Otanganitsidwa m’Ntchito Zakufa Kapena Muutumiki wa Yehova?
“PEPANI, ndiridi wotanganitsidwa.” Chimenechi ndicho chimodzi cha zitsutso zimene Mboni za Yehova zimakumana nazo pamene zimalalikira poyera mbiri yabwino Yaufumu. (Mateyu 24:14) Ndipo pamene kuli kwakuti mawu akuti “ndiridi wotanganitsidwa” nthaŵi zina ali kokha kungodzikhululukira, chenicheni nchakuti anthu ambiri ngotanganitsidwa. Iwo kwenikweni ngomwerekera ndi ‘nkhaŵa za dongosolo lino la zinthu’—zitsenderezo za kupeza zochirikizira moyo, kulipirira ngongole, kumka ndi kuŵeruka kuntchito, kulera ŵana, kusamalira panyumba, galimoto, ndi zinthu zina.—Mateyu 13:22.
Komabe, pamene kuli kwakuti anthu angakhaledi otanganitsidwa, oŵerengeka okha ndiwo amagwira ntchito imene iridi yopindulitsa kapena yothandiza. Ziri monga momwe mwamuna wanzeruyo Solomo analembera panthaŵi ina kuti: “Pakuti munthu ali ndi chiyani m’ntchito zake zonse, ndi m’kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno? Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wake supuma. Ichinso ndi chabe.”—Mlaliki 2:22, 23.
Baibulo limatchanso ntchito zopanda pake zimenezo kuti “ntchito zakufa.” (Ahebri 9:14) Kodi ntchito zotero zimalamulira moyo wanu? Zimenezi ziyenera kukhala zochititsa nkhaŵa yaikulu kwa inu monga Mkristu, popeza kuti Mulungu ‘adzalipira munthu aliyense molingana ndi ntchito yake.’ (Salmo 62:12) Ndipo popeza kuti “nthaŵi yafupika,” ife makamaka tiyenera kukhala odera nkhaŵa kuti sitikuwawanya nthaŵi ndi ntchito zimene ziri zakufa. (1 Akorinto 7:29) Koma kodi ntchito zakufa nchiyani? Kodi tiyenera kuziwona motani? Ndipo tingatsimikizire motani kuti tiri otanganitsidwa ndi ntchito zimene ziri zaphindu lenileni?
Kudziŵikitsa Ntchito Zakufa
Pa Ahebri 6:1, 2, Paulo analemba kuti: “Mwa ichi, polekana nawo mawu a chiyambidwe cha Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu, a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.” Wonani kuti “mawu a chiyambidwe” amaphatikizapo “kusiyana nazo ntchito zakufa.” Monga Akristu, oŵerenga kalata ya Paulowo anali atasiyana kale ndi ntchito zakufa zoterozo. Motani?
Asanavomereze Kristu, ena m’zaka za zana loyamba analikuchita “ntchito zathupi,” ndiko kuti, “dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga,” ndi ntchito zina zoipa. (Agalatiya 5:19-21) Ngati sanasamalire, ntchito zoterozo zikanatsogolera kuimfa yawo yauzimu. Komabe, mokoma mtima Akristu amenewo anali atachoka panjira yawo yachiwonongeko, nalapa, ndi ‘kuyeretsedwa.’ Motero iwo anali ndi kaimidwe koyera ndi Yehova.—1 Akorinto 6:9-11.
Komabe, sali Akristu onse, amene anafunikira kulapa ntchito zawo zimene zinali zoipa kapena chisembwere. Kwakukulukulu kalata ya Paulo inalembedwera Ayuda okhulupirira, amene ambiri a iwo mosakayikira anamamatira gwagwagwa ku Chilamulo cha Mose asanavomereze Kristu. Pamenepo, kodi ndintchito zakufa ziti, ku zimene anali atalapa? Ndithudi panalibe cholakwika ndi kukhala kwawo atatsatira zofunika za Chilamulo za miyambo ndi malamulo okhudza chakudya. Kodi Chilamulo sichinali “choyera, ndi cholungama, ndi chabwino”? (Aroma 7:12) Inde, koma pa Aroma 10:2, 3, Paulo anati ponena za Ayuda: “Ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma simonga mwa chidziŵitso. Pakuti pakusadziŵa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja kuchilungamo cha Mulungu.”
Inde, Ayudawo molakwa anakhulupirira kuti mwa kutsatira Chilamulo mosamalitsa, akatha kupeza chipulumutso chawo. Komabe, Paulo, anafotokoza kuti “munthu sayesedwa wolungama pantchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Kristu.” (Agalatiya 2:16) Dipo la Kristu litagaŵiridwa, ntchito za Chilamulo—mosasamala kanthu za kupatulika kwake kapena kulemekezeka—zinali ntchito zakufa ndi zopanda phindu kotheratu m’kupeza chipulumutso. Motero Ayuda amtima wowongoka anafunafuna chiyanjo cha Mulungu mwa kulapa ntchito zakufa zoterozo ndi kubatizidwa kusonyeza kulapa kwawo.—Machitidwe 2:38.
Kodi timaphunziranji m’zimenezi? Kuti ntchito zakufa zingaphatikizepo zoposa machitachita oipa kapena achisembwere; zimaphatikizapo ntchito iriyonse imene iri yakufa mwauzimu, yopanda pake, kapena yosapindulitsa. Koma kodi Akristu onse samalapa pantchito zakufa zoterozo asanabatizidwe? Zowona, komatu Akristu ena m’zaka za zana loyamba anabwereranso kumkhalidwe wachisembwere pambuyo pake. (1 Akorinto 5:1) Ndipo pakati pa Akristu Achiyuda, panali chikhoterero cha kubwereranso kumachitachita antchito zakufa za Chilamulo cha Mose. Paulo anafunikira kukumbutsa oterowo kusabwereranso kuntchito zakufa.—Agalatiya 4:21; 5:1.
Kuchenjera ndi Ntchito Zakufa
Chifukwa chake anthu a Yehova lerolino ayenera kukhala osamala kusagweranso mumsampha wa ntchito zakufa. Timaputidwa kumbali zonse ndi zitsenderezo kuti tilolere molakwa kumakhalidwe abwino, kukhala osawona mtima, ndi kuloŵa m’machitachita a kusadzisungira kwa kugonana. Nzomvetsa chisoni kunena kuti, chaka chirichonse zikwi zambiri za Akristu amagonjera kuzitsenderezo zotero, ndipo ngati salapa, amathamangitsidwa mumpingo Wachikristu. Pamenepotu, koposa ndi kale lonse, Mkristu ayenera kumvetsera chilangizo cha Paulo pa Aefeso 4:22-24: “Muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma . . . mukhale atsopano mumzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha chowonadi.”
Zowonadi, Aefeso kwa amene Paulo analembera anali atavala kale umunthu watsopano kumlingo waukulu. Koma Paulo anawathandiza kuzindikira kuti kuchita motero kunali mchitidwe wopitirizabe! Popanda kuyesayesa kosalekeza kumeneko, Akristu akanatsogoleredwanso kuntchito zakufa ndi zikhumbo zonyenga zimene zimapitirizabe kukhalapo monga chiyambukiro choipitsa. Zofananazo nzowona kwa ife lerolino. Tiyenera kuyesayesa mosalekeza kuvala umunthu watsopano, osaulola kuipitsidwa ndi zikhoterero zirizonse zopezedwa m’njira yathu yakale ya moyo. Tiyenera kukana—kuda—mpangidwe uliwonse wa ntchito zoipa zathupi. “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa,” amafulumiza motero wamasalmo.—Salmo 97:10.
Moyamikirika, unyinji wa anthu a Yehova lerolino walabadira uphungu umenewu ndi kudzisungira ali oyera mwamakhalidwe. Komabe, ena, apatutsidwa ndi ntchito zimene siziri kwenikweni zoipa mwa izo zokha koma zimene ziri zopanda pake kotheratu ndi zosapindulitsa. Mwachitsanzo, ena aphatikizidwa kotheratu m’njira zopangira ndalama zambiri kapena m’kupeza zinthu zakuthupi. Koma Baibulo limachenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.” (1 Timoteo 6:9) Kwa ena, maphunziro akudziko atsimikizira kukhala msampha. Zowonadi, mlingo wakutiwakuti wa maphunziro akudziko ungakhale wofunikira kuti apeze ntchito. Koma m’kulondola maphunziro audziko odya nthaŵiwo, ena adzivulaza mwauzimu.
Inde, ntchito zambiri sizingakhale zoipa mwamakhalidwe izo zokha. Komatu izo nzakufa ngati sizichirikizadi moyo wathu tsopano kapena kutipezera chiyanjo ndi Yehova Mulungu. Ntchito zoterozo zimadya nthaŵi ndi nyonga koma sizimatulutsa mapindu auzimu, sizimabweretsa mpumulo wokhalitsa.—Yerekezerani ndi Mlaliki 2:11.
Mosakayikira mukuyesayesa mwamphamvu kuti mukhale wokangalika m’ntchito zauzimu zoyenererazo. Komabe, kudzipenda inu mwini mokhazikika kumathandiza. Panthaŵi ndi nthaŵi, mungadzifunse mafunso onga akuti: ‘Kodi kukhala ndi phande kwanga muuutumiki wakumunda ndi kufika pamisonkhano kukudodometsedwa chifukwa chakuti ndaloŵa ntchito yakudziko yosafunikira?’ ‘Kodi ndiri ndi nthaŵi yochulukirapo ya kusanguluka koma nthaŵi yochepa ya phunziro la ine mwini ndi labanja?’ ‘Kodi ndimathera nthaŵi yambiri ndi nyonga kusamalira chuma chakuthupi pamene ndikulephera kusamalira osoŵa amumpingo, monga odwala ndi okalamba?’ Mayankho a mafunso ameneŵa angavumbule kufunikira kwanu kwa kuika ntchito zauzimu choyamba pamlingo wokulirapo.
Khalani Wotanganitsidwa Muutumiki wa Yehova
Monga momwe 1 Akorinto 15:58 amanenera, muli ‘zochuluka zakuchita muntchito ya Ambuye.’ Yoposa zonse ndiyo kulalikidwa kwa Ufumu ndi ntchito ya kupanga ophunzira. Pa 2 Timoteo 4:5, Paulo anafulumiza kuti: “Panga ntchito ya kulalikira Mbiri Yabwino kukhala ya moyo wako, muutumiki wotheratu.” (Jerusalem Bible) Akulu ndi atumiki otumikira nawonso ali nzambiri zochita m’kusamalira zosoŵa za gulu lankhosa. (1 Timoteo 3:1, 5, 13; 1 Petro 5:2) Mitu yabanja—ambiri a iwo ali kholo limodzi lolera ana—nawonso ali ndi mathayo olemetsa m’kusamalira mabanja awo ndi kuthandiza ana awo kukulitsa unansi wawo ndi Mulungu. Ntchito zoterozo zingakhale zotopetsa, ndipo zothodwetsadi panthaŵi zina. Koma mmalo mwa kukhala zakufa, zimadzetsa chikhutiro chenicheni!
Vuto nlakuti: Kodi munthu amapeza motani nthaŵi yochitira ntchito zofunika zoyenerera zimenezi? Kudzilanga ndi kukhala wolinganizika nzofunika. Pa 1 Akorinto 9:26, 27, Paulo analemba kuti: “Ndithamanga chotero, simonga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, simonga ngati kupanda mlengalenga; koma ndipumphuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.” Njira ina yogwiritsirira ntchito lamulo la makhalidwe abwino la lemba ili ikakhala ya kupenda nthaŵi ndi nthaŵi njira yanu yochitira zinthu ndi njira ya moyo. Mungatulukire bwino lomwe kuti mungathe kuchotsa zinthu zingapo zowawanyitsa nthaŵi yanu ndi nyonga zosafunikazo.
Mwachitsanzo, kodi nyonga yanu yochuluka ndi nthaŵi zikuthera pakuwonerera TV, pazosangulutsa, kuŵerenga mabuku audziko, ndi zochita zina zaumwini zosangalatsa? Malinga nkunena kwa nkhani ina mu The New York Times, munthu wauchikulire wachikatikati mu United States amamwerekera m’kuwonerera TV “mopitirira pang’ono chabe maola 30 pamlungu.” Ndithudi, nthaŵi imeneyo ingagwiritsiridwe ntchito moyenerera! Mkazi wina wa woyang’anira woyendayenda akusimba kuti: “Ndinachotsa pafupifupi zowawanyitsa nthaŵi zonse, zonga ngati kuwonerera wailesi yakanema.” Nchotulukapo chotani? Mkaziyo anali wokhoza kuŵerenga mavoliyamu onse aŵiri a nazonse wa Baibulo Insight on the Scriptures!
Nanunso mungafunikire kulingalira ukulu umene mungafeŵetsere njira yanu ya moyo. Solomo anati: “Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.” (Mlaliki 5:12) Kodi nthaŵi yanu yochuluka ndi nyonga zimaperekedwa kukusamalira chuma chosafunikira chakuthupi? Ndithudi, pamene tikhala ndi zinthu zambiri, ndipamenenso timafunikira kusamalira zinthu zambirizo, kuzisunga, kukonzetsera, ndi kuzitetezera. Kodi kungakhale kwaphindu kwa inu kuti mudzimane zinthu zakutizakuti?
Kukhala ndi programu yotsimikizirika ndiko njira ina ya kugwiritsira ntchito nthaŵi yanu bwino kwambiri. Programu yoteroyo iyenera kuphatikizapo kufunika kwa munthuwe kwa kupuma ndi kusanguluka. Koma zinthu zauzimu ziyenera kukhala zoyamba. Nthaŵi iyenera kupatulidwa ya kufika pamisonkhano yonse yampingo mokhazikika. Mungasankhenso pasadakhale kuti ndimasiku ati kapena madzulo amene angaperekedwe kuntchito yolalikira. Limodzi ndi kulinganiza kosamalitsa, inu mungathedi kuwonjezera kukhala ndi phande kwanu muutumiki, mwinamwake kutumikira monga mpainiya wothandiza panthaŵi ndi nthaŵi. Komabe, khalani wotsimikizira kulinganiza nthaŵi ya phunziro laumwini ndi labanja, kuphatikizapo kukonzekera bwino lomwe misonkhano. Mwakukhala wokonzekera, sikokha kuti mudzapeza zowonjezereka pamisonkhano inu eni komanso mudzakhala pamalo abwino kwambiri a ‘kufulumizana kuntchito zabwino’ mwa ndemanga zanu.—Ahebri 10:24.
Kupeza nthaŵi yophunzira kungafunikiritse kudzimana. Mwachitsanzo, padziko lonse mabanja a Beteli amadzuka mmamaŵa mmaŵa uliwonse kuti akhale ndi kukambitsirana kwa lemba latsiku. Kodi kukakhala kotheka kwa inu kupeza nthaŵi pang’ono mmaŵa uliwonse kaamba ka phunziro laumwini? Wamasalmo anati: “Ndinafuula kusanache: Ndinayembekezera mawu anu.” (Salmo 119:147) Ndithudi, kudzuka mmamaŵa kukafunikiritsa kulinganiza ola loyenerera lokagona kuti mukadzuke muli wolimba ndi wotsitsimulidwa tsiku lotsatiralo.
Mapindu a Kukhala Wotanganitsidwa Muutumiki wa Yehova
Kukhala ndi ‘zochita zochuluka muntchito ya Ambuye’ kumafunikiritsa kulinganiza, kudzilanga, ndi kudzimana. Koma mudzasangalala ndi mapindu osaŵerengeka monga chotulukapo chake. Chotero khalanibe wotanganitsidwa, osati muntchito zakufa kapena zopanda pake zimene zimangodzetsa kuwombetsedwa mpeya ndi chisoni, koma muutumiki wa Yehova. Pakuti kuli mwantchito zoterozo kuti mumasonyeza chikhulupiriro chanu, kupeza chivomerezo cha Mulungu, ndipo, potsirizira pake, mphotho ya moyo wosatha!
[Chithunzi patsamba 28]
Kupanga programu yotsimikizirika kumathandiza Mkristu kugwiritsira ntchito nthaŵi yake mwanzeru kwambiri