Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 11/15 tsamba 30
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndimotani Mmene Yesu Kristu Analiri Mneneri Wofanana ndi Mose?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mmene Moyo wa Mose Umakukhudzirani
    Galamukani!—2004
  • Tsanzirani Chikhulupiriro cha Mose
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kuzindikira Mose Wamkulu
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 11/15 tsamba 30

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Pa Ahebri 11:26, kodi Mose akunenedwa kukhala “Kristu,” kapena kodi mmalo mwake anali phiphiritso la Yesu Kristu?

Pofotokoza chikhulupiriro cha Mose, mtumwi Paulo analemba kuti Mose “anaŵerenga thonzo la Kristu chuma choposa zolemera za Aigupto; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho.” (Ahebri 11:26) Kukuwonekera kuti Paulo anali kusonya kwa Mose kuti “Kristu,” kapena m’lingaliro lina, wodzozedwayo.

Ndithudi m’mbali zosiyanasiyana Mose anapereka chitsanzo cha Mesiya amene analinkudza. Ngakhale kuti Mose mwiniyo anali mneneri, iye adaneneratu kudza kwa mneneri wamkulu kwambiri ‘wofanana naye.’ Ayuda ambiri anaganiza kuti Yesu anali ‘Mneneriyo,’ zimene otsatira ake anatsimikizira. (Deuteronomo 18:15-19; Yohane 1:21; 5:46; 6:14; 7:40; Machitidwe 3:22, 23; 7:37) Mose analinso mtetezi wa pangano Lachilamulo, koma Yesu analandira “chitumikiro chomveka choposa” monga ‘nkhoswe yoyenerana yapangano labwinopo,’ pangano latsopano laulemerero. (Ahebri 8:6; 9:15; 12:24; Agalatiya 3:19; 1 Timoteo 2:5) Chotero m’zochitika zina Mose anganenedwe kukhala atachitira chithunzi Mesiya wakudzayo.

Komabe, zimenezo, sizikuwonekera kukhala tanthauzo lalalikulu la Ahebri 11:26. Palibe chisonyezero chakuti Mose anali kuzindikira mfundo zonse zonena za Mesiya, kotero kuti anaŵerengera zimene anakumana nazo mu Igupto kukhala zochitidwa mmalo mwa Mesiya kapena monga woimira wake.

Ena apereka lingaliro lakuti mawu a Paulo pa Ahebri 11:26 anali ndi tanthauzo lofanana ndi landemanga yake yakuti Akristu analoŵa ‘m’masautso kaamba ka Kristu.’ (2 Akorinto 1:5) Akristu odzozedwa anadziŵa kuti Yesu Kristu anavutika ndi kuti ngati iwo ‘akavutika limodzi naye akalemekezedwa pamodzi naye’ kumwamba. Koma Mose sanadziŵe zimene Mesiya amene analinkudzayo akavutika nazo, ndiponso Mose analibe chiyembekezo chakumwamba.​—Aroma 8:17; Akolose 1:24.

Pali chidziŵitso chokhweka kwambiri cha mmene Mose ‘anaŵerengerera thonzo la Kristu kukhala chuma choposa.’

Pamene Paulo analemba kuti “Kristu” mu Ahebri 11:26, anagwiritsira ntchito liwu Lachigiriki Khri·stouʹ, limene liri lolingana ndi Lachihebri Ma·shiʹach, kapena Mesiya. Onse aŵiri “Mesiya” ndi “Kristu” amatanthauza “wodzozedwa.” Chotero Paulo anali kulemba za ‘kuŵerengera thonzo la wodzozedwayo’ kwa Mose. Kodi Mose iyemwiniyo angatchedwe “wodzozedwayo”?

Inde. M’nthaŵi za Baibulo munthu angatsimikiziridwe malo antchito apadera mwakutsanulira mafuta pamutu pake. “Samueli anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake [pa Sauli].” “Samueli anatenga nyanga yamafuta, namdzoza [Davide] pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide.” (1 Samueli 10:1; 16:13; yerekezerani ndi Eksodo 30:25, 30; Levitiko 8:12; 2 Samueli 22:51; Salmo 133:2.) Komabe, ena, monga ngati mneneri Elisa ndi Hazaeli mfumu ya Aaramu, akunenedwa kukhala “atadzozedwa” ngakhale kuti palibe umboni wakuti mafuta enieni anatsanuliridwa pa iwo. (1 Mafumu 19:15, 16; Salmo 105:14, 15; Yesaya 45:1) Chifukwa chake, munthu akakhoza kukhala “wodzozedwa” mwakusankhidwa kapena kutumidwa mwapadera.

M’lingaliro limeneli Mose mwiniyo anali wodzozedwa wa Mulungu, ndipo Mabaibulo ena amaperekadi matembenuzidwe onga akuti “Wodzozedwa wa Mulungu” kapena “Wodzozedwayo” pa Ahebri 11:26. Mose anatumidwa monga woimira wa Yehova ndi wotsogolera Israyeli kutuluka mu Igupto. (Eksodo 3:2-12, 15-17) Ngakhale kuti Mose analeredwera pakati pa chuma cha Igupto ndi ulemerero wake, iye anaŵerengera kwambiri ntchito yake, imene anavomereza ndi kuichita. Chifukwa chake, Paulo anakhoza kulemba kuti Mose “anaŵerenga thonzo la Kristu chuma choposa zolemera za Igupto.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena