Chipiriro—Nchofunika kwa Akristu
“Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro.”—2 PETRO 1:5, 6, NW.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tonsefe tiyenera kupirira kufikira mapeto?
WOYANG’ANIRA woyendayenda wina ndi mkazi wake anali kuchezera Mkristu mnzawo wa m’zaka za m’ma 90. Mkristuyu anali atathera zaka makumi ambiri muutumiki wanthaŵi yonse. Pamene anali kucheza, mbale wokalambayo anasimba za mathayo ena amene anali nawo m’zaka zapita. “Koma,” iye anadandaula pamene misozi inayamba kugwa pamaso pake, “tsopano sindili wokhoza kuchita zambiri.” Woyang’anira woyendayendayo anatsegula Baibulo lake ndi kuŵerenga pa Mateyu 24:13, pamene pali mawu a Yesu Kristu akuti: “Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” Ndiyeno woyang’anira woyendayendayo anayang’ana mbale wokondedwayu nati: “Thayo lomalizira lomwe tonsefe tili nalo, mosasamala kanthu za kuchuluka kapena kuchepa kwa zimene tingachite, ndilo kupirira kufikira mapeto.”
2 Inde, monga Akristu, tonsefe tiyenera kupirira kufikira mapeto a dongosolo lino la zinthu kapena kufikira mapeto a miyoyo yathu. Palibe njira ina yolandirira chivomerezo cha Yehova cha chipulumutso. Tili m’makani a moyo, ndipo tiyenera ‘kuthamanga mwachipiriro’ kufikira mapeto. (Ahebri 12:1) Mtumwi Petro anagogomezera kufunika kwa mkhalidwe umenewu pamene anafulumiza Akristu anzake kuti: “Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro.” (2 Petro 1:5, 6, NW) Koma kodi kwenikweni chipiriro nchiyani?
Chipiriro—Tanthauzo Lake
3, 4. Kodi kupirira kumatanthauzanji?
3 Kodi kupirira kumatanthauzanji? Verebu Lachigiriki la liwu lakuti “pirira” (hy·po·meʹno) kwenikweni limatanthauza “kukhalabe pansi pa chinthu.” Limaonekera nthaŵi 17 m’Baibulo. Malinga nkunena kwa olemba dikishonale W. Bauer, F. W. Gingrich, ndi F. Danker, limatanthauza “kukhalabe pomwepo mmalo mwa kuthaŵa . . . , kuima nji, kuumirira.” Nauni Lachigiriki la liwu lakuti “chipiriro” (hy·po·mo·neʹ) limaonekera nthaŵi 30. Ponena za liwuli, A New Testament Wordbook, lolembedwa ndi William Barclay, limati: “Ilo ndilo mkhalidwe umene ungapirire zinthu, osati chifukwa cha kulolera molakwa, koma umatero chifukwa cha chiyembekezo chaphamphu . . . Ndiwo mkhalidwe umene umalimbitsa munthu kuyang’anizana ndi mavuto. Ndiwo mkhalidwe waukoma umene ungasinthe chiyeso chovuta kwambiri kukhala chaulemerero chifukwa chakuti m’kupwetekako umayang’ana pamphotho.”
4 Pamenepa, chipiriro chimatikhozetsa kukhala olimba nji ndi kusataya chiyembekezo poyang’anizana ndi zopinga kapena mavuto. (Aroma 5:3-5) Chimaona chonulirapo chimene chili mtsogolo pambuyo pa zopweteka—mphotho, kapena mphatso ya moyo wamuyaya, kaya kumwamba kapena padziko lapansi.—Yakobo 1:12.
Chipiriro—Nchifukwa Ninji Chikufunika?
5. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu onse ‘afunikira chipiriro’? (b) Kodi mayesero athu angagaŵidwe m’magulu aŵiri ati?
5 Monga Akristu, tonsefe “tifunikira chipiriro.” (Ahebri 10:36, NW) Chifukwa ninji? Kwakukulukulu chifukwa chakuti ‘timakumana ndi mayesero a mitundumitundu.’ Lemba Lachigiriki pano pa Yakobo 1:2 limapereka lingaliro la chokumana nacho chosayembekezeredwa kapena chosakondweretsa, monga ngati pamene munthu ayang’anizana ndi wachifwamba. (Yerekezerani ndi Luka 10:30.) Timakumana ndi mayesero amene angagaŵidwe m’magulu aŵiri: awo amene ali ofala kwa anthu chifukwa cha choloŵa cha uchimo, ndi aja amene amabuka chifukwa cha kudzipereka kwathu kwaumulungu. (1 Akorinto 10:13; 2 Timoteo 3:12) Kodi ndiati amene ali ena a mayesero ameneŵa?
6. Kodi ndimotani mmene Mboni ina inapiririra pamene inayang’anizana ndi matenda opweteka?
6 Matenda aakulu. Mofanana ndi Timoteo, Akristu ena ayenera kupirira ‘kudwaladwala.’ (1 Timoteo 5:23, NW) Makamaka pamene tiyang’anizana ndi nthenda yosachiritsika, kapena yopweteka kwambiri mpamene tifunikira kupirira, kuima nji, mwachithandizo cha Mulungu ndi kusataya chiyembekezo chathu Chachikristu. Lingalirani za chitsanzo cha Mboni ina ya zaka za kuchiyambiyambi kwa m’ma 50 imene inamenya nkhondo kwanthaŵi yaitali yolimbana ndi chotupa chomakula mofulumira. Iyo inakhalabe yolimba potsimikiza kukana mwazi m’maopaleshoni aŵiri. (Machitidwe 15:28, 29) Koma chotupacho chinayambanso kutupa m’mimba ndipo chinapitiriza kukula pafupi ndi msana. Pamene chinatero, iyeyu anali kumva ululu waukulu umene panalibe mlingo wa mankhwala uliwonse umene ukanathetsa ululuwo. Komabe, iye anayembekezera mphotho ya moyo m’dziko latsopano kuposa ululu umene anali kumva. Anapitiriza kunena za chiyembekezo chake champhamvu kwa madokotala, anamwino, ndi odzamuona. Anapirira kufikira mapeto—mapeto a moyo wake. Matenda anu sangakhale owopseza moyo kapena opweteka mofanana ndi a mbale wathu wokondedwayo, koma angaperekebe chiyeso chachikulu chofuna chipiriro.
7. Kodi chipiriro chimaloŵetsamo zopweteka zotani kwa ena a abale ndi alongo athu auzimu?
7 Kuvutika mtima. Panthaŵi ndi nthaŵi, anthu ena a Yehova akumana ndi ‘kusweka kwa moyo’ kumene kumachitika chifukwa cha “zowawa za mtima.” (Miyambo 15:13) Kupsinjika maganizo kwakukulu nkofala ‘m’nthaŵi zino zowawitsa.’ (2 Timoteo 3:1) Science News ya December 5, 1992, inasimba kuti: “Kaŵirikaŵiri, milingo yaikulu ya kupsinjika maganizo kofoola yawonjezereka mumbadwo uliwonse wa anthu obadwa chiyambire 1915.” Zochititsa kupsinjika maganizo kumeneko nzosiyanasiyana, zikumayambira pazinthu zochititsa kusapeza bwino kwa thupi mpaka kuzochitika zosasangalatsa. Kwa Akristu ena, chipiriro chimaloŵetsamo kumenya nkhondo kwatsiku ndi tsiku kuti akhalebe olimba poyang’anizana ndi kuvutika mtima. Komabe, iwo samagonja. Amakhalabe okhulupirika kwa Yehova mosasamala kanthu za zisonizo.—Yerekezerani ndi Salmo 126:5, 6.
8. Kodi ndimayesero a zandalama otani amene tingakumane nawo?
8 Mayesero osiyanasiyana amene timakumana nawo angaphatikizepo mavuto aakulu a ndalama. Pamene mbale wina wa ku New Jersey, U.S.A. ntchito inamthera mwadzidzidzi, moyenerera iye anali ndi nkhaŵa ya chimene adzadyetsa banja lake ndi kuti asalandidwe nyumba yake. Komabe, sanacheukitsidwe pachiyembekezo cha Ufumu. Pamene anali kufunafuna ntchito ina, anagwiritsiranso ntchito mwaŵiwo kutumikira monga mpainiya wothandiza. Potsirizira pake, anapeza ntchito.—Mateyu 6:25-34.
9. (a) Kodi ndimotani mmene kutayikiridwa wokondedwa muimfa kungafunikiritse chipiriro? (b) Kodi ndimalemba ati amene amasonyeza kuti kulira chifukwa cha chisoni sikoipa?
9 Ngati mwatayikiridwa wokondwedwa wanu muimfa, mufunikira chipiriro chimene chidzakhalapobe pamene anthu amene anadza kudzakutonthozani abwerera kwawo. Mungakuonedi kukhala kovuta kwambiri kwa inu pofika m’nthaŵiyo chaka chilichonse imene wokondedwa wanuyo anamwalira. Kupirira kutayikiridwa koteroko sikumatanthauza kuti kugwetsa misozi yachisoni nkolakwa. Kulira chifukwa cha imfa ya munthu amene timakonda nkwachibadwa, ndipo kumeneku sikumasonyeza kusakhulupirira chiyembekezo cha chiukiriro. (Genesis 23:2; yerekezerani ndi Ahebri 11:19.) Yesu “analira” Lazaro atamwalira, ngakhale kuti Iye anali atauza Marita motsimikiza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Ndipo Lazaro anaukadi!—Yohane 11:23, 32-35, 41-44.
10. Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova afunikira chipiriro mwapadera?
10 Kuwonjezera pakupirira mayesero amene ali ofala kwa anthu onse, anthu a Yehova afunikira chipiriro mwapadera. Yesu anachenjeza kuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Iye anatinso: “Ngati anandilondalonda ine, adzakulondalondani inunso.” (Yohane 15:20) Kodi nchifukwa ninji pali udani wonsewu ndi mazunzo? Chifukwa chakuti mosasamala kanthu za kumene timakhala padziko lapansili monga atumiki a Mulungu, Satana akuyesayesa kuswa umphumphu wathu kwa Yehova. (1 Petro 5:8; yerekezerani ndi Chivumbulutso 12:17.) Ali ndi cholinga chimenechi, kaŵirikaŵiri Satana wasonkhezera chizunzo chachikulu, akumaika chipiriro chathu pachiyeso chachikulu.
11, 12. (a) Kodi Mboni za Yehova ndi ana awo zinayang’anizana ndi chiyeso chotani cha chipiriro m’ma 1930 ndi kuchiyambiyambi kwa ma 1940? (b) Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizimachitira sawatcha chizindikiro cha dziko?
11 Mwachitsanzo, m’ma 1930 ndi kuchiyambiyambi kwa ma 1940, Mboni za Yehova ndi ana awo mu United States ndi Canada zinakhala chandamale cha chizunzo chifukwa chakuti sizinachitire sawatcha chizindikiro cha dziko chifukwa cha zifukwa za chikumbumtima. Mboni zimalemekeza zizindikiro za dziko limene zimakhala, koma zimagwirizana ndi lamulo loperekedwa m’Chilamulo cha Mulungu pa Eksodo 20:4, 5 lakuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako [ndine Mulungu wofuna kudzipereka kwaumulungu kwapadera, NW].” Pamene ana ena a sukulu a Mboni anathamangitsidwa chifukwa chakuti anafuna kupereka kulambira kwawo kokha kwa Yehova Mulungu, Mboni zinayambitsa Masukulu Aufumu kaamba ka maphunziro awo. Ophunzira ameneŵa anabwereranso kusukulu za boma pamene Bwalo Lalikulu Lamilandu la United States linavomereza mkhalidwe wawo wa chipembedzo, monga momwe maiko opanda tsankho amachitira lerolino. Komabe, kupirira molimba mtima kwa achichepere ameneŵa ndiko chitsanzo cholimbikitsa makamaka kwa Akristu achichepere lerolino amene amayang’anizana ndi zitonzo chifukwa chakuti amayesayesa kukhala mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo.—1 Yohane 5:21.
12 Mayesero osiyanasiyana amene timayang’anizana nawo—ponse paŵiri, awo amene ali ofala kwa anthu onse ndi awo amene timayang’anizana nawo chifukwa cha chikhulupiriro chathu Chachikristu—amasonyeza chifukwa chake tifunikira chipiriro. Koma kodi tingapirire motani?
Kupirira Kufikira Mapeto—Motani?
13. Kodi ndimotani mmene Yehova amaperekera chipiriro?
13 Anthu a Mulungu ali ndi mwaŵi wotsimikizirika kuposa anthu amene samalambira Yehova. Kuti tithandizidwe, tikhoza kutembenukira kwa “Mulungu wa chipiriro.” (Aroma 15:5) Komabe, kodi ndimotani mmene Yehova amaperekera chipiriro? Njira imodzi imene amachitira zimenezi ili kupyolera mwa zitsanzo za chipiriro zolembedwa m’Mawu ake, Baibulo. (Aroma 15:4) Pamene tisinkhasinkha za zimenezi, sitimangolimbikitsidwa chabe kupirira, komanso timaphunzira zochuluka ponena za mmene munthu angapiririre. Talingalirani za zitsanzo ziŵiri zapadera—kupirira molimba mtima kwa Yobu ndi kupirira kwa Yesu Kristu kopanda tchimo.—Ahebri 12:1-3; Yakobo 5:11.
14, 15. (a) Kodi ndimayesero otani amene Yobu anapirira? (b) Kodi ndimotani mmene Yobu anakhozera kupirira mayesero amene anakumana nawo?
14 Kodi ndimikhalidwe yotani imene inaika chipiriro cha Yobu pachiyeso? Anasauka pamene anatayikiridwa chuma chake. (Yobu 1:14-17; yerekezerani ndi Yobu 1:3.) Yobu anavutika mtima ndi kutayikiridwako pamene ana ake onse khumi anaphedwa ndi chimphepo. (Yobu 1:18-21) Anadwala matenda aakulu, omvetsa ululu kwambiri. (Yobu 2:7, 8; 7:4, 5) Mkazi wake weniweniyo anamkakamiza kusiya kulambira Mulungu. (Yobu 2:9) Mabwenzi ake apafupi ananena zinthu zimene zinali zopweteka, zankhanza, ndi zonama. (Yerekezerani ndi Yobu 16:1-3 ndi Yobu 42:7.) Komabe, muzonsezi, Yobu anaima nji, akumasunga umphumphu. (Yobu 27:5) Zinthu zimene anapirira nzofanana ndi mayesero amene anthu a Yehova amakumana nawo lerolino.
15 Kodi ndimotani mmene Yobu analiri wokhoza kupirira mayesero amenewo? Chinthu chapadera chimene chinalimbikitsa Yobu chinali chiyembekezo. “Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso, ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasoŵa,” iye anatero. (Yobu 14:7) Kodi Yobu anali ndi chiyembekezo chotani? Monga momwe tingaonere m’mavesi angapo pambuyo pake, iye anati: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? . . . Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Inde, Yobu anali kulingalira za zinthu zamtsogolo kuposa mavuto ake. Iye anadziŵa kuti mayesero ake sadzakhalako kosatha. Chifukwa chake iye anafunikira kupirira kufikira imfa. Chiyembekezo chake chachikulu chinali chakuti Yehova, amene mwachikondi amafuna kuukitsa akufa, akampatsanso moyo.—Machitidwe 24:15.
16. (a) Kodi nchiyani chimene timaphunzira ponena za chipiriro m’chitsanzo cha Yobu? (b) Kodi chiyembekezo cha Ufumu chiyenera kukhala chotsimikizirika motani kwa ife, ndipo chifukwa ninji?
16 Kodi timaphunziranji pachipiriro cha Yobu? Kuti tipirire kufikira mapeto, sitiyenera kutaya chiyembekezo chathu. Kumbukiraninso kuti, kutsimikizirika kwa chiyembekezo cha Ufumu kumatanthauza kuti mavuto alionse amene timakumana nawo ‘ngakanthaŵi.’ (2 Akorinto 4:16-18) Chiyembekezo chathu chamtengo wapatali nchozikidwa kwambiri palonjezo la Yehova lonena za nthaŵi imene ili pafupi mtsogolomu pamene ‘adzapukuta misozi yonse kuichotsa pamaso pathu; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.’ (Chivumbulutso 21:3, 4) Chiyembekezo chimenecho, chimene “sichichititsa manyazi,” chiyenera kutetezera maganizo athu. (Aroma 5:4, 5; 1 Atesalonika 5:8) Chiyenera kukhala chenicheni kwa ife—chenicheni kwakuti tikhoza kudziona ife eni m’dziko latsopano ndi maso achikhulupiriro—popanda kulimbananso ndi matenda ndi kupsinjika maganizo koma tsiku lililonse kudzuka tili ndi thanzi labwino ndi omasuka maganizo; popanda kuvutika mumtima ponena za chitsenderezo chachikulu cha ndalama koma kukhala ndi moyo motetezereka; popanda kulira akufa athu okondedwa koma kukhala nacho chisangalalo cha kuwaona akuukitsidwa. (Ahebri 11:1) Popanda chiyembekezo chotero tingakhale othedwa mphamvu ndi mayesero athu atsopano lino kwakuti tikhoza kugonja. Pokhala ndi chiyembekezo chathu, tili ndi chisonkhezero chachikulu chotani nanga choti tipitirizebe kumenya nkhondo, tipitirizebe kupirira kufikira mapeto!
17. (a) Kodi Yesu anapirira mayesero otani? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza ukulu wa zoŵaŵa zimene Yesu anapirira? (Onani mawu amtsinde.)
17 Baibulo limatilimbikitsa “kupenyerera” pa Yesu ndi ‘kulingalira iye.’ Kodi ndimayesero otani amene anapirira? Ena a iwo anadza chifukwa cha uchimo ndi kusalungama kwa ena. Yesu anapirira osati kokha ndi “ochimwa otsutsana naye” komanso mavuto amene anabuka pakati pa ophunzira ake, kuphatikizapo mkangano wawo wobwerezabwereza wonena za wamkulu pakati pawo. Ndiponso, iye analimbana ndi chiyeso chachikulu koposa cha kukhulupirika. “Anapirira [mtengo wozunzirapo, NW].” (Ahebri 12:1-3; Luka 9:46; 22:24) Nkovutadi kuyerekezera za kuvutika kwamaganizo ndi kwakuthupi koloŵetsedwamo paululu wa kukhomeredwa pamtengo wozunzirapo ndi kunyazitsidwa mwa kuphedwa monga munthu wamwano.a
18. Malinga nkunena kwa mtumwi Paulo, kodi nzinthu ziti ziŵiri zimene zinachilikiza Yesu?
18 Kodi nchiyani chimene chinakhozetsa Yesu kupirira kufikira mapeto? Mtumwi Paulo akutchula zinthu ziŵiri zimene zinachilikiza Yesu kuti: ‘mapemphero ndi mapembedzero’ ndiponso “chimwemwe choikidwacho pamaso pake.” Yesu, Mwana wangwiro wa Mulungu, sanachite manyazi kupempha chithandizo. Iye anapemphera “pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi.” (Ahebri 5:7; 12:2) Iye makamaka anaona kukhala kofunika kupempherera nyonga mobwerezabwereza ndi khama pamene mlandu wake wa m’bwalo lapamwambawo unali kuyandikira. (Luka 22:39-44) Poyankha mapemphero a Yesu, Yehova sanachotse chiyesocho, koma analimbikitsa Yesu kupirira. Yesu anapiriranso chifukwa chakuti anali kulingalira za mphotho yake ya mtsogolo koposa mtengo wozunzirapo—chisangalalo chimene akakhala nacho pochilikiza kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi kuwombola mtundu wa anthu kuimfa.—Mateyu 6:9; 20:28.
19, 20. Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha Yesu chimatithandizira kukhala ndi lingaliro labwino la zimene chipiriro chimaloŵetsamo?
19 M’chitsanzo cha Yesu chimenechi, timaphunzira zinthu zingapo zimene zimatithandiza kukhala ndi lingaliro labwino la zimene chipiriro chimaloŵetsamo. Njira ya chipiriro njovuta. Ngati tiona kupirira chiyeso china kukhala kovuta, chitonthozo chili m’kudziŵa kuti zofananazo zinachitikiranso Yesu. Kuti tipirire kufikira mapeto, tiyenera kupempherera nyonga mobwerezabwereza. Pamene tiyesedwa nthaŵi zina tingadzilingalire kukhala osayenerera kupemphera. Koma Yehova amafuna kuti timuuze zakukhosi kwathu ‘pakuti iye atisamalira.’ (1 Petro 5:7) Ndipo chifukwa cha zimene Yehova walonjeza m’Mawu ake, iye amatsimikiza kupereka “mphamvu yoposa yaumunthu” kwa awo amene amamfikira mwachikhulupiriro.—2 Akorinto 4:7-9, NW.
20 Nthaŵi zina tiyenera kupirira ndi misozi. Ululu wa pamtengo wozunzirapo sunali mwa iwo wokha chifukwa chosangalalira kwa Yesu. Mmalomwake, chisangalalo chake chinali pamphotho imene inali patsogolo pake. Kwa ife nkudzinyenga kuyembekezera kuti nthaŵi zonse tidzakhala achimwemwe ndi okondwa pamene tili pamayesero. (Yerekezerani ndi Ahebri 12:11.) Komabe mwakuyembekezera mphothoyo, ‘tingayese mayeserowo chimwemwe’ ngakhale pamene tikumana ndi mikhalidwe yoyesa kwambiri. (Yakobo 1:2-4; Machitidwe 5:41) Chinthu chofunika nchakuti tikhalebe olimba nji—ngakhale pamene mayeserowo angatiliritse. Ndi iko komwe, Yesu sananene kuti, ‘Iye amene agwetsa misozi yochepa adzapulumuka’ koma anati, “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:13.
21. (a) Kodi pa 2 Petro 1:5, 6 (NW), timalimbikitsidwa kuwonjezera chiyani pachipiriro chathu? (b) Kodi ndimafunso ati amene adzayankhidwa m’nkhani yathu yotsatira?
21 Motero chipiriro nchofunika kaamba ka chipulumutso. Komabe pa 2 Petro 1:5, 6 (NW), tikulimbikitsidwa kuwonjezera kudzipereka kwaumulungu pachipiriro chathu. Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani? Kodi kumagwirizana motani ndi chipiriro, ndipo kodi mungakupeze motani? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Kuvutika kwakukulu kumene Yesu anapirira mwinamwake kungaonedwe m’chenicheni chakuti munthu wangwiroyo anamwalira pambuyo pa maola oŵerengeka chabe pamtengo wozunzirapo, pamene kuli kwakuti ochita zoipa amene anapachikidwa pamodzi naye anafunikira kuthyoledwa miyendo yawo kufulumizitsa imfa yawo. (Yohane 19:31-33) Iwo sanamve kuvutika kwa maganizo ndi kwakuthupi kofanana ndi kumene Yesu anali nako mkati mwa zochitika za kuimbidwa mlandu usiku wonse asanapachikidwe, mwinamwake kufikira pamlingo wakuti sakanathanso kunyamula mtengo wake wozunzirapo.—Marko 15:15, 21.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kupirira kumatanthauzanji?
◻ Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova afunikira chipiriro mwapadera?
◻ Kodi chinakhozetsa Yobu kupirira nchiyani?
◻ Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha Yesu chimatithandizira kukhala ndi lingaliro labwino la chipiriro?
[Chithunzi patsamba 10]
Masukulu Aufumu anakhazikitsidwa kuphunzitsa ana Achikristu amene anathamangitsidwa kusukulu chifukwa chakulunjikitsa kulambira kwawo kwa Yehova yekha
[Chithunzi patsamba 12]
Potsimikizira kulemekeza Atate wake, Yesu anapempherera nyonga kuti apirire