-
Zaka Zoposa 50 za ‘Kuwolokerako’Nsanja ya Olonda—1996 | November 1
-
-
Zaka Zoposa 50 za ‘Kuwolokerako’
YOSIMBIDWA NDI EMMANUEL PATERAKIS
Zaka mazana 19 zapitazo mtumwi Paulo analandira chiitano chachilendo chakuti: “Muwolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.” Paulo mofunitsitsa anavomera mwaŵi umenewu watsopano wa “kulalikira uthenga wabwino.” (Machitidwe 16:9, 10) Pamene kuli kwakuti chiitano chimene ndinalandira sichili chakale kwambiri choncho, komabe zinali zaka zoposa 50 zapitazo pamene ndinavomera ‘kuwolokera’ m’magawo atsopano ndi mzimu wa Yesaya 6:8 wakuti: “Ndine pano; munditumize ine.” Maulendo anga ambiri anandichititsa kupatsidwa dzina losemerera lakuti Mlendo Wosalekeza Woona Malo, koma zochita zanga sizinali zofanana kwambiri ndi maulendo okaona malo. Nthaŵi zambiri, pamene ndinafika m’chipinda changa cha mu hotela, ndinkagwada ndi kuthokoza Yehova chifukwa cha chitetezero chake.
NDINABADWA pa January 16, 1916, ku Hierápetra, ku Crete, m’banja lodzipereka kwambiri pa chipembedzo cha Orthodox. Kuyambira pamene ndinali khanda, Amayi ankatenga ine ndi alongo anga atatu kumka nafe ku tchalitchi pa Sande. Ponena za atate, ankakonda kutsala kunyumba ndi kumaŵerenga Baibulo. Ndinakonda atate kwambiri—munthu woona mtima, wabwino ndi wokhululukira—ndipo imfa yawo, pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi zinayi, inandipweteka kwambiri.
Ndikukumbukira kuti pamene ndinali ndi zaka zisanu, ndinaŵerenga vesi lina kusukulu limene linati: “Zinthu zonse zotizinga zimalengeza kukhalako kwa Mulungu.” Pamene ndinali kukula, ndinakhulupirira kotheratu zimenezi. Motero, pausinkhu wa zaka 11, ndinasankha zolemba nkhani yokhala ndi Salmo 104:24 monga mutu wake: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” Ndinachita chidwi ndi kuzizwitsa kwa chilengedwe, ngakhale ndi zinthu zazing’onong’ono zonga timbewu tokhala ndi mapiko kotero kuti tiuluke mu mphepo kuchokera mumthunzi wa mtengo wake. Patapita mlungu umodzi nditapereka nkhani yangayo, mphunzitsi wanga anaiŵerengera kalasi lonse, ndiyeno pambuyo pake ku sukulu yonse. Panthaŵiyo aphunzitsi anali kulimbana ndi malingaliro achikomyunisti ndipo anali okondwa kumva kuchirikiza kwanga kukhalako kwa Mulungu. Komano ine, ndinali kungosonyeza chikhulupiriro changa cha kukhalapo kwa Mlengi.
Mayankho a Mafunso Anga
Kukumana kwanga koyamba ndi Mboni za Yehova kuchiyambiyambi kwa ma 1930 ndimakukumbukirabe mwamphamvu. Emmanuel Lionoudakis anali kulalikira m’matauni ndi m’midzi yonse ya Crete. Ndinalandira timabuku tingapo kwa iye, komano kamene kananditenga mtima kwambiri kanali ka mutu wakuti Where Are the Dead? Ndinali ndi mantha aakulu kwambiri pa imfa kwakuti sindinkaloŵa nkomwe m’chipinda chimene atate anaferamo. Pamene ndinaŵerenga kabukuka mobwerezabwereza ndi kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za mkhalidwe wa akufa, ndinaona kuti kuwopa kwanga zinthu zosadziŵika kunazimiririka.
Mboni zinkafika m’tauni yakwathu kamodzi pachaka m’nyengo yachilimwe, ndipo zinkandibweretsera mabuku owonjezereka oti ndiŵerenge. Pang’ono ndi pang’ono kumvetsa kwanga Malemba kunawonjezereka, komano ndinapitiriza kupita ku Tchalitchi cha Orthodox. Komabe, buku lakuti Deliverance, linasintha zinthu. Linasonyeza bwino lomwe kusiyana kumene kuli pakati pa gulu la Yehova ndi lija la Satana. Kuyambira pamenepo, ndinayamba kuphunzira Baibulo mokhazikika ndi buku lililonse la Watch Tower Society limene ndinapeza. Popeza kuti Mboni za Yehova zinali zoletsedwa m’Greece, ndinkaphunzira mobisa usiku. Komabe, ndinakondwa kwambiri ndi zimene ndinali kuphunzira kwakuti sindinathe kugwira mtima pa kuuza munthu aliyense zimenezi. Sipanapite nthaŵi yaitali pamene apolisi anayamba kundilonda, akumandifikira nthaŵi zonse pa nthaŵi iliyonse yamasana ndi yausiku kudzafunafuna mabuku.
Mu 1936, ndinafika pa msonkhano kwa nthaŵi yoyamba, pa mtunda wa makilomita 120 ku Iráklion. Ndinali wachimwemwe kwambiri kuonana ndi Mboni. Unyinji wa iwo anali anthu wamba, makamaka alimi, koma anandithandiza kutsimikizira kuti chimenechi chinali choonadi. Ndinadzipatulira kwa Yehova nthaŵi yomweyo.
Ubatizo wanga uli chochitika chimene sindidzaiŵala konse. Usiku wina mu 1938, ine ndi aŵiri a ophunzira Baibulo anga tinatengedwa ndi Mbale Lionoudakis mumdima wa ndiwe yani kumka ku gombe. Atapereka pemphero, anativiika m’madzi.
Wogwidwa
Kukuuzani zoona, nthaŵi yoyamba yeniyeni imene ndinamka kukalalikira inali ndi zochitika zambiri. Ndinakumana ndi mnzanga wina wakale wakusukulu amene anakhala wansembe, ndipo tinakambitsirana bwino kwambiri. Koma pambuyo pake iye analongosola kuti malinga ndi lamulo la bishopu, iyeyo anafunikira kundimangitsa. Pamene tinali kuyembekezera mu ofesi ya meya kuti apolisi a m’mudzi woyandikana nawo afike, khamu linasonkhana panja. Chotero ndinatenga buku la Chipangano Chatsopano lachigiriki limene linali mu ofesimo ndi kuyamba kuwakambira nkhani yozikidwa pa Mateyu chaputala 24. Poyamba anthuwo sanafune kumvetsera, komano wansembeyo analoŵererapo. “Mlekeni alankhule,” iye anatero. “Ndi Baibulo lathu.” Ndinali wokhoza kulankhula kwa ola limodzi ndi theka. Motero, tsiku langa loyamba mu utumiki linalinso nthaŵi ya nkhani yanga yapoyera yoyamba. Popeza kuti apolisi anali asanafike pamene ndinamaliza, meya ndi wansembeyo anasankha kuti gulu la anthulo lindithamangitse m’tauniyo. Pagulaye yoyamba ya msewu, ndinayamba kuthamanga monga momwe ndikanathera kuti ndipeŵe miyala imene anali kuponya.
Tsiku lotsatira apolisi aŵiri, limodzi ndi bishopu, anandimanga ku ntchito. Kupolisi, ndinatha kupereka umboni kwa iwo kuchokera m’Baibulo, koma popeza kuti mabuku anga a Baibulo analibe chidindo cha bishopu chofunidwa ndi lamulo, ndinapatsidwa mlandu wa kutembenuza anthu ndi kugaŵira mabuku osaloledwa ndi lamulo. Anandimasula pomayembekezera kuzengedwa mlandu.
Kuzengedwa mlandu kwanga kunachitidwa patapita mwezi. Podzitetezera ndinasonyeza kuti ndinali kuchita momvera lamulo la Kristu chabe la kulalikira. (Mateyu 28:19, 20) Woweruza anayankha monyodola kuti: “Mwanawe, uyotu Amene anapereka lamulo limeneli anapachikidwa. Mwatsoka, ndilibe ulamuliro wa kupereka chilango chimodzimodzicho kwa iwe.” Komabe, loya wina wachinyamata amene sindinamdziŵe anaimirira monditetezera, akumanena kuti pokhala tinali titazingidwa ndi anthu ochuluka achikomyunizimu ndi okana Mulungu, khotilo liyenera kunyadira kuti pali anyamata amene ali okonzekera kutetezera Mawu a Mulungu. Ndiyeno anafika kwa ine nandiyamikira moona mtima chifukwa cha chodzitetezera changa cholembedwa, chimene chinali mu faelo yanga. Pokhala atachita chidwi chifukwa chakuti ndinali wamng’ono kwambiri, anadzipereka kunditetezera popanda malipiro. M’malo mwa chilango cha miyezi itatu, ndinapatsidwa chilango cha masiku khumi okha m’ndende ndi faindi ya madrakima 300. Chitsutso chotero chinangolimbitsa chitsimikiziro changa cha kutumikira Yehova ndi kuchirikiza choonadi.
Panthaŵi ina pamene ndinagwidwa, woweruza anaona kusavutika kwanga kutchula malemba a m’Baibulo. Anapempha bishopu kutuluka mu ofesi yake, akumati: “Mwachita ntchito yanu. Ineyo ndilankhula naye.” Ndiyeno anatulutsa Baibulo lake, ndipo tinakambitsirana za Ufumu wa Mulungu masana onse. Zochitika zotero zinandilimbikitsa kupitiriza ngakhale kuti panali zovuta.
Chilango cha Imfa
Mu 1940, ndinaitanidwa kukachita utumiki wankhondo ndipo ndinalemba kalata yolongosola chifukwa chake ndinakana kulembedwa. Patapita masiku aŵiri ndinamangidwa ndipo ndinamenyedwa kwambiri ndi apolisi. Ndiyeno ananditumiza ku malo ankhondo ku Albania, kumene anandiimba mlandu m’khoti la ankhondo chifukwa chakuti ndinakana kumenya nkhondo. Akuluakulu a asilikali anandiuza kuti analibe kanthu ndi kudziŵa kuti kaya ndinali wosalakwa kapena wolakwa koma iwo anali ndi nkhaŵa ya mmene chitsanzo changa chingayambukirire asilikali ena. Anandipatsa chilango cha imfa, koma chifukwa cha kulakwika kwina m’zamalamulo, anasintha chilango chimenechi monditonthoza kwambiri, kukhala cha ukaidi wa zaka khumi. Ndinathera miyezi ingapo yotsatira ya moyo wanga m’ndende ya asilikali ku Greece m’mikhalidwe yovuta kwambiri, imene ziyambukiro zake zakuthupi zikali kundisautsa.
Komabe, ndende siinandiletse kulalikira. Kutalitali! Kukambitsirana ndi anthu kunali kosavuta, popeza ambiri anali kufuna kudziŵa chifukwa chake munthu wamba anali m’ndende ya asilikali. Kukambitsirana kumodzi kotere ndi mnyamata wina woona mtima kunayambitsa phunziro la Baibulo m’bwalo la ndende. Zaka 38 pambuyo pake ndinakumananso ndi mwamunayu pamsonkhano. Analandira choonadi ndipo anali kutumikira monga woyang’anira wampingo pa chisumbu cha Lefkás.
Pamene magulu ankhondo a Hitler analanda Yugoslavia mu 1941, anatisamutsira kutali kumpoto ku ndende ya ku Preveza. Pa ulendowo, galimoto zathu zondondozana zinaukiridwa ndi ndege zoponya mabomba za Ajeremani, ndipo akaidife sitinapatsidwe chakudya. Pamene buledi wochepa amene ndinali naye anatha, ndinapemphera kwa Mulungu kuti: “Ngati chili chifuniro chanu kuti ine ndife ndi njala pambuyo pa kundipulumutsa pa chilango cha imfa, chifuniro chanu chichitiketu.”
Tsiku lotsatira ofesala wina anandiitanira pambali popenda maina ndipo, atadziŵa kumene ndinachokera, makolo anga, ndi chifukwa chake ndinali m’ndende, anandiuza kuti ndimtsatire. Anamka nane kuchipinda chodyera cha maofesala m’tauni, kundilozera pathebulo lina kuti ndidye buledi, tchizi, ndi nyama ya nkhosa yowotcha zimene zinalipo. Koma ndinalongosola kuti popeza kuti akaidi ena 60 analibe chakudya chilichonse, chikumbumtima changa sichingandilole kudya. Ofesalayo anayankha kuti: “Sindingathe kudyetsa aliyense! Atate wako anali wooloŵa manja kwambiri kwa atate wanga. Ndili ndi thayo pa iwe koma osati pa ena.” “Ngati zili choncho ndingobwerera,” ndinayankha motero. Anayamba waganiza kaye ndiyeno anandipatsa thumba lalikulu loti ndiikemo chakudya chochuluka chimene ndikanatha kuikamo.
Nditabwerera kundende, ndinatula thumbalo ndi kunena kuti: “Mabwana, zimenezi nzanu.” Modabwitsa, madzulo a dzulo lake, ndinali nditaimbidwa mlandu wobweretsa mavuto kwa akaidi ena chifukwa chakuti ndinakana kugwirizana nawo m’mapemphero a Namwali Mariya. Komabe, mkomyunisti wina ananditetezera. Tsopano poona chakudyacho, iyeyo anati kwa ena: “Nanga ‘Namwali Mariya’ wanu uja ali kuti? Pajatu munati tifa chifukwa cha munthu uyu, komanso ndiye watibweretsera chakudya.” Ndiyeno anatembenukira kwa ine nati: “Emmanuel! Bwera udzapemphere.”
Posapita nthaŵi pambuyo pake, kuyandikira kwa gulu lankhondo la Ajeremani kunachititsa alonda andende kuthaŵa, kukumatsegulira zitseko ogwidwa. Ndinapita ku Patras kuti ndikapeze Mboni zina ndisanamke ku Athens pakutha kwa May 1941. Kumeneko ndinali wokhoza kupeza zovala ndi nsapato ndi kusamba kwa nthaŵi yoyamba patapita nyengo yoposa chaka. Kufikira kumapeto kwa ulamuliro wolanda dzikowo, Ajeremani anali kundiimitsa nthaŵi zonse pamene ndinali kulalikira, koma sanandimange. Wina wa iwo anati: “Ku Germany timaombera Mboni za Yehova. Koma kuno timakhumba kuti bwenzi adani athu onse akanakhala Mboni!”
Zochita za Pambuyo pa Nkhondo
Greece anapasulidwa mowonjezereka ndi nkhondo yachiŵeniŵeni kuyambira mu 1946 kukafika 1949 monga ngati kuti anali asanamenye nkhondo mokwanira, anthu zikwi zambiri akumafa. Abale anafunikira chilimbikitso chochuluka kuti akhalebe olimba panthaŵiyo pamene kufika pamisonkhano kokha kunali kuchititsa munthu kumangidwa. Abale angapo anapatsidwa chilango cha imfa chifukwa cha kaimidwe kawo kauchete. Koma ngakhale kuti panali zimenezi, anthu ambiri analabadira uthenga wa Ufumu, ndipo sabata lililonse tinali kukhala ndi ubatizo wa munthu mmodzi kapena aŵiri. Ponena za 1947, ndinayamba kugwira ntchito pa maofesi a Sosaite ku Athens masana ndi kuchezetsa mipingo usiku monga woyang’anira woyendayenda.
Mu 1948, ndinali ndi chimwemwe chifukwa chakuti ndinaitanidwa kukaloŵa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, ku United States. Komano panali vuto. Chifukwa cha kuimbidwa kwanga milandu kwapapitapo, ndinali wosakhoza kupeza pasipoti. Komabe, mmodzi wa ophunzira Baibulo anga anali paubwenzi ndi mkulu wina wa ankhondo. Ndinapeza pasipoti yanga m’masabata oŵerengeka okha, mwa thandizo la wophunzira ameneyu. Komano ndinavutika mtima pamene ndinagwidwa chifukwa chogaŵira Nsanja ya Olonda nditatsala pang’ono kuchoka. Wapolisi wina ananditengera kwa mkulu wa State Security Police ku Athens. Ndinadabwa kwambiri kuona kuti anali mmodzi wa anansi anga! Wapolisiyo analongosola chifukwa chimene anandigwirira ndipo anampatsa mtokoma wa magazini. Mnansi wangayo anatulutsa mulu wina wa makope a Nsanja ya Olonda m’desiki lake nati kwa ine: “Ndilibe makope atsopano. Kodi ndingatengepo kope?” Ha, ndinatonthozedwa chotani nanga kuona dzanja la Yehova m’nkhani zimenezi!
Kalasi ya 16 ya Gileadi, mu 1950, inali chochitika chokhutiritsa. Pamapeto ake, ananditumiza ku Cyprus, kumene posapita nthaŵi ndinapeza kuti chitsutso cha atsogoleri achipembedzo chinali chokakala monga momwe chinalili ku Greece. Kaŵirikaŵiri tinali kuyang’anizana ndi makamu otengeka maganizo ndi chipembedzo osonkhezeredwa mwauchinyama ndi ansembe a Orthodox. Mu 1953 sanakonzenso visa yanga ku Cyprus, ndipo ananditumiza ku Istanbul, Turkey. Kunonso, ndinakhalako nthaŵi yaifupi. Mavuto a ndale pakati pa Turkey ndi Greece anatanthauza kuti, ngakhale kuti ntchito yolalikira inali kubala zipatso zabwino, ndinafunikira kuchoka kumka ku gawo lina—Egypt.
Pamene ndinali m’ndende, Salmo 55:6, 7 linali kufika m’maganizo mwanga. Mmenemo Davide anafotokozamo za kukhumba kwake kuthaŵira ku chipululu. Sindinaganizire nkomwe kuti tsiku lina ndidzakhaladi kumeneko. Mu 1954, pambuyo pa ulendo wotopetsa wa masiku ambiri ndi sitima yapamtunda ndi boti la mu mtsinje wa Nile, ndinafika kumene ndinali kupita potsirizira pake—Khartoum, ku Sudan. Chinthu chokha chomwe ndinafuna kuchita chinali kusamba m’shawa ndi kukagona. Koma ndinaiŵala kuti dzuŵa linali lili pamutu. Madzi ake, amene anali kusungidwa m’thanki lokhala patsindwi, anandiŵaula m’mutu, zikumandikakamiza kuvala helementi kwa miyezi ingapo kufikira chilonda changa chitapola.
Nthaŵi zambiri ndinali wosungulumwa kumeneko, ndekhandekha pakati pa Sahara, makilomita zikwi zambiri kuchokera ku mpingo wapafupipo, koma Yehova anandichirikiza ndi kundipatsa nyonga ya kupitiriza. Nthaŵi zina chilimbikitso chinali kuchokera kosayembekezereka. Tsiku lina ndinakumana ndi mkulu wa myuziyamu ya Khartoum. Anali munthu womasuka maganizo, ndipo tinakambitsirana mokondweretsa. Atadziŵa kuti ndinali m’Giriki, anandipempha ngati ndingamthandize mwa kumka kumyuziyamu kukatembenuza zilembo zina zolembedwa ndi anthu zopezedwa m’tchalitchi china cha m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi. Nditakhala m’chipinda chapansi chopanda mpweya wabwino wokwanira kwa maola asanu, ndinapeza sosala yokhala ndi dzina la Yehova, Tetragrammaton ija. Tangoganizani mmene chimwemwe changa chinalili! Sikwachilendo kuona dzina la Mulungu m’matchalitchi ku Ulaya, komatu zimenezo zinali zachilendo mkati mwa Sahara!
Pambuyo pa msonkhano wa mitundu mu 1958, ndinasankhidwa kukhala woyang’anira woyendera nthambi kukafikira abale m’maiko ndi magawo 26 ku Middle ndi Near East ndi kumadera a Mediterranean. Kaŵirikaŵiri sindinadziŵe mmene ndingatulukire mu mkhalidwe wovuta, koma Yehova nthaŵi zonse anakonza njira yotulukira.
Ndinachita chidwi nthaŵi zonse ndi chisamaliro chimene gulu la Yehova limasonyeza kwa Mboni zimene zili kutali m’maiko ena. Pa nthaŵi ina, ndinakumana ndi mbale wachimwenye amene anali kugwira ntchito pamalo okumba mafuta. Zichita ngati kuti iyeyo ndiye anali Mboni yokha m’dzikolo. Anali ndi zofalitsa za zinenero 18 zosiyanasiyana m’kabati mwake, zimene anapatsa antchito anzake. Ngakhale kunoko, kumene zipembedzo zonse zachilendo zinali zoletsedwa kwambiri, mbale wathuyo sanaiŵale thayo lake la kulalikira uthenga wabwino. Antchito anzake anachita chidwi kuona kuti woimira chipembedzo chake anatumizidwa kudzamuona.
Chaka cha 1959 ndinafika mu Spain ndi Portugal. Maiko aŵiri onsewo anali mu ulamuliro wotsendereza wa asilikali panthaŵiyo, ntchito ya Mboni za Yehova ili yoletsedwa kwambiri. Ndinali wokhoza kuchititsa misonkhano yoposa zana m’mwezi umodzi ndikumalimbikitsa abale kusagonja ngakhale kuti panali zovuta.
Wosakhalanso Ndekha
Kwa zaka zoposa 20, ndinali kutumikira Yehova mu utumiki wanthaŵi zonse monga mbeta, komano mwadzidzidzi ndinatopa pa maulendo anga osathawo ndilibe malo enieni okhala odziŵika. Inali nthaŵiyi pamene ndinakumana ndi Annie Bianucci, mpainiya wapadera ku Tunisia. Tinakwatirana mu 1963. Kukonda kwake Yehova ndi choonadi, kudzipereka kwake mu utumiki kophatikizidwa ndi luso lake la kuphunzitsa, ndi kudziŵa kwake zinenero zinakhala dalitso lenileni mu ntchito yathu yaumishonale ndi yadera kumpoto ndi kumadzulo kwa Afirika ndi ku Italy.
Mu August 1965 ine ndi mkazi wanga tinatumizidwa ku Dakar, Senegal, kumene ndinali ndi mwaŵi wa kulinganiza ofesi yanthambi ya m’dzikolo. Senegal anali dziko lodziŵika chifukwa cha kulolera kwake zipembedzo, mosakayikira chifukwa cha pulezidenti wake, Leopold Senghor, mmodzi wa atsogoleri oŵerengeka a Maboma a mu Afirika amene analembera Pulezidenti Banda wa Malaŵi mochirikiza Mboni za Yehova pa nthaŵi ya chizunzo chowopsa chimene chinachitika m’Malaŵi m’ma 1970.
Dalitso Lalikulu la Yehova
Mu 1951, pamene ndinachoka ku Gileadi kumka ku Cyprus, ndinayenda ulendowo ndi masutukesi asanu ndi aŵiri. Pochoka kupita ku Turkey, ndinali ndi asanu okha. Koma kuyenda kwambiri choncho, ndinafunikira kuzoloŵera kunyamula katundu wa mlingo wa makilogalamu 20, (mapaundi 44) amene anaphatikizapo mafaelo anga ndi taipi imene inanga “mwana” wanga. Tsiku lina ndinanena kwa Mbale Knorr, pulezidenti wapanthaŵiyo wa Watch Tower Society kuti: “Mumanditchinjiriza pa kukondetsa zinthu zakuthupi. Mumandichititsa kukhala ndi katundu wa makilogalamu 20, ndipo zikundiyendera bwino.” Sindinamve kukhala womanidwa chifukwa cha kusakhala ndi zinthu zambiri.
Vuto langa lalikulu pa maulendo anga linali la kuloŵa ndi kutuluka m’maiko. Tsiku lina, ndili m’dziko limene ntchito inali yoletsedwa, ofesala wina wa kasitomu anayamba kusanthula mafaelo anga. Zimenezi zikanaika Mboni za m’dzikolo pangozi, chotero ndinatulutsa kalata m’jekete langa yochokera kwa mkazi wanga ndipo ndinati kwa ofesala wa kasitomuyo: “Ndikuona kuti mumakonda kuŵerenga makalata. Kodi mungakondenso kuŵerenga kalata iyi ya mkazi wanga, imene siili m’mafaelo?” Atachita manyazi, anasiya nandilola kupyola.
Chiyambire 1982 ine ndi mkazi wanga takhala tikutumikira monga amishonale ku Nice, kummwera kwa France. Sindingathe kuchita zambiri monga kale chifukwa cha kufooka kwa thupi. Koma zimenezo sizikutanthauza kuti chimwemwe chathu chazimiririka. Taona kuti ‘kuchititsa kwathu sikuli chabe.’ (1 Akorinto 15:58) Ndakhala ndi chimwemwe cha kuona anthu ochuluka amene ndakhala ndi mwaŵi wa kuphunzira nawo zaka zapitazo ndiponso ziŵalo zoposa 40 za banja langa zikumatumikira Yehova mokhulupirika.
Palibiretu chisoni chimene ndili nacho chifukwa cha kudzimana kumene ndachita m’moyo wa ‘kuwolokera kwina.’ Ndi iko komwe, palibe kudzimana kumene timapanga kumene tingakuyerekezere ndi zimene Yehova ndi Mwana wake, Kristu Yesu, atichitira. Pamene ndikumbukira zaka 60 zapitazo zimene ndadziŵa choonadi, ndinganene kuti Yehova wandidalitsa kwambiri. Monga momwe Miyambo 10:22 imanenera, “madalitso a Yehova alemeretsa.”
Mosakayikira, “chifundo [cha Yehova] chiposa moyo makomedwe ake.” (Salmo 63:3) Pamene zovuta za ukalamba zikuchuluka, kaŵirikaŵiri ndimatchula mawu a wamasalmo wouziridwa m’mapemphero anga kuti: “Ndikhulupirira inu, Yehova: ndisachite manyazi nthaŵi zonse. Pakuti inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga. Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwiza zanu. Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu.”—Salmo 71:1, 5, 17, 18.
[Chithunzi patsamba 25]
Ine ndi mkazi wanga, Annie, lerolino
-
-
“Mphatso Yodabwitsa Yochokera kwa Yehova”Nsanja ya Olonda—1996 | November 1
-
-
“Mphatso Yodabwitsa Yochokera kwa Yehova”
KOPE la Nsanja ya Olonda ya May 1, 1996, linali ndi nkhani yofotokoza momvekera bwino uchete wachikristu ndi mmene tingalinganizire mathayo athu kwa Yehova ndi kwa “Kaisara.” (Mateyu 22:21) Tamva mawu ambiri oyamikira chidziŵitso chatsopanocho chimene chinaperekedwa. Pakati pa iwo pali kalata yotsatirayi, yolembedwa ndi Mboni mu Greece ndipo inalembera Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova:
“Ndikufuna kukuthokozani kwambiri nonsenu abale okondedwa kaamba ka kutisamalira bwino motere mwauzimu. Pokhala nditathera zaka zisanu ndi zinayi m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro changa chachikristu, ndithudi ndikuyamikira malingaliro odabwitsa amenewo a m’kope la Nsanja ya Olonda ya May 1, 1996. (Yesaya 2:4) Iyi inali mphatso yodabwitsa yochokera kwa Yehova.—Yakobo 1:17.
“Mmene ndimasangalala ndi nkhani zimenezi, ndinakumbukira ndemanga inayake mu Nsanja ya Olonda yapapitapo (August 1, 1994, tsamba 14): ‘Mwachionekere, kulolera kuli mkhalidwe wamtengo wapatali, umene umatisonkhezera kukonda Yehova koposerapo.’ Inde, abale, ndikuthokoza Yehova kuti ndili mbali ya gulu lake lachikondi ndi lachifundo, limene limasonyeza nzeru yake moonekera bwino.—Yakobo 3:17.
“Kuwala kowonjezereka mu Nsanja ya Olonda ya May 1 kwalandiridwa ndi manja aŵiri muno mu Greece, makamaka ndi aja amene anathera zaka zingapo m’ndende kapena amene adakali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ndikukuthokozani kachiŵirinso. Yehova akulimbikitsenitu ndi mzimu wake kuti mupitirize kutipatsa chakudya chauzimu chofunika m’nthaŵi zovuta zino.”
-