-
Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya ChipulumutsoNsanja ya Olonda—1999 | February 15
-
-
20. Kodi ndi njira zina ziti zimene timasungira “mawu” a Yesu?
20 Kodi tingasonyeze motani kuti dipo timaliyamikira kuchokera pansi pa mtima? Atatsala pang’ono kumangidwa, Yesu anati: “Ngati wina akonda Ine, adzasunga mawu anga.” (Yohane 14:23) “Mawu” a Yesu amaphatikizapo lamulo lake lonena kuti tizitengamo mbali mwachangu pokwaniritsa ntchitoyi: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo.” (Mateyu 28:19) Kumvera Yesu kumafunanso kuti tizisonyeza chikondi kwa abale athu auzimu.—Yohane 13:34, 35.
21. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupezeka pa phwando la Chikumbutso pa April 1?
21 Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zimene tingasonyezere kuti dipo timaliyamikira ndiyo mwa kupezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu, chimene chaka chino chidzakhalako pa April 1.a Chimenechonso chili mbali ya “mawu” a Yesu, popeza kuti poyambitsa phwando limeneli, Yesu analamula otsatira ake kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Mwa kupezeka pa chochitika chofunika koposa chimenechi ndiponso mwa kutsatira mosamalitsa zonse zimene Kristu anatilamula, tidzasonyeza kuti timakhulupirira zedi kuti dipo la Yesu ndilo njira ya Mulungu ya chipulumutso. Ndithudi, “palibe chipulumutso mwa wina yense.”—Machitidwe 4:12.
-
-
Njira ya Chikondi SilepheraNsanja ya Olonda—1999 | February 15
-
-
Njira ya Chikondi Silephera
“Funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu.”—1 AKORINTO 12:31.
1-3. (a) Kodi kuphunzira kusonyeza chikondi kukufanana motani ndi kuphunzira chinenero china? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse kuphunzira kusonyeza chikondi kukhala kovuta?
KODI munayesapo kuphunzira chinenero china? N’zovuta, kunena mwachidule. Komatu mwana wamng’ono angaphunzire chinenero mwa kumangochimvetsera. Ubongo wake umasunga mamvekedwe ndi matanthauzo a mawu pamene akuyankhulidwa, moti posapita nthaŵi mwanayo amayamba kuchiyankhula bwino chinenerocho, mwinanso mosaphophonya. Si mmene zilili ndi akulu. Mobwerezabwereza timafufuza m’dikishonale ya chinenero chinacho, kungoti tidziŵe mawu ake angapo osavuta. Koma m’kupita kwa nthaŵi ndiponso mwa kuchiphunzira mokwanira, timayamba kulingalira m’chinenero chatsopanocho ndiponso kuchiyankhula kumakhala kosavuta.
2 Kuphunzira kusonyeza chikondi kuli ngati kuphunzira chinenero china. Zoonadi, anthu amabadwa ndi mlingo winawake wa mkhalidwe waumulungu umenewu. (Genesis 1:27; yerekezerani ndi 1 Yohane 4:8.) Komabe, kuphunzira kusonyeza chikondi kumafuna kuyesetsa kwambiri—makamaka lerolino, pamene chikondi chachibadwidwe chikusoŵa kwambiri. (2 Timoteo 3:1-5) Nthaŵi zina zilidi motero m’banja mwenimwenimo. Inde, ambiri amakulira m’mikhalidwe yovuta mmene mawu osonyeza chikondi satchulidwa kwenikweni—ngati amatchulidwa n’komwe. (Aefeso 4:29-31; 6:4) Choncho kodi tingaphunzire motani kusonyeza chikondi
-