Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 2/1 tsamba 8
  • Kodi Mulungu Amasamala za Ine?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amasamala za Ine?
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • N’chifukwa Chiyani Panopa Timakumana ndi Mavuto Ambiri?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mdani wa Moyo Wosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2009
w09 2/1 tsamba 8

Kodi Mulungu Amasamala za Ine?

Ambiri amanena kuti:

▪ “Mulungu ndi wapamwamba kwambiri moti sangaganizire mavuto anga.”

▪ “Sindikukhulupirira kuti amasamala za ine.”

Kodi Yesu anati chiyani?

▪ “Mpheta zisanu amazigulitsa makobili awiri ochepa mphamvu, si choncho nanga? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imaiwalika kwa Mulungu. Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu analiwerenga. Musachite mantha; ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” (Luka 12:6, 7) Ndithudi, Yesu ankaphunzitsa kuti Mulungu amatisamalira.

▪ “Musamade nkhawa n’kumati, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti amitundu akufunafuna mwakhama zinthu zonse zimenezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti zinthu zonsezi inu mukuzisowa.” (Mateyo 6:31, 32) Yesu ankadziwa kuti Mulungu amadziwa zimene timafunika pamoyo wathu.

BAIBULO limanena mwachindunji kuti Mulungu amatisamalira. (Salmo 55:22; 1 Petulo 5:7) Komano n’chifukwa chiyani timavutika kwambiri masiku ano? Ngati Mulungu amatikonda komanso ndi wamphamvuyonse, n’chifukwa chiyani sakuthetsa mavutowa?

Yankho lake likukhudza mfundo imene anthu ambiri samaidziwa, yakuti Satana Mdyerekezi ndiye wolamulira wa dziko loipali. Pomuyesa Yesu, Satana anamuuza kuti amupatsa maufumu onse adzikoli. Iye anati: “Ndikupatsani ulamuliro wonsewu ndi ulemerero wake wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.”​—Luka 4:5-7.

Kodi ndani anamuika Satana kukhala wolamulira wa dzikoli? Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, atamvera Satana ndi kukana malamulo a Mulungu, anasonyeza kuti asankha Satana kukhala wolamulira wawo. Kuchokera panthawiyi, Yehova Mulungu walola kuti papite nthawi yosonyeza kuti ulamuliro wa Satana ndi wolephera. Yehova sakakamiza anthu kuti azimutumikira koma wapereka mwayi woti tibwerere kwa iye.​—Aroma 5:10.

Popeza Mulungu amatisamalira, wakonza zoti Yesu atipulumutse ku ulamuliro wa Satana. Posachedwapa, Yesu ‘awononga iye amene ali ndi njira yochititsa imfa, ndiye Mdyerekezi.’ (Aheberi 2:14) Mwakuchita zimenezi, iye ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi.’​—1 Yohane 3:8.

Paradaiso adzabwezeretsedwa padziko pano. Panthawi imeneyo, Mulungu “adzapukuta msozi uliwonse m’maso [mwa anthu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4, 5.a

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mumve zambiri pankhani ya chifukwa chake Mulungu walolera kuti tizivutika, onani buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? mutu 11.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Paradaiso adzabwezeretsedwa padziko pano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena