Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Enoke Anayenda ndi Mulungu M’dziko la Anthu Osapembedza
    Nsanja ya Olonda—2001 | September 15
    • Ulosi wa Kuwonongedwa kwa Osapembedza

      Tikakhala pakati pa anthu osapembedza, kusungabe miyezo yapamwamba yamakhalidwe abwino kumavuta kwabasi. Koma Enoke analengezanso uthenga wotsimikizika wa kuŵeruzidwa kwa oipa. Motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, Enoke analosera kuti: “Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pantchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.”​—Yuda 14, 15.

      Kodi uthenga umenewo unakhudza motani anthu osakhulupirira okakamira zoipawo? Si kulakwitsa kuganiza kuti anthu anadana naye Enoke chifukwa cha mawu ochititsa nthumanzi amenewo. Mwinamwake ankamulalatira, kumunyodola ndi kumuopseza. Mwina ena ankafuna kungomupheratu. Komabe, Enoke sanachite mantha. Ankadziŵa zomwe zinachitikira Abele wolungama uja, ndipo mofanana naye, Enoke nayenso anatsimikiza mtima kutumikira Mulungu zivute zitani.

  • Enoke Anayenda ndi Mulungu M’dziko la Anthu Osapembedza
    Nsanja ya Olonda—2001 | September 15
    • [Bokosi patsamba 30]

      Kodi Baibulo Linagwira Mawu Buku la Enoke?

      Buku la Enoke ndi buku lomwe silipezeka pa mndandanda wa mabuku ovomerezeka a m’Baibulo ndipo wolemba wake sadziŵika. Amanena kuti analemba ndi Enoke koma si zoona. Buku limeneli, limene mwina analilemba nthaŵi ina yake m’zaka za zana lachiŵiri ndi loyamba B.C.E., lili ndi nthano za Ayuda zokokomeza, zosamveka ndiponso zosagwirizana ndi mbiri. Mwachionekere, anali kuyesa kufotokoza mwatsatanetsatane nkhani yaifupi ya m’buku la Genesis yonena za Enoke. Umenewu ndi umboni wokwanira wakuti anthu okonda Mawu amene Mulungu anauzira ayenera kupeŵa bukuli.

      M’Baibulo, buku la Yuda lokha ndi limene lili ndi mawu aulosi a Enoke. Mawuwo amati: “Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pantchito zawo zonse zosapembedza, zimene anazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza analankhula pa Iye.” (Yuda 14, 15) Akatswiri ambiri amanena kuti ulosi wa Enoke wotsutsa anthu osapembedza a m’nthaŵi yake, anaugwira mawu mwachindunji m’Buku la Enoke. Kodi n’zotheka kuti Yuda anagwiritsa ntchito buku losadalirika lopanda umboni monga gwero lake?

      Malemba sakunena mmene Yuda anadziŵira za ulosi wa Enoke. Mwina anangogwira mawu nkhani yodziwika, mbiri yodalirika yakale. Paulo ayenera kuti anachitanso chimodzimodzi pamene anatchula Yane ndi Yambre monga a matsenga a m’nyumba ya Farao omwe sanali kudziŵika mayina awo amene anatsutsana ndi Mose. Ngati wolemba Buku la Enoke anapeza magwero akale a mtundu umenewu, tingakanirenji kuti nayenso Yuda anapeza magwero oterowo?a​—Eksodo 7:11, 22; 2 Timoteo 3:8.

      Nkhani yakuti Yuda anadziŵa motani za uthenga wa Enoke kwa anthu osapembedza ndi yaing’ono. Kudalirika kwake kwagona pa mfundo yakuti Yuda analemba mouziridwa ndi Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Mzimu woyera wa Mulungu unam’teteza kuti asalembe zabodza.

      [Mawu a M’munsi]

      a Wophunzira Stefano anafotokozanso mfundo zina zimene sizikupezeka paliponse m’Malemba Achihebri. Anafotokoza za kuphunzira kwa Mose nzeru zonse za Aigupto, zoti anali ndi zaka 40 pothaŵa ku Igupto, zoti anakhala ku Midyani kwa zaka 40, ndiponso zoti angelo anatenga nawo mbali popereka Chilamulo cha Mose.​—Machitidwe 7:22, 23, 30, 38.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena