Khalani Nacho Chikhulupiriro ndi Chikumbumtima Chabwino
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Timoteo Woyamba
PAFUPIFUPI chaka cha 56 C.E, mtumwi Paulo anachenjeza akulu a mumpingo wa Efeso kuti “mimbulu yosautsa” ikauka pakati pawo ndi “olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:29, 30) M’zaka zochepa, chiphunzitso chachipatuko chinakula kwakuti Paulo anasonkhezera Timoteo kumenya nkhondo yauzimu mkati mwa mpingo kuti asungitse chiyero ndikuthandiza okhulupirira anzake kukhalabe m’chikhulupiriro. Chimenecho ndicho chinali chifukwa chachikulu chimene Paulo analembera kalata yake yoyamba kwa Timoteo kuchokera ku Makedoniya pafupifupi 61-64 C.E.
Timoteo analangizidwa ponena za mathayo a akulu, malo aakazi opatsidwa ndi Mulungu, ziyeneretso za akulu ndi atumiki otumikira, ndi nkhani zina. Malangizo oterowo ngopindulitsanso kwa ife lerolino.
Chilangizo cha Chikhulupiriro
Paulo anayamba ndi uphungu wa kukhala ndi chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. (1:1-20) Iye analimbikitsa Timoteo kukhala mu Efeso ndi ‘kulamulira ena kusaphunzitsa chiphunzitso chosiyana.’ Paulo anayamikira uminisitala wogaŵiridwa kwa iye, akuzindikira kuti iye anachita zinthu muumbuli ndi kupanda chikhulupiriro pamene ankazunza otsatira a Yesu. Mtumwiyo anafulumiza Timoteo kupitirizabe kumenya nkhondo yauzimu, ‘kukhala ndi chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino’ ndikusafanana ndi amene ‘chikhulupiriro chawo chidataika.’
Uphungu pa Kulambira
Chotsatira, Paulo anapereka uphungu monga ‘mphunzitsi wa amitundu m’chikhulupiriro ndi chowonadi.’ (2:1-15) Mapemphero anayenera kuperekedwa ponena za okhala m’malo aakulu kotero kuti Akristu angakhale mwamtendere. Nchifuniro cha Mulungu kuti anthu onse apulumutsidwe, ndipo chiphunzitso chofunika kwambiri nchakuti Kristu ‘anadzipereka yekha chiombolo mmalo mwa onse.’ Paulo anasonyeza kuti mkazi ayenera kudzikometsera ndi kudekha ndipo sayenera kuchita ulamuliro pa mwamuna.
Mpingo uyenera kukhala wolinganizidwa bwino lomwe. (3:1-16) Chotero Paulo anandandalitsa ziyeneretso za oyang’anira ndi atumiki otumikira. Kuchokera ku zinthu zimene mtumwiyo anazilemba, Timoteo anadziŵa mmene akadzisungira mumpingo, ‘mzati ndi mchirikizo wa chowonadi.’
Paulo anapatsa Timoteo uphungu waumwini kumthandiza kuti achenjere ndi chiphunzitso chonyenga. (4:1-16) M’nthaŵi zapambuyo pake ena akagwa pa chikhulupiriro. Koma mwakudziyang’anira mwakhama ndi chiphunzitso chake, Timoteo ‘akadzipulumutsa yekha ndi awo omvetsera kwa iye.’
Timoteo analandiranso uphungu wonena zakuchita ndi anthu aliyense payekha, ang’ono ndi akulu. (5:1-25) Mwachitsanzo, makonzedwe oyenerera anafunikira kupangidwa kaamba ka akazi amasiye okalamba okhala ndi kudzisungira kwabwino Kwachikristu. Mmalo mwakumadyerana miseche, akazi amasiye achichepere anayenera kukwatiwa ndi kubala ana. Amuna achikulire otsogoza bwino anayenerera ulemu wowirikiza.
Kudzipereka Kwaumulungu ndi Kukhutira kwa Munthu ndi Zimene Ali Nazo
Kalata ya Paulo inamalizidwa ndi uphungu pa kudzipereka kwaumulungu. (6:1-21, NW) ‘Kudzipereka kwaumulungu limodzi ndi kukhutira kwa munthu ndi zimene ali nazo’ ndiko magwero a phindu lalikulu, koma kufunitsitsa kukhala wolemera kumatsogolera ku chiwonongeko ndi kusakaza. Paulo anafulumiza Timoteo kumenya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro ndi ‘kugwira zolimba moyo wosatha.’ Kuti agwire moyo weniweniwo, achuma anafunikira ‘kusaika chiyembekezo chawo m’chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma pa Mulungu.’
[Bokosi/Chithunzi patsamba 30]
Kupulumutsidwa Kupyolera Mkubala Ana: Paulo sankafotokoza za chipulumutso cha moyo wosatha koma ntchito yoyenerera ya mkazi wowopa Mulungu pamene analemba kuti: ‘Adzapulumutsidwa mwakubala mwana, ngati akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.’ (1 Timoteo 2:11-15) Kupyolera mwakubala ana, kulera ana ake, ndi kusamalira banja lake, mkazi ‘akapulumutsidwa’ ku kukhala wodyera miseche wopanda chochita ndi kazitape m’nkhani za ena. (1 Timoteo 5:11-15) Ntchito zake zapanyumba zikathandizira utumiki wake kwa Yehova. Ndithudi, Akristu onse ayenera kuchinjiriza mayendedwe awo ndikugwiritsira ntchito mwanzeru nthaŵi yawo.—Aefeso 5:15, 16.