Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingamakhoze Kusukulu?
“Makolo anga amakonda kwambiri kuti ndizikhoza. ‘Wakhoza bwanji masamu? Pa tesiti ya Chingelezi wakhoza bwanji?’ Zimandinyansa zimenezo!”—Akutero Sam wazaka 13.
SI Sam yekha amene amakumana ndi zotere. Ndithudi, mlembi wa buku lotchedwa “Could Do Better” analemba kuti: “Sitinapeze kholo lomwe limalingalira kuti mwana wake akuchita mmene ayenera kuchitira kusukulu.” Koma monga Sam, achinyamata ambiri amaona kuti makolo awo akuwapanikiza kwambiri kuti azilimbikira kusukulu—kapena kuti azikhoza kwambiri. M’kalasi akhoza kumakumana ndi mavuto enanso. Wachinyamata wina anadandaula kuti: “Aziphunzitsi ngosadekha kwenikweni. Iwo amafuna kuti muzikumbukira zinthu mwamsanga ndipo ngati sutero, amakupangitsa kuoneka ngati ndiwe chitsiru. Ndiye sindiyesa nkomwe kuyankha.”
Achinyamata amene amalephera kukwanitsa kuchita zimene makolo awo ndiponso aphunzitsi awo amawayembekezera kuchita kaŵirikaŵiri amatchedwa kuti opanda nzeru. Koma pafupifupi ana onse amalephera kusukulu panthaŵi zina. Chifukwa ninji? Chodabwitsa nchakuti, sikuti ulesi kapena kulephera kuphunzira ndicho chifukwa nthaŵi zonse.a
Chifukwa Chake Ena Amalephera
Ndithudi, tikanena za sukulu, pali achinyamata ena amene amaoneka kuti amangokonda kusachitapo kalikonse. Herman wazaka 15 anati: “Kuŵerenga pang’ono chabe kumene ndingathe basi kumandikwana.” Komabe kunena zoona, si achinyamata onse alibe chidwi ndi sukulu. Zikhoza kungokhala kuti sasangalatsidwa ndi phunziro lina. Ndiye pali ena omwe saona kwenikweni phindu la zomwe akuphunzira. Reuben wazaka 17 ananena motere: “Pali maphunziro ena amene ndimaoneratu kuti sindidzawagwiritsa ntchito ndikadzatsiriza sukulu.” Kupanda chidwi kapena chilimbikitso kutha kukulepheretsani mosavuta.
Pali mfundo zinanso. Mwachitsanzo, ngati mphunzitsi amafulumira kwambiri kuposa mmene inu mumafunira, mudzakhumudwa. Ngati amachedwa, zidzakunyansani. Mabwenzi anu nawonso akhoza kupangitsa kuti muzikhoza kapena ayi. Buku lotchedwa Kids Who Underachieve linati: “Ngati mwana wanzeru afuna kuti azigwirizana kwambiri ndi ana opanda nzeru—akhoza kumchititsa kuyamba kulephera.” Motero wachinyamata wina anadandaula kuti pamene ankalimbikira pazaka zake zoyamba kusukulu, ena ankamchitira nsanje ndipo ankamuseka. Ndithudi, wachinyamata akhoza kukumana ndi zomwe zinanenedwa pa Miyambo 14:17 (NW) zakuti: “Munthu wotha kulingalira bwino amadedwa.”
Nthaŵi zina zopangitsa kusakhoza m’kalasi zimakhala zovutirapo. Mwachisoni, achinyamata ena amakula ndi maganizo akuti ndi olephera. Izi zimachitika ngati nthaŵi zonse mwana amanenedwa ndi maina onyoza, monga kuti wamazizi, chitsiru, kapena waulesi. Nzachisoni, kuti pambuyo pake zimadzakhaladi choncho. Monga momwe dokotala wina ananenera, “ngati akuuzani kuti ndinu wouma mutu ndipo inu mwakhulupirira, muzichita mongadi wouma mutu.”
Kaŵirikaŵiri makolo ndi aphunzitsi amakhala ndi zolinga zabwino polimbikitsa. Komabe ngakhale zili tero, achinyamata angamaone kuti akukakamizidwa kuchita zoposa zomwe angathe. Ngati inu mumaona choncho, zindikirani kuti makolo anu ndi aphunzitsi anu safuna kukusoŵetsani mtendere. Mwina iwo angofuna kuti muzichita zonse zomwe mungathe kuti muzikhoza. Komabe chifukwa cha kuopa ntchito yofunika kuti muyambe kumakhoza mutha kulingalira zongosiya. Koma limbikirani: Nzotheka kuti muzikhoza kusukulu.
Kulimbikitsidwa
Choyamba ndicho kuti muyenera kulimbikitsidwa! Kuti mutero, choyamba muyenera kuzindikira cholinga pa zimene mukuphunzira. Baibulo limati: “Popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugaŵana nawo.” (1 Akorinto 9:10) Kuona phindu “lolima” pa maphunziro ena si kwapafupi nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, mukhoza kunena kuti, ‘Ndikufuna kudzakhala kompyuta programa. Tsono pali chifukwa chanji chophunzirira histole?’
Nzoonadi kuti si zonse zimene mumaphunzira kusukulu zingaoneke zaphindu panthaŵi ino. Koma yesani kuona zakutsogolo. Kuphunzira maphunziro ambiri kudzakuthandizani kumvetsetsa dziko. Achinyamata ambiri omwe ndi Mboni za Yehova apeza kuti kuphunzira maphunziro ambiri kwawathandiza kuti akhale “zonse kwa anthu onse,” zikumawapatsa mwaŵi wotha kusinthasintha polalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu a kakhalidwe kosiyanasiyana. (1 Akorinto 9:22) Ngakhale ngati phunziro likuoneka kuti silothandiza kwenikweni, mumapindulabe ngati mulimvetsetsa. Mudzakulitsa luso lanu la “kulingalira,” chinthu chimene chidzakuthandizani kwambiri pambuyo pake.—Miyambo 1:1-4.
Sukulu ikhoza kuvumbula maluso anu amene sankadziŵika. Mtumwi Paulo analemba motere kwa Timoteo: “ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe.” (2 Timoteo 1:6) Mwachionekere Timoteo anali atasankhidwa kuchita mautumiki ena mumpingo wachikristu. Koma luso limene Mulungu anampatsa—“mphatso”—anayenera kuligwitsira ntchito, mwinamwake likanangokhala ndipo likanangowonongeka. Ndithudi, luso lanu lakusukulu silinabwere mwachindunji kuchokera kwa Mulungu, monga mmene inaliri mphatso ya Timoteo. Komabe zomwe mungathe kuchita—kaya pa zaluso, nyimbo, masamu, sayansi, kaya zina—nzapadera kwa inu, ndipo sukulu ikhoza kukuthandizani kuti muzizindikire ndi kukulitsa maluso amenewo.
Njira Zabwino Zoŵerengera
Komabe kuti mupindule zambiri kusukulu, muyenera kukhala ndi ndandanda yabwino yoŵerengera. (Yerekezani ndi Afilipi 3:16.) Gaŵani nthaŵi yochuluka kuti muŵerenge zambiri, lolani kuti muzilekezako kanthaŵi kuti muzipuma. Ngati phunziro lanulo likuphatikizapo zinthu zoyenera kuŵerenga, choyamba yambani mwaona nkhani zake kuti mudziŵe zili mmenemo. Chachiŵiri, pangani mafunso ochokera pa mitu yankhani kapena mitu ya mkati mwankhani. Ndiye kenaka ŵerengani, mukufunafuna mayankho a mafunso anu aja. Pomaliza, yeserani kunena pamtima zimene mwaphunzirazo.
Yerekezani zimene mwaphunzira ndi zimene mukudziŵa kale. Mwachitsanzo, sayansi ikhoza kukhala njira yoonera “zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha” ya Mulungu. (Aroma 1:20) Histole ikhoza kukuthandizani kuzindikira kuti mawu awa ndi oona: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Pamene mulimbikira kuŵerenga mpamene mudzaonadi kuti kuphunzira nkosavuta—ndiponso kosangalatsa! Solomo anaona kuti: “wozindikira saona vuto m’kuphunzira.”—Miyambo 14:6.
Onani Zinthu Moyenera
Komabe nthaŵi zina kulephera m’kalasi kumakhala chifukwa cha mabwenzi amene mumasankha. Kodi mabwenzi anu amalimbikitsa kuti muzikhoza, kapena iwo eni amalakwa? Mwambi wa m’Baibulo umati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Motero sankhani mabwenzi mwanzeru. Gwirizanani ndi amene amakonda sukulu. Musakayike kulankhula ndi aphunzitsi anu inu mwininu zolinga zanu zofuna kuwongolera mmene mumachitira m’kalasi. Nzosakayikitsa kuti aphunzitsi anu adzayesetsa kukuthandizani.
Ngati ena anena monyoza zimene mumachita malinga ndi zomwe mungathe, lingalirani za mtumwi Paulo. Pamene anthu ankati satha kulankhula bwino, iye anayankha kuti: “Ndingakhale ndili wosaphunzira m’manenedwe, koma sinditero m’chidziwitso.” (2 Akorinto 10:10; 11:6) Inde, Paulo anali maso pa zomwe angathe osati kulephera kwake. Kodi inu nziti zimene mungathe? Ngati simukuzidziŵa, bwanji osafunsa munthu wina wamkulu? Munthu woteroyo akhoza kukuthandizani kuzindikira zomwe mumatha ndipo mukhoza kulimbikira zimenezo.
Kulimbikirabe Ngakhale Pali Zovuta
“Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kulimbikira kwako kuonekere kwa onse.” (1 Timoteo 4:15, Phillips) Monga mmene atate amalankhulira kwa mwana wake, Paulo analimbikitsa Timoteo yemwe anali kale wakhama kuti apitirizebe kulimbikira utumiki. M’nthaŵi za Baibulo verebu ya Chigiriki yakuti “kulimbikira” inkatanthauza “kupita patsogolo,” inali ndi lingaliro la munthu yemwe akuyenda kuphotchola m’tchire. Nthaŵi zina sukulu ikhoza kuoneka choncho. Koma zingakhale zosavuta kwambiri kulimbikira sukulu ngati mulingalira zakuti mphotho yake pamapeto ndi yabwino.
Khama, kulimbikitsidwa, ndi kuphunzira zimagwirizana. Mwachitsanzo: Lingalirani za munthu yemwe akuimba chida china choimbira nyimbo. Ngati chimamsangalatsa mpamene amaimba kwambiri. Pamene aimba kwambiri, mpamenenso amaimba bwino, ndipo amasangalala kwambiri. Pamene tikuphunzira, mpamene kuphunzira kumakhala kosavuta ndiponso ndi pamene timaphunzira kwambiri. Choncho musakhumudwe ndi kuŵerenga kwa kusukulu. Limbikirani, gwirizanani ndi amene adzakuthandizani kupambana, ndipo lingalirani mawu a Azariya kwa Mfumu Asa yakaleyo: “Manja anu asalende; pakuti ku ntchito yanu kuli mphotho.”—2 Mbiri 15:7.
[Mawu a M’munsi]
a Ana amene satha kuphunzira akhoza kukumana ndi mavuto ambiri pankhani imeneyi. Kuti mumve zambiri, onani Galamukani! ya July 8, 1996, masamba 28-30.
[Chithunzi patsamba 19]
Musakayike kulankhula ndi aphunzitsi anu za cholinga chanu cha kuyamba kumakhoza m’kalasi
[Chithunzi patsamba 20]
Ngakhale ngati phunziro likuoneka ngati losathandiza kwenikweni, mumapindula ngati mulidziŵa bwino