasi pamaso pa Mulungu.

2 Malingaliro osiyana nawo ndiwo kunyada. Kumeneku kumamasuliridwa kukhala “kudzipatsa ulemu mopambanitsa,” kukhala “wonyansidwa ndi ena.” Munthu woteroyo amangoganizira za iye yekha, ndipo amangofuna kupeza phindu lakuthupi, laumwini, ndi mapindu ena mosasamala kanthu kuti ena zikuwapweteka motani. Baibulo limatchulapo chotsatira chimodzi kuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” Limanena za ‘kuchitira munthu nsanje’ kuti ndi “chabe ndi kungosautsa mtima” chifukwa pa imfa ‘satenga kanthu.’ Kunyada kumeneku n’konyansa kwabasi pamaso pa Mulungu.​—Mlaliki 4:4; 5:15; 8:9.

Mzimu Wofala wa Dziko Lapansi

3. Kodi mzimu wofala m’dziko ndi wotani?

3 Kodi ndi malingaliro ati mwa aŵiriŵa amene ali ofala kwambiri m’dziko lerolino? Kodi mzimu wofala kwambiri m’dziko ndi uti? World Military and Social Expenditures 1996 inati: “Palibe zaka zana zilizonse kumbuyoku zimene zimalingana ndi zaka za zana la 20 pa chiwawa chake . . . chadzaoneni.” Kulimbirana mphamvu m’ndale ndi m’zachuma, komanso udani pakati pa mitundu, zipembedzo, ndi mafuko, zaphetsa anthu oposa mamiliyoni 100 m’zaka za zana lino. Komanso anthu owonjezereka amangosamala za iwo eni basi. Nyuzipepala ya Chicago Tribune inati: “Matenda a chitaganya amaphatikizapo chiwawa chosadziŵika chifukwa chake, kuzunza ana, chisudzulo, uchidakwa, AIDS, kudzipha kwa achinyamata osakwanitsa zaka 20 zakubadwa, mankhwala osokoneza bongo, magulu achifwamba, kugwirira ena, ana apathengo, kuchotsa mimba, nkhani ndi zithunzi zolaula, . . . bodza, chinyengo, katangale m’ndale . . . Malingaliro abwino akuti pali chabwino ndi choipa anatheratu.” Chotero, magazini ya UN Chronicle inachenjeza kuti: “Zitaganya zikuwonongeka.”

4, 5. Kodi ulosi wa m’Baibulo wonena za m’tsiku lathu umafotokoza bwino motani mzimu wa dziko?

4 Mikhalidwe imeneyi ili padziko lonse. Zangokhala ndendende ndi zimene Baibulo linaneneratu ponena za nthaŵi yathuyi kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima.”​—2 Timoteo 3:1-4.

5 Amenewo ndi mafotokozedwe abwino kwambiri a mzimu wofala m’dzikoli. Ndi mzimu wadyera wongosamala za iwe mwini basi. Udani pakati pa mayiko umaonekera mwa udani pakati pa anthu. Mwachitsanzo, pochita maseŵera opikisana, ambiri ochita maseŵerawo amangosamala za iwo eni basi mosasamala kanthu kuti ena zikuwapweteka motani mumtima ngakhalenso kupwetekedwa kwenikweniko kwakuthupi. Mzimu wosafuna kusamala za ena umenewu umakulitsidwa mwa ana ndipo umaonekera m’njira zambiri anawo atakula. Umapangitsa “madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magaŵano.”​—Agalatiya 5:19-21.

6. Kodi ndani amalimbikitsa dyera, ndipo Yehova amamva bwanji za malingaliro ameneŵa?

6 Baibulo limasonyeza kuti mzimu wongosamala za iwe mwini wa m’dzikoli umasonyeza mzimu wa “iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” Ponena za chisonkhezero cha Satana pa anthu okhala m’masiku ovutaŵa, Baibulo linaneneratu kuti: “Tsoka mtunda . . . chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:9-12) Chotero iye ndi ziwanda zinzake akuyesetsa mwamphamvu kuti akulitse dyera m’maganizo mwa anthu. Nanga Yehova amamva bwanji ponena za malingaliro ameneŵa? Mawu ake amati: “Yense wonyada mtima anyansa Yehova.”​—Miyambo 16:5.

Yehova Ali ndi Odzichepetsa

7. Kodi Yehova amawaona motani odzichepetsa, ndipo kodi amawaphunzitsanji?

7 Komano, Yehova amadalitsa anthu odzichepetsa. Poimbira nyimbo Yehova, Mfumu Davide anati: “Mudzapulumutsa anthu osautsidwa [“odzichepetsa,” NW]; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.” (2 Samueli 22:1, 28) Chotero, Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, . . . funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Zefaniya 2:3) Awo amene modzichepetsa amafunafuna Yehova amaphunzitsidwa ndi iye kuti akulitse mzimu wosiyana kotheratu ndi wa dzikoli. “Adzaphunzitsa ofatsa njira yake.” (Salmo 25:9; Yesaya 54:13) Njira imeneyo ndiyo njira yachikondi. N’njozikidwa pa kuchita zoyenera malinga ndi miyezo ya Mulungu. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, chikondi cha lamulo chimenechi “sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza, . . . sichitsata za mwini yekha.” (1 Akorinto 13:1-8) Chimaonekeranso mwa kudzichepetsa.

8, 9. (a) Kodi chikondi cha lamulo chinachokera kuti? (b) Kodi kutsanzira chikondi ndi kudzichepetsa kumene Yesu anasonyeza n’kofunika motani?

8 Paulo ndi Akristu ena a m’zaka za zana loyamba anaphunzira mtundu umenewu wachikondi paziphunzitso za Yesu. Ndipo Yesu anauphunzira kwa Atate wake, Yehova, amene Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Yesu anadziŵa kuti n’chifuniro cha Mulungu kuti azitsatira lamulo la chikondi, ndipo anaterodi. (Yohane 6:38) Ndiye chifukwa chake ankamvera chisoni anthu otsenderezeka, osauka, ndi ochimwa. (Mateyu 9:36) Anawauza kuti: ‘Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.’​—Mateyu 11:28, 29.

9 Yesu anasonyeza ophunzira ake kufunika kwa kutsanzira chikondi ndi kudzichepetsa kwake pamene anawauza kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Anali kudzaonekera kukhala osiyana ndi dziko losafuna kusamala za enali. Ndiye chifukwa chake ponena za otsatira ake, Yesu anati: “Sakhala a dziko lapansi.” (Yohane 17:14) Ndithudi, iwo satsanzira mzimu wonyada, wadyera wa dziko la Satanali. M’malo mwake, amatsanzira mzimu wa chikondi ndi kudzichepetsa umene Yesu anasonyeza.

10. Kodi Yehova akuchitanji ndi anthu odzichepetsa m’tsiku lathu?

10 Mawu a Mulungu ananeneratu kuti m’masiku otsirizaŵa, anthu odzichepetsa adzasonkhanitsidwa kukhala gulu limodzi lapadziko lonse lachikondi ndi lodzichepetsa. Chotero, pakatikati pa dziko limene likuwonjezera kunyada kwake, anthu a Yehova akusonyeza malingaliro osiyana kwambiri​—kudzichepetsa. Iwo amati: “Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova [kulambira kwake koona kokwezeka], . . . ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yesaya 2:2, 3) Mboni za Yehova ndizo gulu lapadziko lonse limeneli loyenda m’njira za Mulungu. Amaphatikizapo “khamu lalikulu [lomakulabe], loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Khamu lalikulu limeneli tsopano n’lopangidwa ndi mamiliyoni a anthu. Kodi Yehova akuwaphunzitsa motani kuti akhale odzichepetsa?

Kuphunzira Kukhala Odzichepetsa

11, 12. Kodi atumiki a Mulungu amasonyeza motani kudzichepetsa?

11 Mzimu wa Mulungu pogwira ntchito pa anthu ake ofunitsitsa umawatheketsa kukana mzimu woipa wa dzikoli ndi kusonyeza chipatso cha mzimu wa Mulungu. Chimenechi chimaoneka mwa “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Pofuna kuwathandiza kukulitsa mikhalidwe imeneyo, atumiki a Mulungu amalangizidwa kusakhala “odzikuza, outsana [“oyambitsa mpikisano pakati pawo,” NW], akuchitirana njiru.” (Agalatiya 5:26) Mofananamo, mtumwi Paulo anati: “Ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha.”​—Aroma 12:3.

12 Mawu a Mulungu amauza Akristu oona kuti asachite “kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake [a atumiki a Mulungu] om’posa iye mwini; munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:3, 4) “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.” (1 Akorinto 10:24) Inde, “chikondi chimangirira” ena mwa mawu ndi zochita zopanda dyera. (1 Akorinto 8:1) Chimalimbikitsa mgwirizano, osati mpikisano. Mzimu wongofuna kukhala woyamba ndi wosavomerezedwa pakati pa atumiki a Yehova.

13. N’chifukwa chiyani kudzichepetsa kuyenera kuphunziridwa, ndipo munthu amakuphunzira motani?

13 Komabe, poti timabadwa tili opanda ungwiro, sitimabadwa tili odzichepetsa. (Salmo 51:5) Mkhalidwe umenewu tiyenera kuchita kuuphunzira. Ndipo zimenezi zingakhale zovuta kwa aja amene sanayambire paubwana wawo kuphunzitsidwa njira za Yehova koma amene amazilandira atakula, ali kale ndi umunthu wozikidwa pa mzimu wa dziko lakale lino. Chotero ayenera kuphunzira “[kuvula], kunena za makhalidwe [awo] oyamba, munthu wakale” ndi “[kuvala] munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.” (Aefeso 4:22, 24) Mothandizidwa ndi Mulungu anthu oona mtima angachite zimene iye amawapempha kuti: ‘Valani . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.’​—Akolose 3:12.

14. Kodi Yesu anati chiyani potsutsa malingaliro ofuna kudzikweza?

14 Ophunzira a Yesu anafunika kuphunzira zimenezo. Iwo anakhala ophunzira ake ali aakulu kale ndipo anali ndi kamzimu ka dziko kokonda kukangana. Pamene amayi wa aŵiri mwa iwo anafuna kuti ana ake aamunawo akakhale ndi malo apamwamba kwambiri, Yesu anati: “Mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:20-28) Pamene Yesu anauza ophunzira ake kuti asagwiritse ntchito mayina aulemu poyesa kudzikweza, anawonjezera kuti: “Inu nonse muli abale.”​—Mateyu 23:8.

15. Kodi awo ofuna udindo ayenera kukhala ndi malingaliro otani?

15 Wotsatira woona wa Yesu ali mtumiki, inde, kapolo wa Akristu anzake. (Agalatiya 5:13) Zili choncho makamaka kwa awo amene akufuna kuyenerera kuti akhale oyang’anira mumpingo. Sayenera konse kupikisana kuti akhale otchuka kapena kuti apeze udindo; sayenera ‘kuchita ufumu pa iwo a udindo [wawo], koma kukhala zitsanzo zawo.’ (1 Petro 5:3) Ndithudi, mzimu wongofuna za iwe mwini umasonyeza kuti munthuyo sakuyenerera kukhala woyang’anira. Munthu woteroyo angakhale wowononga mumpingo. Zoonadi, ndi bwino ‘kukhumba udindo wa woyang’anira,’ koma munthu ayenera kutero chifukwa chakuti akukhumba kutumikira Akristu anzake. Udindo umenewu si malo aukumu kapena osonyeza mphamvu, popeza kuti oyang’anirawo ayenera kukhala ena mwa anthu odzichepetsa kwambiri mumpingo.​—1 Timoteo 3:1, 6.

16. N’chifukwa chiyani Diotrefe anadzudzulidwa m’Mawu a Mulungu?

16 Mtumwi Yohane ananena za munthu wina amene anali ndi malingaliro olakwika, anati: “Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife [“salandira chilichonse chochokera kwa ife mwaulemu,” NW].” Munthu ameneyu sanali kuchitira ena ulemu poyesa kudzikweza. M’malo mwake, mzimu wa Mulungu unasonkhezera Yohane kuphatikiza chidzudzulo cha Diotrefe m’Baibulo chifukwa cha mzimu wake wongofuna kukhala pamwamba pa onse.​—3 Yohane 9, 10.

Malingaliro Abwino

17. Kodi Petro, Paulo, ndi Barnaba anasonyeza motani kudzichepetsa?

17 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za malingaliro abwino, za kudzichepetsa. Petro ataloŵa m’nyumba ya Korneliyo, mwamunayo “[a]nagwa pa mapazi [a Petro], nam’lambira.” Koma m’malo molola munthu kum’lambira, “Petro anamuutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu.” (Machitidwe 10:25, 26) Pamene Paulo ndi Barnaba anali ku Lustra, Paulo anachiritsa mwamuna amene anabadwa wopunduka. Chifukwa cha zimenezi, makamu a anthu ananena kuti atumwi amenewo ndi milungu. Komabe, Paulo ndi Barnaba “anang’amba zofunda zawo, natumphira m’khamu, nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu.” (Machitidwe 14:8-15) Akristu odzichepetsa ameneŵa sanalole kulemekezedwa mopambanitsa ndi anthu.

18. Modzichepetsa, kodi n’chiyani chimene mngelo wamphamvu anauza Yohane?

18 Pamene mtumwi Yohane anali kupatsidwa “chivumbulutso cha Yesu Kristu,” anachilandira kudzera mwa mngelo. (Chivumbulutso 1:1) Chifukwa cha mphamvu ya mngelo, titha kumvetsa chifukwa chimene Yohane anachitira mantha, popeza mngelo wina anawononga Asuri 185,000 mu usiku umodzi. (2 Mafumu 19:35) Yohane anasimba kuti: “Pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo. Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite [“usachite zimenezi,” NW]; ndine kapolo mnzako, ndi mnzawo wa abale ako . . . , lambira Mulungu.” (Chivumbulutso 22:8, 9) Mngelo wamphamvuyu analitu wodzichepetsa kwambiri!

19, 20. Siyanitsani kudzikuza komwe akazembe ankhondo a Roma ankasonyeza atagonjetsa ena ndi kudzichepetsa kwa Yesu.

19 Yesu anali chitsanzo chabwino koposa cha munthu amene anali wodzichepetsa. Iye anali Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, woyembekezera kukhala Mfumu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Podzisonyeza kwa anthu monga munthu woteroyo, sanachite monga momwe akazembe ankhondo ankachitira atagonjetsa ena m’nthaŵi ya Roma. Iwo anali kuyenda ndi gulu lalikulu la asilikali olinganizidwa bwino​—khamu lowaperekeza​—ndipo anali kuyendera m’magaleta okometseredwa ndi golide ndi zokometsera zopangidwa ndi minyanga ya njovu, okokedwa ndi akavalo oyera, mwinanso ngakhale njovu, mikango, kapena njuzi. Pakati pa chinamtindi chimenecho pankakhalanso oimba omwe ankaimba nyimbo zachilakiko, komanso pankakhala ngolo zodzaza ndi zofunkha ndiponso ngolo zina zonyamula zikwangwani zosonyeza zithunzi za nkhondo. Panali kukhalanso mafumu ogonjetsedwawo, akalonga, ndi akazembe ankhondo, ndi mabanja awo, kaŵirikaŵiri atawavula zovala kuti awachititse manyazi. Zochitika zimenezo zinadzala kunyada ndi kudzikuza.

20 Yerekezani zimenezo ndi mmene Yesu anadziperekera. Anali wofunitsitsa kukwaniritsa modzichepetsa ulosi wonena za iye, umene unanena kuti: “Taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa bulu.” Modzichepetsa anakwera pa nyama yonyamula katundu, osati m’galeta lokokedwa ndi nyama zokongola zokoka mafumu. (Zekariya 9:9; Mateyu 21:4, 5) Anthu odzichepetsa alitu okondwa zedi kuti Yesu ndiye adzakhala Mfumu yoikidwa ndi Yehova yolamulira dziko lonse lapansi m’dziko latsopano, munthu wodzichepetsadi, wachikondi, ndi wachifundo.​—Yesaya 9:6, 7; Afilipi 2:5-8.

21. Kodi kudzichepetsa sikumasonyeza chiyani?

21 Mfundo imeneyo yakuti Yesu, Petro, Paulo, ndi amuna ndi akazi ena okhulupirika m’nthaŵi za m’Baibulo anali odzichepetsa imatsutsa malingaliro akuti kudzichepetsa ndi chofooka. M’malo mwake, kudzichepetsa kumasonyeza nyonga ya munthu, popeza anthu ameneŵa anali olimba mtima ndi achangu. Pokhala ndi nyonga yaikulu ya mumtima ndi m’makhalidwe awo, anapirira ziyeso zoopsa. (Ahebri, chaputala 11) Ndipo lerolino, atumiki a Yehova akakhala odzichepetsa, amakhala ndi nyonga yofananayo chifukwa chakuti Mulungu amachirikiza odzichepetsa ndi mzimu wake woyera wamphamvuwo. Ndiye chifukwa chake timalimbikitsidwa kuti: “Nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa. Potero dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni.”​—1 Petro 5:5, 6; 2 Akorinto 4:7.

22. N’chiyani chidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira?

22 Palinso mbali ina yabwino ya kudzichepetsa imene atumiki a Mulungu ayenera kuizoloŵera. Imathandiza kwambiri kukulitsa mzimu wa chikondi ndi mgwirizano m’mipingo. Ndithudi, ndi mbali yofunika ya kudzichepetsa. Imeneyo idzafotokozedwa m’nkhani yotsatira.

Kubwereza

◻ Fotokozani mzimu wofala wa dziko.

◻ Kodi Yehova amawayanja motani odzichepetsa?

◻ N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira kukhala odzichepetsa?

◻ Kodi m’Baibulo muli zitsanzo zina zotani za anthu amene anasonyeza kudzichepetsa?

[Chithunzi patsamba 15]

Mngelo anauza Yohane kuti: “Usachite zimenezo; ndine kapolo mnzako”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena