Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 1/15 tsamba 15-20
  • Abusa ndi Nkhosa M’teokrase

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Abusa ndi Nkhosa M’teokrase
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndim’njira Zotani Zimene Ife Tiliri Ateokratiki Lerolino?
  • Teokrase Wamakono
  • Akulu m’Teokrase
  • Kutumikira ndi Mzimu Wachikristu
  • Nkhosa m’Teokrase
  • Abusa ndi Nkhosa Amagwira Ntchito Pamodzi
  • Umboni wa Chikhulupiriro
  • Khalanibe m’Teokrase
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Yehova Alamulira—Kupyolera mwa Teokrase
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Mpingo wa Chikhristu Umayendetsedwa bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • “Pitirizani Kusunga Amuna Oterowo Okondedwa”
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 1/15 tsamba 15-20

Abusa ndi Nkhosa M’teokrase

“Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; iye adzatipulumutsa.”​—YESAYA 33:22.

1. Kodi kunganenedwe motani kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba ndi Akristu lerolino ali teokrase?

TEOKRASE amatanthauza ulamuliro wochitidwa ndi Mulungu. Amaphatikizapo kuvomereza ulamuliro wa Yehova ndi kutsatira zitsogozo zake ndi malangizo m’zosankha zazikulu ndi zazing’ono zimene timapanga m’moyo. Mpingo wa m’zaka za zana loyamba unali teokrase weniweni. Panthaŵiyo Akristu akanatha kunena mowona mtima kuti: “Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu.” (Yesaya 33:22) Pokhala ndi otsalira odzozedwa monga phata lake, gulu la Yehova Mulungu lerolino mofananamo lili teokrase weniweni.

Kodi Ndim’njira Zotani Zimene Ife Tiliri Ateokratiki Lerolino?

2. Kodi ndiiti imene ili njira ina imene Mboni za Yehova zimagonjera ulamuliro wa Yehova?

2 Kodi tinganene motani kuti gulu la Yehova la padziko lapansi lili teokrase? Chifukwa chakuti awo amene alimo amagonjeradi ulamuliro wa Yehova. Ndipo amatsatira utsogoleri wa Yesu Kristu, uyo amene Yehova wamkhazika pampando wachifumu monga Mfumu. Mwachitsanzo, m’nthaŵi ya mapeto, lamulo lachindunji ili lochokera kwa Teokrati Wamkulu, likuperekedwa kwa Yesu: “Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthaŵi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.” (Chivumbulutso 14:15) Yesu amamvera ndipo amayang’anira ntchito ya kututa ya dziko lapansi. Akristu amachirikiza Mfumu yawo m’ntchito yaikulu imeneyi mwa kulalikira mwachangu mbiri yabwino ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19; Marko 13:10; Machitidwe 1:8) Mwa kuchita motero, iwo alinso antchito anzake a Yehova, Teokrati Wamkulu.​—1 Akorinto 3:9.

3. Kodi ndimotani mmene Akristu amagonjera teokrase m’nkhani za makhalidwe?

3 Namonso m’mayendedwe, Akristu amagonjera ulamuliro wa Mulungu. Yesu anati: “Wochita chowonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.” (Yohane 3:21) Lerolino, pali mikangano yosatha yonena za miyezo ya makhalidwe, koma mikangano imeneyi iribe malo pakati pa Akristu. Zimene Yehova amati nzoipa iwo amaziona kukhala zoipa, ndipo amazipeŵa monga mliri! Iwo amasamaliranso mabanja awo, kumvera makolo awo, ndi kukhalabe ogonjera maulamuliro aakulu. (Aefeso 5:3-5 22-33; 6:1-4; 1 Timoteo 5:8; Tito 3:1) Motero, iwo amachita mwateokratiki, mogwirizana ndi Mulungu.

4. Kodi ndimkhalidwe wa maganizo wolakwa wotani umene unasonyezedwa ndi Adamu ndi Hava ndi Sauli, ndipo kodi ndimotani mmene Akristu amasonyezera mkhalidwe wosiyana nawo?

4 Adamu ndi Hava anatayikiridwa ndi Paradaiso chifukwa chakuti anafuna kudzipangira zosankha zawo ponena za chimene chinali chabwino ndi chimene chinali choipa. Yesu anafuna kuchita zosiyana kwambiri ndi zimenezo. Iye anati: “Sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.” Akristu amafunafuna kuchita zofananazo. (Yohane 5:30; Luka 22:42; Aroma 12:2; Ahebri 10:7) Sauli, mfumu yoyamba ya Israyeli, anamvera Yehova​—koma mwapang’ono chabe. Iye anakanidwa chifukwa cha zimenezi. Samueli anamuuza kuti: “Kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.” (1 Samueli 15:22) Kodi nkwateokratiki kutsata chifuniro cha Yehova kufikira kumlingo wakutiwakuti, mwinamwake mwa kukhala wokhazikika m’ntchito ya kulalikira kapena kufika pamsonkhano, ndiyeno nkulolera molakwa m’nkhani za makhalidwe kapena mwanjira ina? Kutalitali! Timayesayesa ‘kuchita chifuniro cha Mulungu ndi mtima wonse.’ (Aefeso 6:6; 1 Petro 4:1, 2) Mosiyana ndi Sauli, timagonjera kotheratu ulamuliro wa Mulungu.

Teokrase Wamakono

5, 6. Kodi ndimotani mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu lerolino, ndipo kodi kugwirizana ndi makonzedwe ameneŵa kumachititsa chiyani?

5 Kalelo, Yehova analamulira ndi kuvumbula chowonadi kupyolera mwa anthu, onga ngati aneneri, mafumu, ndi atumwi. Lerolino, zimenezo sizili choncho; palibe aneneri ouziridwa kapena atumwi. Mmalomwake, Yesu anati mkati mwa kukhalapo kwake kwachifumu, akadziŵikitsa kagulu kokhulupirika ka otsatira, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo akakakhazika kuyang’anira chuma chake chonse. (Mateyu 24:45-47; Yesaya 43:10) Mu 1919 kapolo ameneyo anadziŵidwa kukhala otsalira a Akristu odzozedwa. Chiyambire pamenepo, moimiridwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, kaguluko kakhala phata la teokrase padziko lapansi. Kuzungulira dziko lonse, Bungwe Lolamulira limaimiridwa ndi Makomiti a Nthambi, oyang’anira oyendayenda, ndi akulu ampingo.

6 Kugwirizana ndi gulu lateokratiki kuli mbali yofunika ya kugonjera teokrase. Kugwirizanika kotero kumachititsa umodzi ndi dongosolo padziko lonse mu “gulu lonse la abale.” (1 Petro 2:17, NW) Ndiponso, zimenezi zimakondweretsa Yehova, amene “sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.”​—1 Akorinto 14:33.

Akulu m’Teokrase

7. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti akulu Achikristu amasankhidwa mwateokratiki?

7 Akulu onse oikidwa, m’malo awo alionse a ulamuliro, amakwaniritsa ziyeneretso zondandalikidwa m’Baibulo za udindo wa woyang’anira, kapena mkulu. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) Ndiponso, mawu a Paulo kwa akulu a ku Efeso amagwira ntchito kwa akulu onse akuti: ‘[Dzipenyerereni ndi gulu lonse lankhosa, NW], pamenepo mzimu woyera unakuikani oyang’anira, kuti muŵete [mpingo, NW] wa Mulungu.’ (Machitidwe 20:28) Inde, akulu amaikidwa ndi mzimu woyera, umene umachokera kwa Yehova Mulungu. (Yohane 14:26) Kuikidwa kwawo nkwateokratiki. Ndiponso, amaŵeta gulu lankhosa la Mulungu. Gulu lankhosalo lili la Yehova, osati la akulu. Ilo lili teokrase.

8. Kodi ndiati amene ali mathayo ozoloŵereka a akulu lerolino?

8 M’kalata yake ya kwa Aefeso, mtumwi Paulo anandandalika mathayo ozoloŵereka a akulu, akumati: “Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki kumangirira thupi la Kristu.” (Aefeso 4:11, 12) Atumwi ndi aneneri anazimiririka pambuyo pa ukhanda wa “thupi la Kristu.” (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:8.) Koma akulu adakali otanganitsidwa kwambiri kulalikira, kuweta, ndi kuphunzitsa.​—2 Timoteo 4:2; Tito 1:9.

9. Kodi akulu ayenera kudzikonzekeretsa motani kukhala oimira chifuniro cha Mulungu mumpingo?

9 Popeza kuti teokrase ndiwo ulamuliro wochitidwa ndi Mulungu, akulu ogwira mtima ali ozoloŵera kwambiri chifuniro cha Mulungu. Yoswa analamulidwa kuŵerenga Chilamulo tsiku ndi tsiku. Akulu nawonso afunikira kuphunzira ndi kufufuza m’Malemba nthaŵi zonse ndi kukhala ozoloŵera kwambiri mabuku a Baibulo ofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (2 Timoteo 3:14, 15) Zimenezi zimaphatikizapo magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi zofalitsidwa zina zimene zimasonyeza mmene malamulo a mkhalidwe a Baibulo amagwirira ntchito pamikhalidwe yakutiyakuti.a Komabe, pamene kuli kwakuti nkofunika kwa mkulu kudziŵa ndi kutsatira zitsogozo zofalitsidwa m’mabuku a Watch Tower Society, iye ayenera kukhalanso wozoloŵera kwambiri malamulo a mkhalidwe a Malemba amene ali maziko ake. Pamenepo adzakhala wokhoza kugwiritsira ntchito zitsogozo za Malemba mozindikira bwino ndi mwachifundo.​—Yerekezerani ndi Mika 6:8.

Kutumikira ndi Mzimu Wachikristu

10. Kodi ndimkhalidwe wamaganizo woipa wotani umene akulu ayenera kupeŵa, ndipo motani?

10 Pafupifupi chaka cha 55 C.E., mtumwi Paulo analemba kalata yake yoyamba kumpingo wa mu Korinto. Limodzi la mavuto amene anasamalira linali lokhudza amuna ena amene anafuna kukhala otchuka mumpingo. Paulo analemba kuti: “Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.” (1 Akorinto 4:8) M’zaka za zana loyamba C.E., Akristu onse anali ndi chiyembekezo cha kulamulira ndi Yesu monga mafumu ndi ansembe kumwamba. (Chivumbulutso 20:4, 6) Komabe, mwachionekere, ena ku Korinto anaiŵala kuti padziko lapansi mulibe mafumu mu teokrase Wachikristu. Mmalo mwa kuchita monga mafumu a dzikoli, abusa Achikristu amakulitsa kudzichepetsa, mkhalidwe umene umakondweretsa Yehova.​—Salmo 138:6; Luka 22:25-27.

11. (a) Kodi nziti zimene zili zitsanzo zina zapadera za kudzichepetsa? (b) Kodi akulu ndi Akristu ena onse ayenera kudziona motani?

11 Kodi kudzichepetsa ndikufooka? Kutalitali! Yehova mwiniyo akufotokozedwa kukhala wodzichepetsa. (Salmo 18:35, NW) Mafumu a Israyeli anatsogolera magulu ankhondo m’nkhondo ndi kulamulira mtunduwo pansi pa Yehova. Komabe, aliyense anafunikira kukhala wosamala ‘kuti mtima wake sunadzikuze pa abale ake.’ (Deuteronomo 17:20) Yesu woukitsidwa ndiye Mfumu yakumwamba. Komabe, pamene anali padziko lapansi, anasambitsa mapazi a ophunzira ake. Nkudzichepetsa kotani nanga! Ndipo posonyeza kuti anafuna kuti atumwi ake akhalenso odzichepetsa mofananamo, iye anati: “Ngati ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake.” (Yohane 13:14; Afilipi 2:5-8) Ulemerero wonse ndi chitamando ziyenera kumka kwa Yehova, osati kwa munthu wina aliyense. (Chivumbulutso 4:11) Kaya akhale akulu kapena ayi, Akristu onse ayenera kudziona mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.” (Luka 17:10) Lingaliro lina lililonse losiyana nalo siliri lateokratiki.

12. Kodi nchifukwa ninji chikondi chili mkhalidwe wofunika kwambiri kukulitsidwa ndi akulu Achikristu?

12 Pamodzi ndi kudzichepetsa, akulu Achikristu amakulitsa chikondi. Mtumwi Yohane anasonyeza kufunika kwa chikondi pamene anati: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Anthu opanda chikondi sali ateokratiki. Sadziŵa Yehova. Ponena za Mwana wa Mulungu, Baibulo limati: “Yesu, . . . anakonda ake a iye yekha a m’dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.” (Yohane 13:1) Polankhula ndi amuna 11 amene akakhala mbali ya bungwe lolamulira mumpingo Wachikristu, Yesu anati: “Lamulo langa ndiili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.” (Yohane 15:12) Chikondi ndicho chizindikiro chodziŵikitsa Chikristu chowona. Chimakopa osweka mtima, olira, ndi ogwidwa ukapolo mwauzimu amene amalakalaka ufulu. (Yesaya 61:1, 2; Yohane 13:35) Akulu ayenera kukhala opereka chitsanzo chabwino m’kuchisonyeza.

13. Ngakhale kuti lerolino mavuto angakhale aakulu kwambiri, kodi ndimotani mmene mkulu angakhalire wachiyambukiro chabwino m’mikhalidwe yonse?

13 Lerolino, akulu amapemphedwa kaŵirikaŵiri kuthandiza kusamalira mavuto ovuta kwambiri. Zovuta za muukwati zingakhale zozika mizu kwambiri ndi zosatha. Achichepere ali ndi mavuto amene anthu achikulire angaone kukhala ovuta kuwazindikira. Matenda a kupsinjika maganizo kaŵirikaŵiri ngovuta kuwazindikira. Mkulu amene wayang’anizana ndi zinthu zotero angakhale wosadziŵa kwambiri zochita. Koma angakhale ndi chidaliro chakuti ngati mwapemphero adalira panzeru ya Yehova, ngati afufuza m’Baibulo ndi m’chidziŵitso chofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, ndipo ngati achita modzichepetsa ndi mwachikondi ndi nkhosa, adzakhala chiyambukiro chabwino ngakhale m’mkhalidwe wovuta kopambana.

14, 15. Kodi ndimawu ena otani amene akusonyeza kuti Yehova wadalitsa anthu ake ndi akulu ambiri abwino kwambiri?

14 Yehova wadalitsa mokulira gulu lake ndi “mphatso mwa amuna.” (Aefeso 4:8, NW) Panthaŵi ndi nthaŵi, Watch Tower Society imalandira makalata othutsa mtima opereka umboni wa chikondi chimene chimasonyezedwa ndi akulu odzichepetsa amene mwachifundo amaŵeta nkhosa za Mulungu. Mwachitsanzo, mkulu wina mumpingo akulemba kuti: “Sindingakumbukire kucheza kwa woyang’anira dera kumene kunandiyambukira koposerapo kapena kumene kudakasimbidwabe mumpingo. Woyang’anira derayo anandithandiza kuona kufunika kwa mkhalidwe wamaganizo wotsimikiza pochita ndi abale, limodzi ndi chigogomezero pakuyamikira.”

15 Mlongo wina amene anafunikira kuyenda ulendo kumka kuchipatala chakutali kukalandira mankhwala akulemba kuti: “Nkolimbikitsa chotani nanga kukhoza kuonana ndi mkulu usiku woyamba wodetsa nkhaŵa umenewo m’chipatala cha kutali kwambiri ndi kwathu! Iyeyo ndi abale ena anatha nthaŵi yambiri ali nane. Ngakhale anthu adziko amene anadziŵa zimene ndinakumana nazo analingalira kuti sindikanachira popanda chitonthozo, chisamaliro, ndi mapemphero za abale achikondi ndi odzipereka amenewo.” Mlongo wina akulemba kuti: “Ndili ndi moyo lerolino chifukwa chakuti bungwe la akulu moleza mtima linandithandiza m’nkhondo yanga yolimbana ndi kupsinjika maganizo kwakukulu. . . . Mbale wina ndi mkazi wake sanadziŵe chonena kwa ine. . . . Koma chimene chinandikhudza mtima kwambiri chinali chakuti ngakhale kuti iwo sanazindikire mokwanira zimene zinali kundichitikira, anandisamalira mwachikondi.”

16. Kodi ndichisonkhezero chotani chimene Petro akupereka kwa akulu?

16 Inde, akulu ambiri akugwiritsira ntchito chisonkhezero cha mtumwi Petro chakuti: “Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:1-3) Akulu ateokratiki otero ali dalitso lotani nanga!

Nkhosa m’Teokrase

17. Tchulani mikhalidwe ina imene ziŵalo zonse mumpingo ziyenera kukulitsa.

17 Komabe, teokrase samapangidwa ndi akulu okha. Ngati abusa ayenera kukhala ateokratiki, nkhosa nazonso ziyenera kukhala zotero. M’njira zotani? Eya, malamulo a mkhalidwe amodzimodziwo amene amatsogolera abusa ayenera kutsogolera nkhosa. Akristu onse, osati akulu okha, ayenera kukhala odzichepetsa ngati ati alandire dalitso la Yehova. (Yakobo 4:6) Onse ayenera kukulitsa chikondi chifukwa chakuti pochisowa nsembe zathu kwa Yehova nzosamkondweretsa. (1 Akorinto 13:1-3) Ndipo tonsefe, osati akulu okha, tiyenera ‘kudzazidwa ndi chizindikiritso cha chifuniro cha [Yehova] munzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu.’​—Akolose 1:9.

18. (a) Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso chochepa cha chowonadi sichili chokwanira? (b) Kodi ndimotani mmene tonsefe tingadzazidwire ndi chidziŵitso cholongosoka?

18 Achichepere ndi achikulire omwe amayang’anizana mosalekeza ndi zosankha zovuta pamene akuyesayesa kukhalabe okhulupirika mosasamala kanthu kuti akukhala m’dziko la Satana. Zizolowezi za dziko m’zovala, nyimbo, akanema, ndi mabuku zimayesa mkhalidwe wauzimu wa ena. Chidziŵitso chochepa cha chowonadi sichiri chokwanira kutithandiza kusunga uchikatikati wathu. Kuti titsimikizire za kukhalabe okhulupirika, tifunikira kudzazidwa ndi chidziŵitso cholongosoka. Tifunikira luntha ndi nzeru zimene Mawu a Mulungu okha angatipatse. (Miyambo 2:1-5) Zimenezi zikutanthauza kukulitsa zizoloŵezi zabwino za phunziro, kusinkhasinkha pazimene tikuphunzira, ndi kuzigwiritsira ntchito. (Salmo 1:1-3; Chivumbulutso 1:3) Paulo anali kulembera Akristu onse, osati akulu okha, pamene anati: “Chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”​—Ahebri 5:14.

Abusa ndi Nkhosa Amagwira Ntchito Pamodzi

19, 20. Kodi ndimalangizo otani amene akuperekedwa kwa onse kuti agwirizane ndi akulu, ndipo chifukwa ninji?

19 Potsirizira pake, kuyenera kunenedwa kuti mzimu wowona wateokratiki umasonyezedwa ndi awo amene amagwirizana ndi akulu. Paulo analembera Timoteo kuti: “Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu woŵirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.” (1 Timoteo 5:17; 1 Petro 5:5, 6) Ukulu ndimwaŵi wabwino kwambiri, koma akulu ochuluka ali a mabanja amene amagwira ntchito yakudziko tsiku lililonse ndi amene ali ndi akazi ndi ana oti awasamalire. Pamene kuli kwakuti ngachimwemwe kutumikira, utumiki wawo umafeŵerapo ndi kukhala wofupa kwambiri pamene mpingo uli wochirikiza, wosasuliza kwambiri ndi kufunsira zambiri.​—Ahebri 13:17.

20 Mtumwi Paulo anati: “Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” (Ahebri 13:7) Ayi, Paulo sanalimbikitse abale kutsatira akulu. (1 Akorinto 1:12) Kutsatira munthu sikuli kwateokratiki. Koma ndithudi nkwanzeru kutsanzira chikhulupiriro chotsimikiziridwa cha mkulu wateokratiki amene ali wokangalika m’ntchito yaulaliki, amene amafika nthaŵi zonse pamisonkhano, ndi amene amachita modzichepetsa ndi mwachikondi ndi mpingo.

Umboni wa Chikhulupiriro

21. Kodi ndimotani mmene Akristu amasonyezera chikhulupiriro cholimba chofanana ndi cha Mose?

21 Ndithudi, kukhalapo kwa gulu lateokratiki m’nthaŵi ino ya kunyonyosoka kowopsa kwa makhalidwe m’mbiri ya anthu kuli umboni wosonyeza mphamvu ya Teokrati Wamkulu. (Yesaya 2:2-5) Kulinso umboni wa chikhulupiriro cha pafupifupi mamiliyoni asanu a amuna, akazi ndi ana Achikristu, amene amalimbana ndi mavuto a moyo watsiku ndi tsiku koma amene samaiŵala konse kuti Yehova ndiye Wolamulira wawo. Monga momwe Mose wokhulupirika “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo,” chotero lerolino Akristu ali ndi chikhulupiriro cholimba chofananacho. (Ahebri 11:27) Iwo ali ndi mwaŵi wa kukhala mu teokrase, ndipo tsiku ndi tsiku amayamikira Yehova chifukwa cha zimenezo. (Salmo 100:4, 5) Pamene akuona mphamvu yopulumutsa ya Yehova, amakondwera kulengeza kuti: “Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; iye adzatipulumutsa.”​—Yesaya 33:22.

[Mawu a M’munsi]

a Pakati pa zofalitsidwa zimenezo pali buku lakuti “Dzipenyerereni ndi Gulu Lonse la Nkhosa,” limene lili ndi zitsogozo za Malemba ndipo limaperekedwa kwa oyang’anira mpingo oikidwa, kapena akulu.

Kodi Baibulo Limasonyezanji?

◻ Kodi Akristu amagonjera teokrase m’njira yotani?

◻ Kodi teokrase ngwolinganizidwa motani lerolino?

◻ Kodi ndim’njira zotani zimene akulu ayenera kukonzekera iwo eni kukwaniritsa mathayo awo?

◻ Kodi ndimikhalidwe Yachikristu yotani yofunika kwa akulu kuikulitsa ndi kuisonyeza?

◻ M’teokrase, kodi ndiunansi wotani umene uyenera kukhala pakati pa nkhosa ndi abusa?

[Chithunzi patsamba 16]

Adamu ndi Hava anatayikiridwa ndi Paradaiso chifukwa chakuti anafuna kudzipangira zosankha zawo ponena za chabwino ndi choipa

[Chithunzi patsamba 18]

Ngati mkulu achita modzichepetsa ndi mwachikondi ndi nkhosa, iye nthaŵi zonse adzakhala wa chiyambukiro chabwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena