Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi wophunzira Yakobo anatanthauzanji pamene anati: “Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziŵa kuti tidzalangika koposa”?—Yakobo 3:1.
Ndithudi Yakobo sanali kuletsa Akristu kuphunzitsa ena choonadi. Pa Mateyu 28:19, 20, Yesu analamulira ophunzira ake ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’ Chotero, Akristu onse ayenera kukhala aphunzitsi. Mtumwi Paulo anapatsa uphungu Akristu Achihebri chifukwa chakuti anali asanakhale aphunzitsi. Analemba kuti: “Mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusoŵanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu.”—Ahebri 5:12.
Nangano, nchiyani chimene Yakobo anali kulankhula? Anali kunena za aja okhala ndi mathayo apadera akuphunzitsa mumpingo. Pa Aefeso 4:11, timaŵerenga kuti: “Iye [Yesu Kristu, Mutu wa mpingo] anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi.” M’mipingo ya m’zaka za zana loyamba munali mathayo apadera a kuphunzitsa monga momwe zilili lerolino. Mwachitsanzo, Bungwe Lolamulira limaimira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndipo lili ndi thayo la kuyang’anira chiphunzitso cha mpingo wa padziko lonse. (Mateyu 24:45) Oyang’anira oyendayenda ndi akulu a m’mipingo alinso ndi mathayo apadera a kuphunzitsa.
Kodi Yakobo anali kuuza amuna Achikristu okhoza kuti sayenera kuvomera thayo la uphunzitsi powopa kulangika koposa kwa Mulungu? Kutalitali. Ntchito ya mkulu ili mwaŵi waukulu, monga momwe kwasonyezedwera ndi 1 Timoteo 3:1, amene amati: “Ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira, aifuna ntchito yabwino.” Chimodzi cha zofunika za kuikidwa kukhala mkulu wa mumpingo nchakuti mwamuna akhale “wokhoza kuphunzitsa.” (1 Timoteo 3:2) Yakobo sanatsutse mawu ouziridwa a Paulo.
Komabe, zichita ngati kuti m’zaka za zana loyamba C.E., ena anali kudzisankha kukhala aphunzitsi, ngakhale kuti sanayenerere ndipo sanaikidwe pamalowo. Mwachionekere, analingalira kuti malowo anali okwezeka, ndipo anafuna kulemekezedwa. (Yerekezerani ndi Marko 12:38-40; 1 Timoteo 5:17.) Mtumwi Yohane anatchula za Diotrefe, amene ‘anafuna kukhala wamkulu wa iwo, koma amene sanalandira kwa Yohane chilichonse mwaulemu.’ (3 Yohane 9) Timoteo Woyamba 1:7 amalankhula za anthu ena amene ‘anafuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale kuti sanadziŵitse zimene ananena kapena analimbikira.’ Mawu a Yakobo 3:1 makamaka ngoyenerera amuna amene amafuna kukhala aphunzitsi komano amene ali ndi cholinga choipa. Otereŵa akhoza kuvulaza kwambiri gulu ndipo angadzalangike koposa.—Aroma 2:17-21; 14:12.
Yakobo 3:1 alinso chikumbutso chabwino kwa awo amene amayenerera ndi amene amatumikira monga aphunzitsi. Popeza aikiziridwa zambiri, zambirinso zidzafunidwa kwa iwo. (Luka 12:48) Yesu anati: “Mawu onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawaŵerengera mlandu wake Tsiku la Kuweruza.” (Mateyu 12:36) Makamaka zimenezi zili choncho ndi aja amene amalankhula mawu osonkhezera, akulu oikidwa.
Akulu adzadziŵerengera mlandu wa mmene anachitira ndi nkhosa za Yehova. (Ahebri 13:17) Zimene amanena zimasonkhezera miyoyo. Nchifukwa chake, mkulu ayenera kusamala kuti asachirikize malingaliro ake a iyemwini kapena kuchitira nkhanza nkhosa monga momwe Afarisi anachitira. Ayenera kuyesetsa kusonyeza chikondi chofanana ndi chimene Yesu anali nacho. Paliponse pamene aphunzitsa, ndipo makamaka pamene aphatikizidwa m’nkhani zachiweruzo, mkulu ayenera kusamala mawu ake, osalankhula mawu osyasyalika kapena kunena malingaliro ake. Mwa kudalira kwambiri pa Yehova, Mawu ake, ndi zitsogozo zake kupyolera m’gulu lake, mbusayo adzalandira madalitso ochuluka a Mulungu, osati ‘kulangika koposa.’