Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Sungani Mtendere m’Banja Mwanu
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 11

      Sungani Mtendere m’Banja Mwanu

      1. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingachititse magaŵano m’mabanja?

      ACHIMWEMWE ali awo amene ali m’mabanja mmene muli chikondi, chifundo, ndi mtendere. Tikhulupirira banja lanu lili lotero. Nzachisoni kuti mabanja ambiri sali otero ndipo ali ogaŵanika pazifukwa zosiyanasiyana. Kodi nchiyani chimene chimagaŵanitsa mabanja? M’mutu uno tidzakambitsirana zinthu zitatu. M’mabanja ena, anthu amakhala ndi zipembedzo zosiyana. Mwa ena, ana angakhale ndi makolo owabala osiyana. Mwa enanso, ntchito yochirikizira moyo kapena kufuna zinthu zakuthupi zambiri zimagaŵanitsa apabanja. Komabe, mikhalidwe imene imagaŵanitsa banja lina siingakhale vuto lalikulu ku banja lina. Kodi nchiyani chimachititsa kusiyana?

      2. Kodi ena amakafuna kuti chithandizo pa moyo wa banja, koma kodi chitsogozo chabwino kopambana chimachokera kuti?

      2 Chimodzi cha izo ndicho kaonedwe ka zinthu. Ngati mumayesayesa moona mtima kumvetsetsa lingaliro la mnzanu, mudzakhala wokhoza kuzindikira mmene mungasungire umodzi wa banja. Chinthu chachiŵiri ndicho amene mumafunako chithandizo. Anthu ambiri amalondola uphungu wa anzawo akuntchito, anansi awo, olemba m’madanga a manyuzipepala, kapena aphungu ena. Komabe, ena apeza zimene Mawu a Mulungu amanena za mkhalidwewo, ndiyeno amagwiritsira ntchito zimene amaphunzira. Kodi kuchita zimenezi kungathandize motani banja kusunga mtendere?—2 Timoteo 3:16, 17.

      NGATI MWAMUNA WANU ALI NDI CHIKHULUPIRIRO CHINA

      Chithunzi patsamba 130

      Yesani kumvetsetsa lingaliro la mnzanu

      3. (a) Kodi uphungu wa Baibulo ndi wotani ponena za kukwatirana ndi munthu wa chikhulupiriro china? (b) Kodi ndi mapulinsipulo ofunika ati amene amagwirabe ntchito ngati wina wa muukwati ali wokhulupirira koma osati mnzakeyo?

      3 Baibulo limatichenjeza mwamphamvu kusakwatirana ndi munthu wa chikhulupiriro china. (Deuteronomo 7:3, 4; 1 Akorinto 7:39) Komabe, mwina inu munaphunzira choonadi cha Baibulo mutakwatirana kale koma mwamuna wanu sanatero. Pamenepo bwanji? Ndithudi, malumbiro aukwati akugwirabe ntchito. (1 Akorinto 7:10) Baibulo limagogomezera kukhalitsa kwa ukwati ndipo limalimbikitsa okwatirana kuthetsa mavuto awo m’malo mwa kuwathaŵa. (Aefeso 5:28-31; Tito 2:4, 5) Nanga bwanji ngati mwamuna wanu amakuletsani mwamphamvu kuchita chipembedzo chanu cha m’Baibulo? Iye angayese kukuletsani kupita kumisonkhano ya mpingo, kapena anganene kuti samafuna mkazi wake kumapita kunyumba ndi nyumba, akumalankhula za chipembedzo. Kodi mungachitenji?

      4. Kodi mkazi angasonyeze motani kumvetsetsa ngati mwamuna wake sali naye m’chikhulupiriro chimodzi?

      4 Dzifunseni kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji mwamuna wanga amaganiza choncho?’ (Miyambo 16:20, 23) Ngati iye sakumvetsetsadi zimene mukuchita, angakhale wodera nkhaŵa za inu. Kapena angakhale akuvutitsidwa ndi achibale ake chifukwa chakuti simukuchitanso miyambo ina yofunika kwambiri kwa iwo. Mwamuna wina anati: “Potsala ndekha m’nyumba, ndinamva monga wosiyidwa.” Mwamunayu anaona monga kuti chipembedzo chinali kumlanda mkazi wake. Komabe, kunyada kunamlepheretsa kuvomera kuti anali kusungulumwa. Mwamuna wanu angafunikire kusonyezedwa kuti kukonda kwanu Yehova sikutanthauza kuti tsopano simumamkonda kwambiri kuposa kale. Patulani nthaŵi ya kucheza naye.

      5. Kodi ndi kulinganiza zinthu kotani kumene mkazi ayenera kuchita amene mwamuna wake ali wa chikhulupiriro china?

      5 Komabe, palinso chinthu china chofunika koposa chimene muyenera kuchilingalira ngati mufuna kuchita ndi mkhalidwewo mwanzeru. Mawu a Mulungu amalimbikitsa akazi kuti: “Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.” (Akolose 3:18) Motero, limachenjeza za mzimu wa kudzigangira. Ndiponso, mwa kunena kuti “monga kuyenera mwa Ambuye,” lembali limasonyeza kuti mkazi wogonjera kwa mwamuna wake ayeneranso kugonjera kwa Ambuye. Pafunika kulinganiza bwino.

      6. Kodi ndi mapulinsipulo otani amene mkazi wachikristu ayenera kukumbukira?

      6 Kwa Mkristu, kupezeka pamisonkhano ya mpingo ndi kuchitira umboni kwa ena za chikhulupiriro chanu cha Baibulo ndiko mbali zofunika kwambiri za kulambira koona zimene siziyenera kunyalanyazidwa. (Aroma 10:9, 10, 14; Ahebri 10:24, 25) Pamenepo, kodi mungachitenji ngati munthu akuletsani mwachindunji kulabadira zofunika za Mulungu zakutizakuti? Atumwi a Yesu Kristu analengeza kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Chitsanzo chawo chimatipatsa choonerapo chogwira ntchito pamikhalidwe yambiri m’moyo. Kodi chikondi chanu pa Yehova chidzakusonkhezerani kumpatsa kulambira koyenera iye yekha? Panthaŵi imodzimodzi, kodi chikondi chanu ndi ulemu kwa mwamuna wanu zidzakuchititsani kuyesa kuchita zimenezi mwa njira yolandirika kwa iye?—Mateyu 4:10; 1 Yohane 5:3.

      7. Kodi mkazi wachikristu ayenera kukhala wofunitsitsa kuchitanji?

      7 Yesu anasonyeza kuti si nthaŵi zonse pamene izi zidzakhala zotheka. Iye anachenjeza kuti chifukwa cha chitsutso pa kulambira koona, okhulupirira a m’mabanja ena angadzione kukhala opatulidwa, monga kuti lupanga linawadula kwa ena onse m’banja. (Mateyu 10:34-36) Zimenezi zinachitika kwa mkazi wina ku Japan. Iye anatsutsidwa ndi mwamuna wake kwa zaka 11. Mwamunayo anamzunza iye ndipo kaŵirikaŵiri anamkhomera kunja. Koma iye anapirira. Mabwenzi mumpingo wachikristu anamthandiza. Anapemphera mosaleka ndi kupeza chilimbikitso chachikulu pa 1 Petro 2:20. Mkazi wachikristu ameneyu anali wokhutira maganizo kuti ngati anakhalabe wolimba, tsiku lina mwamuna wake adzagwirizana naye pakulambira Yehova. Ndipo anaterodi.

      8, 9. Kodi mkazi ayenera kuchita motani kuti apeŵe kuika zopinga zosafunika kwa mwamuna wake?

      8 Pali zinthu zambiri zimene mungachite zothandiza mwamuna wanu kusintha maganizo. Mwachitsanzo, ngati mwamuna wanu amatsutsa chipembedzo chanu, musampatse zifukwa zodandaulira m’zinthu zina. Sungani nyumba kukhala yaukhondo. Samalani maonekedwe anu. Khalani wopatsa m’mawu achikondi ndi oyamikira. M’malo mokhala wosuliza, khalani wochirikiza. Sonyezani kuti mumadalira iye monga mutu wanu. Musabwezere ngati muona kuti wakulakwirani. (1 Petro 2:21, 23) Khalani wololera kupanda ungwiro kwaumunthu, ndipo ngati pabuka mkangano, khalani woyamba kupepesa modzichepetsa.—Aefeso 4:26.

      9 Musalole misonkhano kukhala chifukwa chochedwetsera chakudya chake. Mungagaŵanenso mu utumiki wachikristu panthaŵi zimene mwamuna wanu sali panyumba. Nkwanzeru kwa mkazi wachikristu kusalalikira mwamuna wake ngati samafuna zimenezo. M’malo mwake, ayenera kutsatira uphungu wa mtumwi Petro wakuti: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi [ulemu wanu waukulu, NW].” (1 Petro 3:1, 2) Akazi achikristu amayesayesa kwambiri kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu.—Agalatiya 5:22, 23.

      PAMENE MKAZI ALI NDI CHIKHULUPIRIRO CHINA

      10. Kodi mwamuna wokhulupirira ayenera kuchita motani kulinga kwa mkazi wake ngati ali wa chikhulupiriro china?

      10 Bwanji ngati mwamuna ali wokhulupirira koma osati mkazi wake? Baibulo limapereka chitsogozo pa mikhalidwe yoteroyo. Limati: “Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.” (1 Akorinto 7:12) Limalangizanso amuna kuti: “Kondani akazi anu.”—Akolose 3:19.

      11. Kodi mwamuna angasonyeze motani kuti ali wozindikira bwino ndi wosamala pochita umutu wake pa mkazi wake wa chikhulupiriro china?

      11 Ngati ndinu mwamuna wa mkazi wa chikhulupiriro china, khalani wosamala kwambiri kusonyeza ulemu kwa mkazi wanu ndi kulolera malingaliro ake. Monga munthu wachikulire, ayenera kukhala ndi ufulu winawake wa kutsatira zikhulupiriro za chipembedzo chake, ngakhale ngati simukugwirizana nazo. Panthaŵi yoyamba imene mulankhula naye za chikhulupiriro chanu, musayembekezere kuti pamenepo adzasiya zimene wakhulupirira kwa nthaŵi yaitali ndi kutsatira zina zatsopano. M’malo mwa kufulumira kutsutsa kuti zachipembedzo zimene iye ndi a banja lake akhala akuchita kwa nthaŵi yaitali zili zonyenga, yesani moleza mtima kulingalira naye za m’Malemba. Mwina amaona kukhala wonyalanyazidwa pamene mupereka nthaŵi yaikulu ku zochita za mpingo. Angatsutse zochita zanu za kutumikira Yehova, pamene kwenikweni pansi pa mtima akunena kuti: “Ndifuna muzikhalanso ndi ine nthaŵi yochuluka!” Lezani mtima. Mwa chifundo chanu chachikondi, m’kupita kwa nthaŵi angathandizidwe kuzindikira kulambira koona.—Akolose 3:12-14; 1 Petro 3:8, 9.

      KUPHUNZITSA ANA

      12. Ngakhale ngati mwamuna ndi mkazi ali ndi zikhulupiriro zosiyana, kodi mapulinsipulo a Malemba ayenera kugwiritsidwa ntchito motani pophunzitsa ana awo?

      12 M’banja losagwirizana pakulambira, kuphunzitsa ana malangizo achipembedzo kumakhala kovuta nthaŵi zina. Kodi mapulinsipulo a Malemba ayenera kugwiritsiridwa ntchito motani? Baibulo limapatsa tate thayo lalikulu la kuphunzitsa ana, koma mayinso ali ndi mbali yofunika. (Miyambo 1:8; yerekezerani ndi Genesis 18:19; Deuteronomo 11:18, 19.) Ngakhale ngati savomereza umutu wa Kristu, tate amakhalabe mutu wa banja.

      13, 14. Ngati mwamuna aletsa mkazi wake kupita ndi ana kumisonkhano yachikristu kapena kuphunzira nawo, kodi mkaziyo angachitenji?

      13 Atate ena osakhulupirira samaletsa ngati mayi aphunzitsa ana nkhani zachipembedzo. Ena amaletsa. Bwanji ngati mwamuna wanu sakulolani kupita ndi ana kumisonkhano ya mpingo kapena ngakhale kukuletsani kuphunzira nawo Baibulo panyumba? Pamenepo mudzafunikira kuganizira mathayo anu ena—thayo lanu kwa Yehova Mulungu, kwa umutu wa mwamuna wanu, ndi kwa ana anu okondedwa. Kodi mungayanjanitse motani zimenezi?

      14 Ndithudi mudzapempherera nkhaniyo. (Afilipi 4:6, 7; 1 Yohane 5:14) Koma potsirizira pake, ndinu amene muyenera kupanga chosankha cha njira imene mudzatenga. Ngati muchita mwanzeru, mukumamveketsa bwino kwa mwamuna wanu kuti simukutsutsa umutu wake, chitsutso chake chingachepe m’kupita kwa nthaŵi. Ngakhale ngati mwamuna wanu amakuletsani kupita ndi ana anu kumisonkhano kapena kuphunzira nawo Baibulo, mukhozabe kuwaphunzitsa. Polankhula nawo masiku onse ndi mwa kupereka chitsanzo chabwino, yesani kuwaphunzitsa kukonda Yehova, kukhulupirira Mawu ake, ndi kulemekeza makolo—kuphatikizapo atate awo—kudera nkhaŵa anthu ena, ndi kugwira ntchito mwakhama. M’kupita kwa nthaŵi, tateyo angaone zotulukapo zabwino ndipo angaone phindu la kuyesayesa kwanu kwakhama.—Miyambo 23:24.

      15. Kodi tate wokhulupirira ali ndi thayo lotani pakuphunzitsa ana?

      15 Ngati ndinu mwamuna wokhulupirira koma osati mkazi wanu, pamenepo muyenera kusenza thayo la kulera ana anu “m’chilango cha Yehova ndi kuwawongolera maganizo m’njira yake.” (Aefeso 6:4, NW) Pochita zimenezo, muyenera kukhala wokoma mtima, wachikondi, ndi wachifundo kwa mkazi wanu.

      NGATI CHIPEMBEDZO CHANU CHILI CHOSIYANA NDI CHA MAKOLO ANU

      16, 17. Kodi ndi mapulinsipulo a Baibulo otani amene ana ayenera kukumbukira ngati alondola chikhulupiriro chosiyana ndi cha makolo awo?

      16 Sikulinso kwachilendo kuona ngakhale ana aang’ono akutsatira malingaliro achipembedzo osiyana ndi a makolo awo. Kodi nzimene zachitika kwa inu? Ngati ndi choncho, Baibulo lili ndi uphungu kwa inu.

      17 Mawu a Mulungu amati: “Mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amako.” (Aefeso 6:1, 2) Zimenezo zimaphatikizapo ulemu woyenera kwa makolo. Komabe, ngakhale kuti kumvera makolo kuli kofunika, sikuyenera kuchitidwa mwa kunyalanyaza Mulungu woona. Pamene mwana afika pamsinkhu woyamba kupanga zosankha, amakhala ndi mlingo wokulirapo wa thayo la zochita zake. Zimenezi nzoona osati chabe ndi lamulo la boma komanso makamaka ponena za lamulo laumulungu. Baibulo limati: “Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.”—Aroma 14:12.

      18, 19. Ngati ana ali ndi chipembedzo chosiyana ndi cha makolo awo, kodi angathandize motani makolo awo kumvetsetsa bwino chikhulupiriro chawo?

      18 Ngati zikhulupiriro zanu zikuchititsani kusintha moyo wanu, yesani kumvetsetsa malingaliro a makolo anu. Mwachionekere, iwo angakondwere pamene kuphunzira kwanu Baibulo ndi kugwiritsira ntchito ziphunzitso zake kumakuchititsani kuwalemekeza kwambiri, kuwamvera kwambiri, ndi kukhala wakhama pa zimene akuuzani kuchita. Komabe, ngati chikhulupiriro chanu chatsopano chimakuchititsaninso kukana zikhulupiriro ndi miyambo imene iwo amatsatira, angaone kuti mukutaya choloŵa chimene akufuna kukupatsani. Angaoperenso ubwino wanu ngati zimene mukuchita anthu sakuziyamikira kwanuko kapena ngati zikuchotsa maganizo anu pa kuchita zimene iwo aona kuti zingakuthandizeni kupita patsogolo mwakuthupi. Kunyada kungakhalenso chopinga. Angalingalire kuti, kwenikweni, mukusonyeza kuti ndinu wolondola ndipo iwo ali olakwa.

      19 Chotero, mwamsanga yesani kupanga makonzedwe akuti makolo anu akaonane ndi ena a akulu kapena Mboni zina zokhwima za mpingo wanu. Limbikitsani makolo anu kufika ku Nyumba ya Ufumu kuti akadzimverere okha zimene zimaphunzitsidwa ndi kudzionera okha mtundu wa anthu amene Mboni za Yehova zili. M’kupita kwa nthaŵi, makolo anu angafeŵetse mtima. Ngakhale pamene makolo atsutsa mouma khosi, kuwononga mabuku ofotokoza Baibulo, ndi kuletsa ana kupita kumisonkhano yachikristu, kaŵirikaŵiri pamakhalabe mipata yokaŵerengera kwina kwake, kukambitsirana ndi Akristu anzanu, ndi kuchitira umboni anthu ena mwamwaŵi ndi kuwathandiza. Mungapempherenso kwa Yehova. Achichepere ena ayembekezera kufikira atakula ndi kudzikhalira okha kuti ayambe kuchita zowonjezereka. Komabe, mulimonse mmene mkhalidwe ungakhalire panyumba, musaiŵale ‘kulemekeza atate anu ndi amayi anu.’ Chitani mbali yanu kuthandizira kusunga mtendere panyumba. (Aroma 12:17, 18) Choposa zonse, funani mtendere ndi Mulungu.

      VUTO LA KUKHALA KHOLO LOPEZA

      20. Kodi ana angakhale ndi malingaliro otani ngati tate kapena mayi wawo ali kholo lopeza?

      20 M’nyumba zambiri, mkhalidwe umene umabweretsa vuto lalikulu kwambiri si wa chipembedzo koma chibale. Mabanja ambiri lerolino ali ndi ana ochokera ku ukwati wakale wa kholo limodzi kapena onse aŵiri. M’banja lotero, ana angachite nsanje ndi kuipidwa kapena angakhale ndi vuto pofuna kumvera makolo onse. Chotulukapo, iwo angalefule kuyesayesa koona mtima kwa kholo lopezalo kuti likhale atate kapena amayi wabwino. Kodi nchiyani chimene chingathandize banja lopeza kukhala lachipambano?

      Chithunzi patsamba 138

      Kaya ndinu kholo lenileni kapena lopeza, dalirani chitsogozo cha Baibulo

      21. Mosasamala kanthu za mikhalidwe yawo yovuta, kodi nchifukwa ninji makolo opeza ayenera kufuna chithandizo ku mapulinsipulo opezeka m’Baibulo?

      21 Zindikirani kuti mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta imeneyo, mapulinsipulo a Baibulo amene adzetsa chipambano m’mabanja ena amagwiranso ntchito pambaliyi. Kunyalanyaza mapulinsipulo amenewo mwakanthaŵi, kungaoneke kuti kwathetsa vuto, koma mwachionekere kudzachititsa kusweka mtima pambuyo pake. (Salmo 127:1; Miyambo 29:15) Kulitsani nzeru ndi luntha—nzeru yogwiritsira ntchito mapulinsipulo aumulungu mukumakumbukira za mapindu amtsogolo, ndi luntha la kuzindikira chifukwa chimene ena m’banja amanenera kapena kuchita zinthu zina. Mufunikiranso kukhala wachifundo.—Miyambo 16:21; 24:3; 1 Petro 3:8.

      22. Kodi nchifukwa ninji kungakhale kovuta kwa ana kulemekeza kholo lopeza?

      22 Ngati ndinu kholo lopeza, mungakumbukire kuti pamene munali bwenzi chabe la banjalo, mwinamwake anawo anakulandirani bwino. Koma pamene mwakhala kholo lawo lopeza, mwina maganizo awo asintha. Pokumbukira kholo lawo lowabala limene silikukhalanso nawo, anawo angakhale akulimbana ndi vuto lofuna kumvera makolo onse, mwinamwake akumalingalira kuti mukufuna kulanda chikondi chimene ali nacho kwa kholo lawolo limene palibe. Nthaŵi zina, angakuuzeni poyera kuti sindinu atate wawo kapena amayi wawo. Mawu amenewo amapweteka. Komabe, ‘musakangaze mumtima mwanu kukwiya.’ (Mlaliki 7:9) Luntha ndi chifundo nzofunika kuti muchite ndi malingaliro a ana.

      23. Kodi chilango chingaperekedwe motani m’banja la ana opeza?

      23 Mikhalidwe imeneyo njofunika kwambiri pamene mukupereka chilango. Chilango choyenera nchofunika. (Miyambo 6:20; 13:1) Ndipo popeza kuti ana sali ofanana, chilangonso chingakhale chosiyana kwa wina ndi mnzake. Makolo ena opeza amaona kuti kumakhala bwino ngati kholo lobala nlimene liyamba kupereka chilango. Komabe, nkofunika kuti makolo onse aŵiri agwirizane pa chilangocho ndi kuchichirikiza, osati kukondera mwana amene munabala ndi kuchitira mwina kwa wopeza. (Miyambo 24:23) Kumvera nkofunika kwambiri, koma kulolera kupanda ungwiro kuyeneranso kukhalapo. Musachite mopambanitsa. Perekani chilango mwachikondi.—Akolose 3:21.

      24. Kodi nchiyani chimene chingathandize kupeŵa mavuto a makhalidwe osayenera pakati pa osiyana ziŵalo m’banja lopeza?

      24 Makambitsirano a banja angathandize kwambiri kuchinjiriza vuto. Angathandize banja kukumbukira nkhani zofunika kwambiri m’moyo. (Yerekezerani ndi Afilipi 1:9-11.) Akhozanso kuthandiza aliyense kuona mmene angathandizire banja kufikira zonulirapo zawo. Ndiponso, makambitsirano oona mtima a banja angapeŵetse mavuto a makhalidwe osayenera. Atsikana afunikira kudziŵa kuvala bwino ndi kudzisungira pamaso pa atate wawo wopeza ndi alongo awo opeza, ndipo anyamata ayenera kulangizidwa za khalidwe labwino kulinga kwa amayi wawo wopeza ndi alongo awo opeza.—1 Atesalonika 4:3-8.

      25. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene ingathandize kusunga mtendere m’banja lopeza?

      25 Pochita ndi vuto lapadera la kukhala kholo lopeza, khalani woleza mtima. Kumatenga nthaŵi kukulitsa chibale chatsopano. Kuchititsa ana amene simunabale kuti akukondeni ndi kukulemekezani kungakhale ntchito yaikulu kwambiri. Koma nkotheka. Mtima wanzeru ndi waluntha, limodzi ndi chikhumbo champhamvu chofuna kukondweretsa Yehova, ndizo kiyi yodzetsa mtendere m’banja lopeza. (Miyambo 16:20) Mikhalidwe yoteroyo ingakuthandizeninso kuchita ndi mikhalidwe inanso.

      KODI KUFUNA ZINTHU ZAKUTHUPI KUKUGAŴA BANJA LANU?

      26. Kodi kusoŵa zinthu zakuthupi ndi kaonedwe ka zinthu zakuthupi zingachititse magaŵano m’banja m’njira zotani?

      26 Kusoŵa zinthu zakuthupi ndi kaonedwe ka zinthu zakuthupi kungachititse magaŵano m’mabanja m’njira zambiri. Mwachisoni, mabanja ena amasokonezedwa ndi mikangano ya ndalama ndi chikhumbo cha kufuna kulemera—kapena kulemera koposerapo. Magaŵano angayambe pamene okwatirana onse aŵiri agwira ntchito ndipo akhala ndi maganizo akuti “ndalama zanga, ndi ndalama zako.” Ngakhale ngati mikangano ipeŵedwa, pamene okwatirana aŵiriwo agwira ntchito, angaone kuti ali otanganitsidwa ndi zochita kwakuti alibe nthaŵi yokwanira yokhala pamodzi. Mkhalidwe womakula m’dziko ndiwo wakuti tate akukakhala kutali ndi banja kwa nyengo yaitali—miyezi kapena ngakhale zaka—kuti apeze ndalama zochuluka kuposa zimene angapeze kwawo. Izi zingachititse mavuto aakulu kwambiri.

      27. Kodi ndi mapulinsipulo ena ati amene angathandize banja lokhala pa vuto la ndalama?

      27 Palibe malamulo amene angaikidwe ochitira ndi mikhalidwe imeneyi, chifukwa chakuti mabanja osiyanasiyana amakumana ndi mavuto osiyanasiyana ndi zosoŵa zosiyanasiyana. Chikhalirechobe, uphungu wa Baibulo ungathandize. Mwachitsanzo, Miyambo 13:10 imasonyeza kuti kupikisana kosafunikira kungapeŵedwe mwa kufunsirana “uphungu.” Zimenezi zimaloŵetsamo osati chabe kupereka malingaliro a munthuwe komanso kufuna chilangizo ndi kudziŵa mmene winayo amaonera nkhaniyo. Ndiponso, kupanga bajeti yabwino kungathandize kugwirizanitsa zoyesayesa za banja. Nthaŵi zina kumakhala kofunika—mwinamwake kwakanthaŵi chabe—kwa okwatirana onse aŵiri kukaloŵa ntchito kuti asamalire zolipirira zowonjezereka, makamaka pamene pali ana kapena ena amene amawasunga. Pamene zili choncho, mwamuna ayenera kusonyeza mkazi wake kuti akali ndi nthaŵi yocheza naye. Iye pamodzi ndi ana mwachikondi angathandize ntchito zina zimene kaŵirikaŵiri mkazi wake amazichita yekha.—Afilipi 2:1-4.

      28. Kodi ndi zikumbutso zotani, zimene ngati zitsatiridwa, zingathandize banja kukulitsa umodzi?

      28 Komabe, kumbukirani kuti ngakhale kuti ndalama zili zofunika m’dziko lino, sizimadzetsa chimwemwe. Sizimapatsa moyo ayi. (Mlaliki 7:12) Ndithudi, kukondetsa zinthu zakuthupi kungachititse ngozi yauzimu ndi yamakhalidwe. (1 Timoteo 6:9-12) Nkoposa kotani nanga kufuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake, ndi chidaliro cha kulandira madalitso ake pa zoyesayesa zathu za kupeza zofunika m’moyo! (Mateyu 6:25-33; Ahebri 13:5) Mwa kuika zinthu zauzimu patsogolo ndi kufuna mtendere ndi Mulungu choyamba, mungapeze kuti banja lanu, ngakhale kuti mwina lingakhale logaŵanika chifukwa cha mikhalidwe ina, lidzakhala logwirizana kwenikweni m’mbali zofunika koposa.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . A M’BANJA KUSUNGA MTENDERE M’NYUMBA MWAWO?

      Akristu amakulitsa luntha.—Miyambo 16:21; 24:3.

      Kusonyezana chikondi ndi ulemu muukwati sikumadalira pa kukhala ndi chipembedzo chimodzi.—Aefeso 5:23, 25.

      Mkristu samayesa kuswa lamulo la Mulungu mwadala.—Machitidwe 5:29.

      Akristu ali osunga mtendere.—Aroma 12:18.

      Musafulumire kukwiya.—Mlaliki 7:9.

      MAUKWATI OYENERA AMADZETSA ULEMU NDI MTENDERE

      Masiku ano amuna ndi akazi ambiri amakhala pamodzi popanda ukwati wa lamulo. Uwu ndiwo mkhalidwe umene wokhulupirira watsopano angafunikire kuwongolera. M’zochitika zina ukwatiwo ungavomerezedwe ndi apamudzipo kapena mwambo wa mtunduwo, koma suli walamulo. Komabe, muyezo wa Baibulo umafuna ukwati wolembetsa bwino. (Tito 3:1; Ahebri 13:4) Kwa anthu amene ali mumpingo wachikristu, Baibulo limafunanso kuti akhale ndi mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi muukwati. (1 Akorinto 7:2; 1 Timoteo 3:2, 12) Kutsatira muyezo umenewu ndiko njira yoyamba yopezera mtendere m’nyumba mwanu. (Salmo 119:165) Zofuna za Yehova sizili zosatheka kapena zolemetsa. Zimene amatiphunzitsa nzotipindulitsa.—Yesaya 48:17, 18.

  • Mukhoza Kulaka Mavuto Owononga Banja
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 12

      Mukhoza Kulaka Mavuto Owononga Banja

      1. Kodi ndi mavuto obisika otani amene ali m’mabanja ena?

      GALIMOTO lakale langotsukidwa kumene ndi kupukutidwa bwino ndi mafuta. Kwa anthu odutsa m’njira likuoneka lonyezimira, monga latsopano. Koma mkati mwake, dzimbiri likudya galimotolo. Chimodzimodzi ndi mabanja ena. Ngakhale kuti maonekedwe akunja akusonyeza kuti zonse zili bwino, nkhope zomwetulirazo zimabisa mantha ndi zopweteka. Mkati mwake mikhalidwe yonga dzimbiri ilikudya mtendere wa banja. Mavuto aŵiri amene angachititse zimenezi ndiwo uchidakwa ndi chiwawa.

      KUWONONGA KWA UCHIDAKWA

      2. (a) Kodi lingaliro la Baibulo nlotani ponena za kumwa moŵa? (b) Kodi uchidakwa nchiyani?

      2 Baibulo silimaletsa kumwa moŵa koyenera, koma limaletsa kuledzera. (Miyambo 23:20, 21; 1 Akorinto 6:9, 10; 1 Timoteo 5:23; Tito 2:2, 3) Komabe, uchidakwa umaposa pakuledzera chabe; ndiwo kupereka maganizo onse ku moŵa ndi kulephera kulamulira kamwedwe. Zidakwa zingakhale achikulire. Koma tsoka lake nlakuti zingakhalenso achichepere.

      3, 4. Longosolani mmene uchidakwa umavutitsira mnzake wa muukwati wa chidakwayo ndi ana.

      3 Baibulo linasonyeza kalekale kuti kumwetsa moŵa kungasokoneze mtendere wa banja. (Deuteronomo 21:18-21) Ziyambukiro zowononga za uchidakwa zimakhudza banja lonse. Mnzake wa muukwati angaloŵe ntchito ya kuyesayesa kuletsa chidakwayo kumwa kapena kuyesa kuzoloŵerana ndi machitidwe ake osayembekezereka. Amayesa kubisa moŵa, kuutaya, kubisa ndalama zake, ndi kuchonderera chidakwayo kuti asonyeze chikondi pa banja, pa moyo wake, ngakhale pa Mulungu—koma iye amangopitiriza kumwa. Pamene zoyesayesa zake za kuchepetsa kamwedwe ka mnzake zilephera nthaŵi zonse, amalefulidwa ndi kudziona kukhala wolephera. Angayambe kuvutika ndi mantha, mkwiyo, liwongo, kusaona tulo, nkhaŵa, ndi kutaya ulemu waumwini.

      4 Ananso amakhudzidwa ndi ziyambukiro za uchidakwa wa kholo. Ena amavulazidwa mwakuthupi. Ena amachitidwa nkhanza ya kugonedwa. Angafike ngakhale pakudziona kukhala ndi mlandu wa kuchititsa kholo kukhala chidakwa. Kaŵirikaŵiri kukhulupirira kwawo anthu ena kumawonongedwa ndi mkhalidwe wosayenera wa chidakwa. Chifukwa chakuti satha kulankhula momasuka zimene zikuchitika panyumba, anawo angaphunzire kupondereza malingaliro awo, zimene kaŵirikaŵiri zimawawononga. (Miyambo 17:22) Ana otero angapitirize ndi mkhalidwe wakusadzidalira umenewu kapena kusadzilemekeza mpaka ku uchikulire.

      KODI BANJA LINGACHITENJI?

      5. Kodi uchidakwa ungalamuliridwe motani, ndipo nchifukwa ninji zimenezi zili zovuta?

      5 Ngakhale kuti akatswiri ambiri ndi mabuku amanena kuti uchidakwa sungachiritsidwe, ochuluka amavomereza kuti kuchira pamlingo winawake nkotheka ndi programu ya kusala kumwa kotheratu. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:29.) Komabe, nkovuta kuchititsa chidakwa kuti avomere kulandira chithandizo, popeza kuti kaŵirikaŵiri amakana kuti alibe vuto. Komabe, pamene ena m’banja ayesayesa kuchitapo kanthu povutitsidwa ndi uchidakwawo, chidakwayo angayambe kuzindikira kuti ali ndi vuto. Dokotala wina wodziŵa kwambiri kuthandiza zidakwa ndi mabanja awo anati: “Ndiganiza kuti chinthu chofunika koposa nchakuti banjalo lingopitiriza ndi moyo wawo wa nthaŵi zonse ndi wokhutiritsa. Mpamene chidakwayo amaona kusiyana kwakukulu kwa moyo wake ndi wa ena m’banja.”

      6. Kodi uphungu wabwino koposa wothandiza mabanja amene ali ndi chidakwa umapezeka kuti?

      6 Ngati m’banja mwanu muli ndi chidakwa, uphungu wouziridwa wa Baibulo ungakuthandizeni kukhala ndi moyo wabwino wothekera. (Yesaya 48:17; 2 Timoteo 3:16, 17) Talingalirani mapulinsipulo ena amene athandiza mabanja ambiri kuchita mwachipambano ndi uchidakwa.

      7. Ngati wina m’banja ndi chidakwa, kodi umakhala mlandu wa yani?

      7 Lekani kudziveka mlandu wonsewo. Baibulo limati: “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini,” ndi kuti, “aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.” (Agalatiya 6:5; Aroma 14:12) Chidakwayo angayese kusonyeza kuti enawo m’banja ndiwo ochititsa. Mwachitsanzo, iye anganene kuti: “Mukanandisamalira bwino, bwenzi sindikumwa.” Ngati ena aoneka kuti akuvomerezana naye, amamulimbikitsa kupitiriza kumwa kwakeko. Koma ngakhale ngati tivutitsidwa ndi mikhalidwe kapena anthu ena, tonsefe—kuphatikizapo zidakwa—timakhala ndi thayo la zimene tichita.—Yerekezerani ndi Afilipi 2:12.

      8. Kodi ndi njira zina ziti zimene chidakwa angathandizidwe nazo kuyang’anizana ndi zotulukapo za vuto lake?

      8 Musakhale ndi mtima wofuna kumachinjiriza chidakwayo pa zotulukapo zonse za kumwa kwake. Mwambi wa Baibulo wonena za munthu wokwiya ungagwirenso ntchito kwa chidakwa: “Ukampulumutsa udzateronso.” (Miyambo 19:19) Msiyeni chidakwayo akumane ndi zotulukapo za kumwa kwake. Mlekeni ayeretse yekha zimene aipitsa kapena aimbe yekha foni kuntchito mmaŵa mwake pambuyo pa kuledzera dzulo lake.

      Chithunzi patsamba 146

      Akulu achikristu angathandize kwambiri kuthetsa mavuto a m’banja

      9, 10. Kodi nchifukwa ninji mabanja okhala ndi chidakwa ayenera kulandira thandizo, ndipo ndi thandizo la yani limene ayenera kufuna makamaka?

      9 Landirani thandizo la ena. Miyambo 17:17 imati: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” Pamene muli ndi chidakwa m’banja, muli ndi tsoka. Mufunikira thandizo. Musazengereze kudalira pa chichirikizo cha ‘mabwenzi enieni.’ (Miyambo 18:24, NW) Kukambitsirana ndi ena amene amamvetsetsa vutolo kapena amene akumanapo ndi mkhalidwe umodzimodzi kungakupatseni malingaliro othandiza pa zimene mungachite ndi zimene simuyenera kuchita. Koma khalani wolinganiza bwino zinthu. Lankhulani ndi awo amene mumakhulupirira, aja amene adzasunga ‘chinsinsi’ chanu.—Miyambo 11:13.

      10 Phunzirani kudalira akulu achikristu. Akulu mumpingo wachikristu angakhale othandiza kwambiri. Amuna okhwima ameneŵa anaphunzira Mawu a Mulungu ndipo ali ndi chidziŵitso cha kugwiritsira ntchito mapulinsipulo ake. Iwo angakhaledi “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:2) Akulu achikristu samangotetezera mpingo wonse ku zivulazo komanso amatonthoza, kulimbikitsa, ndi kusamalira mmodzi ndi mmodzi amene ali ndi mavuto. Gwiritsirani ntchito mokwanira mwaŵi wa chithandizo chawo.

      11, 12. Kodi ndani amene amapereka chithandizo chachikulu koposa ku mabanja okhala ndi chidakwa, ndipo kodi chichirikizo chimenecho chimaperekedwa motani?

      11 Koposa zonse, pezani nyonga ya kwa Yehova. Baibulo limatitsimikizira mwachikondi kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:18) Ngati mtima wanu uli wosweka kapena ukuvutika chifukwa cha vuto la kukhala ndi chidakwa m’banja, dziŵani kuti “Yehova ali pafupi.” Amadziŵa vuto la mkhalidwe wa banja lanu.—1 Petro 5:6, 7.

      12 Kukhulupirira zimene Yehova amanena m’Mawu ake kungakuthandizeni kulimbana ndi nkhaŵa. (Salmo 130:3, 4; Mateyu 6:25-34; 1 Yohane 3:19, 20) Kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kutsatira mapulinsipulo ake kumakukhozetsani kulandira chithandizo cha mzimu woyera wa Mulungu, umene ungakupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa” yokukhozetsani kupirira tsiku ndi tsiku.—2 Akorinto 4:7, NW.a

      13. Kodi vuto lachiŵiri limene limavulaza mabanja ambiri ndi lotani?

      13 Kumwetsa moŵa kungachititse vuto lina limene limawononga mabanja ambiri—chiwawa cha m’banja.

      KUWONONGA KWA CHIWAWA CHA M’BANJA

      14. Kodi chiwawa cha m’banja chinayamba liti, ndipo mkhalidwewo uli wotani lero?

      14 Mchitidwe woyamba wachiwawa m’mbiri ya munthu unali chiwawa cha m’banja chimene chinachitika pakati pa abale aŵiri, Kaini ndi Abele. (Genesis 4:8) Chiyambire pamenepo, anthu aona mitundu yosiyanasiyana ya chiwawa cha m’banja. Pali amuna amene amamenya akazi awo, akazi amene amaukira amuna awo, makolo amene amamenya ana awo aang’ono mwankhanza, ndi ana achikulire amene amazunza makolo awo okalamba.

      15. Kodi ena pabanja amakhudzidwa motani m’maganizo ndi chiwawa cha m’banja?

      15 Kuwononga kumene chiwawa cha m’banja chimachita kumaposa zipsera zakuthupi. Mkazi wina womenyedwa anati: “Umamva liwongo ndi manyazi zimene umalimbana nazo. Nthaŵi zambiri mmaŵa, umangofuna kugonabe, ukumaganizira kuti zikanangokhala loto chabe loipa.” Ana amene amaona kapena kuchitidwa chiwawa cha m’banja iwonso angakhale achiwawa atakula ndi kukhala ndi mabanja awo.

      16, 17. Kodi nkhanza ya mawu nchiyani, ndipo imakhudza motani ena pabanja?

      16 Chiwawa cha m’banja sindicho kumenya kokha. Kaŵirikaŵiri pamakhala kunyoza. Miyambo 12:18 imati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.” “Kupyoza” kumeneku kwa chiwawa cha m’banja kumaphatikizapo kutchana maina onyoza ndi kuzazirana, limodzinso ndi kusuliza nthaŵi zonse, kutukwana, ndi ziwopsezo za kumenya. Zivulazo za chiwawa cha mawu opweteka sizimaoneka ndipo kaŵirikaŵiri sizimadziŵika kwa ena.

      17 Chochititsa chisoni makamaka ndicho kuzunza mwana m’maganizo—kumsuliza nthaŵi zonse ndi kuderera zochita zake, nzeru zake, kapena mkhalidwe wake monga munthu. Nkhanza ya mawu imeneyi imawononga mzimu wa mwana. Zoona, ana onse amafunikira chilango. Koma Baibulo limalangiza atate kuti: “Musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”—Akolose 3:21.

      MMENE MUNGAPEŴERE CHIWAWA CHA M’BANJA

      Chithunzi patsamba 151

      Akristu okwatirana amene amakondana ndi kulemekezana amachitapo kanthu mwamsanga kuthetsa mavuto

      18. Kodi chiwawa cha m’banja chimayambira kuti, ndipo Baibulo limasonyeza chiyani kukhala njira yochipeŵera?

      18 Chiwawa cha m’banja chimayambira mumtima ndi m’maganizo; kachitidwe kathu ka zinthu kamayamba ndi kalingaliridwe kathu. (Yakobo 1:14, 15) Kuti aleke chiwawa, wochita nkhanzayo afunikira kusintha kalingaliridwe kake. (Aroma 12:2) Kodi zimenezo nzotheka? Inde. Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yosintha anthu. Akhoza kuchotsa ngakhale malingaliro owononga ‘amphamvu.’ (2 Akorinto 10:4; Ahebri 4:12) Chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chikhoza kusintha anthu kwambiri kwakuti amanenedwa kuti avala umunthu watsopano.—Aefeso 4:22-24; Akolose 3:8-10.

      19. Kodi Mkristu ayenera kumuona motani mnzake wa muukwati ndipo ayenera kuchita naye motani?

      19 Mmene wa muukwati ayenera kuonera mnzake. Mawu a Mulungu amati: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha.” (Aefeso 5:28) Baibulo limanenanso kuti mwamuna ayenera kupatsa mkazi wake “ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.” (1 Petro 3:7) Akazi akulangizidwa kuti “akonde amuna awo,” ndi ‘kuwawopa.’ (Tito 2:4; Aefeso 5:33) Ndithudi, palibe mwamuna wowopa Mulungu amene anganene moona mtima kuti amalemekezadi mkazi wake ngati amammenya kapena kummenya ndi mawu. Ndipo kulibe mkazi amene amazazira mwamuna wake, kulankhula naye monyoza, kapena kumdzudzula nthaŵi zonse amene anganene kuti amamkondadi ndi kumlemekeza.

      20. Kodi makolo ali ndi thayo kwa yani kaamba ka ana awo, ndipo nchifukwa ninji makolo sayenera kuyembekezera zopambanitsa kwa ana awo?

      20 Mmene tiyenera kuonera ana. Ana amafunikira kukondedwa ndi kusamaliridwa ndi makolo awo. Mawu a Mulungu amatcha ana “cholandira cha kwa Yehova” ndi “mphotho.” (Salmo 127:3) Makolo ali ndi thayo pamaso pa Yehova la kusamalira cholandira chimenecho. Baibulo limanena za “chibwana” ndi “utsiru” za paubwana. (1 Akorinto 13:11; Miyambo 22:15) Makolo sayenera kudabwa ngati aona utsiru mwa ana awo. Achichepere sali achikulire. Makolo sayenera kufuna zopambana pa msinkhu wa mwana, zosiyana ndi makulidwe ake, ndi mphamvu yake.—Onani Genesis 33:12-14.

      21. Kodi njira yaumulungu yoonera makolo okalamba ndi yochitira nawo ndi yotani?

      21 Mmene tiyenera kuonera makolo okalamba. Levitiko 19:32 amati: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.” Choncho Chilamulo cha Mulungu chinalimbikitsa kupereka ulemu ndi kuwopa okalamba. Zimenezi zingakhale zovuta pamene kholo lokalamba lioneka lofuna zopambanitsa kapena kudwala ndipo mwinamwake silimayenda msanga kapena kuganiza mwamsanga. Chikhalirechobe, ana akukumbutsidwa “kubwezera akuwabala.” (1 Timoteo 5:4) Zimenezi zikutanthauza kuwachitira ulemu ndi kuwawopa, mwinamwake ngakhale kuwapatsa thandizo la ndalama. Kuzunza makolo okalamba mwa njira iliyonse kumawombana kotheratu ndi njira imene Baibulo limatiuza kuchitiramo.

      22. Kodi mkhalidwe waukulu wolakira chiwawa cha m’banja ndi wotani, ndipo kodi tingausonyeze motani?

      22 Kulitsani kudziletsa. Miyambo 29:11 imati: “Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.” Kodi mungalamulire motani mkwiyo wanu? M’malo mwa kulola mkwiyo kukula mwa inu, chitanipo kanthu mwamsanga kuti muthetse vuto lobukalo. (Aefeso 4:26, 27) Chokani pamalopo ngati muona kuti mukutaya mtima. Pemphererani mzimu woyera wa Mulungu kuti ukupatseni kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Kukawongola miyendo kapena kuchita maseŵero olimbitsa thupi kungakuthandizeni kulamulira mtima wanu. (Miyambo 17:14, 27) Yesayesani ‘kusakwiya msanga.’—Miyambo 14:29.

      KUPATUKANA KAPENA KUKHALABE PAMODZI?

      23. Kodi chingachitike nchiyani ngati wina mumpingo wachikristu achita chiwawa cha mkwiyo mobwerezabwereza ndi mosalapa, mwinamwake kuphatikizapo nkhanza yakumenya a pabanja lake?

      23 Pantchito zimene zimanyansa Mulungu, Baibulo limaphatikizapo “madano, ndewu, . . . zopsa mtima” ndipo limanena kuti ‘akuchita zotero sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.’ (Agalatiya 5:19-21) Chifukwa chake, munthu aliyense amene adzitcha Mkristu amene mobwerezabwereza ndipo mosalapa amachita chiwawa cha kupsa mtima, mwinamwake kuphatikizapo nkhanza ya kumenya mkazi kapena ana, akhoza kuchotsedwa mumpingo wachikristu. (Yerekezerani ndi 2 Yohane 9, 10.) Mwa njira imeneyi mpingo umasungidwa woyera wopanda anthu ankhanza.—1 Akorinto 5:6, 7; Agalatiya 5:9.

      24. (a) Kodi a muukwati ochitidwa nkhanza angasankhe kuchita motani? (b) Kodi mabanja ndi akulu odera nkhaŵa angalimbikitse motani wa muukwati wochitidwa nkhanza, koma kodi nchiyani chimene sayenera kuchita?

      24 Bwanji za Akristu amene pakali pano akumenyedwa ndi mnzawo wa muukwati wankhanza amene sakusonyeza zizindikiro za kusintha? Ena asankha kukhala ndi mnzawo wankhanzayo pa zifukwa zina. Ena asankha kuchoka, poona kuti thanzi lawo lakuthupi, la maganizo, ndi lauzimu—mwinamwake moyo weniweniwo—zili pangozi. Zimene munthu wochitidwa chiwawa m’banja asankha kuchita m’mikhalidwe imeneyi ndi chosankha chake pamaso pa Yehova. (1 Akorinto 7:10, 11) Mabwenzi achifundo, achibale, kapena akulu achikristu angafune kupereka thandizo ndi uphungu, koma sayenera kuumiriza wochitidwa nkhanzayo kutsatira njira yakutiyakuti. Ayenera kupanga yekha chosankha.—Aroma 14:4; Agalatiya 6:5.

      KUTHA KWA MAVUTO OWONONGA

      25. Kodi chifuno cha Yehova pa banja nchotani?

      25 Pamene Yehova anakwatitsa Adamu ndi Hava, sanali ndi cholinga chakuti mabanja akhale ndi mavuto owononga onga uchidakwa kapena chiwawa. (Aefeso 3:14, 15) Banja linayenera kukhala lofunga ndi chikondi ndi mtendere ndipo zosoŵa za aliyense za maganizo, malingaliro, ndi zauzimu zinayenera kusamaliridwa. Koma pamene uchimo unafika, moyo wa banja unawonongeka mwamsanga.—Yerekezerani ndi Mlaliki 8:9.

      26. Kodi aja oyesa kukhala ndi moyo motsatira zofuna za Yehova ali ndi mtsogolo motani?

      26 Mwaŵi wake ngwakuti, Yehova sanataye chifuno chake cha banja. Iye walonjeza kubweretsa dziko latsopano lamtendere mmene anthu “adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwawopsa.” (Ezekieli 34:28) Panthaŵiyo, uchidakwa, chiwawa cha m’banja, ndi mavuto onse amene amawononga mabanja lero adzakhala zinthu zakale. Anthu adzamwetulira, osati kuti abise mkwiyo ndi kupweteka, koma chifukwa chakuti ‘akukondwera nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:11.

      a M’maiko ena, muli malo ochiritsira, zipatala, ndi maprogramu ochiritsa amene amathandiza zidakwa ndi mabanja awo. Kaya muyenera kufuna chithandizo choterocho kapena ayi ndi nkhani yaumwini. Watch Tower Society simasankhira munthu mtundu uliwonse wa kuchiritsa. Komabe, payenera kukhala kusamala, kuti pofuna chithandizo, munthu asadziloŵetse m’machitidwe amene amaswa mapulinsipulo a Malemba.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . MABANJA KUPEŴA MAVUTO AMENE ANGACHITITSE KUWONONGA KWAKUKULU?

      Yehova amatsutsa kumwetsa moŵa.—Miyambo 23:20, 21.

      Munthu aliyense ali ndi thayo la zochita zake.—Aroma 14:12.

      Popanda kudziletsa sitingathe kumtumikira Mulungu movomerezeka.—Miyambo 29:11.

      Akristu enieni amalemekeza makolo awo okalamba.—Levitiko 19:32.

  • Ngati Ukwati Ukufuna Kusweka
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 13

      Ngati Ukwati Ukufuna Kusweka

      1, 2. Pamene ukwati uli pavuto, kodi ndi funso lotani limene liyenera kufunsidwa?

      MU 1988 mkazi wachitaliyana wotchedwa Lucia anali wovutika maganizo kwambiri.a Pambuyo pa zaka khumi ukwati wawo unali kutha. Nthaŵi zambiri anayesa kuti agwirizanenso ndi mwamuna wake, koma sizinatheke. Motero anapatukana chifukwa cha kusayenererana ndiyeno anayang’anizana ndi vuto la kulera ana ake aakazi aŵiri payekha. Pokumbukira za panthaŵiyo, Lucia akunena kuti: “Ndinadziŵa kuti palibe chimene chikanapulumutsa ukwati wathu.”

      2 Ngati muli ndi mavuto a muukwati, mungamvetsetse mkhalidwe wa Lucia. Ukwati wanu ungakhale pavuto ndipo mungaganize kuti mwina sukhoza kupulumuka. Ngati zili choncho, kudzakhala kokuthandizani kudzifunsa funso ili: Kodi ndatsatira uphungu wabwino wonse umene Mulungu wapereka m’Baibulo wochititsa ukwati kupambana?—Salmo 119:105.

      3. Ngakhale kuti kusudzulana kwakhala kofala, kodi malipoti amasonyeza kuti anthu osudzulana ambiri adzimva motani pamodzi ndi mabanja awo?

      3 Pamene kusamvana kukula pakati pa mwamuna ndi mkazi, kuthetsa ukwati kungaoneke kukhala njira yapafupi yothetsera vuto. Koma pamene kuli kwakuti maiko ambiri ali ndi ziŵerengero zomawonjezereka modabwitsa za mabanja osweka, kufufuza kwaposachedwapa kwasonyeza kuti amuna ndi akazi ambiri osudzulana ali achisoni. Ambiri amakhala ndi thanzi lofooka, ponse paŵiri m’thupi ndi m’maganizo, kuposa aja amene amakhalabe muukwati wawo. Kaŵirikaŵiri, kuvutika maganizo ndi chisoni cha ana pamene ukwati watha zimakhala kwa zaka zambiri. Makolo ndi mabwenzi a banja loswekalo amavutika nawonso. Ndipo bwanji ponena za mmene Mulungu, Woyambitsa ukwati, amaonera mkhalidwewo?

      4. Kodi mavuto a muukwati ayenera kuthetsedwa motani?

      4 Monga momwe taonera m’mitu yapitayo, chifuno cha Mulungu chinali chakuti ukwati ukhale mgwirizano wa moyo wonse. (Genesis 2:24) Nanga nchifukwa ninji maukwati ambiri amasweka? Sizimachitika mwadzidzidzi. Kaŵirikaŵiri pamakhala zizindikiro zochenjeza. Mavuto aang’ono muukwati angayambe kukula kufikira aoneka kukhala osathetseka. Koma ngati mavuto ameneŵa athetsedwa mwamsanga ndi chithandizo cha Baibulo, maukwati ambiri sangasweke.

      YANG’ANANI PA ZINTHU ZOTHEKA

      5. Kodi ndi mkhalidwe weniweni wotani umene tiyenera kuyang’anizana nawo muukwati uliwonse?

      5 Mkhalidwe umene nthaŵi zina umatsogolera ku mavuto ndiwo kufuna zinthu zosatheka kwa a muukwati. Mabuku a nkhani zachikondi, magazini okondedwa kwambiri, maprogramu a pawailesi yakanema, ndi mafilimu zingapereke ziyembekezo ndi maloto osatheka m’moyo weniweni. Pamene maloto ameneŵa sakwaniritsika, munthuyo angakhale wokhumudwa, wosakhutira, ndipo ngakhale wokwiya. Komabe, kodi ndi motani mmene anthu aŵiri opanda ungwiro angapezere chimwemwe muukwati? Kukhala ndi unansi wachipambano kumafuna kuyesayesa zolimba.

      6. (a) Kodi Baibulo limapereka lingaliro loyenera lotani la ukwati? (b) Kodi ndi zifukwa zina ziti zimene zimachititsa mikangano muukwati?

      6 Baibulo limanena zenizeni. Limasonyeza chisangalalo cha ukwati, komanso limachenjeza kuti awo amene aloŵa ukwati “adzakhala nacho chisautso m’thupi.” (1 Akorinto 7:28) Monga taonera kale, onse aŵiri ali opanda ungwiro ndi okhoza kuchimwa. Mpangidwe wa maganizo ndi mtima wa munthu aliyense ndi makulidwe ake nzosiyana. Nthaŵi zina a muukwati amakangana pa ndalama, ana, ndi achibale. Kusapeza nthaŵi ya kuchitira zinthu pamodzi ndiponso mavuto a zakugonana zingakhalenso zochititsa mkangano.b Kusamalira nkhani zotero kumafuna nthaŵi, koma musataye mtima! A muukwati ambiri ali okhoza kuyang’anizana ndi mavuto oterowo ndi kupeza njira zowathetsera mogwirizana.

      KAMBIRANANI MIKANGANO

      Chithunzi patsamba 154

      Thetsani mavuto mwamsanga. Musalole dzuŵa kuloŵa muli chikwiyire

      7, 8. Ngati pali kupwetekana mtima ndi kusamvana pakati pa okwatirana, kodi njira ya Malemba yothetsera zimenezo ndi yotani?

      7 Ambiri kumawavuta kukhala odekha pokambirana zopweteka mtima, mikangano, kapena zolakwa zawo. M’malo mwa kunena mosabisa kuti: “Mwandimva molakwa,” mnzakeyo angangokwiya ndi kukulitsa vuto. Ambiri amanena kuti: “Mungosamala zanu zokha,” kapena kuti, “Simundikonda.” Posafuna kukangana, winayo angangokhala chete osafuna kuyankha.

      8 Njira yabwino ndiyo kutsatira uphungu wa Baibulo wakuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Okwatirana ena achimwemwe, pamene anafika chaka cha 60 cha ukwati wawo, anafunsidwa za chinsinsi cha chipambano cha ukwati wawo. Mwamunayo anati: “Tinaphunzira kusagona tisanathetse mkangano, zinalibe kanthu kuti unali waung’ono motani.”

      9. (a) Kodi Malemba amasonyeza chiyani kukhala mbali yofunika ya kulankhulana? (b) Kodi okwatirana afunikira kumachitanji kaŵirikaŵiri, ngakhale kuti zimenezi zimafuna kulimba mtima ndi kudzichepetsa?

      9 Pamene mwamuna ndi mkazi akangana, aliyense afunikira ‘kukhala wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.’ (Yakobo 1:19) Atamvetsera mosamalitsa, onse aŵiri angaone kufunika kwa kupepesa. (Yakobo 5:16) Kunena moona mtima kuti, “Pepani ndakukhumudwitsani,” kumafuna kudzichepetsa ndi kulimba mtima. Koma kuthetsa mikangano mwa njira imeneyi kudzathandiza kwambiri a muukwati, osati kuthetsa mavuto kokha komanso kukulitsa ubwenzi ndi chikondi zimene zidzawachititsa kukonda kukhala pamodzi.

      KUPEREKA MANGAWA A MUUKWATI

      10. Kodi ndi chitetezo chotani chimene Paulo analangiza Akristu a ku Korinto chimene chingagwirenso ntchito kwa Mkristu lerolino?

      10 Pamene mtumwi Paulo analembera Akorinto, analimbikitsa kukwatira, “chifukwa cha madama.” (1 Akorinto 7:2) Dziko lerolino nloipa mofanana ndi Korinto wakaleyo, ndipo ngakhale kuposapo. Nkhani zachisembwere zimene anthu a dziko amakambitsirana poyera, mavalidwe awo onyazitsa, ndi nkhani zodzutsa chilakolako chakugonana zopezeka m’magazini ndi mabuku, pa TV, ndi m’mafilimu, zonse zimasonkhezera zilakolako za chisembwere. Kwa Akorinto amene anazingidwa ndi mikhalidwe imodzimodziyo, mtumwi Paulo anati: “Nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.”—1 Akorinto 7:9.

      11, 12. (a) Kodi mwamuna ndi mkazi ali ndi mangawa otani kwa wina ndi mnzake, ndipo kodi ayenera kuperekedwa ndi mzimu wotani? (b) Kodi ziyenera kuchitika motani ngati mangawa a ukwati ayenera kulekezedwa kwakanthaŵi?

      11 Chifukwa chake, Baibulo limalamula Akristu okwatira kuti: “Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna.” (1 Akorinto 7:3) Onani kuti chigogomezero chili pa kupatsa—osati kuumiriza. Mangawa a muukwati amakhala okhutiritsa pokhapo ngati aliyense asamala za ubwino wa mnzake. Mwachitsanzo, Baibulo limalamula amuna kuchita ndi akazi awo “monga mwa chidziŵitso.” (1 Petro 3:7) Zimenezi nzofunika makamaka popereka ndi polandira mangawa a muukwati. Ngati mkazi sasonyezedwa chikondi, kungakhale kovuta kuti asangalale ndi mbali imeneyi ya ukwati.

      12 Pali nthaŵi zina pamene okwatirana angamanane mangawa a muukwati. Mkazi angachite zimenezo panthaŵi zina m’mwezi kapena pamene akumva kutopa kwambiri. (Yerekezerani ndi Levitiko 18:19.) Mwamunanso angachite zimenezo pamene akuchita ndi vuto lalikulu kuntchito ndipo ali wopsinjika maganizo. Kulekeza kupereka mangawa a muukwati kwakanthaŵi kumeneko kungachitidwe bwino koposa ngati aŵiriwo akambitsirana za mkhalidwewo moona mtima ndi ‘kuvomerezana.’ (1 Akorinto 7:5) Zimenezi zidzachititsa aliyense wa iwo kusaganiza zinazake. Komabe, ngati mkazi amana dala mwamuna wake kapena ngati mwamuna alephera dala kupereka mangawa a ukwati mwa njira yachikondi, mnzakeyo angakhale pangozi ya chiyeso. Mumkhalidwe woterowo, pangabuke mavuto muukwati.

      13. Kodi Akristu angachite motani kuti akhale ndi kalingaliridwe koyenera?

      13 Mofanana ndi Akristu onse, atumiki a Mulungu okwatira ayenera kupeŵa zithunzithunzi zaumaliseche, zimene zingadzutse zikhumbo zonyansa zosakhala zachibadwa. (Akolose 3:5) Ayeneranso kutetezera malingaliro ndi makhalidwe awo pochita ndi onse osiyana nawo ziŵalo. Yesu anachenjeza kuti: “Yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Mwa kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo wonena za kugonana, okwatirana ayenera kukhala okhoza kupeŵa kugwera m’chiyeso ndi kuchita chigololo. Angapitirize kusangalala ndi chikondi cha muukwati umene kugonana kumaonedwa kukhala mphatso yolemekezeka yochokera kwa Woyambitsa ukwati, Yehova.—Miyambo 5:15-19.

      MAZIKO A BAIBULO A CHISUDZULO

      14. Kodi ndi mkhalidwe womvetsa chisoni wotani umene nthaŵi zina ungakhalepo? Chifukwa ninji?

      14 Chokondweretsa nchakuti, m’maukwati ambiri achikristu, mavuto alionse amene amabuka akhoza kuthetsedwa. Komabe, nthaŵi zina sizimatheka. Chifukwa chakuti anthu ali opanda ungwiro ndipo akukhala m’dziko lauchimo lolamuliridwa ndi Satana, maukwati ena amafika pafupi ndi kusweka. (1 Yohane 5:19) Kodi Akristu ayenera kuchita motani ndi mkhalidwe wa chiyeso umenewo?

      15. (a) Kodi pali maziko a Malemba okha ati a chisudzulo amene ali ndi chilolezo cha kukwatiranso? (b) Kodi nchifukwa ninji ena sanafune kusudzula mnzawo wa muukwati wosakhulupirika?

      15 Monga kwatchulidwa m’Mutu 2 wa buku lino, dama ndilo maziko okha a Malemba a chisudzulo ndi chilolezo cha kukwatiranso.c (Mateyu 19:9) Ngati muli ndi umboni wotsimikizika wakuti mnzanu wa muukwati sakuyenda bwino, pamenepo mukuyang’anizana ndi chosankha chovuta. Kodi mudzakhala muukwatiwo kapena mudzasudzulana? Palibe malamulo amene akuperekedwa. Akristu ena akhululukira kwenikweni mnzawo wa muukwati wolapa moona mtimayo, ndipo ukwati wawo wosungikawo wawongokera bwino lomwe. Ena sanafune kusudzulana chifukwa cha ana.

      16. (a) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zachititsa ena kusudzula anzawo a muukwati ochimwa? (b) Pamene wa muukwati wochimwiridwa apanga chosankha cha kusudzulana kapena kusasudzulana, nchifukwa ninji palibe amene ayenera kusuliza chosankha chake?

      16 Komabe, tchimolo lingakhale ndi chotulukapo cha mimba kapena matenda opatsirana. Kapena ana angafunikire kutetezeredwa kwa kholo logona ana. Mwachionekere, pali zambiri zofuna kuzilingalira musanapange chosankha. Komabe, ngati mwadziŵa za kusakhulupirika kwa mnzanu wa muukwati ndiyeno pambuyo pake muyambanso kugona naye, mwasonyeza kuti mwamkhululukira ndipo mukufuna kupitiriza ndi ukwatiwo. Maziko a chisudzulo ndi chilolezo cha Malemba cha kukwatiranso zathera pamenepo. Palibe aliyense amene ayenera kuloŵererapo ndi kukusonkhezerani kupanga chosankha, ndipo aliyense sayenera kusuliza chosankha chanu pamene mwachipanga. Muyenera kukhala wokonzeka kuyang’anizana ndi zotulukapo za chosankha chanu. “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.”—Agalatiya 6:5.

      MAZIKO A KUPATUKANA

      17. Ngati anthu apatukana kapena kusudzulana pachifukwa chosakhala dama, kodi ndi ziletso zotani zimene Malemba amaika pa iwo?

      17 Kodi ilipo mikhalidwe imene ingachititse kukhala koyenera kupatukana kapena kusudzulana ndi wina ngakhale ngati iye sanachite dama? Inde, m’chochitika chimenecho, Mkristu sali womasuka kuloŵa m’chibwenzi ndi munthu wina ndi cholinga cha kukwatirana. (Mateyu 5:32) Pamene kuli kwakuti Baibulo limalola kupatukana koteroko, limalamula kuti wochokayo ‘akhale wosakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso.’ (1 Akorinto 7:11) Kodi ndi mikhalidwe yoipitsitsa yotani imene ingachititse kukhala koyenera kupatukana?

      18, 19. Kodi ndi mikhalidwe yowopsa yotani imene ingachititse wina wa muukwati kulingalira za kufunika kwa kukapatukana kukhoti kapena kukalekana, ngakhale kuti pangakhale palibe chilolezo cha kukwatiranso?

      18 Chabwino, banja lingakhale paumphaŵi chifukwa cha ulesi ndi makhalidwe oipa a mwamuna.d Iye angamatchovere juga ndalama za banja kapena kumagulira anamgoneka kapena moŵa. Baibulo limati: “Ngati wina sadzisungiratu . . . a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Ngati mwamuna woteroyo akana kusintha njira zake, mwinamwake ngakhale kumatenga ndalama zimene mkazi wake amapeza ndi kugulira zinthu zakezo, mkaziyo angafune kusamalira umoyo wake ndi wa ana ake mwa kukapatukana kukhoti.

      19 Kachitidwe ka lamulo kameneko kangalingaliridwe ngati wina wa muukwati ali wachiwawa kwambiri kwa mnzake, mwinamwake kumammenya kaŵirikaŵiri kwakuti thanzi lake ndipo ngakhale moyo wake ukhala pangozi. Ndiponso, ngati wina wa muukwati ayesa kukakamiza mnzake kuswa malamulo a Mulungu mwa njira inayake, wowopsezedwayo angalingalirenso za kupatukana, makamaka ngati nkhaniyo ifika pamlingo wa kuika moyo wake wauzimu pangozi. Wokhala pangoziyo angaone kuti njira yokha yakuti ‘amvere Mulungu koposa anthu’ ndiyo mwa kukapatukana kukhoti.—Machitidwe 5:29.

      20. (a) Ngati banja likufuna kusweka, kodi ndi chithandizo chotani chimene mabwenzi auchikulire ndi akulu angapereke, ndipo nchiyani chimene sayenera kupereka? (b) Okwatirana sayenera kugwiritsira ntchito mfundo za Baibulo za kupatukana ndi kusudzulana monga chodzikhululukira chakuti achite chiyani?

      20 M’zochitika zonse za nkhanza ya wina wa muukwati, palibe amene ayenera kuumiriza wosalakwayo kaya kupatukana ndi mnzakeyo kapena kukhalabe naye. Pamene kuli kwakuti mabwenzi ndi akulu achidziŵitso angapereke chichirikizo ndi uphungu wa Baibulo, iwoŵa sangadziŵe zonse zoloŵetsedwamo zimene zikuchitika pakati pa mwamuna ndi mkazi. Yehova yekha ndiye amaona zimenezo. Ndithudi, mkazi wachikristu sadzakhala akulemekeza kakonzedwe ka Mulungu ka ukwati ngati agwiritsira ntchito zifukwa zodzikhululukira kuti achoke mu ukwati. Koma ngati mkhalidwe wowopsa kwambiri upitirizabe, palibe amene ayenera kumsuliza ngati asankha kupatukana. Zimenezi zimagwiranso ntchito kwa mwamuna wachikristu amene afuna kupatukana ndi mkazi wake. “Tonse tidzaimirira ku mpando wakuweruza wa Mulungu.”—Aroma 14:10.

      MMENE UKWATI WOSWEKA UNAPULUMUTSIDWIRA

      21. Kodi ndi chochitika chotani chimene chimasonyeza kuti uphungu wa Baibulo pa ukwati umagwira ntchito?

      21 Lucia amene tatchula poyamba, atapatukana ndi mwamuna wake kwa miyezi itatu, anakumana ndi Mboni za Yehova nayamba kuphunzira nazo Baibulo. Iye akufotokoza kuti: “Ndinadabwa kuona kuti Baibulo linali kupereka mayankho ogwira ntchito pa mavuto anga. Titangophunzira kwa mlungu umodzi, ndinafuna kubwererana ndi mwamuna wanga. Lerolino ndikhoza kunena kuti Yehova amadziŵa kupulumutsa maukwati okhala pavuto chifukwa chakuti ziphunzitso zake zimathandiza okwatirana kudziŵa mmene ayenera kupatsirana ulemu. Zimene anthu ena amanena nzabodza, kuti Mboni za Yehova zimagaŵanitsa mabanja. Kwa ine zimene zinachitika nzosiyana kwenikweni ndi zimenezo.” Lucia anaphunzira kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’moyo wake.

      22. Kodi onse okwatirana ayenera kudalira chiyani?

      22 Zimenezi sizinachitikire Lucia yekha. Ukwati uyenera kukhala dalitso, osati mtolo. Chifukwa chake, Yehova wapereka magwero abwino koposa a uphungu wa ukwati oposa ena alionse olembedwapo—Mawu ake amtengo wapatali. Baibulo lingapatse “opusa nzeru.” (Salmo 19:7-11) Lapulumutsa maukwati ambiri amene anafuna kusweka ndipo lawongolera ena ambiri amene anali ndi mavuto aakulu. Okwatirana onse akhale ndi chidaliro chokwanira pa uphungu wa ukwati umene Yehova Mulungu akupereka. Umagwiradi ntchito!

      a Dzina lasinthidwa.

      b Zina za mbali zimenezi zafotokozedwa m’mitu yapitayo.

      c Liwu la Baibulo lakuti “dama” limaphatikizapo chigololo, mathanyula, kugona nyama, ndi machitidwe ena osaloleka ophatikizapo kugwiritsira ntchito mpheto.

      d Zimenezi sizimaphatikizapo mikhalidwe imene mwamuna, ngakhale kuti akufuna, sakhoza kupezera banja zofunika chifukwa cha mavuto osapeŵeka, monga matenda kapena kusoŵa ntchito.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . KUPEŴA KUSWEKA KWA UKWATI?

      Ukwati umapatsa chimwemwe limodzi ndi nsautso.—Miyambo 5:18, 19; 1 Akorinto 7:28.

      Mikangano iyenera kuthetsedwa mwamsanga.—Aefeso 4:26.

      Pokambirana, kumvetsera nkofunika mofanana ndi kulankhula.—Yakobo 1:19.

      Mangawa a ukwati ayenera kuperekedwa mwa mzimu wopanda dyera ndi mwachikondi.—1 Akorinto 7:3-5.

  • Kukalambirana
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 14

      Kukalambirana

      1, 2. (a) Kodi ndi masinthidwe otani amene amakhalapo pamene ukalamba ufika? (b) Kodi amuna aumulungu a m’nthaŵi za Baibulo anapeza motani chikhutiro mu ukalamba?

      ZAMBIRI zimasintha pamene tikukalamba. Kufooka kwa thupi kumatilanda nyonga yathu. Tikayang’ana m’kalirole timaona makwinya atsopano ndi imvi zimene zikuyambika—ngakhale dazi. Tingayambe kuiŵala zinthu kaŵirikaŵiri. Pamakhala maunansi atsopano pamene ana akwatira kapena kukwatiŵa, ndiponso pamene adzukulu abadwa. Kwa ena, kupuma pantchito kumadzetsa mkhalidwe wosiyana wa moyo.

      2 Kunena zoona, zaka zaukalamba zingakhaledi zovuta. (Mlaliki 12:1-8) Komabe, talingalirani za atumiki a Mulungu a m’nthaŵi za Baibulo. Ngakhale kuti pomalizira pake anamwalira, anapeza nzeru ndi luntha, zimene zinawapatsa chikhutiro chachikulu mu ukalamba wawo. (Genesis 25:8; 35:29; Yobu 12:12; 42:17) Kodi iwo anakhoza motani kufika paukalamba ali achimwemwe? Ndithudi, kunali mwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mapulinsipulo amene ife lerolino timawapeza m’Baibulo.—Salmo 119:105; 2 Timoteo 3:16, 17.

      3. Kodi Paulo anapereka uphungu wotani kwa amuna ndi akazi okalamba?

      3 M’kalata yake kwa Tito, mtumwi Paulo anapereka chitsogozo chabwino kwa aja amene akukalamba. Iye analemba kuti: “Okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro. Momwemonso akazi okalamba akhale nawo makhalidwe oyenera anthu oyera, osadyerekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma.” (Tito 2:2, 3) Kumvera mawu ameneŵa kungakuthandizeni kuyang’anizana ndi zovuta zaukalamba.

      ZOLOŴERANI PAMENE ANA AKUKAKHALA PAOKHA

      4, 5. Kodi makolo ambiri amamva motani pamene ana awo achoka panyumba, ndipo kodi ena amazoloŵera motani mkhalidwe watsopano?

      4 Kusintha kwa mathayo kumafuna kuzoloŵera. Zimenezi nzoona chotani nanga pamene ana achikulire achoka panyumba ndi kukwatira kapena kukwatiwa! Kwa makolo ambiri chimenechi chimakhala chizindikiro choyamba chakuti akukalamba. Ngakhale kuti amakondwera poona kuti ana awo akula, kaŵirikaŵiri makolo amada nkhaŵa kuti kaya anachita zonse zimene akanakhoza kukonzekeretsa ana kukadzikhalira okha. Ndiponso angalakalake kukhala nawo pafupi.

      5 Zoona, makolo amapitiriza kudera nkhaŵa za umoyo wa ana awo, ngakhale pambuyo pakuti ana achoka panyumba. Mayi wina anati: “Ndikanakonda kumalandira mauthenga kuchokera kwa iwo kaŵirikaŵiri, kuti ndidziŵe ngati ali bwino—zimenezo zikanandipatsa chimwemwe.” Tate wina akuti: “Pamene mwana wathu wamkazi anachoka panyumba, inali nthaŵi yovuta kwambiri. Panakhala kusoŵeka kwakukulu kwa munthu wina m’banja chifukwa chakuti nthaŵi zonse tinkachitira zinthu pamodzi.” Kodi makolo ameneŵa achita motani ndi kusakhalapo kwa ana awo? Nthaŵi zambiri, mwa kusamalira anthu ena ndi kuwathandiza.

      6. Kodi nchiyani chimene chimathandiza kusunga maunansi a banja m’malo ake oyenera?

      6 Pamene ana apita ku ukwati, mathayo a makolo amasintha. Genesis 2:24 imati: ‘Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.’ Kulemekeza mapulinsipulo aumulungu a umutu ndi dongosolo labwino kudzathandiza makolo kusunga zinthu m’malo ake oyenera.—1 Akorinto 11:3; 14:33, 40.

      7. Kodi tate wina anakulitsa maganizo abwino otani pamene ana ake aakazi anachoka panyumba atakwatiwa?

      7 Pamene ana aŵiri aakazi anakwatiwa ndi kuchoka panyumba, makolo awo anamva kutayikidwa m’moyo wawo. Poyamba, tateyo sanali kukondwera nawo akamwini akewo. Koma pamene analingalira pulinsipulo la umutu, anazindikira kuti tsopano amuna a ana ake aakaziwo anali ndi thayo la kusamalira mabanja awo. Motero, pamene ana ake aakaziwo anapempha uphungu kwa iye, anawafunsa zimene amuna awo anaganiza, ndiyeno anawachirikiza kwambiri. Akamwini akewo tsopano amamuona monga bwenzi ndipo amalandira mauphungu ake.

      8, 9. Kodi makolo ena achita motani kuti azoloŵere pamene ana awo akula ndi kukadzikhalira okha?

      8 Bwanji ngati okwatirana chatsopano alephera kuchita chimene makolo awo akulingalira kuti ndicho chabwino koposa, ngakhale kuti sichili chotsutsana ndi Malemba? Okwatirana ena amene ali ndi ana okwatira anati: “Nthaŵi zonse timawathandiza kuona lingaliro la Yehova, koma ngati sitigwirizana ndi chosankha chawo, timavomereza ndipo timawachirikiza ndi kuwalimbikitsa.”

      9 M’maiko ena ku Asia, amayi ena zimawakhalira zovuta kwambiri kuzoloŵera pamene ana awo aamuna akukadzikhalira okha. Komabe, ngati alemekeza dongosolo lachikristu ndi umutu, amaona kuti mikangano ndi azipongozi awo imachepa. Mkazi wina wachikristu amaona kuti kuchoka panyumba kwa ana ake aamuna kwakhala “koyamikirika kwambiri nthaŵi zonse.” Iye ali wokondwa kuona kukhoza kwawo kusamalira mabanja awo atsopano. Ndiponso, zimenezi zapeputsanso mtolo wa zakuthupi ndi wa m’maganizo umene iye ndi mwamuna wake ayenera kusenza pamene akukalamba.

      KULIMBITSA UKWATI WANU

      Chithunzi patsamba 166

      Pamene mukukalamba, limbitsaninso chikondi chanu kwa wina ndi mnzake

      10, 11. Kodi ndi uphungu wotani wa m’Malemba umene ungathandize anthu kupeŵa misampha ina ya msinkhu wapakati?

      10 Anthu amachita mosiyanasiyana pamene afika usinkhu wapakati. Amuna ena amavala mosiyana kuti ayese kuoneka achinyamata. Akazi ambiri amada nkhaŵa ndi masinthidwe amene amafika ndi nyengo yoleka kusamba. Mwachisoni, anthu ena amsinkhu wapakati amakwiyitsa anzawo a muukwati ndi kuwachititsa nsanje mwa kuseŵera ndi anyamata kapena atsikana. Komabe, amuna aumulungu okalamba ali “anzeru,” amapeŵa zikhumbo zosayenera. (1 Petro 4:7) Akazinso achikulire amayesa kusunga maukwati awo kaamba kokonda amuna awo ndi kufuna kukondweretsa Yehova.

      11 Mwa kuuziridwa, Mfumu Lamueli analemba chitamando cha “mkazi wangwiro” amene achitira mwamuna wake ‘zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.’ Mwamuna wachikristu sadzalephera kuyamikira mmene mkazi wake akuyesayesera kulimbana ndi zovutitsa mtima zilizonse zimene angakumane nazo m’zaka za msinkhu wapakati. Chikondi chake chidzamsonkhezera ‘kumtama.’—Miyambo 31:10, 12, 28.

      12. Kodi okwatirana angakalambirane motani mwachikondi?

      12 M’kati mwa zaka zakubala ana zotangwanitsa kwambiri, nonse aŵiri mungakhale mutaika pambali zofuna zaumwini kuti musamalire zofunika za ana anu. Pamene iwo achoka, ndi nthaŵi yakuti musumikenso maganizo onse pa moyo wanu wa ukwati. “Pamene ana anga aakazi anachoka panyumba,” akutero mwamuna wina, “tinayambanso kutomerana ndi mkazi wanga.” Mwamuna wina akuti: “Aliyense amasamalira thanzi la mnzake ndipo timakumbutsana kuchita maseŵero olimbitsa thupi.” Kuti asasungulumwe, iye ndi mkazi wake amachereza ena mumpingo. Inde, kusamalira ena kumadzetsa madalitso. Ndiponso, kumakondweretsa Yehova.—Afilipi 2:4; Ahebri 13:2, 16.

      13. Kodi kukhala womasuka ndi woona mtima kumathandiza mbali yanji pamene a muukwati akukalamba pamodzi?

      13 Musalole kuti kulankhulana kuduke pakati pa inu ndi mnzanu wa muukwati. Kambitsiranani moona mtima. (Miyambo 17:27) Mwamuna wina anati: “Timakulitsa kumvana mwa kusamalirana ndi kulingalirana.” Mkazi wake akuvomerezana naye, akumati: “Pamene takalambirana, timasangalala kumwera pamodzi tiyi, kucheza, ndi kuthandizana.” Kukhala kwanu womasuka ndi woona mtima kungathandize kulimbitsa ukwati wanu, kuupatsa nyonga imene idzalepheretsa ziukiro za Satana, wowononga maukwati.

      SANGALALANI NDI ADZUKULU ANU

      14. Mwachionekere, kodi ndi mbali yanji imene agogo ake aakazi a Timoteo anathandiza pakukula kwake monga Mkristu?

      14 Adzukulu ali “korona” wa okalamba. (Miyambo 17:6) Ubwenzi wa adzukulu ungakhale wosangalatsadi—waumoyo ndi wotsitsimula. Baibulo limatamanda Loisi, amene anali agogo, amene pamodzi ndi mwana wake wamkazi Yunike, anaphunzitsa chikhulupiriro chawo mdzukulu wake wakhanda Timoteo. Wachichepereyu anakula akumadziŵa kuti amake ndi agogo ake analemekeza choonadi cha Baibulo.—2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.

      15. Ponena za adzukulu, kodi ndi chithandizo chofunika chotani chimene agogo angapereke, koma kodi ayenera kupeŵanji?

      15 Iyi ndiyo mbali yofunika imene agogo angathandize kwambiri. Agogo inu, munaphunzitsa kale ana anu chidziŵitso chanu cha zifuno za Yehova. Tsopano mukhoza kuchita chimodzimodzi kwa mbadwo winawo! Ana aang’ono ambiri amakondwera kumvetsera pamene agogo awo akusimba nkhani za m’Baibulo. Simukulanda thayo la atate ayi, la kuphunzitsa choonadi cha Baibulo kwa ana awo. (Deuteronomo 6:7) M’malo mwake, mumathandizira. Pemphero lanu likhale lija la wamasalmo lakuti: “Pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m’mbuyo.”—Salmo 71:18; 78:5, 6.

      16. Kodi agogo angapeŵe motani kuchititsa kusamvana m’banja mwawo?

      16 Mwachisoni, agogo ena amapusika kwambiri adzukulu kwakuti pamakhala kusamvana pakati pa agogo ndi ana awo. Komabe, kukoma mtima kwanu kungachititse adzukulu anu kusapeza vuto kuulula kwa inu nkhani zimene alephera kuulula kwa makolo awo. Nthaŵi zina achichepere amafuna kuti agogo awo amene amamvana nawo akhale kumbali kwawo motsutsana ndi makolo awo. Bwanji pamenepo? Gwiritsirani ntchito nzeru ndi kulimbikitsa adzukulu anu kukhala omasuka kwa makolo awo. Mungafotokoze kuti zimenezi zimakondweretsa Yehova. (Aefeso 6:1-3) Ngati kuli kofunika, mungatsegulire njira achicheperewo mwa kuyamba ndinu kulankhula ndi makolo awo. Khalani woona mtima kwa adzukulu anu pa zimene mwaphunzira kwa zaka zambiri. Kuona mtima kwanu kungawapindulitse.

      SINTHANI PAMENE MUKUKALAMBA

      17. Kodi Akristu okalamba ayenera kutsanzira kutsimikiza mtima kotani kwa wamasalmo?

      17 Pamene zaka zikupita, mudzaona kuti simuthanso kuchita zonse zimene munali kukhoza kapena zimene mungafune kuchita. Kodi munthu ayenera kuchita motani ndi ukalamba? M’maganizo mwanu mungaone monga muli ndi zaka 30 chabe, koma kuyang’ana m’kalirole kumaonetsa zosiyana ndi zimenezo. Musalefulidwe. Wamasalmo anachonderera Yehova kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” Tsanzirani kutsimikiza mtima kwa wamasalmo kwakuti: “Ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzawonjeza kukulemekezani.”—Salmo 71:9, 14.

      18. Kodi Mkristu wokalamba angagwiritsire ntchito bwino motani nthaŵi yake atapuma pantchito?

      18 Ambiri akonzekera pasadakhale kuwonjezera chitamando chawo kwa Yehova atapuma pantchito. “Ndinakonzekera pasadakhale zimene ndidzachita pamene mwana wanga wamkazi amaliza sukulu,” anafotokoza motero tate wina amene tsopano anapuma pantchito. “Ndinatsimikiza mtima kuti ndidzayamba utumiki wolalikira wa nthaŵi zonse, ndipo ndinagulitsa bizinesi yanga kuti ndimasuke ndi kutumikira Yehova mokwanira. Ndinapempherera chitsogozo cha Mulungu.” Ngati mukuyandikira zaka zakupuma pantchito, pezani chitonthozo pa chilengezo cha Mlengi wathu Wamkulu chakuti: “Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, ine ndidzakusenzani inu.”—Yesaya 46:4.

      19. Kodi ndi uphungu wotani umene waperekedwa kwa awo amene akukalamba?

      19 Kupuma pantchito kungakhale kovuta kukuzoloŵera. Mtumwi Paulo analangiza amuna okalamba kukhala “odzisunga.” Zimenezi zimafuna kudziletsa pa zinthu, osagonja pachikhumbo cha kufuna moyo wofeŵa. Pangakhale kufunika kokulirapo kwa kukhala ndi dongosolo ndi kudziyang’anira pamene mwapuma pantchito kuposa ndi kale lonse. Motero, khalani wokangalika, mwa “kuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Wonjezerani zochita zanu ndi kumathandiza ena. (2 Akorinto 6:13) Akristu ambiri amachita zimenezi mwa kulalikira mokangalika uthenga wabwino malinga ndi nyonga yawo. Pamene mukukalamba, khalani “olama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro.”—Tito 2:2.

      MMENE MUNGACHITIRE PAMENE MWATAYA MNZANU WA MUUKWATI

      20, 21. (a) M’dongosolo lino la zinthu, kodi nchiyani chimene potsirizira pake chimalekanitsa okwatirana? (b) Kodi Anna akupereka chitsanzo chabwino chotani kwa ofedwa anzawo a muukwati?

      20 Nzomvetsa chisoni komanso zoona kuti m’dongosolo lino la zinthu, anthu okwatirana potsirizira pake amalekanitsidwa ndi imfa. Akristu ofedwa mnzawo wa muukwati amadziŵa kuti okondedwa awowo akugona tsopano, ndipo ali ndi chidaliro chakuti adzawaonanso. (Yohane 11:11, 25) Koma kutayikako kumamvetsabe chisoni. Kodi wotsalayo angachite motani?a

      21 Kukumbukira zimene munthu wina wotchulidwa m’Baibulo anachita kungakhale kothandiza. Anna anafedwa mwamuna wake patangopita zaka zisanu ndi ziŵiri za ukwati wawo, ndipo pamene tiŵerenga za iye, anali ndi zaka 84 zakubadwa. Ndithudi, iye anagwidwa ndi chisoni pamene anataya mwamuna wake. Kodi anapirira motani? Anapereka utumiki wopatulika kwa Yehova Mulungu pakachisi usana ndi usiku. (Luka 2:36-38) Moyo wa Anna wa utumiki wa mapemphero mosakayikira unali mankhwala amphamvu pa chisoni chake ndi kusungulumwa kwake monga mkazi wamasiye.

      22. Kodi akazi amasiye ena ndi amuna ofedwa akazi awo achita motani ndi kusungulumwa?

      22 “Vuto lalikulu koposa kwa ine lakhala kusoŵa mnzanga wolankhula naye,” akutero mkazi wina wokalamba wazaka 72 amene anafedwa mwamuna wake zaka khumi zapitazo. “Mwamuna wanga anali mmvetseri wabwino. Tinkakambitsirana za mpingo ndi ntchito yathu ya utumiki wachikristu.” Mkazi wina wamasiye akuti: “Ngakhale kuti nthaŵi imachiritsa, ndaona kukhala kolondola kwambiri kunena kuti zimene munthu amachita nayo nthaŵi ndizo zimathandiza kuchira. Umakhala wokhoza kuthandiza ena.” Mwamuna wina wazaka 67 wofedwa mkazi wake akuvomereza zimenezo, akumati: “Njira yabwino koposa yochitira ndi kufedwa ndiyo kudzipereka pa kutonthoza ena.”

      KUŴERENGEREDWA NDI MULUNGU PAUKALAMBA

      23, 24. Kodi Baibulo limapereka chitonthozo chachikulu chotani kwa okalamba, makamaka aja ofedwa anzawo a muukwati?

      23 Ngakhale kuti imfa imatenga bwenzi la muukwati, Yehova amakhalabe wokhulupirika, wonena zoona nthaŵi zonse. “Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova,” inaimba motero Mfumu yakaleyo Davide, “ndidzachilondola ichi: Kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’kachisi wake.”—Salmo 27:4.

      24 “Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu,” akulangiza motero mtumwi Paulo. (1 Timoteo 5:3) Uphungu umene ukutsatira chilangizo chimenechi umasonyeza kuti akazi amasiye oyenerera opanda achibale apafupi angapatsidwe chichirikizo cha zinthu zakuthupi ndi mpingo. Komabe, lingaliro la chilangizo chakuti “chitira ulemu” limaphatikizapo kuwaŵerengera. Nchitonthozo chotani nanga chimene akazi amasiye aumulungu ndi amuna ofedwa akazi awo angachipeze mwa kudziŵa kuti Yehova amawaŵerengera ndi kuti adzawachirikiza!—Yakobo 1:27.

      25. Kodi ndi chonulirapo chotani chimene chidakalipo kwa okalamba?

      25 “Kukongola kwa nkhalamba ndi imvi,” amatero Mawu ouziridwa a Mulungu. “Ndiyo korona wa ulemu, [pamene, NW] idzapezedwa m’njira ya chilungamo.” (Miyambo 16:31; 20:29) Chotero, pitirizani kuika utumiki wa Yehova patsogolo m’moyo wanu, kaya muli muukwati, kapena mwatsalanso nokha. Mukatero, mudzakhala ndi dzina labwino ndi Mulungu tsopano ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko lopanda zopweteka za ukalamba.—Salmo 37:3-5; Yesaya 65:20.

      a Kuti mumve zochuluka pankhaniyi, onani brosha lakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . OKWATIRANA PAMENE AKUKALAMBA?

      Adzukulu ali “korona” wa okalamba.—Miyambo 17:6.

      Ukalamba ungadzetse mwaŵi wowonjezereka wa kutumikira Yehova.—Salmo 71:9, 14.

      Okalamba akulimbikitsidwa kukhala “odzisunga.”—Tito 2:2.

      Ngakhale kuti ofedwa anzawo a muukwati angavutike ndi chisoni, akhoza kupeza chitonthozo m’Baibulo.—Yohane 11:11, 25.

      Yehova amaŵerengera okalamba okhulupirika.—Miyambo 16:31.

  • Kulemekeza Makolo Athu Okalamba
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 15

      Kulemekeza Makolo Athu Okalamba

      1. Kodi tili ndi mangawa otani kwa makolo athu, motero tiyenera kuwaona motani ndi kuwachitira motani?

      “TAMVERA atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba,” anatero mwamuna wanzeru wakale. (Miyambo 23:22) ‘Sindingayese kuchita zimenezo!’ inuyo mungatero. M’malo mwa kupeputsa amayi athu—kapena atate athu—ambirife timawakonda kwambiri. Timadziŵa kuti tili ndi mangawa aakulu kwa iwo. Choyamba, makolo athu anatipatsa moyo. Pamene kuli kwakuti Yehova ndiye Kasupe wa moyo, popanda makolo athu sitikanakhalapo. Palibe chinthu chimene tingapatse makolo athu cha mtengo wapatali wofanana ndi moyo. Pamenepo, tangolingalirani za kudzimana, nkhaŵa ya kusamalira, ndalama zotayidwa, ndi chisamaliro chachikondi chimene kukulitsa mwana kumafuna. Chotero, nkoyenera chotani nanga, pamene Mawu a Mulungu amatilangiza kuti: “Lemekeza atate wako ndi amako . . . kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko”!—Aefeso 6:2, 3.

      KUZINDIKIRA ZOKHUMBA MTIMA WAWO

      2. Kodi ana aakulu ‘angabwezere’ motani makolo awo?

      2 Mtumwi Paulo analembera Akristu kuti: “Ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala [ndi agogo awo, NW]; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” (1 Timoteo 5:4) Ana aakulu ‘amabwezera’ mwa kusonyeza chiyamikiro kaamba ka zaka zambiri za chikondi chawo, ntchito, ndi chisamaliro zimene makolo awo ndi agogo awo anapereka pa iwo. Njira imodzi imene ana angachitire zimenezi ndiyo mwa kuzindikira kuti mofanana ndi munthu wina aliyense, okalamba amafuna kukondedwa ndi kulimbikitsidwa—kaŵirikaŵiri amazilakalaka kwambiri zimenezo. Mofanana ndi tonsefe, iwo amafuna kuona kuti akuŵerengeredwa. Amafuna kuona kuti moyo wawo uli wofunika.

      3. Kodi tingalemekeze motani makolo ndi agogo athu?

      3 Motero, tingalemekeze makolo athu ndi agogo athu mwa kuwachititsa kudziŵa kuti timawakonda. (1 Akorinto 16:14) Ngati makolo athu sakukhala nafe, tiyenera kukumbukira kuti pamene iwo alandira mawu kuchokera kwa ife, amalimbikitsidwa kwambiri. Kalata yabwino, foni, kapena kuwachezera zingawapatse chimwemwe chachikulu. Miyo, amene akukhala ku Japan, pamene anali ndi zaka 82 zakubadwa analemba kuti: “Mwana wanga wamkazi [amene mwamuna wake ndi mtumiki woyendayenda] amandiuza kuti: ‘Mayi, chonde “yendani” nafe paulendo.’ Amanditumizira ndandanda ya kucheza kwawo ndi nambala ya foni mlungu uliwonse. Ndimatsegula mapu anga ndi kunena kuti: ‘Eya. Tsopano ali apa!’ Ndimayamikira Yehova nthaŵi zonse pondidalitsa ndi mwana wotere.”

      KUTHANDIZA NDI ZOSOŴA ZAKUTHUPI

      4. Kodi mwambo wachipembedzo chachiyuda unaphunzitsa motani anthu kuumira mtima makolo awo okalamba?

      4 Kodi kulemekeza makolo kungaphatikizeponso kusamalira zosoŵa zawo zakuthupi? Inde. Kaŵirikaŵiri kumatero. M’tsiku la Yesu atsogoleri achipembedzo achiyuda anali ndi mwambo wakuti ngati munthu walengeza kuti ndalama zake kapena katundu wake anali “choperekedwa kwa Mulungu,” iye anali womasuka pa thayo la kuchigwiritsira ntchito kusamalira makolo ake. (Mateyu 15:3-6) Nkuuma mtima kotani nanga! Kwenikweni, atsogoleri achipembedzo amenewo anali kulimbikitsa anthu kusalemekeza makolo awo koma kuwapeputsa mwa kuwamana zosoŵa zawo mwadyera. Sitikufuna konse kuchita zimenezo!—Deuteronomo 27:16.

      5. Mosasamala kanthu za thandizo loperekedwa ndi boma m’maiko ena, kodi nchifukwa ninji kulemekeza makolo nthaŵi zina kumaphatikizapo thandizo la ndalama?

      5 M’maiko ambiri lerolino, maprogramu ochirikizidwa ndi boma amapereka thandizo la zinthu zina zakuthupi kwa okalamba, monga chakudya, zovala, ndi nyumba. Kuwonjezera pa zimenezo, okalamba angakhale atasungiratu chuma chowathandiza paukalamba wawo. Koma ngati chumacho chitha kapena ngati chichepa, ana amalemekeza makolo awo mwa kuchita zimene angathe kuti apezere makolo zosoŵa zawo. Kwenikweni, kusamalira makolo okalamba kuli umboni wa kudzipereka kwaumulungu, ndiko kuti, kudzipereka kwa munthu kwa Yehova Mulungu, Woyambitsa kakonzedwe ka banja.

      CHIKONDI NDI KUDZIMANA

      6. Kodi ena apanga makonzedwe otani a kakhalidwe kotero kuti asamalire zosoŵa za makolo awo?

      6 Ana aakulu ambiri athandiza pa zosoŵa za makolo awo okalamba mwa chikondi ndi kudzimana. Ena atenga makolo awo ndi kukhala nawo panyumba pawo kapena kusamuka kukakhala pafupi nawo. Ena asamuka kukakhala pamodzi ndi makolo awo. Kaŵirikaŵiri, makonzedwe oterowo akhala dalitso kwa makolo ndi ana omwe.

      7. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kusachita mofulumira popanga zosankha zokhudza makolo okalamba?

      7 Komabe, nthaŵi zina zimenezo sizimayenda bwino. Chifukwa ninji? Mwinamwake chifukwa chakuti zosankha zapangidwa mofulumira kapena zangosonkhezeredwa ndi kukhudzidwa mtima. “Wochenjera asamalira mayendedwe ake,” limachenjeza mwanzeru Baibulo. (Miyambo 14:15) Mwachitsanzo, tinene kuti amayi anu okalamba akupeza vuto kukhala okha ndipo muganiza kuti kungakhale kothandiza kudzakhala nawo. Posamalira mayendedwe anu mochenjera, mungapende mfundo izi: Kodi zosoŵa zawo zenizeni nzotani? Kodi pali makonzedwe alionse a anthu kapena aboma amene angakhale njira ina yoperekera chithandizo? Kodi iwo akufuna kusamuka? Ngati akutero, kodi moyo wawo udzakhudzidwa motani? Kodi adzasiya mabwenzi? Kodi zimenezi zidzakhudza motani maganizo awo? Kodi mwakambitsirana nawo zinthu zimenezi? Kodi kuchita zimenezo kungayambukire motani inuyo, mnzanu wa muukwati, kapena ana anu? Ngati amayi anu amafunikira chisamaliro, kodi adzachipereka ndani? Kodi mungagaŵane thayo limenelo? Kodi mwakambitsirana nkhaniyo mwachindunji ndi ena oloŵetsedwamo?

      8. Kodi mungafunsire kwa yani pamene mufuna kudziŵa mmene mungathandizire makolo anu okalamba?

      8 Popeza kuti thayo la kusamalira makolo lili pa ana onse m’banja, kungakhale kwanzeru kukhala ndi msonkhano wa banja kotero kuti onse akhale ndi mbali pakupanga zosankha. Kukambitsirana ndi akulu mumpingo wachikristu kapena ndi mabwenzi amene anakumanapo ndi vuto limenelo kungakhalenso kothandiza. “Zolingalira zizimidwa popanda upo,” limachenjeza motero Baibulo, “koma pochuluka aphungu zikhazikika.”—Miyambo 15:22.

      KHALANI WACHIFUNDO NDI WOMVETSETSA

      Chithunzi patsamba 179

      Si bwino kupangira kholo chosankha popanda kulankhula nalo choyamba

      9, 10. (a) Mosasamala kanthu za ukalamba wawo, kodi tiyenera kukumbukiranji za iwo? (b) Mosasamala kanthu za zimene mwana angachitire makolo ake, kodi ayenera kuwapatsanji nthaŵi zonse?

      9 Kulemekeza makolo athu okalamba kumafuna chifundo ndi kuwamvetsetsa. Pamene achikulire afika m’zaka zaukalamba weniweni, angayambe kupeza vuto kwambiri pakuyenda, kudya, ndi kukumbukira zinthu. Angafunikire chithandizo. Kaŵirikaŵiri, ana amafuna kuwatetezera ndipo amayesa kupereka chithandizo. Koma okalambawo ali achikulire okhala ndi nzeru za zaka zambiri ndi chidziŵitso, adzisamalira okha kwa zaka zonsezo ndipo akhala akupanga zosankha zawo. Iwo akhala odziŵika ndipo apeza ulemu chifukwa cha ukholo wawo ndi uchikulire wawo. Makolo amene aona kuti tsopano thayo la kusamalira moyo wawo likutengedwa ndi ana awo angapsinjike maganizo ndi kukhala okwiya. Ena amaipidwa ndi kukana zoyesayesa zimene angaone kuti zikuwalanda ufulu wawo.

      10 Palibe njira zofeŵa zothetsera mavuto oterowo, koma kumakhala kukoma mtima ngati tilola makolo okalamba kudzisamalira okha ndi kupanga zosankha zawo zimene angakhoze. Kuli kwanzeru kusasankhira zinthu makolo anu popanda kulankhula nawo choyamba. Ukalamba wawalanda zambiri. Athandizeni kusunga zimene akali nazo. Mungapeze kuti pamene simukulamulira kwambiri moyo wa makolo anu, mpamenenso unansi wanu umakhala bwino kwambiri. Adzakhala achimwemwe mokulirapo, inunso mudzatero. Ngakhale ngati kuli kofunika kuumirira pa zinthu zina kaamba ka ubwino wawo, kulemekeza makolo anu kumafuna kuti muwaope ndi kuwapatsa ulemu wowayenera. Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.”—Levitiko 19:32.

      KHALANI NDI MAGANIZO ABWINO

      11-13. Ngati unansi wa mwana wachikulire ndi makolo ake sunali bwino kumbuyoku, kodi mwanayo angachitebe motani ntchito yowasamalira m’zaka zawo zaukalamba?

      11 Nthaŵi zina vuto limene ana aakulu amakumana nalo pakulemekeza makolo awo okalamba limaphatikizapo unansi umene anali nawo ndi makolo awo nthaŵi zakumbuyo. Mwinamwake atate anu analibe chifundo ndi chikondi, amayi anu mwina anali olamulira ndi aukali. Mwina mukali wokhumudwa, wokwiya, kapena wopwetekedwa mtima chifukwa sanakhale makolo amene munafuna kuti akhale. Kodi mungagonjetse maganizo otero?a

      12 Basse, amene anakulira ku Finland, akusimba kuti: “Atate anga opeza anali aofesala a SS m’Germany wa Nazi. Iwo anali kutaya mtima mwamsanga, ndipo anali owopsa. Anali kumenya amayi nthaŵi zambiri pamaso panga. Tsiku lina pamene anakwiya nane, anandikwapula ndi lamba lawo ndipo chitsulo chake chinandikantha kunkhope. Chinandikantha kwambiri kwakuti ndinagwera pa mbedi.”

      13 Komabe, analinso ndi mkhalidwe wina. Basse akuwonjezera kuti: “Ngakhale ndi choncho, iwo anagwira ntchito zolimba ndipo sanaleke kusamalira zofunika za banja. Sanandisonyeze chikondi cha tate, koma ndinadziŵa kuti anali osweka mtima. Amayi awo anawapitikitsa panyumba pamene anali mnyamata wamng’ono. Kukula kwawo kunali komenyana ndi anthu nthaŵi zonse, ndipo anapita kunkhondo akali achichepere. Pamlingo wina wake ndinadziŵa chifukwa chake ndipo sindinawapatse mlandu. Pamene ndinakula, ndinafuna kuwathandiza kwambiri kufikira imfa yawo. Zinali zovuta, koma ndinachita zimene ndinakhoza. Ndinayesa kukhala mwana wabwino kufikira imfa yawo, ndipo ndikhulupirira kuti anakhutira kuti ndinali wotero.”

      14. Kodi ndi lemba liti limene limagwira ntchito m’mikhalidwe yonse, kuphatikizapo imene imabuka posamalira makolo okalamba?

      14 M’mikhalidwe ya banja, mofanana ndi m’nkhani zina, uphungu wa Baibulo umagwira ntchito: “Valani, . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso [Yehova, NW] anakhululukira inu, teroni inunso.”—Akolose 3:12, 13.

      OSAMALIRA NAWONSO AMAFUNA KUSAMALIRIDWA

      15. Kodi nchifukwa ninji kusamalira makolo nthaŵi zina kumakhala kosautsa maganizo?

      15 Kusamalira kholo lokalamba ndi ntchito yaikulu, yoloŵetsamo zochita zambiri, thayo lalikulu, ndi maola ochuluka. Koma mbali yovuta kwambiri ndiyo yokhudza maganizo. Kumavutitsa maganizo kuona makolo anu akutaya thanzi lawo, kuiŵala, ndi kulephera kudziimira paokha. Sandy, wa ku Puerto Rico, akusimba kuti: “Amayi anga ndiwo anali nkhaŵa yaikulu pabanja. Kunali kopweteka kwambiri kumawasamalira. Anayamba ndi kutsimphina, kenako anafunikira ndodo, walker [chothandiza kuyenda] ndiyeno mpando wa magudumu. Pambuyo pake, matenda anakulirakulira kufikira anamwalira. Anadwala kansa ya m’mafupa ndipo anafunikira chisamaliro cha nthaŵi zonse—usana ndi usiku. Tinawasambitsa ndi kuwadyetsa ndi kuwaŵerengera. Zinali zovuta kwambiri—makamaka m’maganizo. Pamene ndinaona kuti amayi anali kumwalira, ndinalira chifukwa ndinawakonda kwambiri.”

      16, 17. Kodi ndi uphungu wotani umene ungathandize wopereka chisamaliro kukhala ndi kaonedwe kabwino ka zinthu?

      16 Ngati mukhala mumkhalidwe umodzimodziwo, kodi mungachitenji kuti mulimbane nazo? Kumvetsera Yehova mwa kuŵerenga Baibulo ndi kulankhula naye m’pemphero kungakuthandizeni kwambiri. (Afilipi 4:6, 7) Mwa njira yothandiza, yesani kudya zakudya zopatsa thanzi ndi kupeza tulo tokwanira. Mwa kuchita zimenezi, mudzakhala mumkhalidwe wabwino, ponse paŵiri m’maganizo ndi kuthupi, kuti musamalire wokondedwa wanu. Mwinamwake mungapange makonzedwe a kupumulako pa umoyo wa masiku onse. Ngakhale ngati kutenga tchuthi nkosatheka, kumakhalabe kwanzeru kupatula nthaŵi ya kupumula. Kuti mupezeko nthaŵi, mungamvane ndi wina kuti akhaleko ndi kholo lanu lodwalalo.

      17 Sikwachilendo kwa opereka chisamaliro achikulire kuona monga zimene akuchita sizokwanira. Koma musadzimve waliwongo posachita zimene simungathe. M’mikhalidwe ina mungafunikire kupereka wokondedwa wanuyo kunyumba yosamalira okalamba. Ngati ndinu wopereka chisamaliro, ikani zonulirapo zotheka. Muyenera kulingalira bwino zofunika, osati za makolo anu zokha, komanso za ana anu, za mnzanu wa muukwati, ndi zanu.

      NYONGA YOPOSA YACHIBADWA

      18, 19. Kodi Yehova wapereka lonjezo lotani la chichirikizo, ndipo nchochitika chiti chimene chimasonyeza kuti amasunga lonjezo limeneli?

      18 Kupyolera m’Mawu ake Baibulo, Yehova wapereka mwachikondi chitsogozo chimene chingathandize kwambiri munthu wosamalira makolo okalamba, koma chimenecho sindicho chithandizo chokha chimene amapereka. “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa iye,” analemba motero wamasalmo mwa kuuziridwa. “Nadzamva kufuula kwawo, nadzawapulumutsa.” Yehova adzapulumutsa, kapena kulanditsa, okhulupirika ake ngakhale m’mikhalidwe yovuta kwenikweni.—Salmo 145:18, 19.

      19 Myrna, ku Philippines, anadziŵa zimenezi pamene anali kusamalira amake, amene anapuŵala ndi stroko. “Palibe chinthu chovutitsa maganizo kwambiri monga kuona wokondedwa wako akuvutika, wosakhoza kukuuzani chimene chikupweteka,” analemba motero Myrna. “Zinali monga kuwaona akumira pang’onopang’ono, popanda zimene ndikanachita. Nthaŵi zambiri ndinkagwada ndi kupemphera kwa Yehova ponena za kutopa nazo kwanga. Ndinalira monga Davide, amene anachonderera Yehova kuti asunge misozi yake m’nsupa ndi kumkumbukira. [Salmo 56:8] Ndipo monga momwe Yehova analonjezera, anandipatsa nyonga imene ndinafunikira. ‘Yehova anali mchirikizo wanga.’”—Salmo 18:18.

      20. Kodi ndi malonjezo a Baibulo otani amene amathandiza awo opereka chisamaliro kukhala achidaliro, ngakhale ngati uyo amene akumsamalira amwalira?

      20 Ena amati kusamalira makolo okalamba kuli monga “nkhani ya mapeto achisoni.” Mosasamala kanthu za kuyesayesa kuwasamalira mwakhama, okalamba amamwalirabe, monga momwe anachitira amake Myrna. Koma awo okhulupirira Yehova amadziŵa kuti imfa sindiyo mapeto a nkhani. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndikukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Awo amene ataya makolo awo okalamba mu imfa amapeza chitonthozo m’chiyembekezo cha chiukiriro limodzi ndi lonjezo la dziko latsopano losangalatsa lopangidwa ndi Mulungu mmene ‘simudzakhalanso imfa.’—Chivumbulutso 21:4.

      21. Kodi kulemekeza okalamba kumakhala ndi zotulukapo zabwino zotani?

      21 Atumiki a Mulungu amalemekeza kwambiri makolo awo, ngakhale kuti iwoŵa angakhale atakalamba. (Miyambo 23:22-24) Amawapatsa ulemu. Mwa kutero, amaona zimene mwambi wouziridwa umanena kuti: “Atate wako ndi amako akondwere, amako wakukubala asekere.” (Miyambo 23:25) Ndipo choposa zonse, awo amene amalemekeza makolo awo okalamba amakodweretsa ndi kulemekezanso Yehova Mulungu.

      a Pano sitikunena za makolo amene anachitira nkhanza ana awo zimene zinachititsa anawo kutaya chidaliro chawo mwa iwo, zimene zingaonedwe kukhala mlandu.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATITHANDIZE MOTANI . . . KULEMEKEZA MAKOLO ATHU OKALAMBA?

      Tiyenera kubwezera makolo ndi agogo athu.—1 Timoteo 5:4.

      Zinthu zathu zonse ziyenera kuchitika mwa chikondi.—1 Akorinto 16:14.

      Zosankha zazikulu siziyenera kupangidwa mofulumira.—Miyambo 14:15.

      Ngakhale ngati makolo okalamba angakhale odwalira ndi ofooka, ayenera kulemekezedwa.—Levitiko 19:32.

      Chiyembekezo cha kukalamba ndi kumwalira sitidzakhala nacho kwamuyaya.—Chivumbulutso 21:4.

  • Mangirani Banja Lanu Mtsogolo Mokhalitsa
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 16

      Mangirani Banja Lanu Mtsogolo Mokhalitsa

      1. Kodi chifuno cha Yehova chinali chotani pa kakonzedwe ka banja?

      PAMENE Yehova anakwatitsa Adamu ndi Hava, Adamu anasonyeza chisangalalo chake mwa kulakatula ndakatulo yachihebri yoyambirira kulembedwa. (Genesis 2:22, 23) Komabe, Mlengi anali ndi zochuluka m’maganizo kuposa kudzetsa chabe chimwemwe kwa ana ake aumunthu. Iye anafuna kuti anthu okwatirana ndiponso mabanja achite chifuniro chake. Anauza okwatirana oyambawo kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.” (Genesis 1:28) Imeneyo inali ntchito yaulemerero ndi yofupa kwambiri! Ndipo iwo pamodzi ndi ana awo amtsogolo akanakhala achimwemwe kwabasi, ngati Adamu ndi Hava akanachita chifuniro cha Yehova mwa kumvera konse!

      2, 3. Kodi ndi motani mmene mabanja angapezere chimwemwe chachikulu koposa lerolino?

      2 Lerolinonso, mabanja amakhala achimwemwe pamene achitira pamodzi chifuniro cha Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chipembedzo [“kudzipereka kwaumulungu,” NW] chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Banja lokhala ndi kudzipereka kwaumulungu limenenso limatsatira chitsogozo cha Yehova chopezeka m’Baibulo lidzapeza chimwemwe mu “moyo uno.” (Salmo 1:1-3; 119:105; 2 Timoteo 3:16) Ngakhale ngati mmodzi yekha m’banja ndiye amagwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo, zinthu zimakhalapo bwino kuposa ngati palibe amene amatero.

      3 Buku lino lafotokoza mapulinsipulo ambiri a Baibulo amene amathandiza kupeza chimwemwe cha banja. Mwachionekere, mwaona kuti ena a iwo aonekera mobwerezabwereza m’buku lonseli. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amanena za mfundo zamphamvu za choonadi zimene zimagwira ntchito kaamba ka ubwino wa onse m’mbali zosiyanasiyana za moyo wa banja. Banja limene limayesayesa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo ameneŵa limapeza kuti kudzipereka kwaumulungu kulidi ndi “lonjezano la ku moyo uno.” Tiyeni tionenso anayi a mapulinsipulo ofunika amenewo.

      PHINDU LA KUDZILETSA

      4. Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kuli kofunika muukwati?

      4 Mfumu Solomo anati: “Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga.” (Miyambo 25:28; 29:11) ‘Kulamulira mtima,’ kudziletsa, nkofunika kwambiri kwa amene akufuna ukwati wachimwemwe. Kugonja ku maganizo owononga, onga ukali kapena chilakolako chachisembwere, kudzawononga zinthu zimene zidzatenga zaka zambiri kukonza—ngati zingakonzedwe nkomwe.

      5. Kodi munthu wopanda ungwiro angakulitse motani kudziletsa, ndipo pali mapindu otani?

      5 Ndithudi, palibe aliyense amene ali mbadwa ya Adamu amene angakhoze kulamulira kotheratu thupi lake lopanda ungwiro. (Aroma 7:21, 22) Komabe, kudziletsa ndiko chipatso cha mzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Chifukwa chake, mzimu wa Mulungu udzabala chipatso cha kudziletsa mwa ife ngati tipempherera mkhalidwe umenewu, ngati tigwiritsira ntchito uphungu woyenera wopezeka m’Malemba, ndipo ngati tiyanjana ndi ena amene amausonyeza ndi kupeŵa awo amene samatero. (Salmo 119:100, 101, 130; Miyambo 13:20; 1 Petro 4:7) Kachitidwe kameneko kadzatithandiza ‘kuthaŵa dama,’ ngakhale pamene tiyesedwa. (1 Akorinto 6:18) Tidzakana chiwawa ndi kupeŵa kapena kugonjetsa uchidakwa. Ndipo tidzakhala odekha pamene tiputidwa ndi pochita ndi mikhalidwe yovuta. Tiyeni tonsefe—kuphatikizapo ana—tikulitse chipatso cha mzimu chofunika chimenechi.—Salmo 119:1, 2.

      LINGALIRO LOYENERA LA UMUTU

      6. (a) Kodi makonzedwe okhazikitsidwa ndi Mulungu a umutu ali otani? (b) Kodi mwamuna ayenera kukumbukira chiyani kuti umutu wake ubweretse chimwemwe pabanja?

      6 Pulinsipulo lofunika lachiŵiri ndilo kuzindikira umutu. Paulo anafotokoza kakonzedwe koyenera ka zinthu pamene anati: “Ndifuna kuti mudziŵe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Zimenezi zimatanthauza kuti mwamuna amatsogolera m’banja, mkazi wake amakhala wochirikiza wokhulupirika, ndipo ana amamvera makolo awo. (Aefeso 5:22-25, 28-33; 6:1-4) Komabe, dziŵani kuti umutu umadzetsa chimwemwe kokha pamene uchitidwa mwa njira yoyenera. Amuna amene amatsatira kudzipereka kwaumulungu amadziŵa kuti umutu sikupondereza wina. Iwo amatsanzira Yesu, Mutu wawo. Ngakhale kuti Yesu anali kudzakhala “mutu pamtu pa zonse,” iye “sanadza kutumikiridwa koma kutumikira.” (Aefeso 1:22; Mateyu 20:28) Mwamuna wachikristu amachita umutu wake mwa njira imodzimodziyo, osati modzipindulitsa iye yekha, koma kusamalira zofunika za mkazi wake ndi ana ake.—1 Akorinto 13:4, 5.

      7. Kodi ndi mapulinsipulo otani a m’Malemba amene adzathandiza mkazi kukwaniritsa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu m’banja?

      7 Mkazi wotsatira kudzipereka kwaumulungu samapikisana kapena kuyesa kulamulira mwamuna wake. Amakondwera kumchirikiza ndi kuthandizana naye. Nthaŵi zina Baibulo limanena mkazi kukhala “wa” mwamuna wake, likumamveketsa bwino kuti mwamuna ndiye mutu. (Genesis 20:3) Mwa ukwati mkazi amakhala pansi pa “lamulo kwa mwamuna wake.” (Aroma 7:2) Panthaŵi imodzimodzi, Baibulo limatcha mkazi “womthangatira.” (Genesis 2:20) Iye amapereka mikhalidwe ndi maluso amene mwamuna wake alibe, ndipo amampatsa chichirikizo chofunikira. (Miyambo 31:10-31) Baibulo limanenanso kuti mkazi ndi “mnzake,” wogwira naye ntchito wa mwamuna wake. (Malaki 2:14) Mapulinsipulo a m’Malemba ameneŵa amathandiza mwamuna ndi mkazi kumvetsetsa malo a wina ndi mnzake ndi kuchitirana ulemu woyenera.

      ‘KHALANI WOTCHERA KHUTU’

      8, 9. Longosolani mapulinsipulo ena amene adzathandiza onse m’banja kukulitsa maluso awo a kulankhulana.

      8 M’buku lino kufunika kwa kulankhulana kwagogomezeredwa kaŵirikaŵiri. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kuthetsa mavuto sikumakhala kovuta kwambiri pamene anthu akambitsirana ndi kumvetserana. Kwagogomezeredwa kaŵirikaŵiri kuti kulankhulana ndi kwa anthu aŵiri. Wophunzira Yakobo ananena motere: “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula.”—Yakobo 1:19.

      9 Nkofunikanso kusamala ndi mmene timalankhulira. Mawu aukali, amkangano, kapena osuliza kwambiri samapanga kulankhulana kwabwino. (Miyambo 15:1; 21:9; 29:11, 20) Ngakhale pamene zonena zathu zili zoona, ngati tizinena mwa njira yankhanza, monyada, kapena mosalingalira ena, zikhoza kupweteka ena m’malo mwa kuwathandiza. Mawu athu ayenera kukhala abwino, “okoleretsa.” (Akolose 4:6) Mawu athu ayenera kukhala ngati “zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.” (Miyambo 25:11) Mabanja amene amaphunzira kulankhulana bwino ali pafupi kwambiri kupeza chimwemwe.

      NTCHITO YAIKULU YA CHIKONDI

      10. Kodi ndi mtundu wotani wa chikondi umene uli wofunika koposa muukwati?

      10 Liwu lakuti “chikondi” likupezeka kambiri m’buku lonseli. Kodi mukukumbukira mtundu wa chikondi umene ukunenedwa kwenikweni? Nzoona kuti chikondi cha mwamuna ndi mkazi (Chigiriki, eʹros) nchofunika muukwati, ndipo m’maukwati achipambano, chikondano chozama ndi ubwenzi (Chigiriki, phi·liʹa) zimakula pakati pa mwamuna ndi mkazi. Koma chofunika koposa ndicho chikondi chotchedwa a·gaʹpe m’Chigiriki. Ichi ndicho chikondi chimene tiyenera kukhala nacho kwa Yehova, kwa Yesu, ndi kwa mnansi wathu. (Mateyu 22:37-39) Ndicho chikondi chimene Yehova amasonyeza kwa anthu onse. (Yohane 3:16) Nkwabwino chotani nanga kuti ifenso tikhoza kusonyeza chikondi chimodzimodzicho kwa anzathu a muukwati ndi ana athu!—1 Yohane 4:19.

      11. Kodi chikondi chimathandiza motani kukhala ndi ukwati wabwino?

      11 Muukwati chikondi cholemekezeka chimenechi chimakhaladi “chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:14) Chimamanga pamodzi aŵiri okwatirana ndi kuwachititsa kufuna kuchita zabwino koposa kwa wina ndi mnzake ndi kwa ana awo. Pamene mabanja akumana ndi mikhalidwe yovuta, chikondi chimawathandiza kusamalira zinthu mogwirizana. Pamene okwatirana akukula, chikondi chimawathandiza kuchirikizana ndi kupitiriza kumvetsetsana. “Chikondi . . . sichitsata za mwini yekha, . . . chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthaŵi zonse.”—1 Akorinto 13:4-8.

      12. Kodi nchifukwa ninji kukonda Mulungu kumachititsa okwatirana kulimbitsa ukwati wawo?

      12 Umodzi wa ukwati umakhala wolimba makamaka pamene umangidwa, osati ndi chikondi cha pakati pa okwatiranawo chokha, koma kwenikweni ndi chikondi chawo kwa Yehova. (Mlaliki 4:9-12) Chifukwa ninji? Chabwino, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.” (1 Yohane 5:3) Chotero, okwatirana ayenera kuphunzitsa ana awo kudzipereka kwaumulungu osati chabe chifukwa chakuti amakonda kwambiri ana awo koma chifukwa chakuti Yehova amalamula zimenezi. (Deuteronomo 6:6, 7) Ayenera kupeŵa chisembwere osati chabe chifukwa chakuti amakondana koma makamaka chifukwa amakonda Yehova, amene ‘adzaweruza adama ndi achigololo.’ (Ahebri 13:4) Ngakhale ngati wina wa okwatirana achititsa mavuto aakulu muukwati, chikondi cha pa Yehova chidzasonkhezera winayo kutsatirabe mapulinsipulo a Baibulo. Ndithudi, alidi achimwemwe mabanja amene chikondi chawo kwa wina ndi mnzake nchomangidwa ndi chikondi kwa Yehova!

      BANJA LIMENE LIMACHITA CHIFUNIRO CHA MULUNGU

      13. Kodi kukhala wofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu kudzathandiza motani anthu kusumika maso pa zinthu zofunika kwenikweni?

      13 Moyo wonse wa Mkristu wazikidwa pa kuchita chifuniro cha Mulungu. (Salmo 143:10) Ichi nchimene kudzipereka kwaumulungu kumatanthauza kwenikweni. Kuchita chifuniro cha Mulungu kumathandiza mabanja kusumika maso pa zinthu zofunika kwenikweni. (Afilipi 1:9, 10, NW) Mwachitsanzo, Yesu anachenjeza kuti: “Ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake: ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.” (Mateyu 10:35, 36) Mogwirizana ndi chenjezo la Yesu, otsatira ake ambiri azunzidwa ndi apabanja pawo enieniwo. Nzachisoni ndi zopweteka chotani nanga! Komabe, maunansi a banja sayenera kupambana chikondi chathu kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. (Mateyu 10:37-39) Ngati munthu apirira mosasamala kanthu za chitsutso cha banja, otsutsawo angasinthe pamene aona zipatso zabwino za kudzipereka kwaumulungu. (1 Akorinto 7:12-16; 1 Petro 3:1, 2) Ngakhale ngati zimenezo sizichitika, palibe ubwino wokhalitsa umene umapezeka mwa kuleka kutumikira Mulungu chifukwa cha chitsutso.

      14. Kodi chikhumbo cha kuchita chifuniro cha Mulungu chidzathandiza motani makolo kupindulitsa ana awo?

      14 Kuchita chifuniro cha Mulungu kumathandiza makolo kupanga zosankha zoyenera. Mwachitsanzo, m’malo ena anthu amakonda kuona ana monga chuma choikizira, ndipo amadalira ana awo kuti adzawasunge akakalamba. Pamene kuli kwakuti nkwabwino ndi koyenera kwa ana kusamalira makolo awo okalamba, malingaliro amenewo sayenera kuchititsa makolo kulimbikitsa ana awo kukhala ndi moyo wokondetsa chuma. Makolo samathandiza ana awo ngati awaphunzitsa kukonda chuma kuposa zinthu zauzimu.—1 Timoteo 6:9.

      15. Kodi ndi motani mmene Yunike, amake Timoteo, analili chitsanzo chabwino koposa cha kholo limene linachita chifuniro cha Mulungu?

      15 Chitsanzo chabwino pa zimenezi ndicho cha Yunike, mayi wake wa Timoteo, bwenzi lachichepere la Paulo. (2 Timoteo 1:5) Ngakhale kuti iye anakwatiwa kwa munthu wosakhulupirira, Yunike, limodzi ndi Loisi, gogo wake wa Timoteo, anaphunzitsa bwino lomwe Timoteo kulondola kudzipereka kwaumulungu. (2 Timoteo 3:14, 15) Timoteo atakula, Yunike anamlola kuchoka panyumba ndi kuyamba ntchito yolalikira Ufumu monga mmishonale mnzake wa Paulo. (Machitidwe 16:1-5) Ayenera kukhala atakondwera chotani nanga kuona mwana wake akukhala mmishonale wokangalika! Kudzipereka kwake kwaumulungu monga munthu wachikulire kunasonyeza kuphunzitsidwa kwabwino kumene analandira paubwana. Ndithudi, Yunike anapeza chikhutiro ndi chisangalalo pakumva malipoti a utumiki wokhulupirika wa Timoteo, ngakhale kuti mwinamwake analakalaka kukhala naye pafupi.—Afilipi 2:19, 20.

      BANJA NDI MTSOGOLO MWANU

      16. Monga mwana, kodi ndi nkhaŵa yoyenera yotani imene Yesu anasonyeza, koma kodi cholinga chake chachikulu chinali chotani?

      16 Yesu analeredwa m’banja laumulungu, ndipo monga munthu wachikulire, anasonyeza nkhaŵa yoyenera ya mwana kwa amake. (Luka 2:51, 52; Yohane 19:26) Komabe, cholinga chachikulu cha Yesu chinali kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo kwa iye zimenezi zinaphatikizapo kutsegulira anthu njira ya ku moyo wosatha. Anachita zimenezi pamene anapereka moyo wake wangwiro waumunthu monga dipo kaamba ka anthu ochimwa.—Marko 10:45; Yohane 5:28, 29.

      17. Kodi ndi ziyembekezo zaulemerero zotani zimene njira ya moyo yokhulupirika ya Yesu inatsegulira awo ochita chifuniro cha Mulungu?

      17 Yesu atamwalira, Yehova anamuukitsira ku moyo wakumwamba ndi kumpatsa ulamuliro waukulu, potsirizira pake akumamukhazika monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba. (Mateyu 28:18; Aroma 14:9; Chivumbulutso 11:15) Nsembe ya Yesu inatheketsa anthu ena kusankhidwa kuti akalamulire pamodzi naye mu Ufumuwo. Inatseguliranso njira anthu onse owongoka mtima kudzasangalala ndi moyo wangwiro padziko lapansi lobwezeretsedwa ku mikhalidwe yaparadaiso. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 4; 21:3-5; 22:1-4) Umodzi wa mwaŵi waukulu koposa umene tili nawo lero ndiwo wa kulalikira uthenga wabwino waulemerero umenewu kwa anansi athu.—Mateyu 24:14.

      18. Kodi ndi chikumbutso ndi chilimbikitso chotani chimene chikuperekedwa ku mabanja ndi kwa anthu ena?

      18 Monga momwe mtumwi Paulo anasonyezera, kukhala ndi moyo wa kudzipereka kwaumulungu kuli ndi lonjezo lakuti anthu akhoza kupeza madalitso amenewo mu moyo “ulinkudza.” Ndithudi, imeneyi ndiyo njira yabwino koposa yopezera chimwemwe! Kumbukirani, “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17) Chifukwa chake, kaya ndinu mwana kapena kholo, mwamuna kapena mkazi, kapena ndinu wachikulire wosakwatira wokhala ndi ana kapena wopanda ana, yesetsani kuchita chifuniro cha Mulungu. Ngakhale pamene muli wopanikizika kapena kuyang’anizana ndi mavuto aakulu, musaiŵale kuti ndinu mtumiki wa Mulungu wamoyo. Motero, lolani kuti machitidwe anu akondweretse Yehova. (Miyambo 27:11) Ndipo lolani kuti mayendedwe anu akupatseni chimwemwe tsopano ndi moyo wosatha m’dziko latsopano likudzalo!

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . BANJA LANU KUKHALA LACHIMWEMWE?

      Tikhoza kukulitsa kudziletsa.—Agalatiya 5:22, 23.

      Ndi lingaliro loyenera la umutu, onse aŵiri mwamuna ndi mkazi amayesa kupezera banja zabwino koposa.—Aefeso 5:22-25, 28-33; 6:4.

      Kulankhulana kumaphatikizapo kutchera khutu.—Yakobo 1:19.

      Chikondi kwa Yehova chidzalimbitsa ukwati.—1 Yohane 5:3.

      Kuchita chifuniro cha Mulungu ndiko cholinga chachikulu cha banja.—Salmo 143:10; 1 Timoteo 4:8.

      MPHATSO YA UMBETA

      Si munthu aliyense amene amakwatira kapena kukwatiwa. Ndipo si okwatirana onse amene amasankha kukhala ndi ana. Yesu anali mbeta, ndipo ananena kuti umbeta ndi mphatso pamene ukhalapo “chifukwa cha Ufumu wakumwamba.” (Mateyu 19:11, 12) Mtumwi Paulonso anasankha kusakwatira. Ananena za umbeta ndi ukwati womwe kukhala “mphatso.” (1 Akorinto 7:7, 8, 25-28) Chifukwa chake, pamene kuli kwakuti buku lino lafotokoza kwambiri nkhani zokhudza ukwati ndi kulera ana, tisaiŵale za madalitso ndi mfupo zothekera za kukhala mbeta kapena kukwatira koma popanda ana.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena