Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tisabwerere Kuloŵa Kuchitayiko!
    Nsanja ya Olonda—1999 | December 15
    • Tisabwerere Kuloŵa Kuchitayiko!

      “Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko.”​—AHEBRI 10:39.

      1. Kodi ndi zochitika zotani zimene zinapangitsa mtumwi Petro kugwidwa ndi mantha?

      ATUMWI ayenera kuti anadabwa kwambiri pamene Ambuye wawo wokondedwa, Yesu, anawauza kuti onse adzabalalika kum’siya. Kodi zimenezi zingatheke bwanji makamaka panthaŵi imene adzafunikira chichirikizo kwambiri ngati imeneyi? Petro ananena motsimikiza kuti: “Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iyayi.” Zoonadi, Petro anali mwamuna wolimba mtima. Koma pamene Yesu anaperekedwa ndi kumangidwa, atumwiwo, ndi Petro yemwe, anabalalika. Pambuyo pake, pomwe Yesu ankafunsidwa m’nyumba ya Kayafa Mkulu wa Ansembe, Petro sanachoke msanga ndipo anali m’bwalo la nyumbayo. Mkati mwa usiku wozizirawo, Petro ayenera kuti anayamba kuopa kuti Yesu ndi aliyense wogwirizana naye adzaphedwa. Pamene anthu ena amene anali pafupi anazindikira Petro kuti ndi mmodzi wa anzake a Yesu, mantha anam’gwira. Katatu konse anakana zoti ndi mnzake wa Yesu. Petro anakananso n’zoti amam’dziŵa n’komwe!​—Marko 14:27-31, 66-72.

      2. (a) N’chifukwa chiyani mantha a Petro usiku womwe Yesu anamangidwa sanam’pangitse kukhala wa “iwo obwerera”? (b) Kodi tiyenera kutsimikizira m’mtima kuti chiyani?

      2 Imeneyotu inali nthaŵi yomvetsa chisoni kwambiri m’moyo wa Petro, nthaŵi imene mosakayikira anachita chisoni poikumbukira m’moyo wake wonse. Koma kodi zimene Petro anachita usikuwo zinam’pangitsa kukhala munthu wamantha? Kodi zinam’panga kukhala mmodzi wa “iwo” amene mtumwi Paulo anadzafotokoza pamene analemba kuti: “Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko”? (Ahebri 10:39) Ambiri a ife tingavomereze kuti mawu a Paulo sakukhudza Petro. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mantha a Petro anali akanthaŵi kochepa, kufooka kosakhalitsa kwa munthu wolimba mtima ndi wachikhulupiriro chabasi. Mofananamo, ambiri a ife tilinso ndi nthaŵi zina m’mbuyomu zimene timachitabe chisoni tikazikumbukira, nthaŵi pamene tinadzidzimuka, n’kugwidwa ndi mantha amene anatilepheretsa kuimira choonadi molimba mtima monga momwe tinafunira. (Yerekezani ndi Aroma 7:21-23.) Ndife otsimikiza kuti kulephera kwa kanthaŵi kochepa kumeneku sikumatipanga kukhala m’gulu lobwerera kuchitayiko. Komabe, tiyenera kutsimikizira m’mtima kuti sitidzakhala m’gulu limenelo. Chifukwa chiyani? Ndipo tingapeŵe motani kukhala munthu wotero?

      Zimene Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko Kumatanthauza

      3. Kodi aneneriwo Eliya ndi Yona anachita mantha motani?

      3 Pamene Paulo analemba za “iwo akubwerera kuloŵa chitayiko,” sanali kunena za awo amene angagwidwe ndi mantha kwa kanthaŵi kochepa. Paulo analidi kudziŵa za nkhani ya Petroyo ndi nkhani zina zofanana nazo. Eliya, mneneri wolimba mtima ndiponso woyankhula mopanda mantha, anagwidwa ndi mantha panthaŵi inayake ndipo anathaŵa kuti apulumutse moyo wake chifukwa chakuti Mfumukazi Yezebeli woipayo anamuuza kuti adzamupha. (1 Mafumu 19:1-4) Mneneri Yona anachita mantha aakulu kwambiri. Yehova anamuuza kupita kumzinda wotchuka ndi chiwawa wa Nineve. Nthaŵi yomweyo Yona anakwera chombo chopita ku Tarisi​—mtunda wa makilomita 3,500 kuchokera ku Nineveko! (Yona 1:1-3) Komabe, aneneri okhulupirika ameneŵa ngakhalenso Petro sanganenedwe kuti ndi iwo obwerera m’mbuyo. Chifukwa chiyani?

      4, 5. (a) Kodi nkhaniyi ikutithandiza motani kudziŵa zimene Paulo anatanthauza ponena kuti “chitayiko” pa Ahebri 10:39? (b) Kodi Paulo anatanthauzanji ponena kuti: “Ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko”?

      4 Onani chiganizo chonse chimene mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito: ‘Koma ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko.’ Kodi anatanthauzanji ponena kuti “chitayiko”? Mawu achigiriki amene anagwiritsa ntchito, nthaŵi zina amatanthauza kuwonongedwa kwamuyaya. Tanthauzo limeneli likugwirizana ndi nkhaniyi. Paulo anali atangochenjeza kumene kuti: “Tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziŵitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuwononga otsutsana nawo.”​—Ahebri 10:26, 27.

      5 Chotero pamene Paulo anali kunena kwa okhulupirira anzake kuti, “Si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko,” ankatanthauza kuti iyeyo ndi Akristu okhulupirika oŵerenga kalata yakeyo anali otsimikizira kuti sadzachoka kwa Yehova ndipo sadzasiya kum’tumikira. Kubwerera kuloŵa kuchitayiko kungatsogolere kuchiwonongeko chosatha. Yudasi Isikariote ndi mmodzi mwa amene anabwerera kuloŵa kuchitayiko choterocho, monganso anachitira adani ena a choonadi amene mochita kufuna ankatsutsana ndi mzimu wa Yehova. (Yohane 17:12; 2 Atesalonika 2:3) Anthu oterowo ndiwo ena mwa “amantha” amene adzawonongedwa kosatha m’nyanja ya moto yophiphiritsayo. (Chivumbulutso 21:8) Ndithudi, sitikufuna kukhala m’gulu limenelo!

      6. Kodi Satana Mdyerekezi amafuna kuti titenge njira yotani?

      6 Satana Mdyerekezi akufuna kuti tibwerere kuloŵa kuchitayiko. Pokhala katswiri wa “machenjerero,” amadziŵa kuti njira yoipa imeneyi nthaŵi zambiri imayamba pang’onopang’ono. (Aefeso 6:11) Ngati chizunzo sichinakwaniritse zolinga zake, amayesa kuwononga chikhulupiriro cha Akristu oona mwa njira zina zosaonekera msanga. Amafuna kuona Mboni za Yehova zolimba mtima ndi zachangu zitazizira. Tiyeni tione machenjera amene anagwiritsa ntchito pa Akristu achihebri amene Paulo anawalembera kalata.

      Mmene Akristu Anapanikizidwira Kuti Abwerere

      7. (a) Kodi mpingo wa ku Yerusalemu unali utaona zotani? (b) Kodi ena mwa oŵerenga kalata ya Paulo anali mumkhalidwe wotani wauzimu?

      7 Umboni ukusonyeza kuti Paulo analembera Ahebri kalata yake cha mu 61 C.E. Mpingo wa ku Yerusalemu unali utakumana ndi zovuta zambiri. Pambuyo pa imfa ya Yesu, panabuka chizunzo choopsa, chimene chinakakamiza Akristu ochuluka mumzindawo kubalalika. Komabe panadzakhala nthaŵi inayake ya mtendere imene inalola Akristu kuwonjezeka. (Machitidwe 8:4; 9:31) M’kupita kwa zaka, zizunzo ndi mavuto ena zinkayamba ndi kutha. Zikuoneka kuti mmene Paulo ankalemba kalata yakeyo kwa Ahebri, mpingowo unalinso pamtendere. Komabe, panali ziyeso zina. Pafupifupi zaka makumi atatu zinali zitadutsa kuchokera pamene Yesu analosera kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Zikuoneka kuti panali ena amene anali kuona kuti mapeto achedwa mopitirira muyeso motinso mwina sadzadza iwo adakali amoyo. Ena, makamaka amene anali achatsopano m’chikhulupirirocho, anali asanayesedwebe ndi chizunzo chachikulu ndipo sanali kudziŵa kufunika kwenikweni kwa chipiriro poyesedwa. (Ahebri 12:4) Ndithudi Satana anayesetsa kupezerapo mpata pamikhalidwe imeneyo. Kodi ndi “machenjero” otani amene anagwiritsa ntchito?

      8. Kodi Ayuda ambiri ankauona motani mpingo watsopano wachikristu?

      8 Ayuda a m’Yerusalemu ndi m’Yudeya ankanyansidwa ndi mpingo wachikristu watsopanowo. Kungoona zimene Paulo analemba m’kalata yake, titha kudziŵa china mwa chitonzo chimene atsogoleri achipembedzo achiyuda amwanowo ndi otsatira awo ankanena kwa Akristu. Kwenikweni, ayenera kuti amati: ‘Ifeyo tili ndi kachisi wamkuluyo m’Yerusalemu, amene wakhalako zaka mazana! Tili ndi mkulu wa ansembe wolemekezeka kumeneko, limodzinso ndi ansembe ake aang’ono. Tsiku ndi tsiku nsembe zimaperekedwa. Tili ndi Chilamulo, chimene chinaperekedwa kwa Mose kudzera mwa angelo ndipo chinakhazikitsidwa ndi zizindikiro zazikulu pa Phiri la Sinai. Kagulu katsopanoka ka mpatuko, Akristuwa, amene apatuka ku Chiyuda, alibe zinthu ngati zimenezi!’ Kodi chitonzo chimenechi chinakwaniritsa zilizonse? Zikuoneka kuti Akristu ena achihebri anavutika maganizo ndi chitsutsocho. Kalata ya Paulo inawapatsa chichirikizo chapanthaŵi yake.

      Chifukwa Chake Sayenera Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko

      9. (a) Kodi nkhani yaikulu m’kalata ya Ahebri ndi yotani? (b) Kodi Akristu anali kutumikira m’kachisi wabwino kuposa wa m’Yerusalemu m’lingaliro lotani?

      9 Tiyeni tipende zifukwa ziŵiri zimene Paulo anapatsa abale ndi alongo ake a ku Yudeyako zimene sayenera kubwererera kuloŵa kuchitayiko. Chifukwa choyamba, chimenenso chili nkhani yaikulu m’kalata yonseyo yopita kwa Ahebri, ndicho ukulu wa dongosolo lachikristu la kulambira. M’kalata yake yonseyo, Paulo anafotokoza nkhani imeneyi. Kachisi wa m’Yerusalemu anali chithunzi chabe cha kachisi wamkulu koposa, kachisi wauzimu wa Yehova, nyumba ‘yosamangika ndi manja.’ (Ahebri 9:11) Akristu amenewo anali ndi mwayi wotumikira m’makonzedwe auzimu amenewo a kulambira koona. Anatumikira m’pangano labwino koposa, pangano latsopano lolonjezedwa kalelo, limene Nkhoswe yake ndi winawake wamkulu kwa Mose, Yesu Kristu.​—Yeremiya 31:31-34.

      10, 11. (a) N’chifukwa chiyani mzere wa Yesu wobadwiramo sunam’letse kutumikira monga Mkulu wa Ansembe m’kachisi wauzimu? (b) Kodi Yesu anali motani Mkulu wa Ansembe woposa amene anali kutumikira pakachisi m’Yerusalemu?

      10 Akristu amenewo analinso ndi Mkulu wa Ansembe wabwino kwambiri, Yesu Kristu. Inde, sanali mbadwa ya Aroni. Mmalo mwake, anali Mkulu wa Ansembe “monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke.” (Salmo 110:4) Melikizedeke, amene mzere wake wobadwiramo sunalembedwe, anali mfumu ya mzinda wakalewo wa Salemu komanso mkulu wa ansembe kumeneko. Chotero anali woyenerera kuphiphiritsa Yesu mwaulosi, amene unsembe wake sunadalire pa mzere uliwonse wobadwiramo wa anthu opanda ungwiro, koma pa chinachake chachikulu koposa​—lumbiro la Yehova Mulungu iye mwini. Monga Melikizedeke, Yesu sakungotumikira monga Mkulu wa Ansembe komanso monga Mfumu, mfumu imene sidzafa.​—Ahebri 7:11-21.

      11 Komanso, mosiyana ndi mkulu wa ansembe wa pakachisi ku Yerusalemu, Yesu sanafunikire kupereka nsembe chaka ndi chaka. Nsembe yake inali moyo wake wangwirowo, umene anaupereka kamodzi, kwatha. (Ahebri 7:27) Nsembe zonsezo zoperekedwa pakachisi zinali mithunzi, zithunzi za zimene Yesu anapereka. Nsembe yake yangwiro inatheketsa kukhulukidwa kwenikweni kwa machimo a anthu onse amene anasonyeza chikhulupiriro. Mawunso a Paulo ndi osangalatsa popeza akusonyeza kuti Mkulu wa Ansembe ndiye Yesu mmodzimodziyo wosasintha amene Akristu a mu Yerusalemu anam’dziŵa. Anali wodzichepetsa, wokoma mtima, amenenso ‘amamva chifundo ndi zofooka zathu.’ (Ahebri 4:15; 13:8) Akristu odzozedwawo anali ndi chiyembekezo chotumikira monga ansembe aang’ono a Kristu! Akanaganiza bwanji zobwerera ku “miyambo yofooka ndi yaumphaŵi” ya Chiyuda chowonongekacho?​—Agalatiya 4:9.

      12, 13. (a) Kodi Paulo anapereka chifukwa chachiŵiri chotani chomwe sayenera kubwererera? (b) N’chifukwa chiyani mbiri yawo yakale ya kupirira ikanalimbikitsa Akristu achihebri kusabwerera kuloŵa kuchitayiko?

      12 Ngati kuti chifukwacho sichinali chokwanira, Paulo anapatsa Ahebri chifukwa chachiŵiri chimene sayenera kubwererera kuchitayiko​—mbiri yawo ya chipiriro. Iye analemba kuti: “Tadzikumbutsani masiku akale, mmenemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zoŵaŵa.” Paulo anawakumbutsa kuti iwo anali “chinthu chooneredwa” potonzedwa ndi kusautsidwa. Ena anaponyedwa m’ndende; ena anasonyeza chifundo ndi kuchirikiza a m’ndendewo. Inde, anasonyeza chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro ndi kulimbikira. (Ahebri 10:32-34) Nangano n’chifukwa chiyani Paulo anawapempha ‘kukumbukira’ zokumana nazo zoŵaŵa ngati zimenezo? Kodi zimenezo sizikanawafooketsa?

      13 Iyayi, ‘kukumbukira masiku akale’ kukanakumbutsa Ahebri za mmene Yehova anawachirikizira m’mayesero awo. Ndi thandizo limeneli, iwo anali atalaka kale ziukiro zambiri za Satana. Paulo analemba kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Inde, Yehova anakumbukira ntchito zawo zonse zokhulupirikazo, kuwasunga m’chikumbumtima chake chosaiŵalacho. Zikutikumbutsa malangizo a Yesu akuti tizisungira chuma kumwamba. Palibe wakuba amene angabe chuma chimenechi; njenjete ndi dzimbiri sizingachiwononge. (Mateyu 6:19-21) Kwenikweni, chuma chimenechi chimawonongeka pokhapokha Mkristu atabwerera kuloŵa kuchitayiko. Kumenekotu kungawonongetse chuma chilichonse chimene anasungira kumwamba. N’chifukwatu champhamvu kwambiri chimene Paulo anapatsa Akristu achihebri chimene sanayenere kutenga njira imeneyo! N’kuwonongeranji zaka zonsezo za utumiki wokhulupirika? Kupitirizabe kupirira kungakhale koyenerera ndiponso kwabwino kwambiri.

      Chifukwa Chake Sitiyenera Kubwerera Kuloŵa Kuchitayiko

      14. Ndi zovuta zotani zimene tikuyang’anizana nazo lerolino zofanana ndi zimene Akristu a m’zaka zana loyamba anakumana nazo?

      14 Akristu oona lerolino alinso ndi zifukwa zamphamvu zimene sayenera kubwererera. Choyamba, tiyeni tione dalitso limene tili nalo pa kulambira koyera kumene Yehova watipatsa. Mofanana ndi Akristu a m’zaka zana loyamba, tikukhala panthaŵi imene anthu a m’zipembedzo zotchuka kwambiri amatinyogodola ndi kutitonza, ponyadira matchalitchi awo a mtengo wapatali ndi miyambo yawo yomwe inayamba kalekale. Komano Yehova akutitsimikizira kuti akuvomereza mtundu wathu wa kulambira. Kwenikweni, tili ndi madalitso lerolino amene Akristu a m’zaka zana loyamba analibe. Mungadabwe kuti, ‘Zingatheke bwanji?’ Iwotu analiko pamene kachisi wauzimu anali atangoyamba kumene. Kristu anakhala Mkulu wa Ansembe m’kachisiyo atangobatizidwa mu 29 C.E. Ena mwa Akristuwo anaona Mwana wa Mulungu wochita zozizwitsayo. Ngakhale pambuyo pa imfa yake, zozizwitsa zinanso zinkachitikabe. Koma monga momwe zinanenedweratu, mphatso zimenezo zinatha m’kupita kwa nthaŵi.​—1 Akorinto 13:8.

      15. Kodi Akristu oona lerolino akukhala m’nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa ulosi uti, ndipo zimenezo zimatanthauzanji kwa ife?

      15 Komabe, tikukhala m’nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwapadera kwa ulosi wa kachisi wamkuluyo wa Ezekieli m’machaputala 40-48.a Chotero, taona kukonzedwanso kwa kulambira koona kwa Mulungu. Kachisi wauzimu ameneyo wayeretsedwa, zoipitsa zonse zachipembedzo ndi kupembedza mafano zachotsedwamo. (Ezekieli 43:9; Malaki 3:1-5) Talingalirani za mapindu amene kuyeretsaku kwatipatsa.

      16. Kodi Akristu a m’zaka zana loyamba anakumana ndi chokhumudwitsa chotani?

      16 M’zaka zana loyamba, tsogolo la mpingo wachikristu wolinganizidwawo silinali kuoneka bwino. Yesu anali ataneneratu kuti zidzakhala monga kuti m’munda momwe mwangodzalidwa kumene tirigu mwadzalidwanso namsongole, kupangitsa tirigu kukhala wovuta kum’siyanitsa ndi namsongoleyo . (Mateyu 13:24-30) Ndipo zinaterodi. Podzafika kumapeto kwa zaka zana loyamba, pamene mtumwi Yohane wokalambayo anali yekhayo woti n’kuletsa zoipitsa, mpatuko unali utayamba kale. (2 Atesalonika 2:6; 1 Yohane 2:18) Mosakhalitsa atumwi atamwalira, gulu lina la atsogoleri achipembedzo linabadwa, lopondereza nkhosa ndiponso lovala zovala zachilendo. Mpatukowo unafala ngati mpweya woipa. Zimenezo zinali zokhumudwitsa kwambiri kwa Akristu okhulupirika! Iwo anaona kulambira koyera kokhazikitsidwa chatsopanoko kukuloŵedwa m’malo ndi kulambira koipa. Zimenezi zinayamba zaka zana limodzi zisanathe kuchokera pamene Kristu anakhazikitsa mpingo.

      17. Kodi mpingo wamakono wachikristu wakhala motani kwanthaŵi yaitali kuposa wa m’zaka zana loyamba?

      17 Tsopano, naku kusiyana kwake. Lerolino, kulambira koyera kwakhalapo kale kwanthaŵi yaitali kuposa mmene kunakhalirapo m’nthaŵi yonseyo kufikira atumwi anamwalira. Kuchokera pamene kope loyamba la magazini ino linafalitsidwa kalelo mu 1879, Yehova watidalitsa ndi kulambira komwe kukumkabe kukhala koyera. Yehova ndi Kristu Yesu analoŵa m’kachisi wauzimu mu 1918 kuti ayeretsemo. (Malaki 3:1-5) Chiyambire 1919, kulambira Yehova Mulungu kwakhala kukuyeretsedwa mopita patsogolo. Tikumvetsetsa kwambiri maulosi a Baibulo ndi mfundo zake zachikhalidwe. (Miyambo 4:18) Kodi tiyenera kuthokoza ndani? Osati anthu wamba opanda ungwiro. Yehova yekha, pamodzi ndi Mwana wake monga Mutu wa mpingo, ndiwo amene angateteze anthu Ake kuti asaipitsidwe m’nthaŵi zoipa zino. Chotero tisalephere konse kuthokoza Yehova potilola kutengamo mbali m’kulambira koyera lerolino. Ndipo tikhale otsimikiza m’mtima zolimba kuti sitidzabwerera kuloŵa kuchitayiko!

      18. Kodi tili ndi chifukwa chotani chosabwererera kuloŵa kuchitayiko?

      18 Mofanana ndi Akristu achihebriwo, tili ndi chifukwa chachiŵiri chokanira kuchita mantha ndi kubwerera. Ndicho mbiri yathu yachipiriro. Kaya sitinathe zaka zambiri tikutumikira Yehova kapena takhala tikum’tumikira mokhulupirika zaka zambirimbiri, tadzipangira mbiri ya ntchito zachikristu. Ambiri a ife tazunzidwa, kaya mwa kuponyedwa m’ndende, kutsekedwa kwa ntchito yathu, nkhanza, kapena kulandidwa katundu. Ambiri takhala tikutsutsidwa ndi achibale athu, kunyozedwa, ndi kunyalanyazidwa. Tonsefe tapirira, kupitirizabe utumiki wathu wokhulupirika kwa Yehova mosasamala kanthu za mavuto ndi mayesero a m’moyo. Mwa kutero, tapanga mbiri ya kulimbikira imene Yehova sadzaiŵala, nkhokwe ya chuma chosungidwa kumwamba. Chotero, inoyi si nthaŵinso yobwerera kudongosolo loipa lakaleli limene tinasiya kumbuyo! N’kuwonongeranji ntchito yathu yaikuluyo? Zimenezi zilidi motero makamaka lerolino, pamene kwatsala “kanthaŵi kakang’onong’ono” kuti mapeto afike.​—Ahebri 10:37.

      19. Kodi n’chiyani chidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira?

      19 Inde, tiyeni tikhale otsimikiza m’mtima kuti “ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko”! M’malo mwake, tiyeni tikhale “iwo a chikhulupiriro.” (Ahebri 10:39) Nanga tingatsimikizire motani kuti ndifedi otero, ndipo tingawathandize motani Akristu anzathu kuchita chimodzimodzi? Nkhani yotsatira idzafotokoza mfundo imeneyi.

  • Tikhaletu iwo Achikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1999 | December 15
    • Tikhaletu iwo Achikhulupiriro

      “Ndife . . . a iwo a chikhulupiriro cha kuchipulumutso cha moyo.”​—AHEBRI 10:39.

      1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikhulupiriro cha mtumiki aliyense wokhulupirika wa Yehova n’chamtengo wapatali?

      NTHAŴI ina mukadzakhalanso m’Nyumba ya Ufumu yodzaza ndi olambira Yehova, mukayang’ane kaye anthu onse okuzungulirani. Mukalingalire za njira zambiri zimene anthuwo amasonyezera chikhulupiriro. Mutha kudzaona achikulire amene atumikira Mulungu zaka zambirimbiri, achinyamata amene masiku onse amalimbana ndi chisonkhezero cha mabwenzi awo, ndi makolo amene akulimbikira kuphunzitsa ana awo kuopa Mulungu. Palinso akulu ndi atumiki otumikira, okhala ndi maudindo ambiri. Inde, mungadzaone abale ndi alongo auzimu a misinkhu yonse amene amagonjetsa zopinga zamitundumitundu kuti atumikire Yehova. Chikhulupiriro cha aliyense wa iwo n’chamtengo wapatali zedi!​—1 Petro 1:7.

      2. N’chifukwa chiyani uphungu wa Paulo m’machaputala 10 ndi 11 a Ahebri uli wopindulitsa kwa ife lerolino?

      2 Ndi anthu opanda ungwiro ochepa okha, ngati alipo n’komwe, amene amaposa mtumwi Paulo pa kuzindikira kwawo kufunika kwa chikhulupiriro. Pauloyo ananenanso kuti chikhulupiriro chenicheni chimatsogolera ku “chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Koma Paulo anadziŵanso kuti chikhulupiriro chingawonongedwe ndi kufafanizidwa m’dziko lino lopanda chikhulupiriro. Anali kuwadera nkhaŵa kwambiri Akristu achihebri a ku Yerusalemu ndi ku Yudeya, amene anali kuyesetsa kuti asataye chikhulupiriro chawo. Pamene tipenda mbali zina za machaputala 10 ndi 11 a Ahebri, tiyeni tione njira zimene Paulo anagwiritsa ntchito pomangirira chikhulupiriro chawo. Pamene tikutero, tidzaona mmene tingamangire chikhulupiriro cholimba mwa ife eni ndiponso mwa anzathu.

      Sonyezani Kuti Mumakhulupirirana

      3. Kodi mawu a Paulo opezeka pa Ahebri 10:39 akusonyeza motani kuti iye anali ndi chikhulupiriro mwa abale ndi alongo ake a m’chikhulupiriro?

      3 Chinthu choyamba chimene tingaone ndicho maganizo abwino a Paulo kwa anthu omwe ankawalembera kalatayo. Iye analemba kuti: “Koma ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko; koma a iwo achikhulupiriro cha kuchipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Paulo anali kuganiza zabwino, osati zoipa, ponena za Akristu anzake okhulupirikawo. Taonaninso kuti anagwiritsa ntchito mawu akuti “ife.” Paulo anali munthu wolungama. Komabe, sanayankhule modzitukumula kwa anthu omwe ankawalembera kalatayo, ngati kuti iyeyo ndiye anali wolungama kwambiri kuposa iwo. (Yerekezani ndi Mlaliki 7:16.) M’malo mwake, anadziphatika pagulu lawo. Anasonyeza chikhulupiriro chochokera pansi pa mtima chakuti iyeyo ndi Akristu okhulupirika omwe anaŵerenga kalata yake onse adzakumana ndi zopinga zothetsa nzeru zomwe zinali pafupi, kuti molimba mtima iwo adzakana kubwerera kuloŵa kuchitayiko, ndi kuti adzasonyeza kuti ali achikhulupiriro.

      4. Kodi Paulo anali ndi chikhulupiriro mwa okhulupirira anzake pazifukwa ziti?

      4 Chifukwa chiyani Paulo anali ndi chikhulupiriro chimenechi? Kodi sanali kuona zolakwa za Akristu achihebri? Iyayi. Anawapatsa uphungu wolunjika kuti awathandize kuthetsa zofooka zawo zauzimu. (Ahebri 3:12; 5:12-14; 6:4-6; 10:26, 27; 12:5) Komabe, Paulo anali ndi zifukwa zomveka ziŵiri zokhalira ndi chikhulupiriro mwa abale ake. (1) Monga wotsanzira Yehova, Paulo ankafuna kuona anthu a Mulungu monga momwe Yehova amawaonera. Sanali kungoona zolakwa zawo zokha koma mikhalidwe yawo yabwino ndi chiyembekezo chakuti iwo atha kusankha kuchita zabwino m’tsogolo. (Salmo 130:3; Aefeso 5:1) (2) Paulo anali kukhulupirira kwambiri mphamvu ya mzimu woyera. Anadziŵa kuti palibe zopinga, palibe zofooka zaumunthu, zimene zingaletse Yehova kuti asapereke “ukulu woposa wamphamvu” kwa Mkristu wina aliyense amene akufuna kutumikira Iye mokhulupirika. (2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13) Chotero chikhulupiriro cha Paulo mwa abale ndi alongo ake sichinali chophonyeka, chopanda pake, kapena chosaona zenizeni. Chinali chokhazikikadi ndiponso cha m’Malemba.

      5. Kodi chikhulupiriro cha Paulo tingachitsanzire motani, ndipo pangatsatire chiyani?

      5 Ndithudi, chikhulupiriro chimene Paulo anasonyeza chinasonkhezeranso ena. Pamene Paulo anayankhula molimbikitsa chotero ndi mipingo ku Yerusalemu ndi Yudeya, anthu a m’mipingomo ayenera kuti anakhudzidwa mtima kwambiri. Poyang’anizana ndi chitonzo choŵaŵa ndi kusoŵa chidwi kwa Ayuda odzitukumula omwe ankawatsutsa, mawu amenewo anathandiza Akristu achihebri kukhala otsimikizira m’mtima mwawo kuti akhale achikhulupiriro. Kodi lerolino tingachitenso chimodzimodzi kwa wina ndi mnzake? M’posavuta kungoona zolakwa zokhazokha ndi mikhalidwe yosasangalatsa mwa ena. (Mateyu 7:1-5) Komabe, tingathandizane kwambiri ngati tiyang’ana chikhulupiriro chapadera chimene aliyense ali nacho ndi kuchiyamikira kwambiri. Chikhulupirirotu chimakula ndi chilimbikitso choterechi.​—Aroma 1:11, 12.

      Kugwiritsa Ntchito Bwino Mawu a Mulungu

      6. Kodi Paulo anali kutchula mawu ochokera kuti pamene analemba mawu opezeka pa Ahebri 10:38?

      6 Paulo anamangiriranso chikhulupiriro mwa okhulupirira anzake pogwiritsa ntchito Malemba mwaluso. Mwachitsanzo, analemba kuti: “Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m’chikhulupiriro: ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.” (Ahebri 10:38) Paulo panopo anali kutchula mawu a m’buku la mneneri Habakuku.a Mawu ameneŵa ayenera kuti anali odziŵika kwa oŵerenga kalata ya Paulo, Akristu achihebri amene anali kuwadziŵa bwino kwambiri mabuku amaulosi. Poona cholinga chake, chomwe chinali kulimbitsa chikhulupiriro cha Akristu a m’Yerusalemu ndi m’madera oyandikana ndi mzindawo cha m’chaka cha 61 C.E., chitsanzo cha Habakuku chinali choyenerera zedi. Chifukwa chiyani?

      7. Kodi Habakuku anaulemba liti ulosi wake, ndipo zinthu zinali motani m’dziko la Yuda panthaŵiyo?

      7 Zikusonyeza kuti Habakuku analemba buku lake patangotsala zaka 20, kapena kuposapo pang’ono, kuti Yerusalemu awonongedwe mu 607 B.C.E. M’masomphenya, mneneriyo anaona Akasidi (kapena kuti, Ababulo), ‘mtundu woŵaŵa ndi waliŵiro,’ akukantha Yuda ndi kuwononga Yerusalemu, kumeza anthu ndi mitundu. (Habakuku 1:5-11) Koma tsoka limenelo linali litaloseredwa kuyambira m’tsiku la Yesaya, zaka zoposa zana limodzi m’mbuyo mwake. M’nthaŵi ya Habakuku, Yehoyakimu analoŵa m’malo Mfumu Yosiya yabwinoyo, ndipo kuipa kunachulukanso m’dziko la Yuda. Yehoyakimu anazunza ngakhalenso kupha anthu amene anali kuyankhula m’dzina la Yehova. (2 Mbiri 36:5; Yeremiya 22:17; 26:20-24) Ndiye chifukwa chaketu mneneri wachisoniyo Habakuku anafuula kuti: “Yehova, . . . mpaka liti?”​—Habakuku 1:2.

      8. N’chifukwa chiyani chitsanzo cha Habakuku chinathandiza Akristu m’zaka zana loyamba ndiponso lerolino?

      8 Habakuku sanali kudziŵa kuti chiwonongeko cha Yerusalemu chinali pafupi motani. Mofananamo, Akristu a m’zaka zana loyamba sanali kudziŵa kuti dongosolo lazinthu lachiyuda lidzatha liti. Ifenso lerolino sitikudziŵa “tsiku ilo ndi nthaŵi yake” pamene chiweruzo cha Yehova chidzadza padongosolo loipa lino la zinthu. (Mateyu 24:36) Chotero tiyeni tione yankho la mbali ziŵiri la Yehova kwa Habakuku. Choyamba, iye anatsimikizira mneneriyo kuti mapeto adzadza panthaŵi yake. ‘Sadzazengereza,’ anatero Mulungu, ngakhale kuti kwa munthu, angaoneke ngati kuti akuchedwa. (Habakuku 2:3) Chachiŵiri, Yehova anakumbutsa Habakuku kuti: “Wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Habakuku 2:4) Chimenechi ndi choonadi chosangalatsa ndiponso chosavuta kumva! Chofunika kwambiri si nthaŵi pamene mapetowo adzadza ayi, koma ngati tingapitirizebe kukhala moyo wachikhulupiriro.

      9. Kodi atumiki omvera a Yehova anakhalabe motani ndi moyo mwa chikhulupiriro chawo (a) mu 607 B.C.E.? (b) pambuyo pa 66 C.E.? (c) N’chifukwa chiyani kulimbitsa chikhulupiriro chathu kuli kofunika zedi?

      9 Yerusalemu atasakazidwa mu 607 B.C.E., Yeremiya, mlembi wake Baruki, Ebedi-Meleki, ndi Arekabu okhulupirikawo anaona choonadi cha lonjezo la Yehova kwa Habakuku. ‘Anakhalabe ndi moyo’ mwa kupulumuka chiwonongeko chowopsacho cha Yerusalemu. Chifukwa chiyani? Yehova anafupa kukhulupirika kwawo. (Yeremiya 35:1-19; 39:15-18; 43:4-7; 45:1-5) Mofananamo, Akristu achihebri a m’zaka zana loyamba ayenera kuti analabadira uphungu wa Paulo, popeza kuti pamene magulu ankhondo a Roma anazinga Yerusalemu mu 66 C.E. kenako n’kubwerera pachifukwa chosadziŵika bwino, Akristuwo anamvera mokhulupirika chenjezo la Yesu lakuti ayenera kuthaŵa. (Luka 21:20, 21) Anakhalabe ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Momwemonso, ifeyo tidzakhalabe ndi moyo ngati tikhalabe okhulupirika pamene mapeto afika. N’chifukwa chofunikatu zedi cholimbitsira chikhulupiriro chathu tsopano!

      Kulongosola Bwino Lomwe Zitsanzo za Chikhulupiriro

      10. Kodi Paulo anachilongosola motani chikhulupiriro cha Mose, ndipo kodi tingam’tsanzire motani Mose pambaliyi?

      10 Paulo anamangiriranso chikhulupiriro mwa kugwiritsa ntchito zitsanzo. Poŵerenga Ahebri chaputala 11, onani mmene akulongosolera bwino lomwe zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, iye ananena kuti Mose ‘anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.’ (Ahebri 11:27) M’mawu ena, Yehova anali weniweni kwa Mose moti zinali ngati kuti akuona ndi maso Mulungu wosaonekayo. Kodi ena anganenenso chimodzimodzi za ife? M’posavuta kungoyankhula za unansi ndi Yehova, koma kumangirira ndi kulimbitsa unansiwo ndi ntchito ndithu. Imeneyo ndiyo ntchito imene tiyenera kuchita! Kodi timaona Yehova kukhala weniweni moti timaganiza za iye posankha zopanga, ngakhale zioneke ngati zazing’ono? Chikhulupiriro choterocho chidzatithandiza kupirira ngakhale chitsutso choŵaŵa.

      11, 12. (a) Kodi chikhulupiriro cha Enoke chiyenera kuti chinayesedwa m’mikhalidwe yotani? (b) Kodi Enoke analandira mfupo yotani yolimbikitsa?

      11 Lingaliraninso chikhulupiriro cha Enoke. N’kovuta kwa ife kuyerekeza chitsutso chimene anakumana nacho. Enoke anayenera kulengeza uthenga wopyoza mtima wachiweruzo pa anthu oipa omwe analiko m’nthaŵiyo. (Yuda 14, 15) Mwachionekere chizunzo chimene mwamuna wokhulupirikayu akanakumana nacho chinali choopsa kwambiri, chankhanza zedi, moti Yehova ‘anam’tenga,’ kum’samutsira kutulo ta imfa adani ake asanamuukire. Chotero Enoke kunalibe pamene ulosi umene ananena unakwaniritsidwa. Komabe, analandira mphatso imene, m’lingaliro lina, inali yabwino koposa.​—Ahebri 11:5; Genesis 5:22-24.

      12 Paulo anafotokoza kuti: “Asanam’tenge, [Enoke] anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu.” (Ahebri 11:5) Kodi mawuŵa anatanthauzanji? Asanagone tulo ta imfa, mwina Enoke anaona masomphenya ena ake, mwina anaona Paradaiso wapadziko lapansi mmene adzaukitsidwira tsiku lina posachedwapa. Mulimonse mmene zinalili, Yehova anadziŵitsa Enoke kuti Iye anakondwera ndi moyo wake wachikhulupiriro. Enoke anakondweretsa mtima wa Yehova. (Yerekezani ndi Miyambo 27:11.) Kuganiza za moyo wa Enoke n’kosangalatsa, kodi sitero? Kodi mungakonde kukhala ndi moyo wachikhulupiriro woterowo? Ndiyetu sinkhasinkhani pazitsanzo zimenezi; onani anthuwo monga kuti ali pambali panu. Khalani wotsimikizira mumtima kuti mudzasonyeza chikhulupiriro, tsiku ndi tsiku. Kumbukiraninso kuti iwo okhala ndi chikhulupiriro satumikira Yehova chifukwa chodziŵa tsiku kapena nthaŵi pamene Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake onse. M’malo mwake, tinasankha kutumikira Yehova kosatha! Kuchita zimenezi ndiko njira yabwino koposa ya moyo m’dongosolo la zinthu linolo komanso likudzalo.

      Mmene Tingakhalire ndi Chikhulupiriro Cholimba

      13, 14. (a) Kodi mawu a Paulo olembedwa pa Ahebri 10:24, 25 angatithandize motani kupanga misonkhano yathu kukhala chochitika chosangalatsa? (b) Kodi cholinga chachikulu cha misonkhano yachikristu n’chiyani?

      13 Paulo anasonyeza Akristu achihebri njira zingapo mmene akanalimbitsira chikhulupiriro chawo. Tiyeni tikambirane ziŵiri zokha. Mwachionekere tikudziŵa chilimbikitso chake cha pa Ahebri 10:24, 25, chotilimbikitsa kusonkhana nthaŵi zonse pamisonkhano yathu yachikristu. Komano, kumbukirani kuti mawu ouziridwawo a Paulo sakunena kuti tiyenera kukhala pamisonkhano imeneyo n’kumangopenyerera. M’malo mwake, Paulo analongosola kuti misonkhanoyo ili mpata woti tidziŵane, tisonkhezerane kutumikira Mulungu mowonjezereka, ndi kuti tilimbikitsane. Timapezeka pamisonkhanoyo kuti tipatse, osati kungolandira. Zimenezo zimapangitsa misonkhano yathu kukhala zochitika zosangalatsa kwambiri.​—Machitidwe 20:35.

      14 Komabe, chachikulu kwambiri n’chakuti timafika pamisonkhano yachikristu kuti tilambire Yehova Mulungu. Timachita zimenezo mwa kugwirizana m’pemphero ndi kuimba nawo nyimbo, kumvetsera mosamala kwambiri, ndiponso mwa kupereka “chipatso cha milomo,” chimene chili mawu otamanda Yehova m’ndemanga zathu ndi m’nkhani zathu za pamisonkhanoyo. (Ahebri 13:15) Ngati tikhala ndi zolinga zimenezi m’maganizo mwathu ndi kuzichita pamsonkhano uliwonse, chikhulupiriro chathu chidzamangiriridwa nthaŵi zonse.

      15. N’chifukwa chiyani Paulo anauza Akristu achihebri kuti agwiritse utumiki wawo, nanga n’chifukwa chiyani uphungu umodzimodziwo uli wofunikanso lerolino?

      15 Njiranso ina yomangirira chikhulupiriro ndiyo mwa ntchito yolalikira. Paulo analemba kuti: “Tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika.” (Ahebri 10:23) Mumauza munthu kuti agwiritse chinachake chimene akuoneka kuti ali pafupi kuchileka. Ndithudi Satana anali kuvutitsa Akristu achihebri amenewo kuti asiye utumiki wawo, ndipo akuvutitsanso anthu a Mulungu lerolino. Poyang’anizana ndi mavuto ngati amenewo, kodi tiyenera kuchitanji? Talingalirani zimene Paulo anachita.

      16, 17. (a) Kodi Paulo anakhala motani wolimba mtima muutumiki? (b) Kodi tiyenera kutani tikapeza kuti mbali inayake ya utumiki wathu wachikristu imatichititsa mantha?

      16 Kwa Akristu a ku Tesalonika, Paulo analemba kuti: “Tingakhale tidamva zoŵaŵa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziŵa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa [“tinalimba mtima,” NW] mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.” (1 Atesalonika 2:2) Kodi Paulo ndi anzake ‘anachitiridwa chipongwe’ motani ku Filipi? Malinga n’kunena kwa akatswiri ena, mawu achigiriki amene Paulo anagwiritsa ntchito amatanthauza kutukwanidwa, kuselewulidwa, kapena kunyozedwa. Akuluakulu a ku Filipi anawakwapula ndi ndodo, kuwaponya m’ndende, ndi kuwamanga m’zigologolo. (Machitidwe 16:16-24) Kodi chokumana nacho choŵaŵa chimenecho chinam’khudza motani Paulo? Kodi anthu a mumzinda wotsatira, Tesalonika, omwe anawachezera paulendo wake waumishonalewo anaona kuti Paulo akuchita mantha? Iyayi, iye “analimba mtima.” Anagonjetsa mantha napitirizabe kulalikira molimba mtima.

      17 Kodi kulimba mtima kwa Paulo kunachokera kuti? Mumtima mwake? Iyayi, ananena kuti analimba mtima “mwa Mulungu wathu.” Buku lina lothandiza otembenuza Baibulo linafotokoza kuti mawu ameneŵa angatembenuzidwenso kuti, “Mulungu anachotsa mantha m’mitima yathu.” Chotero ngati mumachita mantha muutumiki wanu, kapena ngati pali mbali ina yautumiki imene imakuchititsani mantha, bwanji osam’pempha Yehova kuti achitenso chimodzimodzi kwa inu? M’pempheni kuti achotse mantha mumtima mwanu. M’pempheni kuti akuthandizeni kulimba mtima kuti muchite ntchitoyo. Ndiponso, chitaninso zinthu zina zothandiza. Mwachitsanzo, linganizani kuti mukachite ntchitoyo ndi winawake waluso pamtundu wa umboni umene umakuchititsani manthawo. Mwina ndi ulaliki wa m’malo amalonda, umboni wa mu msewu, ulaliki wamwamwayi, kapena umboni wapatelefoni. Mwina mnzanuyo angalole kusonyeza chitsanzo kaye. Ngati zili motero, onani mmene akuchitira ndipo phunzirani. Komano kenako, limbani mtima kuti muyese kuchita zomwezo.

      18. Kodi tingalandire madalitso otani ngati tilimba mtima muutumiki wathu?

      18 Ngati mulimba mtima, lingalirani zimene zingatsatire. Mutalimbikira ndi kusalefuka, mungakhale ndi zokumana nazo zabwino pogaŵana choonadi ndi ena, zokumana nazo zimene mwina simukanakhala nazo. (Onani patsamba 25.) Mudzakhutira podziŵa kuti mwakondweretsa Yehova mwa kuchita chinthu chovuta kwa inu. Mudzalandira dalitso ndi thandizo lake pogonjetsa mantha anu. Chikhulupiriro chanu chidzalimba. Ndithudi, simungamangirire chikhulupiriro cha ena popanda kumangiriranso chanu panthaŵi imodzimodziyo.​—Yuda 20, 21.

      19. Kodi “iwo achikhulupiriro” adzalandira mfupo yotani yamtengo wapatali?

      19 Pitirizanibe kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndi chikhulupiriro cha anzanu. Mungachite zimenezi mwa kumangirira chikhulupiriro chanu ndi cha ena pogwiritsa ntchito mwaluso Mawu a Mulungu, kuphunzira zitsanzo za m’Baibulo za chikhulupiriro ndi kuziona ngati zikungochitika kumene, kukonzekera ndi kutengamo mbali m’misonkhano yachikristu, ndiponso mwa kugwiritsa mwayi wamtengo wapatali wa utumiki wapoyera. Pamene mukuchita zinthu zimenezi, dziŵani kuti ndinudi mmodzi wa “iwo achikhulupiriro.” Kumbukiraninso kuti anthu a m’gulu limeneli ali ndi mfupo yamtengo wapatali. Amenewo ndiwo “iwo achikhulupiriro cha kuchipulumutso cha moyo.”b Chikhulupiriro chanu chipitirizebe kukula, ndipo Yehova Mulungu akusungeni amoyo kosatha!

      [Mawu a M’munsi]

      a Paulo anatchula mawu a pa Habakuku 2:4 monga momwe alili mu Septuagint, imene ili ndi mawu akuti “ngati wina abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.” Mawu ameneŵa sakupezeka m’mipukutu yachihebri imene ilipo tsopano. Ena anena kuti Septuagint inazikidwa pa mipukutu yachihebri yakale kwambiri imene kulibenso lerolino. Mulimonse mmene zinalili, Paulo anawaphatikiza pano mawuwo mosonkhezeredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Chotero mawuwo ndi ouziridwa ndi Mulungu.

      b Lemba la chaka la Mboni za Yehova m’chaka cha 2000 lidzakhala lakuti: “Ife si ndife a iwo akubwerera . . . koma a iwo a chikhulupiriro.”​—Ahebri 10:39.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena