‘Chotsani Okana Mulungu!’
UNYINJI wa anthu unamulingalira iye kukhala wokana Mulungu, munthu amene ankafunafuna kudodometsa kulambira ndi kuwononga milungu yawo. Atanyazitsidwa ndi kuchepsyedwa, iye anabweretsedwa kwa iwo pa bwalo losonkhanira. Pamene bwanamkubwa anafunsa, mwamuna wodzinzana wa msinkhu wa zaka 86 zakubadwa anabwera kutsogolo ndi kudzilongosola. Dzina lake anali Polycarp.
Bwanamkubwa Wachiroma wa chigawocho Statius Quadratus anapitiriza ndi mawu akuti: “Lumbira m’dzina la Kaisara; sintha maganizo ako ndi kunena kuti, ‘Chotsani osakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu!’” Kenaka Polycarp anayang’ana ku khamu lalikulu la akunja osaweruzika odzaza bwalo lamaseŵeralo. Akumaloza kwa iwo, anabuula, kuyang’ana kumwamba, ndi kunena kuti: “Chotsani osakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu!” Ndithudi, ‘Chotsani okana Mulungu!’
Kenaka wolemekezekayo analankhula ndi chifulumizo, akumati: “Lumbira ndipo ndidzakumasula; tonza Kristu.” Komatu Polycarp anayankha kuti: “Kwa zaka makumi asanu ndi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi ndakhala ndikutumikira Iye, ndipo Iye sanandilakwire. Kodi ndingatonze bwanji Mfumu yomwe yanditumikira?”
Pamenepo makonzedwe anapangidwa akupha munthu wachikulireyo. Mnofu wake unafunikira kuwotchedwa pamoto. Chifukwa ninji? Kodi Polycarp anali yani? Ndipo kodi ndi zochitika zotani zimene zinatsogolera ku imfa yake?
Moyo Woyambirira wa Polycarp
Polycarp anabadwa chifupifupi mu 69 C.E. mu Asia Minor, pa Smurna (mzinda wa Turkey wamakono wa Izmir). Zikusimbidwa kuti iye analeredwa ndi makolo Achikristu. Atakula kukhala mwamuna wotchuka ndithu, Polycarp anali wodziŵika chifukwa cha kuoloŵa manja, kudzikana, kuchitira ena mwachifundo, ndi kuphunzira Malemba mwakhama. M’kupita kwa nthaŵi anakhala woyang’anira mu mpingo wa Smurna.
Zasimbidwa kuti m’zaka zake zoyambirira, Polycarp anatenga mwaŵi wa kuphunzira mwachindunji kuchokera kwa atumwi ena. Mwachiwonekere mtumwi Yohane anali m’modzi wa aphunzitsi ake. M’chenicheni, Irenaeus akusimba kuti Polycarp “sanalangizidwe kokha ndi atumwi, ndi kuyanjana ndi ambiri amene anawona Kristu, komanso anaikidwa kaamba ka Asia ndi atumwi, m’tchalitchi chimene chiri mu Smurna monga woyang’anira.” Tingangolingalira chisangalalo ndi chikhutiro chimene Polycarp anakhala nacho kuchokera ku kuyanjana kolemeretsa koteroko. Chingakhale chinamthandiza kumkonzekeretsa kaamba ka ntchito yake monga woyang’anira mu mpingo.—Machitidwe 20:28; 1 Petro 5:1-4.
Achirikiza Chowonadi Chenicheni
Kuyang’anira mpingo kwa Polycarp kunayamba m’zaka zopatsa chitokoso za mpatuko wonenedweratu. (2 Atesalonika 2:1-3) Mwachiwonekere iye anali wofunitsitsa kudzipereka yekha kaamba ka ena. Chotero, pamene Ignatius wa ku Antiokeya, Siriya, anali paulendo wake wopita kukaphedwera chikhulupiriro mu Roma, anafunsa Afilipi kutumiza kalata ku mpingo wakwawo, Polycarp wa ku Smurna anatsimikizira za kuperekedwa kwake. Pa nthaŵi imeneyo anawatumizira Afilipi kalata yake.
M’kalata ya Polycarp kwa Afilipi, timapeza chitsimikizo cha chowonadi china cha Malemba. Iye amalekanitsa Mulungu ndi Kristu, Atate ndi Mwana, ndi kunena kuti chiri “mwa chifuniro cha Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu” kuti timapeza chipulumutso. Polycarp akuchenjeza za kuchenjera ndi kukonda ndalama ndi kukumbutsa aŵerengi ake kuti adama ndi amuna ogonana ndi amuna sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. (Yerekezani ndi 1 Timoteo 6:10; 1 Akorinto 6:9, 10.) Iye akuphatikizaponso chenjezo kwa akazi kukonda amuna awo ndi kwa akulu kukhala “achikondi ndi achifundo.” Onse akufulumizidwa kukhala “achangu m’kulondola zomwe ziri zabwino.” Pomalizira, Polycarp akuchonderera kuti: “Lolani kuti Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi Yesu Kristu Iyemwini, yemwe ali Mwana wa Mulungu, ndi Mkulu wathu Wansembe wosatha, akumangilireni m’chikhulupiriro ndi chowonadi, ndi m’chifatso chonse, chifundo, kuleza mtima, kupirira, kulekerera, ndi chiyero.”
Polycarp anagwira mawu mwaufulu kuchokera ku Malemba. M’kalata yake kwa Afilipi, iye analozera ku Mateyu, Machitidwe, Aroma, 1 Akorinto, 2 Akorinto, Agalatiya, Aefeso, 2 Atesalonika, 1 Timoteo, 1 Petro, ndipo mwachidziŵikire mbali zina za Malemba. Ichi chikutipatsa umboni wakuti ena odzinenera kukhala Akristu anayesera kumamatira ku malamulo a makhalidwe abwino a Malemba mkati mwa nyengo yovuta pambuyo pa imfa ya atumwi.
Ntchito Yake mu Smurna
Smurna, mzinda wakale wa kugombe la nyanja wa Asia Minor, unali malo amalonda opita patsogolo. Unalinso malo apakati a kulambira Boma. Mwachitsanzo, olamulira Achiroma anawonetsedwa motchuka monga milungu pa ndalama ndiponso m’zozokotedwa. Nthanthi zachipembedzo zachikunja zinachilikizidwa ndi olamulira a boma.
Mwachiwonekere, unyinji wa awo oyanjana ndi mpingo wa Smurna anali osauka mwakuthupi. Koma pa nthaŵi ina, anayamikiridwa chifukwa cha kulemera kwawo kwauzimu. Ncholimbikitsa chotani nanga mmene chinaliri kwa Akristu a ku Smurna kumva mawu a Yesu olembedwa ndi mtumwi Yohane! Kristu anati kwa “mngelo,” kapena oyang’anira odzozedwa, a ku Smurna: “Ndidziŵa chisautso chako, ndi umphaŵi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana. Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.”—Chibvumbulutso 2:8-10.
Kulemera kwauzimu kulikonse kumene kungakhale kunalipo pakati pa odzinenera kukhala Akristu mu Smurna mosakaikira kunali kogwirizana mwachindunji ndi uyang’aniro wabwino wa akulu mu mpingo. Nyengo imeneyo inali ya kulimbana kwakukulu kwa chipembedzo, ndipo ziŵalo za mpingo zinatumikira pakati pa zikhulupiriro ndi madzoma owombana. Gawo lawo lochitiramo umboni linali lodzazidwa ndi machitachita a uchiwanda, kuphatikizapo matsenga ndi kupenda nyenyezi, ndipo chotero mkhalidwewo unali umodzi wa kukana Mulungu.
Kuwonjezera ku unyinji wa anthu akunja panali chidani chosonyezedwa ndi Ayuda. Pamene kuphedwera chikhulupiriro kwa Polycarp kunachitika pa February 23, 155 C.E., kukusimbidwa kuti Ayuda a chikhulupiriro chopanda maziko anathandiza kusonkhanitsa nkhuni. Anachita zimenezi ngakhale kuti kuphako kunachitika pa tsiku la Sabata!
Kodi Ndani Omwe Ali Okana Mulungu?
Polycarp anafuna kukhalabe mu Smurna ndi kuyang’anizana ndi ngozi pamene adani ake anabwera kudzamfuna. Koma pamene anafulumizidwa ndi ena, iye anathaŵira ku famu yapafupipo. Pamene kumene anali kunadziŵika, iye anakana kuchokanso ndi kunyenga omfunafunawo koma anangonena kuti: “Chifuno cha Mulungu chichitike.”
Pamene analoŵa m’bwalo lamaseŵera, Polycarp anaima pamaso pa bwanakumbwa ndi khamu lalikulu, lokwiya. Pamene bwanamkubwayo analimbikira kumufulumiza iye kusonyeza ulemu wa kulambira kwa Kaisara, Polycarp anangonena mosabisa kuti: “Ndine Mkristu . . . Ngati mukufuna kudziŵa tanthauzo la Chikristu, mungondipatsa tsiku ndipo mudzandimvetsere.” Bwanamkubwayo anayankha kuti: “Longosola mitsutso yako kwa khamuli.” Koma Polycarp anayankha kuti: “Ndinuyo amene ndinaganiza kuti muli woyenera kulankhula nanu, chifukwa taphunzitsidwa kupereka ulemu woyenerera wonse kwa olamulira ndi maulamuliro . . . malinga ngati sikutipatutsa ife.” Mwamsanga pambuyo pake Polycarp anatenthedwa mpaka imfa chifukwa anakana kukana Yesu Kristu.
Kaimidwe ka Polycarp monga Mkristu kali chinachake chimene Mulungu yekha ndiye angagamule. Bwanji ponena za lerolino? Gulu lalikulu la Akristu owona sadzakananso Kristu. M’malomwake, iwo akulengeza kuti iye ndi Mfumu yakumwamba ya Mulungu Yaumesiya yoikidwa paufumu. Mboni za Yehova zimenezi zikusonyezanso kuti tiri pafupi kuwona kukwaniritsidwa kwa mawu a ulosi a Yesu onena za “chisautso chachikulu,” chochitika chowopsya kwambiri chimene dziko silinachiwonepo. Komabe, ichi sichimatanthauza kutha kwa mtundu wa anthu koma kwa kuipa. Kupulumuka kuli kothekera kuloŵa dziko latsopano la mtendere ndi chisangalalo.—Mateyu 24:13, 21, 34; 2 Petro 3:13.
Kodi ndani amene angasankhe kulimbana ndi athenga a mbiri yabwino yoteroyo? Kokha awo amene alidi okana Mulungu, ngakhale kuti ali ndi “maonekedwe a chipembedzo.” (2 Timoteo 3:5) Ziphunzitso za chipembedzo chonyenga zachititsa khungu maganizo a ena, ndipo ambiri ‘akusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda.’ (1 Timoteo 4:1) Akristu amakono avutitsidwa ndi okana Mulungu, ena kufikira pa kuphedwa. Komatu atumiki okhulupirika a Yehova sadzagonja, pakuti potsirizira pake yawo idzakhala mphatso ya Mulungu ya moyo wamuyaya. Pakali pano, alengezi okhulupirika ameneŵa a Ufumu wa Mulungu adakali achilikizi olimba mtima a chowonadi Chamalemba.