Kodi Mumakumbukira?
Kodi mwasangalala kuŵerenga makope a posachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, onani ngati mungayankhe mafunso otsatirawa:
◻ Nchiyani chomwe chiri maziko a ukwati wachipambano?
Anthuwo ayenera kusonyeza unansi wachikondi, ulemu, ndi kukhulupirika, kuyamikira maubwino a wina ndi mnzake ndi kuphunzira kunyalanyaza ndi kukhululukira zifooko za wina ndi mnzake.—5/15, tsamba 15.
◻ Kodi ndi m’njira zotani zimene malamulo a Mulungu operekedwa kwa Israyeli anathandizira iwo kukhala oyera?
Malamulo a Yehova anathandidza Aisrayeli kukhalabe a udongo mwauzimu, mwamakhalidwe, mwamaganizo, mwakuthupi, ndi mwamwambo, lomaliziralo likumakhala m’chigwirizano ndi kulambira kwawo.—6/1, tsamba 11.
◻ Kodi kalongosoledwe kakuti “ukhondo wa maganizo” kamatanthauzanji?
“Ukhondo wa maganizo” umatanthauza kuyesayesa kozindikira ku mbali yathu kukhala a udongo m’maganizo mwa kukhalirira pa zinthu zomwe ziri ‘zowona, zolungama, ndi zoyera’ ndipo mwa ‘kupitiriza kulingalira zinthu zoterezi.’ (Afilipi 4:8)—6/1, tsamba 16.
◻ Nchifukwa ninji Yesu ananena kuti kukhalapo kwake kukakhala “monga mphezi”? (Luka 17:24)
Yesu pano anali kusonyeza kuti umboni wa kukhalapo kwake mu mphamvu ya Ufumu ukawonekera pa gawo lokulira, kutheketsa onse okhumba kuwona iko kukhala ozindikira za nsongayo.—6/15, tsamba 8.
◻ Nchifukwa ninji mayendedwe Achikristu ali ogwirizana mwachindunji ndi chikondi Chachikristu?
Mayendedwe Achikristu—njira mu imene timachitira ndi ena, khalidwe lathu, kawonedwe kathu ka ena, ndi mkhalidwe wathu wachizoloŵezi—ziri chisonyezero cha ukulu umene timasamalira ponena za anthu ena. Mayendedwe athu amasonyeza kuzama kwa chikondi chathu kaamba ka iwo. (Yohane 13:35; 1 Akorinto 10:24; 13:4-7)—6/15, tsamba 14.
◻ Ndi liti pamene ukwati wa Yesu ndi “mkazi wake” wa atsatiri odzozedwa okhulupirika a 144,000 udzachitika? (Chibvumbulutso 19:7, 8)
Ukwati umenewu udzachitika pambuyo pa nkhondo ya Armagedo ndi kuikidwa ku pompho kwa Satana. Kenaka Yehova adzakhala atayeretsa ulamuliro wake mwa kuchotsa pa dziko lapansi awo omwe amatokosa ulamuliro wake ndi kuthetseratu chisonkhezero choipa cha Satana ndi ziwanda zake.—7/1, tsamba 24.
◻ Ndimotani mmene goli la kukhala wophunzira lingabweretsere mpumulo, monga momwe chasonyezedwera m’mawu a Yesu pa Mateyu 11:29, 30?
Popeza kuti Yesu sali wosalingalira, chiri chodzetsa mpumulo kugwira ntchito limodzi naye pansi pa goli limodzimodzilo. Iye amalingalira kukhala ndi polekezera kwathu ndi zifooko. Ndipo ndi chodzetsa mpumulo chotani nanga kuwuza ena kuti angakhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso!—7/15, tsamba 20.
◻ Kodi nchiyani chomwe chiri “kubadwanso” kumene Yesu analankhula ponena za iko pa Mateyu 19:28?
Yesu anasonyeza pano kuti pakakhala “kubadwanso” kwa mikhalidwe pa dziko lapansi kotero kuti zinthu zikakhala monga momwe zinali m’munda wa Edene.—8/1, tsamba 9.