Aneneri Onyenga
Tanthauzo: Anthu alionse paokha ndi magulu olengeza mauthenga amene amati ngochokera kumagwero oposa aumunthu koma amene sakuchokera kwa Mulungu wowona ndipo saali ogwirizana ndi chifuniro chake chovumbulutsidwa.
Kodi aneneri owona ndi onyenga angadziŵike motani?
Aneneri owona amalengeza chikhulupiriro chawo mwa Yesu, koma zowonjezereka zikufunika kuposa kudzinenera kukhala akulalikira m’dzina lake
1 Yoh. 4:1-3: “Yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kuloŵa m’dziko lapansi. Mmenemo muzindikira mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Kristu anadza m’thupi, uchokera mwa Mulungu; ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu.”
Mat. 7:21-23: “Siyense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu ufumu wakumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wakumwamba. Ambiri adzati kwa ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu . . . ? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kasayeruzika.”
Aneneri owona amalankhula m’dzina la Mulungu, koma kunena kokha kukhala akumuimira sikuli kokwanira
Deut. 18:18-20: “Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale awo, wonga iwe [wonga Mose]; ndipo ndidzampatsa mawu anga mkamwa mwake, ndipo adzanena nawo zonse ndinamuuzazi. Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mawu anga amene amanena m’dzina langa, ndidzamfunsa. Koma mneneri wa kuchita modzikuza ndi kunena mawu m’dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m’dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.” (Yerekezerani ndi Yeremiya 14:14; 28:11, 15.)
Yesu anati: “Sindichita kanthu kwa ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” (Yoh. 8:28) Iye anati: “Ndadza ine m’dzina la Atate wanga.” (Yoh. 5:43) Yesu anatinso: “Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha.”—Yoh. 7:18.
Ngati anthu alionse kapena magulu adzinenera kukhala akuimira Mulungu koma nalephera kugwiritsira ntchito dzina lenileni la Mulungu, napanga chizoloŵezi cha kulankhula malingaliro a iwo eni pazinthu, kodi iwo akuyenerana ndi chiyeneretso chofunika chimenechi cha mneneri wowona?
Mphamvu ya kuchita “zizindikiro zazikulu,” kapena “zozizwitsa,” siri kwenikweni umboni wa kukhala mneneri wowona
Mat. 24:24: “Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzawonetsa zizindikiro zazikulu [“zozizwitsa,” TEV] ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe.”
2 Ates. 2:9, 10: “[Wosayeruzika] amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuwonongeka, popeza chikondi cha chowonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo.”
Kumbali ina, Mose anachita zozizwitsa mwachitsogozo cha Yehova. (Eks. 4:1-9) Yehova anaperekanso mphamvu kwa Yesu za kuchita zozizwitsa. (Mac. 2:22) Koma zoposa zozizwitsa zinapereka umboni wakuti Mulungu analidi atawatuma.
Zimene aneneri owona amanenera zimachitika, koma iwo angakhale osazindikira kwenikweni nthaŵi kapena mmene zidzachitikira
Dan. 12:9: “Pita Danieli; pakuti mawuwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthaŵi yachitsiriziro.”
1 Pet. 1:10, 11: “Aneneri . . . ndi kusanthula nthaŵi iti, kapena nthaŵi yanji mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo unalozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero wotsatana nawo.”
1 Akor. 13:9, 10: “Pakuti ife tidziŵa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. Koma pamene changwiro chafika, tsono cha mderamdera chidzakhala chabe.”
Miy. 4:18: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbee.”
Atumwi ndi ophunzira ena Achikristu oyambirira anali ndi ziyembekezo zina zolakwa, koma Baibulo silimawaika m’kagulu ka “aneneri onyenga.”—Wonani Luka 19:11; Yohane 21:22, 23; Machitidwe 1:6, 7.
Mneneri Natani analimbikitsa mfumu Davide kukwaniritsa zimene zinali mu mtima mwake ponena za kumanga nyumba kaamba ka kulambiridwa kwa Yehova. Koma pambuyo pake Yehova anauza Natani kuuza Davide kuti sanali iye amene akamanga nyumbayo. Yehova sanakane Natani kaamba ka zimene anali atanena poyamba koma anapitirizabe kumgwiritsira ntchito chifukwa chakuti analungamitsa nkhaniyo modzichepetsa pamene Yehova anaimveketsa kwa iye.—1 Mbiri 17:1-4, 15.
Mawu a mneneri wowona amachirikiza kulambira kowona ndipo ngogwirizana ndi chifuniro chovumbulutsidwa cha Mulungu
Deut. 13:1-4: “Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani zizindikiro kapena chozizwa; ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu ina, imene simunaidziŵa, ndi kuitumikira; musamamvera mawu a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu, popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziŵe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Mudziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuwopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mawu ake, ndi kumtumikira iye, ndi kummamatira.”
Popeza Baibulo limanena kuti “bwenzi ladziko” ndiro mdani wa Mulungu, kodi atsogoleri achipembedzo amene amalimbikitsa magulu awo ankhosa kuti aphatikizidwe m’zochitika za dziko akuchirikiza kulambira kowona? (Yak. 4:4; 1 Yoh. 2:15-17) Mulungu wowona ananena kuti amitundu “adzadziŵa kuti ndine Yehova,” ndipo Baibulo limalongosola kuti Mulungu akatenga mwa amitundu “anthu a dzina lake,” koma kodi magulu azipembedzo amene amaluluza kufunika kwa kugwiritsira ntchito dzina lake la Mulungu akuchita mogwirizana ndi chifuniro chovumbulutsidwa chimenechi cha Mulungu? (Ezek. 38:23; Mac. 15:14) Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera Ufumu wa Mulungu, ndipo Baibulo limachenjeza motsutsa kuika chidaliro chamunthuwe mwa anthu athupi lanyama, chotero kodi atsogoleri achipembedzo kapena magulu andale zadziko amene amalimbikitsa anthu kuika chidaliro chawo mu ulamuliro wa anthu ali aneneri owona?—Mat. 6:9, 10; Sal. 146:3-6; yerekezerani ndi Chivumbulutso 16:13, 14.
Aneneri owona ndi onyenga angadziŵike mwa chipatso chosonyezeka m’miyoyo yawo ndi m’miyoyo ya awo amene amawatsatira
Mat. 7:15-20: “Yang’anirani mupeŵe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. . . . Chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.”
Kodi nchiyani chimene chimadziŵikitsa moyo wawo? “Ntchito zathupi . . . ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; . . . iwo akuchitachita zotere sadzaloŵa ufumu Mulungu. Koma chipatso chamzimu [wa Mulungu] ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”—Agal. 5:19-23; wonaninso 2 Petro 2:1-3.
Kodi Mboni za Yehova sizinapange zolakwa m’ziphunzitso zawo?
Mboni za Yehova sizimanena kuti ziri aneneri ouziridwa. Izo zapanga zolakwa. Mofanana ndi atumwi a Yesu Kristu, panthaŵi zina izo zakhala ziri ndi ziyembekezo zolakwa.—Luka 19:11; Mac. 1:6.
Malemba amapereka zochitika za nthaŵi zophatikizapo kukhala pafupi kwa Kristu, ndipo Mboni za Yehova zapenda zimenezi ndi chikondwerero chachikulu. (Luka 21:24; Dan. 4:10-17) Yesu anafotokozanso chizindikiro cha zochitika zambiri chimene chikagwirizanitsidwa ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi a nthaŵi odziŵikitsa mbadwo umene ukawona mapeto a dongosolo loipa la zinthu la Satana. (Luka 21:7-36) Mboni za Yehova zasonya ku umboni m’kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chimenechi. Nzowona kuti Mboni zapanga zolakwa m’kumvetsetsa zimene zikachitika pamapeto a nthaŵi zina, koma izo sizinapange cholakwa cha kutayikiridwa ndi chikhulupiriro kapena kuleka kukhala maso ponena za kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova. Izo zapitirizabe kupita patsogolo m’kusinkhasinkha kwawo uphungu woperekedwa ndi Yesu wakuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”—Mat. 24:42.
Nkhani zimene kulungamitsidwa kwa lingaliro kwakhala kofunika zakhala zochepa kwambiri poyerekezeredwa ndi chowonadi Chabaibulo chofunika chimene izo zazindikira ndi kulengeza. Pakati pa zimenezi pali zotsatirazi: Yehova ndiye Mulungu wowona yekha. Yesu Kristu saali mbali ya Mulungu wa mitu Itatu koma ndiye Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Kuomboledwa ku uchimo nkotheka kokha kupyolera mwa kukhulupirira nsembe ya dipo la Kristu. Mzimu woyera suuli munthu koma ndiwo mphamvu yogwira ntchito ya Yehova, ndipo zipatso zake ziyenera kuwoneka m’miyoyo ya olambira owona. Moyo wamunthu suuli wosakhoza kufa, monga momwe akunja akalero adanenera; umafa, ndipo chiyembekezo cha moyo wamtsogolo ndicho m’chiukiriro. Chilolezo cha Mulungu cha kuipa chakhalako chifukwa cha nkhani ya ufumu wachilengedwe chonse. Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu. Kuyambira 1914 takhala tiri m’masiku otsiriza a dongosolo loipa lazinthu ladziko lonse. Akristu okhulupirika okwanira 144 000 okha adzakhala mafumu ndi ansembe ndi Kristu m’mwamba, pamene otsala a anthu onse omvera adzalandira moyo wamuyaya padziko lapansi laparadaiso.
Mfundo ina ya kuilingalira ponena za ziphunzitso za Mboni za Yehova ndi iyi: Kodi zimenezi zapititsadi patsogolo anthu mwa makhalidwe? Kodi omamatira ku ziphunzitso zimenezi ali apadera m’zitaganya zawo chifukwa cha kuwona mtima kwawo? Kodi moyo wawo wabanja ngwoyambukiridwa mopindulitsa mwa kugwiritsira ntchito ziphunzitsozi? Yesu ananena kuti ophunzira ake akadziŵika mosavuta chifukwa cha kukhala ndi chikondi pakati pawo. (Yoh. 13:35) Kodi mkhalidwe umenewu uli wapadera pakati pa Mboni za Yehova? Timalola zochitika kuti zilankhule zokha.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Minisitala wanga ananena kuti Mboni za Yehova ndizo aneneri onyenga’
Mungayankhe kuti: ‘Ndingafunse, Kodi iye anakusonyezani chiri chonse m’Baibulo chofotokoza zimene timakhulupirira kapena kuchita ndi chimene chimanena kuti anthu amtundu umenewo akakhala aneneri onyenga? . . . Kodi ndingakusonyezeni chonde mmene Baibulo limafotokozera aneneri onyenga? (Ndiyeno gwiritsirani ntchito mfundo imodzi kapena zoposa zondandalikidwa pa tsamba 32-36.)’
Kapena munganene kuti: ‘Ndiri wotsimikizira kuti mudzavomereza kuti umboni weniweni uyenera kuchirikiza chinenezo chachikulu choterocho. Kodi minisitala wanu anatchula zitsanzo zenizeni zirizonse? (Ngati mwininyumba atchula “zonenedweratu” zina zimene sizinachitike, gwiritsirani ntchito mawu a patsamba 33, ndi pa tsamba 35 mpaka pamwamba pa 36.)’
Kuthekera kwina: ‘Ndiri wotsimikizira kuti ngati munthu wina anakuimbani mlandu wofananawo, mukanalola mwaŵi wooti mufotokoze ganizo lanu kapena lingaliro, kodi sichoncho? . . . Chotero kodi ndingakusonyezeni kuchokera m’Baibulo . . . ?’