Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kristu Amatsogolera Mpingo Wake
    Nsanja ya Olonda—2002 | March 15
    • 5, 6. (a) M’masomphenya amene mtumwi Yohane anaona, kodi “zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri” ndi “nyenyezi zisanu ndi ziŵiri” zikuimira chiyani? (b) Kodi zikutanthauzanji kuti “nyenyezi zisanu ndi ziŵiri” zili m’dzanja lamanja la Yesu?

      5 Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limasonyeza kuti Yesu Kristu akulamulira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru mwachindunji. Mtumwi Yohane m’masomphenya a “tsiku la Ambuye,” anaona “zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri zagolidi; ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga Mwana wa munthu” amene “m’dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziŵiri.” Yesu pofotokozera Yohane masomphenyawo, anati: “Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zimene unaziona pa dzanja langa lamanja, ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri zagolidi: nyenyezi zisanu ndi ziŵiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iŵiri; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri ndizo Mipingo isanu ndi iŵiri.”​—Chivumbulutso 1:1, 10-20.

      6 “Zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri” zikuimira mipingo yonse yoona yachikristu ya mu “tsiku la Ambuye,” limene linayamba mu 1914. Koma bwanji za “nyenyezi zisanu ndi ziŵiri”? Poyambirira, zimenezi zinaimira oyang’anira onse odzozedwa, obadwa ndi mzimu amene anali kusamalira mipingo ya m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino.a Oyang’anira anali m’dzanja lamanja la Yesu kutanthauza kuti anali kuwalamulira ndi kuwatsogolera. Inde, Kristu Yesu anali kutsogolera gulu lonse la kapolo. Komabe, oyang’anira odzozedwa ndi ochepa masiku ano. Kodi utsogoleri wa Kristu umafika motani m’mipingo yoposa 93,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse?

      7. (a) Kodi Yesu akugwiritsa ntchito motani Bungwe Lolamulira kutsogolera mipingo padziko lonse? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti oyang’anira achikristu amaikidwa ndi mzimu woyera?

      7 Monga mmene zinalili m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, kagulu kochepa ka amuna oyenerera mwa oyang’anira odzozedwa tsopano akutumikira monga Bungwe Lolamulira, kuimira gulu lonse la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Mtsogoleri wathu amagwiritsa ntchito Bungwe Lolamulira limeneli kuika amuna oyenerera, kaya odzozedwa ndi mzimu kapena ayi, kukhala akulu m’mipingo. Pamenepa, mzimu woyera umagwira ntchito yofunika kwambiri chifukwa chakuti Yehova wapatsa Yesu ulamuliro wougwiritsa ntchito. (Machitidwe 2:32, 33) Choyamba, oyang’anira ameneŵa ayenera kukwaniritsa ziyeneretso zimene zili m’Mawu a Mulungu, amene anauziridwa ndi mzimu woyera. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9; 2 Petro 1:20, 21) Kuvomereza ndi kuika oyang’aniraŵa kumachitika atapemphera ndiponso motsogozedwa ndi mzimu woyera. Ndiponso, munthu amene waikidwayo amapereka umboni woti ali ndi zipatso za mzimuwo. (Agalatiya 5:22, 23) Motero, uphungu wa Paulo umagwira ntchito mofanana kwa akulu onse, kaya odzozedwa kapena ayi. Uphunguwo umati: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira.” (Machitidwe 20:28) Amuna oikidwa ameneŵa amalandira malangizo kuchokera ku Bungwe Lolamulira ndipo amakonda kubusa mpingo. Mwa njira imeneyi, Kristu ali nafe lerolino ndipo akutsogolera mpingo.

  • Kristu Amatsogolera Mpingo Wake
    Nsanja ya Olonda—2002 | March 15
    • a “Nyenyezi” panopa sizikuimira angelo enieni. Yesu sangagwiritse ntchito munthu kulembera uthenga zolengedwa zauzimu zosaoneka. Motero, “nyenyezi” zikuimira oyang’anira aumunthu, kapena akulu, m’mipingo, amene ali monga amithenga a Yesu. Chiŵerengero chawocho, asanu ndi aŵiri, chikutanthauza kukwanira malinga ndi muyezo wa Mulungu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena