Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2008 | December 15
    • “Mkulu wa Ansembe”

      15. N’chifukwa chiyani udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe ndi wosiyana ndi wa akulu ansembe ena?

      15 Anthu ambiri m’mbuyomu anakhalapo pa udindo wa mkulu wa ansembe. Koma Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wapadera. N’chifukwa chiyani zili choncho? Paulo anati: “Iye safunikira kupereka nsembe tsiku ndi tsiku za machimo a iye mwini choyamba, kenako za anthu ena, monga amachitira akulu a ansembe. (Iye anachita zimenezi kamodzi kwatha pamene anadzipereka nsembe.) Pakuti Chilamulo chimaika amuna okhala ndi zofooka kukhala akulu a ansembe. Koma mawu a lumbiro onenedwa pambuyo pa Chilamulo anaika Mwana, amene anakhalitsidwa wangwiro kosatha.”​—Aheb. 7:27, 28.a

      16. N’chifukwa chiyani nsembe ya Yesu ilidi yapadera kwambiri?

      16 Yesu anali munthu wangwiro ngati mmene analili Adamu asanachimwe. (1 Akor. 15:45) Pachifukwa chimenechi, Yesu anali munthu yekhayo amene akanatha kupereka nsembe yangwiro komanso yokwanira, moti singafunike kubwerezedwa. M’chilamulo cha Mose, nsembe zinkaperekedwa tsiku ndi tsiku. Nsembe zonsezo ndiponso ntchito zonse zimene ansembe ankagwira zinali kuimira zimene Yesu anali kudzakwaniritsa. (Aheb. 8:5; 10:1) Motero Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wapadera chifukwa chakuti anakwaniritsa zimene anthu ena sakanatha kuchita komanso chifukwa chakuti adzatumikira pa udindo umenewu kosatha.

  • Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2008 | December 15
    • b Ayuda m’nthawi ya atumwi ankadziona kuti ndi mtundu woyanjidwa ndi Mulungu, chifukwa chakuti anali mbadwa za Abulahamu. Komabe iwo ankayembekezera kuti kudzabwera munthu mmodzi amene adzakhale Mesiya kapena kuti Khristu.​—Yoh. 1:25; 7:41, 42; 8:39-41.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena