Zimene Owerenga Amafunsa
N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Tizivutika?
Mulungu si amene amachititsa kuti tizivutika. Baibulo limati: “N’kutali ndi Mulungu kuchita choipa.” (Yobu 34:10) Nangano ndi ndani amene amachititsa kuti tizivutika?
Yesu ananena kuti Satana ndi “wolamulira wa dziko” lino. (Yohane 14:30) N’zoona kuti Yehova ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ndipo udindo umenewu sangasiyire wina aliyense. Komabe, Mulungu walola kuti Satana alamulire anthu ambiri kwakanthawi.—1 Yohane 5:19.
Koma kodi Satana ndi wolamulira wotani? Iye ndi wakupha ndiponso wabodza kungoyambira panthawi yoyamba imene analankhula ndi anthu. Satana ndi amene akusokoneza ndiponso kubweretsa mavuto ambiri pa anthu. Yesu anamuimba mlandu Satana kuti: “Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Yesu ananenanso kuti anthu amene ankafuna kumupha anali ana a Satana. Iwo anadzipanga okha kukhala ana ake chifukwa chotsatira zochita zake mogwirizana ndi mwambi wakuti mwana mbuu make mbuu.
Satana ndi amene akulimbikitsa anthu kuti akhale ndi maganizo ochita zinthu zoipa monga kuphana. Mwachitsanzo, pulofesa R. J. Rummel, yemwe anali pa yunivesite ya Hawaii, ku America, anayerekezera kuti kuyambira m’chaka cha 1900 mpaka 1987, maboma osiyanasiyana anapha anthu okwana 169,198,000 polimbana pa nkhani zandale, populula anthu afuko lina, ndi kupha anthu mwachisawawa. Chiwerengero chimenechi sichikuphatikizapo anthu amene anaphedwa pa nkhondo zimene zinkachitika pa nthawi imeneyi.
Ngati Mulungu si amene amachititsa mavuto, n’chifukwa chiyani amalola kuti tizivutika? N’chifukwa choti pali nkhani zina zimene zinachitika kalekale zokhudza wina aliyense zoti zithetsedwe kaye. Tiyeni tione imodzi mwa nkhani zimenezi.
Pachiyambi penipeni, Adamu ndi Hava anasankha okha kukhala ku mbali ya Satana. Iwo anakana ulamuliro wa Mulungu, n’kusankha kumadzilamulira okha ndipo mwakuchita zimenezi anasankha kulamuliridwa ndi Mdyerekezi.—Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9.
Popeza Yehova ndi Mulungu wa chilungamo, walola kuti papite nthawi yaitali anthu tikudzilamulira tokha n’cholinga choti tione kuti ulamuliro wabwino ndi uti. Kodi taona zotani? Taona kuti ulamuliro wa anthu wotsogozedwa ndi Satana umangobweretsa mavuto okhaokha. Ndithudi, zimene Mulungu wachitazi zathandiza kwambiri anthu. Zathandiza bwanji? Anthu amene akuzindikira zimenezi ndi kuzikhulupirira ali ndi mwayi wosonyeza kuti ndi ofunitsitsa kulamuliridwa ndi Mulungu. Anthu amene akuphunzira mfundo za Mulungu ndi kuzitsatira angayembekezere kudzakhala ndi moyo kosatha.—Yohane 17:3; 1 Yohane 2:17.
Ndithudi, masiku ano Satana akulamulira dzikoli mwankhanza. Koma sachita zimenezi kwa nthawi yaitali chifukwa posachedwapa Yehova adzagwiritsa ntchito Mwana wake kuti “awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yohane 3:8) Motsogozedwa ndi Mulungu, Yesu adzathetseratu mavuto athu onse ndipo tidzakhala osangalala. Iye adzaukitsa anthu mabiliyoni ambirimbiri amene akhala akuvutika ndiponso kumwalira.—Yohane 11:25.
Kuukitsidwa kwa Yesu ndi chitsanzo chabwino chosonyeza kupambana kwa Mulungu pantchito za Mdyerekezi. Chimenechi n’chitsanzo cha zimene zidzachitikire anthu amene akusankha ulamuliro wa Mulungu. (Machitidwe 17:31) Baibulo limatithandiza kumvetsa zimene zidzachitike nthawi imeneyi ndi mawu olimbikitsa awa: “Mulungu mwini adzakhala nawo [anthu]. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.