Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 3/8 tsamba 12-13
  • Kukhala Mayi Woberekera Kodi Kuli kwa Akristu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala Mayi Woberekera Kodi Kuli kwa Akristu?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kukhala Mayi Woberekera Nchiyani?
  • Mavuto a Kuberekera
  • Kodi Kukhala Mayi Woberekera Kumalemekeza Ukwati?
  • Njira Zatsopanozi Zabweretsanso Mavuto Atsopano
    Galamukani!—2004
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2002
  • Ana Ambiri Akubadwa Kudzera M’njira Zothandizira Anthu Osabereka Kuti Abereke
    Galamukani!—2004
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 3/8 tsamba 12-13

Lingaliro la Baibulo

Kukhala Mayi Woberekera Kodi Kuli kwa Akristu?

WOLEMBA ndakatulo wamakedzana Wachiroma wotchedwa Horace sanadziŵe kali konse ponena za kukhala mayi woberekera pamene analemba kuti: “Ziribe kanthu kuti ndimakolo ati anabala munthuyo, malinga ngati iye ali munthu wabwino.” Mwambi wa mlembi Wachifalansa wa m’zaka za zana la 17 wakuti, “Kubadwa sikanthu koma ubwino ndiwo,” nawonso unalembedwa kale kwambiri lingaliro la kuberekera wina lisanakhale chothetsa nzeru kwa oweruza. Koma, monga momwe Mary Thom anasimbira m’magazini a Ms., pokhala ndi njira zatsopano zobalira, “ntchito ya wopereka dzira, wosunga mluza umene udzakhala mwana, ndi wosamalira mwanayo atabadwa” ingagaŵidwe pakati pa “amayi” aŵiri kapena atatu. Nkhani ya “ubwino” ndi “chotulukapo” yakhala ponse paŵiri yosamveka ndi yovuta.

Mchitidwe wa kugwiritsira ntchito amayi oberekera unafalikira mwadzidzidzi padziko lonse chapakati pa ma 1970, ukumadzuutsa mavuto a kakhalidwe ka anthu, chikhalidwe cha mtima, ndi a zamalamulo amene sanakhalepo ndi kale lonse. Okwatirana ena osabala anali ofunitsitsa kupindula ndi njira yakubala yosakhala yachibadwa imeneyi. Kumbali ina, madokotala, maloya, ndi opanga malamulo ayesayesa mwamphamvu kuyendera limodzi ndi njira yobalitsa yomakulakulabe imeneyi m’zoyesayesa za kupereka malangizo amene angayankhe mafunso odzutsidwa a mwambo ndi a chikhalidwe cha mtima.

Kodi Kukhala Mayi Woberekera Nchiyani?

Kukhala mayi woberekera, kapena wapangano, ndiko kuchita kuti mkazi woikidwa ubwamuna m’chibaliro chake abalire mwana mkazi wina mwanjira ina yosakhala yakugonana. Kotchedwa kuberekera kwa mwambo kumachitika pamene mayi woberekera amatenga mimba mwa kuikidwa m’chibaliro chake mwa njira ina yosakhala yakugonana ubwamuna wa mwamuna wokwatira mkazi woberekeredwa amene apangana naye. Chotero woberekerayo ndiye mayi weniweni wa mwanayo. Kuberekera mwa kungonyamulira mluza kumatanthauza kuti dzira la mkazi ndi ubwamuna wa mwamuna wake zimagwirizanitsidwa kunja kwa chibaliro mwa njira yotchedwa in-vitro (test-tube) fertilization, ndipo mluza wotsatirapo umaikidwa m’chibaliro cha woberekerayo kuti aunyamule pamene ukukula.

Kodi nchifukwa ninji kukhala mayi woberekera kwakhala kofala? Choyamba, sayansi yopita patsogolo yatulukira njira zingapo zothandizira akazi kukhala ndi ana. Okwatirana angakhale ndi chikhumbo champhamvu cha kukhala ndi mwana, koma chifukwa cha kusabala, kuvuta kwa mkhalidwe wawo, kapena kusoŵeka kwa ana athanzi labwino amene angalere, iwo satha kukhala ndi mmodzi yemwe. Chotero amabwereka thupi la munthu wina kuti akhale ndi mwana. Popeza kuti ndalama zochuluka zikuloŵetsedwamo, kuberekera kwafotokozedwa m’mawu osakondweretsa, onga ngati “ukapolo wokakamiza” ndi “kupindulira pa kubala kwa osauka mosasamala kanthu ndi zimene zingatsatirepo.”

Mu United States, New Jersey Supreme Court inazindikira kuthekera kwa olemera kudyera masuku pamutu osauka ndipo pamlandu wa kuberekera inati: “Pomaliza, pali miyezo imene chitaganya chimawona kukhala yofunika koposa kulola chuma kugula chirichonse chimene chingathe, kaya chikhale kubala, chikondi, kapena moyo.” Supreme Court ya ku Falansa inafotokoza kuti kukhala mayi woberekera kumaluluza thupi la mkazi ndi kuti “thupi la munthu siloti libwerekedwe, siloti lichitidwe lendi, siloti ligulitsidwe.”

Mavuto a Kuberekera

Kuberekera kumayambitsa mavuto angapo. Limodzi ndilo kuthekera kwa milandu yosakondweretsa ya m’makhoti ngati mkazi woberekayo afuna kusunga mwana. Kodi mwanayo ngwayani, ngwamkazi woberekayo kapena mkazi amene amapereka dzira? Chotero kubadwa kwa mwana, kumene kaŵirikaŵiri kuli nthaŵi yachisangalalo, nthaŵi zina kumachititsa milandu ya m’makhoti. Vuto lina ndi ili: Akazi ena amene amavomereza kukhala amayi oberekera amawona kuti mtima wawo umayamba kumasintha pakukula ndi kubadwa kwa mwana wapangano. Pangano lochitidwa m’miyezi yapitayo limakhala lovutirapo kulisunga. Unansi wolimba zedi umapangika pakati pa mayiyo ndi mwana ali mwa iye. Mayi wina woberekera, amene sanayembekezere unansi wolimba umenewu, akufotokoza mmene anadzimvera ponena za kupereka mwana: “Ndinawona ngati kuti wina wamwalira. Thupi langa linali kulirira mwana wanga wamkazi.”

Ndiponso, kodi ndiziyambukiro zachikhalire zotani zimene kubala kotero kungadzetse pa ana ena a mayi woberekera, banja limene lilandira mwanayo, ndi mwana iyemwiniyo? Kapena kodi nchiyani chimene chingachitike ngati mwana woberekedwa ndi mayi woberekera ali wolemala? Kodi tate ali ndi thayo la kutenga mwanayo? Ngati saali, kodi adzapereka ndalama zosamalirira mwanayo ndani? Ndiponso funso lofunika kwambiri nlakuti, Kodi lingaliro la Mulungu nlotani ponena za kukhala mayi woberekera?

Kodi Kukhala Mayi Woberekera Kumalemekeza Ukwati?

Mawu a Mulungu amatiuza kuti iye amawona ukwati kukhala chinthu chopatulika. Mwachitsanzo, Ahebri 13:4 imafotokoza kuti: ‘Ukwati uchititdwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.’a Mulungu amayembekezera Akristu onse kuwona ukwati kukhala wolemekezeka ndi kuusunga motero. Kodi chimene chimadetsa ukwati nchiyani? Dama, limene limaluluza ukwati usanachitike, ndi chigololo, chimene chimaluluza ukwati pambuyo poti wachitika.

Kodi kukhala mayi woberekera kumalemekeza ukwati ndi kusunga pogona kukhala posadetsedwa? Yankho lapafupi ndilo, ayi. Kuberekera kwamwambo kumafuna kuti mkazi atenge mimba mwa kuikidwa ubwamuna woperekedwa ndi wina mwa njira ina yosakhala yakugonana. Lingaliro la Baibulo lingapezeke pa Levitiko 18:20, (NW), pamene pamati: “Suyenera kupatsa ubwamuna wako kwa mkazi wa mnzako kuti adetsedwe nawo.” Palibe maziko Abaibulo osiyanitsira kuika ubwamuna mumkazi mwa kugonana ndi kuika ubwamuna mumkazi osati mwa kugonana koma mwa kungoutenga kwa mwamuna woupereka. Chotero, m’zochitika ziŵirizi, dama kapena chigololo chimachitika pamene ubwamuna umaikidwa mwa mkazi ndi mwamuna wina amene saali mwamuna wake walamulo.

Bwanji za kuberekera mwa kungonyamulira mluza? Kumenekonso kumadetsa pogona. Zowona, dzira lamoyo limakhalapo mwa kugwirizanitsidwa kwa ubwamuna wa mwamuna ndi dzira la mkazi wake, koma pambuyo pake limaikidwa m’chibaliro cha mkazi wina ndipo, kunena zowona, limamchititsa kukhala ndi mimba. Mimba imeneyi simachititsidwa ndi kugonana kwa mkazi woberekera ndi mwamuna wakewake. Chotero, ziŵalo zake zobalira tsopano zimakhala zikugwiritsiridwa ntchito ndi munthu wina wosakhala mwamuna wake. Zimenezi zimawombana ndi malamulo a chikhalidwe chabwino akuti mkazi ayenera kuberekera mwana mwamuna wakewake. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 23:2.) Kuli kosayenera kwa mwamuna amene saali mwamuna wake wa mkazi woberekera kugwiritsira ntchito ziŵalo zake zobalira. Kumeneku ndiko kugwiritsira ntchito mosayenera pogona. Chotero, kukhala mayi woberekera sikuli kwa Akristu.

[Mawu a M’munsi]

a Bukhu lamaumboni lakuti New Testament Word Studies limasonyeza kuti liwulo “pogona” pa Ahebri 13:4 limatanthauza kuti simkhalidwe wa ukwati wokha umene suyenera kudetsedwa komanso ntchito yake.

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

Chithunzithunzi ndi Mary Cassatt, The Metropolitan Museum of Art, Mphatso ya Mrs. Ralph J. Hines, 1960. (60.181)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena