Kodi Tsogolo la Dziko Lathu Lapansi Nlotani?
“Kulibe zaka za zana lililonse zimene zikufanana ndi za zana la 20 pankhani ya chiwawa cha m’maiko, chiŵerengero cha nkhondo zimene zamenyedwa, unyinji wa othaŵa kwawo chifukwa cha nkhondozo, mamiliyoni a anthu amene aphedwa m’nkhondo, ndi ndalama zosaneneka zimene zawonongedwera pa ‘chitetezo,’” ikutero World Military and Social Expenditures 1996. Kodi zinthu zimenezi zidzasintha?
Mtumwi Petro anakumbutsa Akristu za lonjezo limene Mulungu analonjeza zaka mazana ambiri kumbuyoko: “Monga mwa lonjezano [la Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Mawu amenewo anatchulidwa koyamba mu ulosi wa Yesaya. (Yesaya 65:17; 66:22) Israyeli wakale anaona kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwo pamene mtunduwo unabwerera kudziko lake lolonjezedwa atakhala mu ukapolo ku Babulo zaka 70. Mwa kubwereza lonjezo la “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano,” Petro anasonyeza kuti ulosiwo udzakwaniritsidwabe pamlingo waukulu—padziko lonse!
Chifuniro cha Mulungu nchakuti akhazikitse mikhalidwe yachilungamo padziko lonse lapansi, ndipo chifunirocho chidzakwaniritsidwa ndi Ufumu wakumwamba wokhala ndi Kristu monga Mfumu. “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Mtendere waukulu koposa umenewu ndi chisungiko padziko lapansi nzimene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti aziziyembekezera ndi kuzipempherera m’pemphero limene limatchedwa kuti Atate Wathu Wakumwamba, kapena kuti Pemphero la Ambuye, kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.
Kodi mungasangalale kukhala m’dziko lolungama monga kumwamba? Chimenecho ndicho chiyembekezo chimene Baibulo limapereka kwa aliyense amene akufunitsitsa ndi mtima wonse kuti adziŵe Mulungu ndi kutsatira njira zake zolungama.