Armagedo
Tanthauzo: Liwu Lachigiriki Har Ma·ge·donʹ, lotengedwa ku Chihebri ndi kutembenuzidwa kukhala “Armagedo” ndi otembenuza ambiri, limatathauza “Phiri la Megido,” kapena “Phiri la Msonkhano wa Magulu Ankhondo.” Baibulo limagwirizanitsa dzinali, osati ndi chipiyoyo cha nyukliya koma ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” irinkudza ya chilengedwe chonse. (Chiv. 16:14, 16) Dzinali likugwiritsiridwa ntchito mwachindunji kusonya “malo [Chigiriki toʹpon; ndiko kuti, khalidwe kapena mkhalidwe]” amene olamulira andale zadziko a dziko lapansi akusonkhanitsidwirako motsutsana ndi Yehova ndi Ufumu wake wokhala mmanja mwa Yesu Kristu. Chitsutso chotero chidzasonyezedwa mwa chochitika cha dziko lonse chotsutsana ndi atumiki a Yehova padziko lapansi, oimira owoneka a Ufumu wa Mulungu.
Kodi anthu adzaloledwa ndi Mulungu kuwononga dziko lapansi ndi chimene ena amatcha “Armagedo yamoto wanyukliya”?
Sal. 96:10, NW: “Yehova iyemwiniyo wakhala mfumu. Dziko lobala zipatso [Chihebri, te·velʹ; dziko lapansi, monga lachonde ndi lokhalidwa ndi anthu, mbali yadziko lapansi yokhoza kukhalidwa ndi anthu] nalonso lafikira kukhala lokhazikitsidwa zolimba kotero kuti silingachititsidwe kugwedezeka.”
Sal. 37:29: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”
Chiv. 11:18, NW: “Mitundu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu [wa Yehova] unafika, ndi nthaŵi yoikidwiratu . . . ya kuwononga awo owononga dziko lapansi.”
Kodi Armagedo nchiyani, monga momwe ikutchulidwira m’Baibulo?
Chiv. 16:14, 16, NW: “Iwo, kunena zowona, ali mawu ouziridwa ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro, ndipo iwo amapita kwa mafumu a dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kuwasonkhanitsira pamodzi ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse. Ndipo anawasonkhanitsira pamodzi ku malo amene akutchedwa m’Chihebri Har–Magedo [Armagedo].”
Kodi Armagedo idzamenyedwera ku Middle East kokha?
Olamulira ndi magulu ankhondo amitundu yonse adzasonkhanitsidwa kumenyana ndi Mulungu
Chiv. 16:14, NW: “Amapita kwa mafumu a dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu, kuwasonkhanitsira pamodzi ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”
Chiv. 19:19, NW: “Ndinawona chirombo [ulamuliro wandale zadziko waumunthu] ndi mafumu a dziko lapansi ndi magulu awo ankhondo atasonkhana kuchita nkhondo ndi wokwera pakavalo limodzi ndi gulu lake lankhondo.”
Yer. 25:33: “Akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera kumalekezero ena a dziko lapansi kumka kumalekezero a dziko lapansi.”
Kugwiritsiridwa ntchito kwa dzina lakuti Armagedo (Har–Magedo) sikungatathauze kuti nkhondoyo idzamenyedwera ku Phiri lenileni la Megido
Kulibe Phiri lenileni la Megido; kuli kokha mulu wa pafupifupi mapazi 70 (21 m) kumene mabwinja a Megido wakale akupezeka.
Mafumu ndi magulu ankhondo a “dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu” sakakwana m’Chigwa chenichenicho cha Esdraelon, mtsinde mwa Megido. Chigwacho nchangondya zitatu, chamamailo 20 okha (32 km) m’litali ndi mamailo 18 (29 km) m’bwambi kumalekezero akummaŵa.—The Geography of the Bible (New York, 1957), Denis Baly, p. 148.
Dzinalo nloyenerera chifukwa cha mbali ya Megido m’mbiri; chigwa chokhala mtsinde mwa Megidocho chinali malo ankhondo zotha makani
Kumeneko Yehova anachititsa kugonjetsedwa kwa Sisera, kazembe wankhondo wa gulu la nkhondo la Akanani, pamaso pa Woweruza Baraki.—Ower. 5:19, 20; 4:12-24.
Thutmose III, farao wa Igupto, anati: “Kulandidwa kwa Megido ndiko kulandidwa kwa matauni chikwi!”—Ancient Near Eastern Texts Relating to the Old Testament (Princeton, N.J.; 1969), lolembedwa ndi James Pritchard, p. 237.
Dzina lakuti Megido (kutanthauza “Msonkhano wa Magulu Ankhondo”) nloyenerera chifukwa chakuti Armagedo uli mkhalidwe wa padziko lonse mu umene magulu ankhondo ndi ochirikiza ena a olamulira amitundu yonse adzaloŵetsedwamo.
Kodi ndani kapena nchiyani chimene chidzawonongedwa pa Armagedo?
Dan. 2:44, NW: “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu onse amenewa, ndipo uwo wokha udzakhala kosatha.”
Chiv. 19:17, 18, NW: “Ndinawonanso mngelo ataima m’dzuŵa, ndipo anafuula ndi mawu aakulu ndi kunena kwa mbalame zonse zimene zimauluka m’mlengalenga: ‘Idzani kuno, sonkhanani ku chakudya chamadzulo chachikulu cha Mulungu, kuti mudzadye minofu ya mafumu ndi minofu ya atsogoleri ankhondo ndi minofu ya anthu amphamvu ndi minofu ya akavalo ndi ya owakwera, ndi minofu ya onse, ya mfulu kudzanso ya akapolo ndi ya aang’ono ndi akulu.’”
1 Yoh. 2:16, 17, NW: “Chirichonse m’dziko—chikhumbo chathupi ndi chikhumbo chamaso ndi kuwonetsera chuma chomwe uli nacho—sizimachokera kwa Atate, koma zimachokera ku dziko. Ndiponso, dziko likupita ndipo chomwechonso chikhumbo chake, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kosatha.”
Chiv. 21:8: “Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse amabodza, cholandira chawo chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure; ndiyo imfa yachiŵiri.”
Kodi chiwonongekocho chidzakhala chosatha?
Mat. 25:46, NW: “Awa [amene amakana kuchitira zabwino “abale” a Kristu] adzachoka kuloŵa m’kudulidwa kosatha.”
2 Ates. 1:8, 9: “Iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu; adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.”
Kodi padzakhala opulumuka?
Zef. 2:3: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”
Aroma 10:13, NW: “Aliyense amene amaitana dzina la Yehova adzapulumutsidwa.”
Sal. 37:34: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko: pakudulidwa oipa udzapenya.”
Yoh. 3:16, NW: “Mulungu . . . anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuchitira kuti aliyense wosonyeza chikhulupiriro mwa iye asawonongedwe koma akhale nawo moyo wosatha.”
Chiv. 7:9, 10, 14, NW: “Ndinawona, ndipo, tawonani! khamu lalikulu limene palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, lochokera m’mitindu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, lirinkuimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, litavala miinjiro yoyera; ndipo m’manja mwawo munali makhwatha akanjedza. Ndipo amafuula ndi mawu aakulu, kumati: ‘Chipulumutso tichipeza kwa Mulungu wathu, amene wakhala pa mpando wachifumu ndi kwa Mwanawankhosa.’ . . . ‘Amenewa ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.’”
Kodi nchiyani chimene chidzachitikira ana achichepere pa Armagedo?
Baibulo silimayankha mwachindunji funso limenelo, ndipo ife sindife oweruza. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amawona ana achichepere a Akristu owona kukhala “oyera.” (1 Akor. 7:14) Limavumbulanso kuti nthaŵi zakale pamene Mulungu anawononga oipa anawononganso ana awo. (Num. 16:27, 32; Ezek. 9:6) Mulungu samafuna kuti aliyense awonongedwe, chotero akuchititsa chenjezo kuperekedwa tsopano kuti lipindulitse makolo ndi ana omwe. Kodi sikukakhala kwanzeru kwa makolo kulondola njira imene ikachititsa ana awo kukhala owonedwa mwachiyanjo ndi Mulungu tsopano ndi pa Armagedo pomwe?
Kodi chikondi cha Mulungu chimaswedwa mwa kuwonongedwa kwa oipa?
2 Pet. 3:9: “Ambuye . . . aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”
Luka 18:7, 8: “Kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nawo mtima? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa.”
2 Ates. 1:6: “Nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu [atumiki ake] chisautso.”
Kodi nkotheka kukhala mu mkhalidwe wauchete?
2 Ates. 1:8, NW: “Amadzetsa kulipsira pa awo amene [mwa kudzisankhira] samadziŵa Mulungu ndi awo amene samamvera mbiri yabwino yonena za Ambuye Yesu.”
Mat. 24:37-39: “Monga masiku a Nowa . . . iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.”
Mat. 12:30: “Iye wosakhala pamodzi ndi ine akana ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi ine amwazamwaza.”
Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:19, 20.
Kodi nchisonkhezero chayani chimene chikukankhira amitundu kumkhalidwe wa padziko lonse umene udzachititsa kumenyana ndi Mulungu?
Chiv. 16:13, 14, NW: “Ndinawona mawu atatu onyansa ouziridwa amene anawonekera ngati achule amene atuluka mkamwa mwa chinjoka [Satana Mdyerekezi; Chiv. 12:9] ndi mkamwa mwa chirombo ndi mkamwa mwa mneneri wonyenga. Iwo, kunena zowona, ali mawu ouziridwa ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro, ndipo iwo amapita kwa mafumu a dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu, kuwasonkhanitsira pamodzi ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”
Yerekezerani ndi Luka 4:5, 6; 1 Yohane 5:19; ndiponso Machitidwe 5:38, 39; 2 Mbiri 32:1, 16, 17.