Kuwafika Pamtima ndi Luso la Kukopa
ANTHU ambiri amadodoma akamva liwu lakuti “kukopa.” Ena angaganize za munthu wogulitsa malonda mokakamiza kapena za kusatsa malonda monamiza kapena monyengerera ogula. Ngakhale m’Baibulo, liwu lakuti kukopa nthaŵi zina limapereka malingaliro olakwika, likumasonyeza kuipitsa kapena kusokeretsa. Mwachitsanzo, mtumwi wachikristu Paulo analembera Agalatiya kuti: “Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi? Kukopa kumene sikuchokera kwa Iye anakuitanani.” (Agalatiya 5:7, 8) Paulo anachenjezanso Akolose kuti asalole munthu ‘kuwasokeretsa ndi mawu okopakopa.’ (Akolose 2:4) Kukopa koteroko kumachitika mwa kulankhula kochenjera kwabodza.
Komabe m’kalata yake yachiŵiri kwa Timoteo, mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito liwu la kukopa m’lingaliro lina. Iye analemba kuti: “Koma iwe, uzichitabe zinthu zimene unaphunzira ndipo unakopeka kuzikhulupirira, podziŵa anthu amene anakuphunzitsa.” (2 Timoteo 3:14, NW) Mwa ‘kukopeka kuti akhulupirire,’ Timoteo sanali kunyengedwa ndi amayi ndi agogo ake, amene anamphunzitsa choonadi cha Malemba.—2 Timoteo 1:5.a
Pamene Paulo anali mkaidi wokhala panyumba pake ku Roma, anapereka umboni wokwanira kwa anthu ambiri, “ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m’chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamaŵa kufikira madzulo.” (Machitidwe 28:23) Kodi Paulo anali kunamiza omvetsera ake? Kutalitali! Motero nkwachionekere kuti kukopa sikoipa nthaŵi zonse.
Pamene lagwiritsiridwa ntchito m’lingaliro labwino, liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “kopa” limatanthauza kukhutiritsa, kupangitsa munthu kusintha maganizo ake chifukwa cha makambitsirano ogwira mtima ndi omveka. Motero mphunzitsi angadalire pa Malemba, nkugwiritsira ntchito kukopa kuti akhomereze choonadi cha Baibulo mwa ena. (2 Timoteo 2:15) Ichi ndichodi chinali chizindikiro cha utumiki wa Paulo. Ngakhale Demetriyo wosula siliva, amene ankati ziphunzitso zachikristu nzonama, ananenapo kuti: “Si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja.”—Machitidwe 19:26.
Kukopa mu Utumiki
Yesu Kristu analangiza otsatira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) M’maiko oposa 230, Mboni za Yehova zikumvera lamulo limeneli. Mwezi uliwonse m’chaka chawo cha utumiki cha 1997, anali kuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba okwanira avareji ya 4,552,589 padziko lonse.
Ngati muli ndi mwayi wochititsa phunziro la Baibulo la panyumba, mungathe kuoneratu mbali zovuta zomwe zidzafuna kugwiritsira ntchito luso la kukopa. Mwachitsanzo, tiyerekezere kuti paphunziro lanu lotsatira padzabuka funso lokhudza Utatu. Bwanji ngati mukudziŵa kuti wophunzira wanu amakhulupirira chiphunzitso chimenechi? Mungampatse chofalitsa chimene chikulongosola nkhaniyo. Ataŵerenga, mungaone kuti wazindikira kuti Mulungu ndi Yesu ndi osiyana. Koma bwanji ngati padakali mafunso ena, kodi mungapitirize motani?
Mvetserani mosamalitsa. Zidzakuthandizani kudziŵa zimene wophunzira wanu akudziŵa kale pankhaniyo. Mwachitsanzo, ngati wophunzira wanu anganene kuti, “ndimakhulupirira Utatu,” mwamsanga mungakambirane naye mwamalemba kuti mutsutse chiphunzitsochi. Koma pali zikhulupiriro zosiyanasiyana zokhudza Utatu. Wophunzira wanu angamakhulupirire zosiyana kotheratu nzimene inu mungati nchiphunzitso cha Utatu. Nzofanananso ndi zikhulupiriro zina, monga zakuti munthu akafa amabadwanso kwina, kusafa kwa mzimu, ndi chipulumutso. Choncho mvetserani mosamalitsa musanalankhule. Musangolingalira kuti wophunzirayo amakhulupirira zakutizakuti.—Miyambo 18:13.
Funsani mafunso. Angakhale monga awa: ‘Kodi chiyambire mwakhala mukukhulupirira Utatu? Kodi munaphunzirapo mosamalitsa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi? Ngati Mulungu ali wautatu, kodi Mawu ake, Baibulo, sakanatiuza momveka bwino ndi mwachindunji?’ Pophunzitsa wophunzirayo, nthaŵi ndi nthaŵi imani ndi kufunsa mafunso onga awa: ‘Kodi zimene taphunzirazi mukuzimvetsetsa?’ ‘Kodi mukugwirizana ndi malongosoledwe amenewa?’ Mwa kugwiritsira ntchito kwanu mafunso mwaluso, mumamthandiza munthuyo kuphunzira. Iye sayenera kumangokumvetserani pamene mukulongosola nkhani.
Gwiritsani ntchito mfundo zogwira mtima. Mwachitsanzo, ngati mukukambirana za chiphunzitso cha Utatu, munganene kwa wophunzirayo kuti: ‘Pamene Yesu anali kubatizidwa, mawu anamveka kumwamba kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa.” Ngati Mulungu analidi kubatizidwa padziko lapansi, kodi akanapititsa mawu ake m’mwamba ndi kuwatsitsanso kotero kuti amveke padziko lapansi? Kodi sizikanakhala zosokeretsa? Kodi Mulungu, “wosanamayo,” angachite zachinyengo zoterozo?’—Luka 3:21, 22; Tito 1:1, 2.
Mfundo zokambidwa mwaluso kaŵirikaŵiri zimathandiza. Talingalirani za mkazi wina amene timutche kuti Barbara. Pamoyo wake wonse ankakhulupirira kuti Yesu ali Mulungu ndipo ali mbali ya utatu umene umaphatikizapo mzimu woyera. Koma mmodzi wa Mboni za Yehova anadzamuuza kuti Mulungu ndi Yesu ndi anthu osiyana, ndipo anamuonetsa malemba kuchirikiza zonena zakezo.b Barbara sakanatsutsa Baibulo. Komabe anakhumudwa. Ndi iko komwe, chiphunzitso cha Utatu chinkamsangalatsa.
Mboniyo mofatsa inalingalira naye Barbara. Inamfunsa kuti: “Ngati munali kufuna kundiphunzitsa kuti anthu aŵiri ngofanana, kodi mungagwiritse ntchito unansi uti wa pabanja?” Ataganizaganiza anati: “Ndingagwiritse ntchito abale aŵiri.” Mboniyo inayankha kuti: “Zoonadi, mwinanso ngakhale mapasa ofanana. Koma potiphunzitsa kuti tiziona Mulungu ngati Atate ndi iye mwini ngati Mwana, kodi Yesu anali kusonyezanji?” “Chabwino,” anayankha Barbara, maso ake akutseguka. “Akulongosola kuti wina ngwamkulu ndipo ali ndi mphamvu zambiri.”
“Inde, ndipo omvetsera a Yesu achiyuda, amene ankalemekeza makolo, mosakayikira analingalira motero,” Mboniyo inayankha. Pogogomezera nsonga yakeyo, Mboniyo inati: “Ngati ifeyo tapereka chitsanzo chabwino chonchi polongosola kufanana kwa anthu—cha abale kapena mapasa ofanana—ndithudi Yesu, Mphunzitsi Wamkulu, akanateronso. M’malo mwake anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘atate’ ndi ‘mwana’ kulongosola unansi wake ndi Mulungu.”
Tsopano Barbara anamvetsetsa, ndipo anagwirizana nazo. Anali atafikidwa pamtima ndi luso la kukopa.
Kulimbana ndi Malingaliro
Zikhulupiriro zikuluzikulu zazipembedzo kaŵirikaŵiri zimakhudzanso malingaliro a munthu. Talingalirani za Edna, Mkatolika wodzipereka. Adzukulu ake achinyamata anamsonyeza mwamalemba kuti Mulungu ndi Yesu ndi anthu osiyana. Edna anamvetsetsa zimene anamvazo. Komabe, mosakalipa koma motsimikiza anati: “Ndimakhulupirira Utatu woyera.”
Mwina inunso mwakumanapo nzoterezi. Ambiri amaona ziphunzitso za chipembedzo chawo ngati zowadziŵikitsa. Pamafunika zambiri kuti mukope ophunzira Baibulo oterowo m’malo mongolongosola zenizeni kapenanso kungofotokoza malemba angapo kusonyeza kuti zomwe munthuyo amaganiza ndi zolakwika. Zoterezi zingasamaliridwe bwino mwa kugwirizanitsa luso la kukopa ndi chifundo. (Yerekezerani ndi Aroma 12:15; Akolose 3:12.) Zoonadi, mphunzitsi wogwira mtima ayenera kukhala ndi zikhulupiriro zolimba. Mwachitsanzo, Paulo anagwiritsirapo ntchito mawu akuti “ndakopeka mtima” ndi kuti “ndidziŵa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu.” (Aroma 8:38; 14:14) Komabe, pofotokoza zikhulupiriro zathu tisamalankhule mosonyeza kuti tili oumirira pazimenezo, tisamadzilungamitse, ndiponso tisamatonze kapena kuchepetsa ena powafotokozera choonadi cha Baibulo. Ndithudi, sitifuna kulakwira kapena ngakhale kukhumudwitsa wophunzira.—Miyambo 12:18.
Nkopindulitsa kwambiri kulemekeza zikhulupiriro za wophunzira ndi kuzindikira kuti ali ndi ufulu wakuzikhulupirira. Kukhala wodzichepetsa nkofunika. Mphunzitsi wofatsa sadzimva kukhala wodziŵa kupambana wophunzira wake. (Luka 18:9-14; Afilipi 2:3, 4) Kukopa kwaumulungu kumaphatikizapo kudzichepetsa, kumene kungapangitse munthu kunena kuti: ‘Yehova mwachifundo wandithandiza kudziŵa zimenezi. Tiyeni tigaŵane.’
Kwa Akristu anzake mu Korinto, Paulo analemba kuti: ‘Zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga; ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziŵitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu.’ (2 Akorinto 10:4, 5) Lerolino, Mboni za Yehova zikugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kupasula malinga a ziphunzitso zonyenga ndiponso machitachita ndi makhalidwe amene samkondweretsa. (1 Akorinto 6:9-11) Pamene zikutero, Mboni zimakumbukira kuti Yehova mwachikondi waleza nawo mtima. Ngosangalala chotani nanga kuti ali ndi Mawu ake, Baibulo, nkuti amagwiritsa ntchito chida champhamvu chimenechi kuzula ziphunzitso zonyenga ndi kufika anthu pamtima ndi luso la kukopa!
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Yunike ndi Loisi—Aphunzitsi Opereka Chitsanzo Chabwino,” pa masamba 7-9 a kope lino la Nsanja ya Olonda.
b Onani Yohane 14:28; Afilipi 2:5, 6; Akolose 1:13-15. Kuti mumve zambiri onani brosha lakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
[Bokosi patsamba 23]
Kufika Wophunzira Wanu Pamtima
◻ Pempherani kuti Yehova akutsogolereni kuti mumfike pamtima wophunzira Baibulo.—Nehemiya 2:4, 5; Yesaya 50:4.
◻ Zindikirani zimene wophunzirayo amakhulupirira ndi chifukwa chake angamakopeke ndi chikhulupiriro chonama.—Machitidwe 17:22, 23.
◻ Mokoma mtima ndi mofatsa, fotokozani mfundo zotsatirika, za m’Malemba komabe mukumavomerezana pamfundo imodzi.—Machitidwe 17:24-34.
◻ Ngati nkotheka, chirikizani choonadi cha Baibulo ndi mafanizo omveka bwino.—Marko 4:33, 34.
◻ Sonyezani wophunzira phindu la kulandira chidziŵitso cholongosoka cha m’Baibulo.—1 Timoteo 2:3, 4; 2 Timoteo 3:14, 15.