Amithenga a Mtendere Waumulungu Asonkhana
“MSONKHANO wachigawo uliwonse umene tapezekapo watimangirira,” akutero mkulu wina wachikristu wa ku United States. “Komabe, chaka chino sungazifotokoze nkomwe. Tsiku lililonse tinali kuchokapo tikulingalira mmene tsiku lotsatira lidzapambanira ziyembekezo zathu, ndipo sitinagwire mwala!”
Ngati munapezeka pa umodzi wa Misonkhano Yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu,” ndithudi mungavomerezane nayo nthumwi yotenthedwa maganizo imeneyi. Tsiku lililonse la msonkhano panali kufotokoza mbali yosiyana ya ntchito imene Mboni za Yehova zimachita monga amithenga a Mulungu. Tiyeni tiipende programu ya masiku atatu imeneyo.
“Ha, Akongolatu . . . Amene Abukitsa Mtendere”
Uwu ndiwo unali mutu wa tsiku loyamba la msonkhano. Unazikidwa pa Yesaya 52:7. M’nthaŵi zovuta zino, ambiri akutumikira Yehova m’mikhalidwe yovuta. Nkhani yakuti “Kumvetsera kwa Olengeza Mtendere Achangu” inaphatikizapo kufunsa ena a okhulupirika ameneŵa. Kumva zonena zawo kunalidi kolimbikitsa, ndipo anatsimikizira osonkhana kuti iwonso Yehova akhoza kuwalimbitsa, ngakhale kuwapatsa “ukulu woposa wamphamvu” kuti uwathandize kupirira.—2 Akorinto 4:7.
Zimene Yehova amafuna si zolemetsa. (1 Yohane 5:3) Zimenezi anazimveketsa bwino m’nkhani yomaliza ya programu ya mmaŵa, imene inafika pachimake ndi kutulutsidwa kwa brosha lamasamba 32 lamutu wakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Chothandizira kuphunzira chimenechi cha zithunzithunzi zokongola chidzachitadi mbali yaikulu pakuthandiza enanso ambiri kuphunzira za zifuno za Mulungu. Ndemanga pantchito ya chofalitsa chatsopano chimenechi zikupezeka m’magazini ano m’nkhani yophunzira yomaliza ndi pamasamba 16 ndi 17.
Nkhani yakuti “Kupirira Pantchito Zabwino” inagogomezera mfundo yakuti Yehova amazidziŵa bwino lomwe ziyeso zathu. Kupirira kumatanthauza kulimbikira ndi kusataya chiyembekezo. Yehova watipatsa Mawu ake, mzimu wake, ndi gulu lake kuti zitithandize. Kulalikira kumafuna chipiriro, komabe kulalikira kumatithandiza kupirira, chifukwa kumasunga chikhulupiriro chathu chili cha moyo. Pokhala tayandikira kwambiri mapeto, sitiyenera kulola mavuto athu kupha changu chathu, popeza awo okha amene adzapirira kufikira mapeto ndi amene adzapulumuka.—Mateyu 24:13.
Nkhani yaikulu yakuti, “Mbali Yathu Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu,” inanena za kumasulidwa kwa andende achiyuda ku Babulo ndi kubwezeretsa kulambira koona ku Yerusalemu mu 537 B.C.E. Mlankhuli anafotokoza kuti chochitika chimenechi chinali chabe mthunzi wa chimene Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa posachedwapa padziko lonse. (Salmo 72:7; Yesaya 9:7) Gawo lathu tsopano lino ndilo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu umenewu ndi kukhala mogwirizana ndi uthengawo. Chikondi cha pa Mulungu ndi mnansi chiyenera kutikakamiza kupitiriza ntchito imeneyi mosaleka.—Machitidwe 5:42.
Mbali yaikulu ya programu pa Lachisanu inali nkhani yosiyirana yakuti “Chenjerani ndi Misampha Yobisika ya Kusanguluka.” Nyimbo zamasiku ano, mafilimu, mavidiyo, maprogramu apawailesi yakanema, maseŵero apavidiyo, mabuku, magazini ndi makomiki nthaŵi zambiri zimasonyeza maganizo auchiŵanda. Choncho tiyenera ‘kudana nacho choipa’ ndi ‘kugwirizana nacho chabwino.’ (Aroma 12:9) Inde, zosangulutsa zoipa tiyenera kunyansidwa nazo ndi kuzipeŵa, ndi kusinkhasinkha pa zinthu zoyera, zokoma mtima, ndi zotamandika. (Afilipi 4:8) Zofalitsa ndi ziŵiya zofufuzira zogaŵiridwa ndi gulu la Yehova zimasonkhezera maganizo athu ndi malingaliro omangirira ndi kutiphunzitsa kusiyanitsa chabwino ndi choipa. (Ahebri 5:14) Tiyenera kumamatira ku zogaŵira zimenezi monga momwe tingachitire ku phaka panyanja yoŵinduka.
Ndiyeno panabwera nkhani yakuti “Kanizani Mdyerekezi—Chitani Nsanje.” Kutatsala pang’ono kuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Aisrayeli zikwi zambiri anagwidwa mumsampha wa chisembwere. Pinehasi anachitira nsanje kulambira koona. Anachitapo kanthu motsimikiza mtima potsutsa ochimwa, ndipo kulambira kwake kosagaŵanika kunamkondweretsa Yehova. (Numeri 25:1-13) Chonulirapo cha Satana ndicho kuchititsa aliyense wa ife kukhala wosayenerera kuloŵa m’Dziko Latsopano la Mulungu. Choncho monga Pinehasi, tiyenera kutsutsa zoyesayesa za Mdyerekezi za kutidetsa. Kaya tili muukwati kaya ndife mbeta, tiyenera ‘kuthaŵa dama.’—1 Akorinto 6:18.
“Kuchirikiza Umphumphu wa Mawu a Mulungu Mokhulupirika” inali nkhani yomaliza patsiku loyamba la msonkhano. Otembenuza ambiri amasintha kapena kuchotsa mbali zina za Malemba. Mwachitsanzo, kuti akondweretse ochirikiza zoyenera za akazi, otembenuza The New Testament and Psalms: An Inclusive Version samatcha Mulungu kuti Atate, koma Atate-Amayi. Mosiyana ndi zimenezo, New World Translation imamamatira mokhulupirika ku malemba a m’chinenero choyamba kwakuti lachititsa kuwongolera maganizo athu pankhani zingapo za m’Malemba. Mwachitsanzo, mlankhuli anati: “Anali matembenuzidwe olondola a New World Translation amene anapereka maziko a kukonzanso mipingo mwa kuika mabungwe a akulu, motsatira chitsanzo cha mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba.” Timasonyeza kukhulupirika kwathu ku Mawu a Mulungu mwa kuwaŵerenga tsiku ndi tsiku ndi mwa kugwiritsira ntchito uphungu wake. Mlankhuliyo ananenanso kuti: “Timasonyeza kuti tikuchirikiza Mawu a Mulungu mokhulupirika mwa kuwalalikira mokangalika kwa ena ndi mwa kuwagwiritsira ntchito mosamalitsa pophunzitsa ena, ndi kusayesa konse kuwapotoza kapena kuwonjezera pa zimene amanena kuti agwirizane ndi malingaliro athu.”
‘Mtendere wa Mulungu Upambana Chidziŵitso Chonse’
Mutuwu, wozikidwa pa Afilipi 4:7, unayambitsa tsiku lachiŵiri lamsonkhano. Chidziŵitso chochuluka chimene chinaperekedwa chinakhudza kaonedwa kabwino ka utumiki wa munthu, banja lake, kudzipatulira kwake, ndi mbali zina za moyo watsiku ndi tsiku.
Pambuyo pa kukambitsirana lemba latsiku, nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Amithenga Obweretsa Uthenga Wabwino wa Mtendere” inaperekedwa. Uthenga wathu ndi wamtendere, ndipo tiyenera kuupereka mwamtendere. (Aefeso 6:15) Cholinga chathu ndicho kukopa mitima, osati kupambana pamikangano. Maphunziro ndi zofalitsa zimene timalandira ku gulu la Yehova zimatithandiza kuchita zimenezo. Tisalole mphwayi kutilefula. M’malo mwake, tiyenera kupitiriza ‘kuchita changu,’ kukhala ndi ndandanda yabwino ya phunziro laumwini, kusonkhana, ndi kukhala ndi phande pantchito yolalikira. (2 Timoteo 2:15) Sitiyeneranso kuiŵala kuchitira ena zabwino, makamaka iwo apabanja lachikhulupiriro. (Agalatiya 6:10) Komabe, kuchita changu sikumatanthauza kugwira ntchito mopambanitsa. Zimene aliyense angathe kuchita malinga ndi mphamvu ndi mikhalidwe yake Yehova amazilandira.
Anthu a Mulungu amapereka nthaŵi yawo, nyonga yawo, ndi chuma chawo kuti apititse patsogolo zinthu za Ufumu. Nkhani yakuti “Kupatsa Mokondwerera m’Gulu la Yehova” inafotokoza kuti pamene onga nkhosa ochuluka akulabadira uthenga wa Ufumu, pakufunikanso ziŵiya zowonjezereka, malo osonkhanira, ndi nthambi. Zopereka zathu zimakhozetsa gululi kukhala ndi zonse zofunika kuti likwaniritse ntchito yolalikira yapadziko lonse. Kupatsa kwamataya kumalemekezanso Yehova ndipo kumapatsa chimwemwe wopatsayo. Chotero, monga Akristu, sitiyenera kunyalanyaza mbali yofunikayi ya kulambira kwathu.—2 Akorinto 8:1-7.
Chigawo chammaŵa chinatha ndi nkhani yaubatizo—imene nthaŵi zonse imakhala mbali yaikulu pamisonkhano yaikulu ya Mboni za Yehova. Nkosangalatsa chotani nanga kuona odzipatulira chatsopano akutsatira mapazi a Yesu mwa kudzipereka kuubatizo wa m’madzi! (Mateyu 3:13-17) Onse amene amatenga sitepe limeneli aphunzitsidwa magwero a nzeru yaikulu koposa—Baibulo. Ndiponso, iwo apeza chifuno chenicheni m’moyo, ndipo adala ndi mtendere umene umadza podziŵa kuti akuchita choyenera.—Mlaliki 12:13.
Uphungu womveka unaperekedwa m’nkhani yakuti “Kuzindikira Kukuchinjirizeni.” Kuzindikira nkofunika kwambiri m’malonda. Sitiyenera kuchita malonda athu m’Nyumba ya Ufumu, ndiponso sitiyenera kudyerera Akristu anzathu kuti tipindule ndalama. (Yerekezerani ndi Yohane 2:15, 16.) Kuzindikira nkofunikanso poikiza ndalama m’malonda kapena pobwerekana ndalama. “Kulephera kwa malonda pakati pa Akristu kwagwiritsa ena mwala ndipo kwatayitsa ngakhale mkhalidwe wauzimu wa ena amene anafulumira kuloŵa m’malonda angozi opezetsa ndalama zambiri,” anatero mlankhuli. Ngakhale kuti Akristu salakwa ngati achitana malonda, ndithudi kuchenjera kuli bwino. Ndipo pamene anthu aŵiri avomerezana kuchitana malonda, zimvano zake ayenera kuzilemba.
Nkhani yakuti “Analenga Iwo Mwamuna ndi Mkazi” inalongosola miyezo ya Mulungu ya amuna ndi akazi. Mbali za amuna ndi akazi zasokonezeka m’mbiri yonse. “Ambiri amaganiza kuti umuna ndiwo kupondereza mwankhanza, liuma, kapena mangolomera,” anatero mlankhuli. “Kumalo ena ndi kwakamodzikamodzi, ndipo kochititsa manyazi kuona mwamuna akulira poyera, kapena ngakhale mwamseri. Komabe, Yohane 11:35 amanena kuti pamene anali pakati pa anthu kunja kwa manda a Lazaro, ‘Yesu analira.’” Bwanji nanga za akazi? Nthaŵi zambiri amaona kukongola kwakuthupi kukhala ukazi. Koma mlankhuli anafunsa kuti: “Ngati mkazi ali wokongola koma alibe nzeru ndipo ali wamakani, wamwano, kapena waliuma, kodi angakhaledi wokongola m’lingaliro lenileni la liwulo, ukazi weniweni?” (Yerekezerani ndi Miyambo 11:22; 31:26.) M’nkhani zawo, khalidwe, ndi kapesedwe, amuna ndi akazi achikristu amalimbikira kutsatira miyezo ya Baibulo. Mlankhuliyo anati: “Mwamuna amene amasonyeza zipatso za mzimu samavuta kulemekeza, ndipo mkazi amene amachita zimenezo samavuta kukonda.”—Agalatiya 5:22, 23.
Ndiyeno panabwera nkhani yosiyirana yakuti “Mulungu Wamtendere Amasamala za Inu.” Akristu ambiri ali ndi nkhaŵa ya ndalama. Komabe, Yehova akulonjeza kuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Mosasamala kanthu za mavuto a zachuma, ena adalira lonjezo limeneli mwa kuloŵa utumiki waupainiya wothandiza kapena upainiya wokhazikika. Ena amene sangathe kuchita upainiya tsopano amaika zinthu za Ufumu patsogolo mwa kugwiritsira ntchito mpata uliwonse wochitira umboni. (Mateyu 6:33) Kuyesayesa konse kumeneku nkoyamikirika! Gulu la Yehova latipatsa zofalitsa zambirimbiri zotithandiza mu utumiki wathu ndi kutithandiza kulimbana ndi mavuto athu. Ngati tiyamikira zogaŵira zauzimu za Yehova, adzatidalitsa ndi mtendere m’nthaŵi zino za mavuto a zachuma.—Salmo 29:11.
Patsikulo kumapeto a nkhani yomaliza yakuti, “Londolani Mtendere Waumulungu m’Moyo wa Banja,” osonkhana anakondwera kulandira buku latsopano lakuti, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. “Liphunzireni mwakhama panokha ndi pamodzi ndi mabanja,” analimbikitsa motero mlankhuli. “Yesayesani kugwiritsira ntchito uphungu wake wozikidwa pa Baibulo, ndipo mudzawonjezeradi mtendere ndi chimwemwe m’banja lanu.”
‘Musamalitse Kusunga Umodzi . . . mwa Chimangiriro cha Mtendere’
Mutu umenewu, wozikidwa pa Aefeso 4:3, unayenerana ndi tsiku lomaliza la msonkhanowu. Mboni za Yehova, zotengedwa m’mitundu yonse ya dziko lapansi, zaphunzitsidwa ndi Mulungu. Choncho, zimakonda mtendere. Zimatsatira chitsanzo cha Yesu nizisamalitsa “kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.”
Mtendere umene uli ponseponse m’gulu la Mulungu unalongosoledwa m’nkhani yosiyirana yakuti “Kudziŵa Mtundu Wabwino wa Amithenga.” Aneneri onyenga analiko m’Israyeli wakale. Komabe, amithenga oona a Mulungu—aneneri onga Yesaya, Ezekieli, ndi Yeremiya—ananeneratu mosaphonya za kugwa kwa Yerusalemu, nthaŵi ya ukapolo, ndi kumasuka kwa anthu a Mulungu m’kupita kwa nthaŵi. Palinso mkhalidwe wofananawo lerolino. Muli aneneri onyenga ambirimbiri m’ndale ndi m’chipembedzo chonyenga. Komabe, Yehova wadzutsa Mboni zake kuti zilengeze chimene akufuna kuchita pa dongosolo ili la zinthu. Makamaka kuyambira 1919, atumiki a Yehova agwiritsiridwa ntchito kulengeza uthenga wa Mulungu. Ha, mmene alili osiyana ndi amithenga onyenga a Dziko Lachikristu! Tichitetu mbali yathu mwakhama m’ntchitoyi kufikira pamene Yehova adzati yatha.
Nkhani yakuti “Mvetserani ndi Kulabadira Mawu a Mulungu” inanena mogogomezera kuti Malemba ndiwo magwero opambana a chitsogozo, chitonthozo, ndi chiyembekezo. (Yesaya 30:20, 21; Aroma 15:4) Dziko lalero nlolekerera zinthu kwambiri. Choncho, kuposa ndi kale lonse, tifunikira kumvetsera uphungu wochokera m’Mawu a Mulungu ndi kugulu lake. Yehova amadziŵa zifooko zathu, ndipo m’Mawu ake waisonyeza bwino lomwe njira imene idzatipindulitsa. Kudziŵa kuti Yehova akutichirikiza kumatipatsa chidaliro cha kuchita chilichonse chimene amafuna kwa ife.
Zimenezi zinatsegulira bwalo seŵero la nthaŵi zakale limene linatsatira. Linali ndi mutu wakuti: “Kodi Nkulemekezeranji Makonzedwe Ateokrase?” Mwa kugwiritsira ntchito nkhani ya m’Baibulo ya Gideoni monga maziko ake, mbaliyi inagogomezera kwambiri phunziro lina lamphamvu—tiyenera kutsatira malangizo a Mulungu ndi kusaloŵetsamo zoganiza zathu kapena kuyesa kupatuka pa uphungu wateokrase.
Nkhani yapoyera inali ndi mutu wakuti “Mtendere Weniweni Potsirizira Pake!—Kuchokera ku Magwero Ati?” Mtendere umene Mulungu akulonjeza ukuposa chilichonse chimene dzikoli lingaganizire. “Mtendere weniweni umatanthauza mtendere masiku onse,” anatero mlankhuli. “Mtendere wa Mulungu umatanthauza dziko lopanda matenda, zopweteka, chisoni, ndi imfa.” Baibulo limatiuza kuti Yehova “aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi.” (Salmo 46:9) Kodi adzazichita motani zimenezi? Mwa kuchotsapo wosonkhezera nkhondo, Satana Mdyerekezi. (Chivumbulutso 20:1-3) Zimenezi zidzalola ofatsa ‘kulandira dziko lapansi ndi kukondwera nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:11.
Pambuyo pa chidule cha Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo, nkhani yomaliza ya msonkhano inaperekedwa. Nkhani yosonkhezera imeneyi yamutu wakuti “Kupita Patsogolo Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu,” inagogomezera mfundo yakuti ntchito yathu yolalikira njapadera ndiponso yofulumira. Ino sinthaŵi yogwetsa manja, kuzengereza, kapena kubwerera ku malingaliro olakwika. Tili ndi ziŵiya zimene tifunikira—uthenga wa Mulungu, mzimu wake woyera, ndi makonzedwe ambirimbiri a gulu lake lachikondi lateokrase. Chotero monga atumiki a Yehova, tipitirizetu kupita patsogolo monga amithenga a mtendere waumulungu!
[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]
Chogaŵira Chachikondi cha Mabanja
Awo omwe anapezekapo patsiku lachiŵiri la Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” anakondwera kwambiri kulandira chofalitsa chatsopano chamutu wakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Buku limeneli lili ndi chidziŵitso cha m’Malemba chimene chidzapindulitsa mabanja onse okonda Mulungu.
Mkulu wina wa ku Connecticut, U.S.A., akuti: “Pa June 15, tinalandira buku lathu la Chimwemwe cha Banja. Pa June 16, ndinali nditaŵerenga theka lake. Pa 17, tinachita phunziro lathu labanja loyamba m’bukuli, ndipo tinalimbikitsidwa kwambiri! Tsiku limodzimodzilo ndinatsiriza kuliŵerenga bukulo. Chofalitsa chabwino chimenechi chidzakhaladi chamtengo wapatali kwa onse amene adzachigwiritsira ntchito. Kulunjika kwa bukuli ndi chidziŵitso chatsopano lino zikupereka umboni winanso wakuti ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru’ akutipatsa ‘zakudya panthaŵi yake’ ndipo akuzidziŵa bwino lomwe zosoŵa zathu m’nthaŵi zino zamayesero.”—Mateyu 24:45-47.
[Chithunzi patsamba 7]
Achichepere ndi achikulire omwe amafuna kudziŵa chimene Mulungu amafuna