Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ufumu wa Mulungu Umaposa Mafumu Onse
    Nsanja ya Olonda—2006 | July 15
    • Yesu ndi mafumu anzake akulamulira ali pamalo apamwamba.

      M’masomphenya omwe Danieli anaona m’maloto, anaonanso kuti ‘ufumu, ndi ulamuliro, . . . zinapatsidwa kwa anthu a opatulika.’ (Danieli 7:27) Yesu sakulamulira yekha. Ali ndi anthu ena omwe akulamulira naye ngati mafumu ndi kutumikira monga ansembe. (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Pofotokoza za anthu amenewa, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi . . . ogulidwa kuchokera kudziko.”​—Chivumbulutso 14:1-3.

      Mwanawankhosayu ndi Yesu Kristu ataikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Yohane 1:29; Chivumbulutso 22:3) Phiri la Ziyoni limene latchulidwali likuimira kumwamba.a (Ahebri 12:22) Yesu ndi mafumu anzake, okwana 144,000, akulamulira kuchokera kumwamba. Awatu ndi malo apamwamba kwambiri! Popeza ali kumwamba, iwo amaona zambiri. Chifukwa chakuti likulu lake lili kumwamba, “Ufumu wa Mulungu” umatchedwanso kuti “Ufumu wa Kumwamba.” (Luka 8:10; Mateyu 13:11) Palibe chida chilichonse, ngakhale kuphulitsa zida za nyukiliya, chomwe chingaopseze ndi kuwononga boma lakumwamba limeneli. Boma limeneli ndi losagonjetseka ndipo lidzakwaniritsa cholinga chomwe Yehova analikhazikitsira.​—Ahebri 12:28.

  • Ufumu wa Mulungu Umaposa Mafumu Onse
    Nsanja ya Olonda—2006 | July 15
    • a Kale, Mfumu Davide ya Israyeli inalanda Ajebusi phiri la Ziyoni la padziko lapansi pano, n’kulisandutsa likulu la ufumu wake. (2 Samueli 5:6, 7, 9) Inasamutsanso Likasa lopatulika n’kupita nalo komweko. (2 Samueli 6:17) Popeza Likasa linkaimira kukhalapo kwa Yehova, Ziyoni ankatchedwa malo omwe Mulungu ankakhala, zomwe zinachititsa kuti malowa akhale oyenera kuimira kumwamba.​—Eksodo 25:22; Levitiko 16:2; Salmo 9:11; Chivumbulutso 11:19.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena