Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 12/1 tsamba 9-14
  • Musaleme!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musaleme!
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Ena Atikhumudwitsa
  • Pamene Tilephera
  • Pamene Tilingalira Kuti Sitikuchita Zokwanira
  • Pamene Zambiri Zifunidwa kwa Ife
  • Chifukwa Chakuti Mapeto Sanafikebe
  • Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Maso Ako Aziyang’ana pa Zinthu Zakutsogolo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Kodi Ndachita Tchimo Losakhululukidwa?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Kuti Ndisiye Kudziimba Mlandu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 12/1 tsamba 9-14

Musaleme!

“Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda [kutopa, NW].”​—AGALATIYA 6:9.

1, 2. (a) Kodi mkango umasaka nyama motani? (b) Kodi Mdyerekezi amafunitsitsa kugwira ayani monga nyama?

MKANGO umasaka nyama m’njira zosiyanasiyana. Nthaŵi zina umalalira nyama pamalo pake pomwera madzi kapena mmene zimadzera. Koma nthaŵi zina, likufotokoza motero buku lakuti Portraits in the Wild, mkango “umangogwiritsira ntchito mwaŵi umene wapezeka​—mwachitsanzo, pamene upeza mwana wa mbidzi amene wagona.”

2 ‘Mdani wathu Mdyerekezi,’ akufotokoza motero mtumwi Petro, “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Podziŵa kuti nthaŵi yake yomtsalira njaifupi, nthaŵi zonse Satana akutsendereza anthu mokulirapo kuti awaletse kutumikira Yehova. Komabe, “mkango wobuma” umenewu makamaka ukufunitsitsa kulikwira atumiki a Yehova. (Chivumbulutso 12:12, 17) Njira zake zosakira nzofanana ndi za nyama ija ya m’nkhalango yonga iye. Motani?

3, 4. (a) Kodi Satana amagwiritsira ntchito njira zotani posaka atumiki a Yehova monga nyama? (b) Popeza kuti zino ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa,” kodi ndi mafunso otani amene akubuka?

3 Nthaŵi zina Satana amayesa kulalira​—chizunzo kapena chitsutso chimene cholinga chake ndi kuswa umphumphu wathu kotero kuti tileke kutumikira Yehova. (2 Timoteo 3:12) Koma, monga mkango, nthaŵi zina Mdyerekezi amangogwiritsira ntchito mwaŵi umene wapezeka. Amayembekezera kufikira pamene tagwiritsidwa mwala kapena kutopa, ndiyeno amayesa kugwiritsira ntchito kupsinjika kwathu kuti atilemetse. Sitiyenera kukhala nyama yake yosavuta kugwira!

4 Komabe, tikukhala ndi moyo m’nyengo yovuta kwambiri m’mbiri yonse ya anthu. Mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, ambiri a ife tingalefuke kapena nthaŵi zina kulemetsedwa. (2 Timoteo 3:1) Nangano, tingapeŵe motani kutopa kwambiri ndi kukhala nyama ya Mdyerekezi yosavuta kugwira? Inde, kodi tingalabadire motani uphungu wouziridwa wa mtumwi Paulo wakuti: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda [kutopa, NW]”?​—Agalatiya 6:9.

Pamene Ena Atikhumudwitsa

5. Kodi nchiyani chimene chinachititsa Davide kutopa, koma iye sanachitenji?

5 M’nthaŵi za Baibulo, nthaŵi zina ngakhale atumiki a Yehova okhulupirika koposa mwina analemetsedwa. “Ndalema nako kuusa moyo kwanga,” analemba motero wamasalmo Davide. “Ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga. Lapuŵala diso langa chifukwa cha chisoni.” Kodi nchifukwa ninji Davide anamva motero? “Chifukwa cha onse akundisautsa.” iye anafotokoza motero. Machitidwe okhumudwitsa a ena anasautsa mtima wa Davide kwakuti misozi yake inatuluka yokha. Chikhalirechobe, Davide sanafulatire Yehova chifukwa cha zimene anzake anamchitira.​—Salmo 6:6-9.

6. (a) Kodi tingayambukiridwe motani ndi mawu kapena machitidwe a ena? (b) Kodi ndimotani mmene ena amakhalira nyama ya Mdyerekezi yosavuta kugwira?

6 Mofananamo, mawu kapena machitidwe a ena angatifoole moŵaŵitsa mtima kwambiri. “Alipo wonena mwasontho ngati kupyoza kwa lupanga,” imatero Miyambo 12:18. Pamene wonena mwasonthoyo ali mbale kapena mlongo Wachikristu, ‘popyozedwapo’ pangakhale pakuya. Mwachibadwa tingakwiye, mwinamwake tikumasunga mkwiyo. Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati tiona kuti tachitiridwa mosakoma mtima kapena mopanda chilungamo. Tingapeze kukhala kovuta kuti tilankhulane ndi wotichimwirayo; mwina tingafune kumupeŵa. Pokhala olemetsedwa ndi mkwiyo, ena aleka kufika ku misonkhano Yachikristu. Mwachisoni, iwowo mwa kutero ‘amampatsa malo Mdyerekezi’ kuti apeze mwaŵi wa kuwagwira monga nyama yosavuta kugwira.​—Aefeso 4:27.

7. (a) Kodi tingapeŵe motani kugwera m’manja mwa Mdyerekezi ngati ena atikhumudwitsa? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchotsa mkwiyo?

7 Kodi tingapeŵe motani kugwera m’manja mwa Mdyerekezi pamene ena atikhumudwitsa? Tiyenera kuyesayesa kusasunga mkwiyo. M’malo mwake, tiyambe ifeyo kupanga mtendere kapena kuthetsa nkhaniyo msanga. (Aefeso 4:26) Akolose 3:13 amatilimbikitsa kuti: “[Pitirizani, NW] . . . kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake.” Kukhululukira nkoyenera makamaka pamene munthu amene wachimwayo avomera cholakwa napepesa moona mtima. (Yerekezerani ndi Salmo 32:3-5 ndi Miyambo 28:13.) Komabe, ndi bwino kukumbukira kuti kukhululukira si kulekerera kapena kuchepetsa zolakwa zimene ena achita. Kukhululukira kumaphatikizapo kuleka kukwiya. Mkwiyo uli katundu wolemetsa. Ungathe kuwononga malingaliro athu, kutilanda chimwemwe. Ungayambukirenso thanzi lathu. Mosiyana ndi zimenezo, kukhululukira, pamene kuli koyenera, kumatipindulitsa. Monga Davide, tisagonjetu ndi kufulatira Yehova chifukwa cha zimene anthu ena anena kapena kutichitira!

Pamene Tilephera

8. (a) Kodi nchifukwa ninji anthu ena amamva kukhala aliwongo kwambiri nthaŵi zina? (b) Kodi ndi ngozi yotani imene imakhalapo pamene tilola liwongo kukula kwambiri kwakuti nkutitayitsa mtima?

8 “Timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri,” amatero Yakobo 3:2. Pamene titero, kumva kukhala waliwongo nkwachibadwa. (Salmo 38:3-8) Malingaliro a kukhala waliwongo angakhale aakulu makamaka ngati tikulimbana ndi chifooko china cha thupi ndipo timalephera kaŵirikaŵiri.a Mkristu wina amene anachita nkhondo yotero akufotokoza kuti: “Sindinafunenso kukhala ndi moyo, pokhala wosadziŵa kuti kaya ndinali nditapanga tchimo losakhululukidwa kapena ayi. Ndinalingalira kuti sindiyeneranso kuyesayesa mu utumiki wa Yehova chifukwa mwina ndachedwa kale.” Pamene liwongo litikulira kwakuti nkutaya mtima, timapatsa Mdyerekezi mpata​—ndipo iye angaugwiritsire ntchito msanga! (2 Akorinto 2:5-7, 11) Mwina chimene chimafunika ndicho kukhala ndi lingaliro loyenera la liwongo.

9. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti Mulungu adzachita chifundo?

9 Pamene tichimwa nkoyenera kumva kukhala waliwongo. Komabe, nthaŵi zina, malingaliro a kukhala waliwongo amapitiriza chifukwa chakuti Mkristu amalingalira kuti ali wosayenerera chifundo cha Mulungu. Komabe, mwachikondi Baibulo limatitsimikizira kuti: “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.” (1 Yohane 1:9) Kodi pali chifukwa chilichonse chabwino chokhulupirira kuti Mulungu sadzachita zimenezi kwa ife? Kumbukirani kuti, m’Mawu ake, Yehova amanena kuti ali “wokonzekera kukhululukira.” (Salmo 86:5, NW; 130:3, 4) Popeza kuti sanganame, adzachita motero monga momwe Mawu ake amalonjezera, ngati timfikira ndi mtima wolapa.​—Tito 1:2.

10. Kodi ndi chilimbikitso chosonkhezera mtima chotani chimene Nsanja ya Olonda ina kumbuyoku inafalitsa ponena za kulimbana ndi chifooko china chakuthupi?

10 Kodi muyenera kuchitanji ngati mukulimbana ndi chifooko china ndipo mwachibwerezanso? Musagonje! Kuchibwerezako sikumathetsa kupita patsogolo kumene mwapanga kale. Kope la magazini ano la February 15, 1954, linapereka chilimbikitso chosonkhezera mtima ichi: “Ti[nga]khumudwe ndi kulephera kaŵirikaŵiri pa chizoloŵezi china choipa chimene chinakhomerezeka kwambiri m’moyo wathu wakale kuposa mmene tinadziŵira. . . . Musathedwe nzeru. Musanene kuti mwapanga tchimo losakhululukidwa. Umo ndimo mmenedi Satana akufuna kuti mulingalirire. Kumva chisoni kwanu kwenikweniko ndi kuvutika kokhako kuli umboni wakuti simunankitse. Musatope pa kutembenukira kwa Mulungu modzichepetsa ndi mwakhama, mukumapempha chikhululukiro chake ndi chiyeretso ndi thandizo. Pitani kwa iye monga momwe mwana amapitira kwa atate wake pamene ali m’mavuto, mosasamala kanthu kuti mumachita zimenezo kangati pa chifooko chimodzimodzicho, ndipo mwachifundo Yehova adzakupatsani thandizo chifukwa cha chisomo chake ndipo, ngati muli woona mtima, adzakupatsani chikumbumtima choyera.”

Pamene Tilingalira Kuti Sitikuchita Zokwanira

11. (a) Kodi tiyenera kulingalira motani ponena za kukhala ndi phande mu ntchito yolalikira Ufumu? (b) Kodi ndi malingaliro otani onena za kukhala ndi phande mu utumiki amene Akristu ena amalimbana nawo?

11 Ntchito yolalikira Ufumu njofunika kwambiri m’moyo wa Mkristu, ndipo kukhalamo ndi phande kumabweretsa chimwemwe. (Salmo 40:8) Komabe, Akristu ena amaona kukhala aliwongo kwambiri chifukwa chosatha kuchita zambiri mu utumiki. Liwongo limenelo likhoza kuthetsa chimwemwe chathu ndi kutichititsa kugonja, tikumaganiza kuti Yehova akulingalira kuti sitimachita zambiri. Talingalirani za malingaliro amene ena amalimbana nawo.

“Kodi mudziŵa mmene umphaŵi umadyera nthaŵi?” analemba motero mlongo wina Wachikristu amene akulera ana atatu ndi mwamuna wake. “Ndifunikira kusinira pa kalikonse kamene ndingathe. Zimenezi zitanthauza kuthera nthaŵi ndikumafunafuna kugula zovala zakale m’masitolo ake, zovala zimene zatsitsidwa mtengo kuti zithe m’sitolo, kapena ngakhale kusoka zovala. Ndimatheranso ola limodzi kapena maola aŵiri mlungu uliwonse ndikumakonza makuponi [a chakudya chotsitsidwa mtengo]​—kuwadula, kuwaika m’faelo, ndi kuwagwiritsira ntchito pogula. Nthaŵi zina ndimaona kukhala waliwongo kwambiri pochita zinthu zimenezi, ndikumaganiza kuti ndiyenera kuthera nthaŵi imeneyo mu utumiki wakumunda.”

“Ndinalingalira kuti sindikonda Yehova kwambiri,” mlongo wina wa ana anayi wokhala ndi mwamuna wosakhulupirira anafotokoza motero. “Chotero kutumikira kwanga Yehova kunali kovuta. Ndinayesadi mwamphamvu, koma sindinakhutire. Mwaona nanga, sindinadziŵerengere, chotero sindinathe kuona mmene Yehova akanavomerezera utumiki wanga kwa iye.”

Mkazi wina Wachikristu amene anaganiza kuti ndi bwino kusiya utumiki wanthaŵi yonse anati: “Sindinathe kupirira ndi lingaliro lakuti ndinali kulephera pa choŵinda changa cha kutumikira Yehova nthaŵi yonse. Simungathe kudziŵa mmene ndinakhumudwira! Tsopano ndimalira pokumbukira zimenezi.”

12. Kodi nchifukwa ninji Akristu ena amaona kukhala aliwongo kwambiri chifukwa cha kusatha kuchita zambiri mu utumiki?

12 Nkwachibadwa kufuna kutumikira Yehova mokwanira bwino. (Salmo 86:12) Komabe, kodi nchifukwa ninji ena amaona kukhala aliwongo chifukwa cha kusatha kuchita zambiri? Kwa ena, zichita ngati kuti zimagwirizana ndi kusadziŵerengera, zimene ambiri amaganiza, mwinamwake chifukwa cha zokumana nazo zina zosakondweretsa m’moyo. Kwa ena, liwongo losayeneralo lingakhalepo chifukwa cha kusadziŵa bwino zimene Yehova amafuna kwa ife. “Ndinkalingalira kuti pokhapokha ngati munthuwe ugwira ntchito modzitopetsa, mpamene ungakhale ukuchita zokwanira,” mkazi wina Wachikristu anavomereza motero. Chotero, anadziikira miyezo yapamwamba yonkitsa​—nakhalanso waliwongo kwambiri pamene sanathe kuifikira.

13. Kodi Yehova amayembekezeranji kwa ife?

13 Kodi Yehova amayembekezeranji kwa ife? Kunena mosavuta, Yehova amayembekezera kuti timtumikire ndi mtima wonse, tikumachita zimene mikhalidwe yathu imalola. (Akolose 3:23) Komabe, pangakhale kusiyana kwakukulu pakati pa zimene tingafune kuchita ndi zimene tingathedi kuchita. Tingakhale osatha kuchita zimenezo chifukwa cha zinthu zonga ukalamba, matenda, nyonga yakuthupi, kapena mathayo a banja. Komabe, pamene tichita zonse zimene tikhoza, tingatsimikizire kuti utumiki wathuwo kwa Yehova ngwamtima wonse​—wofanana ndendende ndi wa munthu wina amene thanzi lake ndi mikhalidwe zikumlola kukhala mu utumiki wanthaŵi yonse.​—Mateyu 13:18-23.

14. Kodi mungachitenji ngati mufuna thandizo pofuna kudziŵa zimene mungathedi kuchita?

14 Nangano, kodi ndimotani mmene mungadziŵire zimene mukhozadi kuchita? Mwina mungakambitsirane nkhaniyo ndi bwenzi Lachikristu lodalirika ndi lokula msinkhu, mwinamwake mkulu kapena mlongo wodziŵa zinthu, amene amadziŵa maluso anu, zofooka zanu, ndi mathayo anu a banja. (Miyambo 15:22) Kumbukirani kuti kufunika kwanu m’maso mwa Mulungu monga munthu panokha sikumapimidwa ndi zimene mumachita mu utumiki wakumunda. Atumiki onse a Yehova ngamtengo wapatali kwa iye. (Hagai 2:7; Malaki 3:16, 17) Zimene mumachita mu ntchito yolalikira zingakhale zambiri kapena zochepa kuposa zimene ena amachita, komano malinga ngati zili zabwino zanu zoposa, Yehova amakondwera, ndipo simufunikira kudziona kukhala waliwongo.​—Agalatiya 6:4.

Pamene Zambiri Zifunidwa kwa Ife

15. Kodi zambiri zimafunidwa m’njira ziti kwa akulu a mumpingo?

15 “Kwa munthu aliyense adampatsa zambiri,” Yesu anatero, “kwa iye adzafuna zambiri.” (Luka 12:48) Zoonadi ‘zambiri zimafunidwa’ kwa awo amene amatumikira monga akulu mumpingo. Monga Paulo iwo amadzipereka kuti atumikire mpingo. (2 Akorinto 12:15) Amakhala ndi nkhani zoti akonzekere, kupanga maulendo aubusa, kusamalira nkhani zachiweruzo​—zonsezo popanda kunyalanyaza mabanja awo. (1 Timoteo 3:4, 5) Akulu ena amatanganitsidwanso ndi kuthandiza kumanga Nyumba za Ufumu, kutumikira m’Hospital Liaison Committee (Makomiti Olankhulana ndi Zipatala), ndi kudzipereka pantchito pamisonkhano yadera ndi yachigawo. Kodi amuna ameneŵa odzipereka ogwira ntchito zolimba angapeŵe motani kuyamba kutopa pa kulemera kwa mathayo ameneŵa?

16. (a) Kodi ndi lingaliro lothandiza lotani limene Yetero anapereka kwa Mose? (b) Kodi ndi mkhalidwe uti umene ungakhozetse mkulu kugaŵana ndi ena mathayo oyenera?

16 Pamene Mose, mwamuna wodekha ndi wodzichepetsayo, anayamba kutopa kwambiri posamalira mavuto a ena, mpongozi wake, Yetero, anapereka lingaliro lothandiza: kugaŵira mathayo ena kwa amuna oyenerera. (Eksodo 18:17-26; Numeri 12:3) “Nzeru ili ndi odzichepetsa,” Miyambo 11:2 imatero. Kukhala wodzichepetsa kumatanthauza kuzindikira ndi kuvomereza zimene simungathe kuchita. Munthu wodzichepetsa amafuna kugaŵira ena mathayo, ndiponso samawopa kuti mwina adzalandidwa ulamuliro chifukwa cha kugaŵana mathayo oyenera ndi amuna ena oyenerera.b (Numeri 11:16, 17, 26-29) M’malo mwake, amakhala wokondwera kuwathandiza kuti apite patsogolo.​—1 Timoteo 4:15.

17. (a) Kodi ziŵalo za mpingo zingapeputse motani mtolo wa akulu? (b) Kodi ndi kudzimana kotani kumene akazi a akulu amapanga, ndipo tingawasonyeze motani kuti sitimaona zimenezi mwawamba?

17 Ziŵalo za mpingo zingathandize kwambiri kupeputsira akulu mtolo wawo. Pozindikira kuti akulu ali ndi mabanja awo oti awasamalire, ena sayenera kuwonongera akulu nthaŵi yawo yochuluka ndi kufuna chisamaliro chawo mopambanitsa. Ndiponso sadzaona mwawamba kudzimana kwaufulu kumene akazi a akulu amasonyeza pamene amalola amuna awo kutumikira mpingo. Nakubala wina wa ana atatu amene mwamuna wake akutumikira monga mkulu anafotokoza kuti: “Chinthu chimene sindimang’ung’udza nacho ndiwo mtolo wina umene ndimasenza mwaufulu m’banja kotero kuti mwamuna wanga atumikire monga mkulu. Ndikudziŵa kuti dalitso la Yehova nlalikulu pa banja lathu chifukwa cha kutumikira kwake, ndipo sindimachita nsanje ndi zimene amapereka. Komabe, kunena zoona, kaŵirikaŵiri ndimachita ntchito yambiri ya pabwalo ndipo ndimachita zambiri pa kulanga ana athu kuposa mmene ndikanachitira chifukwa chakuti mwamuna wanga amakhala wotanganitsidwa.” Mwachisoni, mlongo ameneyu anapeza kuti ena, m’malo moyamikira mtolo wake winawo, ananena mawu okhumudwitsa onga akuti, “Kodi nchifukwa ninji simuchita upainiya?” (Miyambo 12:18) Nkwabwino kwambiri chotani nanga kuyamikira ena chifukwa cha zimene akuchita m’malo mwa kuwasuliza pa zimene sakhoza kuchita!​—Miyambo 16:24; 25:11.

Chifukwa Chakuti Mapeto Sanafikebe

18, 19. (a) Kodi nchifukwa ninji ino sili nthaŵi ya kuleka kuthamanga mu mpikisano wa moyo wosatha? (b) Kodi ndi chilangizo cha panthaŵi yake chotani chimene mtumwi Paulo anapereka kwa Akristu a ku Yerusalemu?

18 Pamene wothamanga adziŵa kuti akuyandikira mapeto a mpikisano wamtunda wautali, samagonja. Thupi lake lingafike poti silikhozanso kupirira​—kutopa, kutenthedwa, kumva ludzu​—koma pamene wayandikira kwambiri mapeto sindiyo nthaŵi ya kuleka kuthamanga. Mofananamo, ife monga Akritsu tili mu mpikisano wa mphotho ya moyo, ndipo tili pafupi kwambiri ndi mzera wake womalizira. Ino si nthaŵi yathu ya kuleka kuthamanga!​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:24; Afilipi 2:16; 3:13, 14.

19 Akristu a m’zaka za zana loyamba anayang’anizana ndi mkhalidwe umodzimodziwu. Cha ku ma 61 C.E., mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Yerusalemu. Nthaŵi inali kutha​—“mbadwo” woipa, dongosolo la zinthu Lachiyuda lampatuko, linali pafupi ‘[kutha, NW].’ Makamaka Akristu a ku Yerusalemu anafunikira kukhala atcheru ndi okhulupirika; anafunikira kuthaŵa mzindawo pamene anaona utazingidwa ndi magulu ankhondo. (Luka 21:20-24, 32) Pamenepo, chilangizo chouziridwa cha Paulo chinali cha panthaŵi yake: “Musaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.” (Ahebri 12:3) Pano mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito maverebu amphamvu: “lema” (kaʹmno) ndi “komoka” (e·klyʹo·mai). Malinga ndi kunena kwa katswiri wina wa Baibulo, mawu Achigiriki ameneŵa “Aristotle amawagwiritsira ntchito ponena za othamanga liŵiro amene amalefuka ndi kugwa atadutsa mzera womalizira. Oŵerenga [kalata ya Paulo] anali akali mu mpikisano. Sanafunikire kuleka mwamsanga. Sanafunikire kulefuka ndi kugwa chifukwa cha kutopa. Kachiŵirinso pali kufunika kwa kuchita khama polimbana ndi ndi zovuta.”

20. Kodi nchifukwa ninji chilangizo cha Paulo chili cha panthaŵi yake kwa ife lerolino?

20 Chilangizo cha Paulo nchapanthaŵi yake chotani nanga kwa ife lerolino! Poyang’anizana ndi zitsenderezo zowonjezereka, pangakhale nthaŵi zina pamene timamva ngati wothamanga wotopa amene ali pafupi kukomoka. Komatu tili pafupi kwambiri ndi mzera womalizira, sitiyenera kugonja! (2 Mbiri 29:11) Zimenezo nzimene Mdani wathu, “mkango wobuma” umenewo, akufuna kuti tichite. Mwamwaŵi, Yehova wapanga makonzedwe amene amapatsa “mphamvu iye amene alibe mphamvu.” (Yesaya 40:29) Mu nkhani yathu yotsatira tidzakambitsirana kuti makonzedwe ameneŵa nchiyani ndi kuti tingawagwiritsire ntchito motani.

[Mawu a M’munsi]

a Mwachitsanzo, ena angakhale akulimbana ndi chibadwa china choipa chokhomerezeka kwambiri, monga ngati kuchita ukali, kapena kugonjetsa vuto la psotopsoto.​—Onani Galamukani! wa July 8, 1988, masamba 11-13; Awake! ya November 8, 1981, masamba 16-20; Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza, masamba 198-211, zofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Onani nkhani yakuti “Akulu​—Gaŵirani Mathayo!” m’kope la October 15, 1992, la Nsanja ya Olonda, masamba 20-3.

Kodi Yankho Lanu Nlotani?

◻ Kodi tingapeŵe motani kugonja pamene ena atigwiritsa mwala kapena kutikhumudwitsa?

◻ Kodi ndi lingaliro loyenera lotani la liwongo limene lidzatipeŵetsa kugonja?

◻ Kodi Yehova amayembekezeranji kwa ife?

◻ Kodi kudzichepetsa kungathandize motani akulu a mumpingo kupeŵa kutopa?

◻ Kodi nchifukwa ninji chilangizo cha Paulo pa Ahebri 12:3 chili cha panthaŵi yake kwa ife lerolino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena